Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/15 tsamba 13-18
  • Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwopa Mulungu ndi Kuda Choipa
  • Kudziletsa, Kuli Njira Yanzeru
  • Chikondi Chopanda Dyera Chimathandiza
  • Chikhulupiriro ndi Kudzichepetsa Monga Zothandiza
  • Kudziletsa m’Banja
  • Kugwiritsira Ntchito Chithandizo Choperekedwa ndi Mulungu
  • Kudziletsa—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kofunika Motero?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/15 tsamba 13-18

Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa

‘Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.’​—AGALATIYA 5:22, 23.

1. Kodi ndani amene atipatsa zitsanzo zabwino koposa za kudziletsa, monga momwe zikuwonedwera m’malemba ati?

YEHOVA MULUNGU ndi Yesu Kristu atipatsa zitsanzo zabwino koposa za kudziletsa. Chiyambire pa kusamvera kwa munthu m’munda wa Edene, Yehova wakhala akusonyeza mkhalidwe umenewu. (Yerekezerani ndi Yesaya 42:14.) Nthaŵi zisanu ndi zinayi m’Malemba Achihebri timaŵerenga kuti iye ali “wolekereza.” (Eksodo 34:6) Kuteroko kumafunikira kudziletsa. Ndipo ndithudi Mwana wa Mulungu anasonyeza kudziletsa kwakukulu, popeza kuti ‘pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa.’ (1 Petro 2:23) Komabe, Yesu akanakhoza kupempha kwa Atate wake wakumwamba chichirikizo cha ‘mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri.’​—Mateyu 26:53.

2. Kodi ndizitsanzo zabwino Zamalemba ziti zimene tiri nazo za kudziletsa kosonyezedwa ndi anthu opanda ungwiro?

2 Tirinso ndi zitsanzo zina zabwino Zamalemba za kudziletsa kosonyezedwa ndi anthu opanda ungwiro. Mwachitsanzo, mkhalidwe umenewu unawonetsedwa m’chochitika chapadera m’moyo wa Yosefe, mwana wa kholo Yakobo. Yosefe anasonyeza kudziletsa kotani nanga pamene mkazi wa Potifara anayesa kumnyenga! (Genesis 39:7-9) Panalinso chitsanzo chabwino cha achichepere anayi Achihebri amene anasonyeza kudziletsa mwakukana kudya zakudya za mfumu ya Babulo chifukwa cha ziletso za Chilamulo cha Mose.​—Danieli 1:8-17.

3. Kodi ndani amene amadziŵika chifukwa cha khalidwe lawo labwino, monga momwe zawonedwera ndi umboni uti?

3 Kaamba ka zitsanzo zamakono za kudziletsa, tingaloze kwa Mboni za Yehova zonse pamodzi. Izo ziyenera chiyamikiro choperekedwa ndi New Catholic Encyclopedia​—kuti izo ziri “gulu limodzi la magulu akhalidwe labwino koposa m’dziko.” Mlangizi wapayunivesite wa ku Philippines ananena kuti “Mboni zimachita mosamalitsa zimene zimaphunzira m’Malemba.” Ponena za msonkhano wa Mboni mu Warsaw mu 1989, mtola nkhani wa ku Poland analemba kuti: “Anthu 55,000 sanasute ndudu ndi imodzi yomwe kwa masiku atatu! . . . Chisonyezero chimenechi cha kudziletsa koposa kwaumunthu chinandisangalatsa ndi kundichititsa mantha.”

Kuwopa Mulungu ndi Kuda Choipa

4. Kodi nchiti chimene chiri chimodzi cha zithandizo zazikulu koposa posonyeza kudziletsa?

4 Chimodzi cha zithandizo zazikulu koposa m’kukulitsa kudziletsa ndicho kuwopa Mulungu, mantha abwino a kusakondweretsa Atate wathu wakumwamba wachikondi. Kufunika kwa mmene kuwopa Mulungu kuyenera kukhalira kwa ife kukuwonekera ndi chenicheni chakuti Malemba amakutchula nthaŵi zambiri. Pamene Abrahamu anali pafupi kupereka nsembe mwana wake Isake, Mulungu anati: ‘Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziŵa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.’ (Genesis 22:12) Mosakaikira anali ndi chipsinjo chamaganizo chachikulu, chotero Abrahamu anafunikira kudziletsa kwakukulu kuti achite lamulo la Mulungu kufikira pa kunyamula mpeni wake kuti aphe mwana wake wokondedwa Isake. Inde, kuwopa Mulungu kudzatithandiza kusonyeza kudziletsa.

5. Kodi kuda choipa kumachita mbali yanji m’kusonyeza kwathu kudziletsa?

5 Kogwirizana kwambiri ndi kuwopa Yehova ndiko kuda choipa. Pa Miyambo 8:13 timaŵerenga kuti: “Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa.” Ndiponso, kudana ndi choipa kumatithandizanso kusonyeza kudziletsa. Kaŵirikaŵiri, Malemba amatiuza kuda​—inde, kunyansidwa​—ndi choipa. (Salmo 97:10; Amosi 5:14, 15; Aroma 12:9) Chinthu choipa kaŵirikaŵiri chimakhalanso chosangalatsa, chokopa, chonyengerera kwakuti timangofunikira kuchida kotero kuti tidzilimbitse motsutsana nacho. Kuda zoipa konseko kuli ndi chiyambukiro chakulimbitsa kutsimikiza mtima kwathu kwa kusonyeza kudziletsa ndipo chotero kumatumikira monga chitetezo kwa ife.

Kudziletsa, Kuli Njira Yanzeru

6. Kodi nchifukwa ninji kuthetsa zilakolako zadyera mwakusonyeza kudziletsa kuli njira yanzeru?

6 Chothandiza china chachikulu m’kusonyeza kwathu kudziletsa ndicho kuzindikira nzeru yakusonyeza mkhalidwe umenewu. Yehova amatipempha kusonyeza kudziletsa kaamba ka phindu lathulathu. (Yerekezerani ndi Yesaya 48:17, 18.) Mawu ake ali ndi uphungu wochuluka wosonyeza mmene kuliri kwanzeru kuthetsa zilakolako zathu zadyera mwakusonyeza kudziletsa. Sitingathaŵe konse malamulo osasinthika a Mulungu. Mawu ake amatiuza kuti: ‘Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mu mzimu adzatuta moyo wosatha.’ (Agalatiya 6:7, 8) Chitsanzo chodziŵikiratu nchija cha kudya ndi kumwa. Matenda ambiri amatulukapo chifukwa chakuti anthu amadya kapena kumwa mopambanitsa. Kugonjera ku dyera konseko kumalanda munthu ulemu waumwini. Kuposa zimenezo, munthuyo sangagonjere ku dyera popandanso kuwononga maunansi ake ndi ena. Choipitsitsa cha zonse nchakuti, kusadziletsa kumawononga unansi wathu ndi Atate wathu wakumwamba.

7. Kodi ndiuti umene uli mutu waukulu wa bukhu la Miyambo, monga momwe kwasonyezedwera ndi malemba a Baibulo atiwo?

7 Chotero, tiyenera kupitiriza kudziuza kuti dyera ndilo kudzigonjetsa. Mutu waukulu wa bukhu la Miyambo, limene linagogomezera kudzilanga, ngwakuti dyera silimapindulitsa ndipo kudziletsa kuli kwanzeru. (Miyambo 14:29; 16:32) Ndipo zindikirani kuti kudzilanga kumaphatikizapo zoposa kungopeŵa choipa. Kudzilanga, kapena kudziletsa, kumafunikiranso kuti tichite chabwino, chimene chingakhale chovuta chifukwa chakuti chimatsutsana ndi zilakolako zathu zochimwa.

8. Kodi nchokumana nacho chotani chimene chikugogomezera nzeru ya kusonyeza kudziletsa?

8 Yomwe ikuchitira fanizo nzeru ya kusonyeza kudziletsa ndi nkhani ya mmodzi wa Mboni za Yehova amene anaimirira pamzera pabanki pamene mwamuna wina anamdulira kutsogolo. Ngakhale kuti Mboniyo inakwiya pang’ono, inasonyeza kudziletsa. Tsiku lomwelo anafunikira kuwonana ndi injiniya wina kuti asaine mapulani a Nyumba Yaufumu. Ndipo kodi injiniyayo anali yani? Eya, mwamuna yemwe uja amene anamdulira kutsogolo kubanki! Injiniyayo sanangotsimikizira kukhala waubwenzi kwambiri komanso analipiritsa Mboniyo mtengo wotsika ndi mbali imodzi mwa khumi kuposa mtengo wanthaŵi zonse. Mboniyo inali yachimwemwe chotani nanga kuti inasonyeza kudziletsa kuchiyambi kwa tsikulo, kusadzilola kukwiyitsidwa!

9. Kodi pamene takumana ndi mayankhidwe amwano muuminisitala, njira yanzeru ikakhala kuchita chiyani?

9 Kwanthaŵi ndi nthaŵi pamene tipita kukhomo ndi khomo kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kapena kuimirira pangondya ya khwalala kuyesayesa kukopera odutsa ku uthenga wathu, timakumana ndi malankhulidwe amwano. Kodi njira yanzeru ndiyo kutani? Ndemanga yanzeru imeneyi yapangidwa pa Miyambo 15:1: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” M’mawu ŵena, tifunikira kusonyeza kudziletsa. Ndipo sikuti ndi Mboni za Yehova zokha zimene zapeza zimenezi kukhala zowona koma anthu ena ateronso. Phindu lakuchiritsa la kudziletsa likuzindikiridwa mokulira ndi akatswiri a zamankhwala.

Chikondi Chopanda Dyera Chimathandiza

10, 11. Kodi nchifukwa ninji chikondi chiri thandizo lenileni m’kusonyeza kudziletsa?

10 Kufotokoza chikondi kwa Paulo pa 1 Akorinto 13:4-8 kumasonyeza kuti mphamvu yake ingatithandize kusonyeza kudziletsa. “Chikondi chiri choleza mtima.” (NW) Kukhala woleza mtima kumafunikira kudziletsa. ‘Chikondi sichidukidwa, chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.’ Mkhalidwe wa chikondi umatithandiza kulamulira maganizo ndi malingaliro athu, kuthetsa chikhoterero chirichonse chakukhala wodukidwa, kudzitama, kapena kudzikuza. Chikondi chimatisonkhezera kuchita zosiyana kotheratu, kutipanga kukhala odzichepetsa, odzichepetsa maganizo, monga momwe Yesu analiri.​—Mateyu 11:28-30.

11 Paulo akupitiriza kunena kuti chikondi ‘sichichita zosayenera.’ Kuchita zoyenera panthaŵi zonse kumafunikiranso kudziletsa. Mkhalidwe wa chikondi umatiletsa kukhala aumbombo, kuleka ‘kufunafuna zabwino zathu.’ Chikondi ‘sichipsa mtima.’ Ha, kuli kopepuka chotani nanga kupsa mtima ndi zimene ena amanena kapena kuchita! Koma chikondi chidzatithandiza kusonyeza kudziletsa ndipo sitidzanena kapena kuchita zinthu zomwe tidzaipidwa nazo pambuyo pake. Chikondi ‘sichilingirira zoipa.’ Chibadwa cha anthu ndicho kusunga zinthu kukhosi kapena kukulitsa chidani. Koma chikondi chidzatithandiza kuchotsa malingaliro amenewo m’maganizo mwathu. Chikondi “sichikondwera ndi chosalungama.” (NW) Kudziletsa kumafunikira kuti tisakondwere ndi zosalungama, monga ngati zaumaliseche kapena maprogramu a TV oluluzika. Chikondi ‘chikwirira zinthu zonse’ ndipo ‘chipirira zinthu zonse.’ Kumafunikira kudziletsa kuti tilake zinthu, kupirira zinthu zopereka chiyeso kapena zolemetsa ndi kusazilola kutilefula, kutipangitsa kubwezera, kapena kutipangitsa kufuna kusiya kutumikira Yehova.

12. Kodi ndinjira imodzi iti yosonyezera chiyamikiro chathu kaamba ka zonse zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu atichitira?

12 Ngati timakondadi Atate wathu wakumwamba ndi kuyamikira mikhalidwe yake yabwino koposa ndi zonse zimene watichitira, tidzafuna kumkondweretsa mwakusonyeza kudziletsa panthaŵi zonse. Ndiponso, ngati timakondadi Ambuye ndi Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, ndikuyamikira zonse zimene watichitira, tidzalabadira lamulo lake la ‘kunyamula mtengo wathu wozunzirapo ndikumtsata.’ (Marko 8:34, NW) Zimenezo ndithudi zimafunikira kuti tisonyeze kudziletsa. Chikondi kaamba ka abale ndi alongo athu Achikristu chidzatithandizanso kusawavulaza mwakuchita mwadyera.

Chikhulupiriro ndi Kudzichepetsa Monga Zothandiza

13. Kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro chingatithandize kusonyeza kudziletsa?

13 Thandizo lina lalikulu m’kusonyeza kudziletsa ndilo chikhulupiriro mwa Mulungu ndi malonjezo ake. Chikhulupiriro chidzatitheketsa kukhulupirira Yehova ndi kuyembekeza kaamba ka nthaŵi yake yoikika yolungamitsira zinthu. Mtumwi Paulo akumveketsa mfundo imodzimodziyi pamene akunena pa Aroma 12:19 kuti: ‘Musabwezere choipa, okondedwa, . . . pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].’ M’zimenezi, kudzichepetsa kungatithandizenso. Ngati ndife odzichepetsa, sitidzafulumira kukwiya chifukwa cha kulakwiridwa kongolingaliridwa kapena kwenikweni. Sitidzafulumira kubwezera, koma tidzasonyeza kudziletsa ndikukhala ofunitsitsa kuyembekeza pa Yehova.​—Yerekezerani ndi Salmo 37:1, 8.

14. Kodi nchokumana nacho chotani chimene chimasonyeza kuti kudziletsa kungapezedwe ngakhale ndi awo amene amakusoŵa mokulira?

14 Chenicheni chakuti tingaphunzire kusonyeza kudziletsa chinasonyezedwa mwamphamvu ndi chokumana nacho cha munthu wamkwiyo wachiwawa. Eya, iye anali ndi mkwiyo waukulu kwakuti pamene apolisi anafika kudzafunsa za phokoso lomwe iye ndi atate wake anali kuchititsa, anagwetsa apolisi atatu ena asanamgonjetse! Komabe, m’kupita kwanthaŵi, iye anafikiridwa ndi Mboni za Yehova ndipo anaphunzira kusonyeza kudziletsa, chimodzi cha zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Lerolino, zaka 30 pambuyo pake, mwamuna ameneyu adakali kutumikira Yehova mokhulupirika.

Kudziletsa m’Banja

15, 16. (a) Kodi nchiyani chimene chidzathandiza mwamuna kusonyeza kudziletsa? (b) Kodi kudziletsa kumafunikira mwapadera m’mkhalidwe wotani, monga momwe kwawonedwera ndi chokumana nacho chiti? (c) Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kumafunikira kwa mkazi?

15 Kudziletsa kulidi kofunikira m’banja. Kuti mwamuna akonde mkazi wake monga momwe amadzikondera kumafunikira kuti alamulire mokulira maganizo, mawu, ndi zochita zake. (Aefeso 5:28, 29) Inde, kumafunikira kudziletsa kuti amuna alabadire mawu a mtumwi Petro a pa 1 Petro 3:7 akuti: ‘Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso.’ Mwamuna wokhulupirira amafunikira kusonyeza kudziletsa makamaka ngati mkazi wake ali wosakhulupirira.

16 Mwafanizo: Panali mkulu wina yemwe anali ndi mkazi wosakhulupirira wokwiya msanga. Komabe, mkuluyo anasonyeza kudziletsa, ndipo izi zinampindulitsa kwakukulu kwakuti dokotala wake anamuuza kuti: “John, uyenera kuti ndiwe munthu woleza mtima kwambiri mwachibadwa apo ayi uli ndi chipembedzo champhamvu.” Tiridi ndi chipembedzo champhamvu, popeza kuti ‘Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso,’ wotitheketsa kusonyeza kudziletsa. (2 Timoteo 1:7) Ndiponso, kumafunikira kudziletsa kuti mkazi akhale wogonjera, makamaka pamene mwamuna wake ali wosakhulupirira.​—1 Petro 3:1-4.

17. Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kuli kofunika muunansi wa kholo ndi mwana?

17 Kudziletsa kumafunikiranso muunansi wa kholo ndi mwana. Kuti akhale ndi ana amene amadziletsa, choyamba makolowo ayenera kukhazikitsa chitsanzo chabwino. Ndipo pamene ana afunikira chilango chakutichakuti, nthaŵi zonse chiyenera kuperekedwa mwabata ndi chikondi, zomwe zimafunikira kudziletsa kwenikweni. (Aefeso 6:4; Akolose 3:21) Ndiyenonso, kuti ana asonyeze kuti amawakondadi makolo awo afunikira kumvera, ndipo kumvera kumafunikiradi kudziletsa.​—Aefeso 6:1-3; yerekezerani ndi 1 Yohane 5:3.

Kugwiritsira Ntchito Chithandizo Choperekedwa ndi Mulungu

18-20. Kodi ndimakonzedwe atatu auzimu otani amene tiyenera kugwiritsira ntchito kuti tikulitse mikhalidwe imene idzatithandiza kusonyeza kudziletsa?

18 Kuti tikule m’kuwopa Mulungu, chikondi chopanda dyera, chikhulupiriro, kuda choipa, ndi kudziletsa, tifunikira kugwiritsira ntchito chithandizo chonse chimene Yehova Mulungu wapereka. Tiyeni tikambitsirane makonzedwe atatu auzimu amene angatithandize kusonyeza kudziletsa. Choyamba cha zonse, pali mwaŵi wamtengo wake wa pemphero. Sitifunikira konse kukhala otanganitsidwa kuchita kulephera kupemphera. Inde, tiyenera kukhumba ‘kupemphera kosaleka,’ ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera.’ (1 Atesalonika 5:17; Aroma 12:12) Tiyeni tiipange nkhani ya kukulitsa kudziletsa kukhala ya pemphero. Koma pamene tilephera kusonyeza kudziletsa, tiyeni tipembedzere Atate wathu wakumwamba modzichepetsa kaamba ka chikhululukiro.

19 Mbali yachiŵiri yothandiza m’kusonyeza kudziletsa ndiyo kupeza chithandizo chochokera m’kuŵerenga Mawu a Mulungu ndi mabuku amene amatitheketsa kumvetsetsa ndi kugwiritsira ntchito Malemba. Kuli kokhweka kwambiri kunyalanyaza mbali imeneyi ya utumiki wathu wopatulika! Tiyenera kusonyeza kudziletsa ndikupitirizabe kudziuza kuti palibe zinthu zoŵerenga zofunika koposa kuposa Baibulo ndi zija zoperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo chotero tiyenera kuzipatsa malo oyamba. (Mateyu 24:45-47) Kwanenedwa bwino lomwe kuti sikuli kotheka kuchita zinthu zonse m’moyo watsiku ndi tsiku, koma tiyenera kusankha zimene tidzagwiritsira ntchito nthaŵi yathu kuzichita. Kodi ndifedi amuna ndi akazi auzimu? Ngati ndife odera nkhaŵa ndi zosoŵa zathu zauzimu, tidzasonyeza kudziletsa kofunikira kuzima TV ndikukonzekera misonkhano yathu kapena kuŵerenga Nsanja ya Olonda yomwe tingakhale titangolandira papositi.

20 Chachitatu, pali nkhani yakuchita mwachilungamo ndi misonkhano yathu yampingo ndi misonkhano yaikulu. Kodi misonkhano yonseyo timaiwona kukhala yosafunika kuiphonya? Kodi timafika okonzekera kutengamo mbali ndiyeno kuchita tero pamene tipeza mpata? Kuukulu umene timachita mwachilungamo ndi misonkhano yathu, kuukulu umenewo tidzalimbitsa chitsimikizo chathu chakusonyeza kudziletsa pansi pa mikhalidwe yonse.

21. Kodi ndimphotho zina ziti zimene tingasangalale nazo chifukwa chokulitsa chipatso cha mzimu cha kudziletsa?

21 Kodi ndi mphotho zotani zimene tingayembekezere mwakuyesayesa zolimba kusonyeza kudziletsa panthaŵi zonse? Choyamba, sitidzatuta konse zipatso zowawa za dyera. Tidzakhala ndi ulemu waumwini ndi chikumbumtima chabwino. Tidzadzipulumutsa ku mavuto ambiri ndipo tidzakhalabe pamsewu wopita ku moyo. Ndiponso, tidzakhala okhoza kuchitira ena zabwino koposa. Kuposa zonse, tidzakhala tikulabadira Miyambo 27:11 imene imati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Ndipo imeneyo ndi mphotho yaikulu koposa yomwe tingakhale nayo​—mwaŵi wakukondweretsa mtima wa Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova!

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi ndimotani mmene kuwopa Mulungu kumatithandizira kusonyeza kudziletsa?

◻ Kodi nchifukwa ninji chikondi chimatithandiza kusonyeza kudziletsa?

◻ Kodi kudziletsa kumathandiza motani m’maunansi abanja?

◻ Kodi ndimakonzedwe otani amene tiyenera kuwagwiritsira bwino ngati titi tikulitse kudziletsa?

[Chithunzi patsamba 15]

Yosefe anasonyeza kudziletsa pamene anayesedwa

[Chithunzi patsamba 17]

Kulanga mwana koperekedwa mwabata ndi chikondi kumafunikira kudziletsa kwenikweni

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena