Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g19 No. 2 tsamba 4-5
  • Kudziletsa N’kofunika Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudziletsa N’kofunika Kwambiri
  • Galamukani!—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI MUNTHU WODZILETSA AMATANI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?
  • MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODZILETSA?
  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Akhale Odziletsa
    Galamukani!—2015
  • Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—2019
g19 No. 2 tsamba 4-5
Mayi akukaniza mwana wake kuti asatenge maswiti mushopu

PHUNZIRO 1

Kudziletsa N’kofunika Kwambiri

KODI MUNTHU WODZILETSA AMATANI?

Munthu amene amadziletsa

  • amatha kudikira ngakhale akufunitsitsa zinazake

  • samangotsatira zimene mtima wake ukufuna

  • amatha kumalizitsa zimene akuchita ngakhale zitakhala kuti sizikumusangalatsa

  • amaganizira zofuna za ena m’malo mwa zofuna zake zokha

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?

Ana amene amadziletsa amatha kupewa mayesero ngakhale atakhala okopa bwanji. Koma ana omwe samadziletsa

  • amakhala ovuta

  • amavutika maganizo

  • amasuta, kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo

  • amalephera kusankha zakudya zoyenera

Kafukufuku wina anasonyeza kuti ana amene amadziletsa, akadzakula sadwaladwala, kuvutika maganizo ndi nkhani zandalama komanso savutika kutsatira malamulo. Pomaliza kuchita kafukufukuyu, Pulofesa Angela Duckworth wa ku University of Pennsylvania ananena kuti: “Munthu amapewa mavuto ambiri akakhala wodziletsa.”

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODZILETSA?

Musamasinthesinthe.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mukati ‘Inde’ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayi’ akhaledi ayi.”​—Mateyu 5:37.

Nthawi zina ana amayamba kuvuta, ngakhale pagulu la anthu, n’cholinga chokakamiza makolo awo kuwachitira zimene akufuna. Makolo akamapereka zinthu kwa mwana wawo chifukwa choti akuwavutitsa, mwanayo amayamba kuona kuti kuvutitsa ndi njira yabwino yopezera zimene akufuna.

Koma ngati makolo amapewa kuchita zimenezi, anawo amaphunzira mfundo yakuti: n’zosatheka kupeza chilichonse chimene ukufuna. Dr David Walsh analemba m’buku lina kuti: “Anthu amene amamvetsa mfundo imeneyi ndi amene amakhala osangalala. Choncho kungakhale kulakwa ngati titachititsa ana athu kuyamba kuganiza kuti azidzangoyenda moyera n’kumapeza chilichonse chimene akufuna.”a

Mukamakana kupatsa mwana wanu chilichonse chimene akufuna, sadzavutika kukhala wodziletsa akadzakula. Mwachitsanzo sangadzavutike kudziletsa akadzakopeka kuti ayambe kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kugonana asanakhale pabanja kapena kuchita zinthu zina zolakwika.

Muziwathandiza kudziwa zomwe zingatsatirepo ngati atachita zabwino kapena zoipa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

Mwana wanu afunika kudziwa kuti chilichonse chimakhala ndi zotsatirapo zake. Choncho ngati atalephera kudziletsa akhoza kukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo ngati mwana wanu sachedwa kupsa mtima, anthu akhoza kumamupewa. Koma ngati amatha kuugwira mtima ambiri angamamukonde. Muzimuthandiza kudziwa kuti zinthu zidzamuyendera bwino akamayesetsa kukhala wodziletsa.

Muziwaphunzitsa kuti azichita zinthu zofunika kwambiri.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

Sikuti kudziletsa kumangotanthauza kupewa kuchita zinthu zolakwika, kumaphatikizaponso kuchita zinthu zoyenera ngakhale zitakhala kuti sizikutisangalatsa. Mwana wanu ayenera kudziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, n’kumayambirira kuchita zimenezo. Mwachitsanzo ndi bwino kuti aziyamba walemba homuweki yake asanapite kosewera.

Muziwapatsa chitsanzo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.”​—Yohane 13:15.

Zinthu zokhumudwitsa zikakuchitikirani, ana anu amaona zimene mumachita. Zimene mumachita zingawaphunzitse kudziwa kuti kukhala wodziletsa kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Mwachitsanzo ngati mwana wachita zokukhumudwitsani, kodi mumapsa mtima n’kuyamba kumukalipira kapena mumatha kuugwira mtima?

a Kuchokera m’buku lakuti, No: Why Kids​—of All Ages​—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.

Mayi akukaniza mwana wake kuti asatenge maswiti mushopu

YAMBANI PANOPO KUWAPHUNZITSA

Mukamakana kupatsa mwana wanu chilichonse chimene akufuna, sadzavutika kukhala wodziletsa akadzakula. Mwachitsanzo sangadzavutike kudziletsa akadzakopeka kuti ayambe kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kugonana asanakhale pabanja kapena kuchita zinthu zina zolakwika

Muziwapatsa Chitsanzo Chabwino

  • Kodi mwana wanga amaona kuti sindipsa mtima msanga zinthu zina zokhumudwitsa zikandichitikira?

  • Kodi ndinayamba ndamufotokozerapo mwana wanga chifukwa chimene ndimakhalira wodekha zokhumudwitsa zikandichitikira?

  • Kodi mwana wanga anganene zotani zokhudza ineyo. Anganene kuti ndimapsa mtima msanga kapena ndine wodziletsa?

Zimene Makolo Ena Ananena . . .

“Tinkadziwa kuti mwana wathu akhoza kukwiya ndi zinazake komabe tinamuphunzitsa kuti akakhumudwa asamasokoneze mtendere wa anthu ena. Akalephera kuchita zimenezi, tinkamuchotsa pagulu la anzake kufikira mtima wake utakhala pansi.”​—Theresa.

“Ine ndi mkazi wanga tinkayamikira ana athu akasonyeza khalidwe labwino. Mwachitsanzo akakumana ndi mavuto n’kusonyeza kudziletsa, tinkawauza kuti ‘tasangalala kwambiri ndi zimene mwachita.’”​—Wayne.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena