Kudziletsa—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kofunika Motero?
‘Pakutengeraponso changu chonse, muwonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa.’—2 PETRO 1:5.
1. Kodi nchiwonetsero chozizwitsa cha kudziletsa kwakuthupi chotani chimene chinachitika m’zaka za zana la 19?
MOSAKAIKIRA, chimodzi cha ziwonetsero zozizwitsa koposa za kulamulira thupi chinasonyezedwa ndi Charles Blondin chakumapeto kwa theka la zaka za zana la 19. Malinga ndi kunena kwa lipoti lina, iye anawoloka mathithi a Niagara nthaŵi zambiri, yoyamba mu 1859, pakachingwe kakang’ono pamtunda wotalika mamita 340 ndi mamita 50 pamwamba pa madzi. Pambuyo pa chimenecho, anabwereza zimenezo nthaŵi zonse akumasonyeza luso lake losiyana: atamangidwa kumaso, ali m’saka, akukankha wilibala, akuyendera magobodo, ndiponso atabereka munthu. M’chochitika china, anapanga mipidigoli ali pamagobodo pachingwe chotalika mamita 52 kuchokera pansi. Kukhala ndi kulinganizika koteroko kunafunikira kudziletsa kwakuthupi kwakukulu kwambiri. Monga mphotho yake, Blondin anafupidwa ponse paŵiri kutchuka ndi chuma.
2. Kodi nzochitika zina zotani zimene zimafunikira kulamulira kwakuthupi?
2 Pamene kuli kwakuti oŵerengeka okha angatsanzire ziwonetsero zimenezo, kufunika kwa kudziletsa kwakuthupi pochita maluso kapena maseŵera kuli kodziŵikiratu kwa tonsefe. Mwachitsanzo, pofotokoza luso lopambana la woliza piyano malemu Vladimir Horowitz, katswiri wina woimba anati: “Kwa ine chinthu chosangalatsa chinali lingaliro lakudzilamulira kotheratu . . . , lingaliro la kugwiritsira ntchito nyonga kosakhulupiririka.” Lipoti lina lonena za Horowitz limanena za “zaka makumi asanu ndi atatu za kuyenda mofulumira ndi molinganizika bwino koposa kwa zala.”
3. (a) Kodi ndikudziletsa kofunika koposa kotani kumene kulipo, ndipo kodi kwamasuliridwa motani? (b) Kodi liwu Lachigiriki lomasuliridwa ‘kudziletsa’ m’Baibulo limatanthauzanji?
3 Kukulitsa maluso oterowo kumatenga kuyesayesa kwakukulu. Komabe, chofunika koposa ndiponso chotokosa ndicho kudziletsa. Iko kwamasuliridwa kukhala “chiletso choikidwa pa zilakolako, malingaliro, kapena zikhumbo za munthu mwini.” M’Malemba Achikristu Achigiriki, liwu lotembenuzidwa ‘chodziletsa’ pa 2 Petro 1:5 ndi m’malo ena, lamasuliridwa kukhala “ukoma wa munthu amene amalamulira zikhumbo ndi zilakolako zake, makamaka zilakolako zake zamaganizo.” Kudziletsa kwaumwini kwatchedwa “chimake cha chokwaniritsa cha anthu.”
Chifukwa Chake Kudziletsa Kuli Kofunika Koposa
4. Kodi kusadziletsa kwatuta zipatso zoipa zotani?
4 Kusadziletsa kukututa zotulukapo zotani nanga! Mavuto ambiri m’dziko lerolino amapangitsidwa kwakukulukulu chifukwa cha kusoŵeka kwa kudziletsa. Zowonadi, tiri ‘m’masiku otsiriza,’ pamene ‘nthaŵi zovuta kuchita nazo ziri pano.’ Anthu ali “osakhoza kudziletsa” kaŵirikaŵiri chifukwa cha umbombo, mpangidwe wake umodzi ndiwo kukhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-5) Chowonadi chomvetsa chisoni chimenechi chawonekera bwino lomwe mwakuchotsedwa mumpingo Wachikristu kwa anthu ochimwa oposa 40,000 m’chaka chautumiki chapita, kwakukulukulu chifukwa cha mayendedwe oipitsitsa. Kuchiŵerengerochi tiyenera kuwonjezerako ambiri amene anadzudzulidwa, kwakukulukulu chifukwa cha chisembwere chakugonana koma zonsezi chifukwa chakulephera kudziletsa. Ndiponso chomvetsa chisoni nchakuti akulu ena otumikira kwa nthaŵi yaitali anataya mathayo awo onse monga oyang’anira kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho.
5. Kodi kufunika kwa kudziletsa kungachitiridwe fanizo motani?
5 Kufunika kwa kudziletsa kungafotokozedwe mwafanizo ndi galimoto. Ilo liri ndi magudumu anayi amene amaitheketsa kuyenda, injini yamphamvu imene ingayendetse magudumuwo mofulumira kwambiri, ndi mabuleki amene angawaimike. Komabe, ngozi ikhoza kuchitika kusiyapo kokha ngati pali munthu wina pampando wa woyendetsa kusankha kumene magudumu amenewo ayenera kupita, liŵiro limene afunikira kuyendera, ndi pamene afunikira kuima, mwakugwiritsira ntchito molamulira chiwongolero, accelerator, ndi mabuleki.
6. (a) Kodi ndilamulo lotani lokhudza chikondi limene lingagwiritsiridwe ntchito pa kudziletsa? (b) Kodi ndiuphungu wowonjezereka wotani umene tiyenera kuukumbukira?
6 Kungakhale kovuta kugogomezera mopambanitsa kufunika kwa kudziletsa. Zimene mtumwi Paulo ananena pa 1 Akorinto 13:1-3 ponena za kufunika kwa chikondi zinganenedwenso ponena za kudziletsa. Mosasamala kanthu kuti ndife alankhuli apoyera abwino motani, kaya tikhale ndi chidziŵitso chochuluka ndi chikhulupiriro chomwe timachipeza kupyolera m’zizoloŵezi zabwino za kuphunzira, kaya timachita ntchito zabwino zotani zopindulitsa ena, pokhapo ngati tisonyeza kudziletsa, zonsezi zidzapita pachabe. Tiyenera kukumbukira mawu aŵa a Paulo: ‘Kodi simudziŵa kuti iwo akuchita makani a liŵiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire. Koma yense wakuyesetsana [asonyeza kudziletsa m’zinthu, NW] zonse.’ (1 Akorinto 9:24, 25) Uphungu uwu wa Paulo wa pa 1 Akorinto 10:12 umatithandiza kukhala odziletsa m’zinthu zonse: ‘Iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.’
Zitsanzo Zopereka Chenjezo
7. (a) Kodi ndimotani mmene kusadziletsa kunayambitsira fuko la anthu kuyenda panjira yoipa? (b) Kodi ndizitsanzo zina zakale za kusadziletsa zotani zimene Malemba amatipatsa?
7 Adamu analephera kusonyeza kudziletsa chifukwa cholola malingaliro m’malo mwa kuganiza kulamulira zochita zake. Monga chotulukapo, ‘uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo.’ (Aroma 5:12) Mbanda yoyambirira inachitidwanso chifukwa cha kusoŵeka kwa kudziletsa, popeza kuti Yehova Mulungu anachenjeza Kaini kuti: ‘Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Uchimo ubwatama pakhomo, ndipo iwe udzaulamulira kodi?’ Popeza kuti Kaini sanaulamulire uchimo, anapha mbale wake Abele. (Genesis 4:6-12) Mkazi wa Loti analepheranso kusonyeza kudziletsa. Iye analephereratu kupeŵa chiyeso chakuyang’ana m’mbuyo. Kodi kusadziletsa kwake kunamtengera chiyani? Eya, moyo wake weniweniwo!—Genesis 19:17, 26.
8. Kodi ndizokumana nazo za anthu atatu akale ati zimene zimapereka chenjezo kwa ife la kufunika kwa kudziletsa?
8 Rubeni, mwana woyamba wa Yakobo, anataya ukulu wake chifukwa cha kusadziletsa. Iye anaipitsa kama wa atate wake mwakugonana ndi mmodzi wa akazi aang’ono a Yakobo. (Genesis 35:22; 49:3, 4; 1 Mbiri 5:1) Chifukwa chakuti Mose anakwiya ndi njira imene Aisrayeli anamuikira pachiyeso chifukwa cha kung’ung’udza, kudandaula, ndi kupanduka kwawo, iye anamanidwa mwaŵi wokhumbidwa kwakukulu wakuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 20:1-13; Deuteronomo 32:50-52) Ngakhale Mfumu yokhulupirika Davide, ‘munthu wapamtima pa Mulungu,’ analoŵa m’vuto lalikulu chifukwa cha kusadziletsa pa chochitika china. (1 Samueli 13:14; 2 Samueli 12:7-14) Zitsanzo zonsezi zimatipatsa machenjezo abwino kuti tifunikira kusonyeza kudziletsa.
Zimene Tifunikira Kuzilamulira
9. Kodi ndimalemba ena ati amene amagogomezera kufunika kwa kudziletsa?
9 Choyamba, kudziletsa kumaphatikizapo maganizo ndi malingaliro athu. Kaŵirikaŵiri izi zimalozeredwako m’Malemba mwakugwiritsira ntchito mawu ophiphiritsira akuti “mtima” ndi “imso.” Zimene timadzilola kusumikapo maganizo athu zimatithandiza kapena kutsekereza kuyesayesa kwathu kwa kukondweretsa Yehova. Kudziletsa kumafunikira ngati titi tilabadire uphungu Wamalemba wopezeka pa Afilipi 4:8, kupitiriza kulingalira zinthu zowona, zoyera, ndi zokoma mtima. Wamasalmo Davide anafotokoza malingaliro ofananawo m’pemphero, akumati: ‘Maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.’ (Salmo 19:14) Lamulo lakhumi—kusasirira chinthu cha munthu wina—linafunikira kuletsa maganizo. (Eksodo 20:17) Yesu anagogomezera kufunika kwa kulamulira maganizo ndi malingaliro athu pamene ananena kuti: ‘Yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.’—Mateyu 5:28.
10. Kodi ndimalemba Abaibulo ati amene amagogomezera kufunika kwa kulamulira kalankhulidwe kathu?
10 Kudziletsa kumaphatikizaponso mawu athu, kalankhulidwe kathu. Palidi malemba ambiri amene amapereka uphungu wa kulamulira malirime athu. Mwachitsanzo: ‘Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mawu ako akhale oŵerengeka.’ (Mlaliki 5:2) ‘Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.’ (Miyambo 10:19) ‘Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo . . . chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.’ Ndipo Paulo akupitiriza kupereka uphungu wakuti tidzichotsere kulankhula zopanda pake ndi kulankhula zopusa.—Aefeso 4:29, 31; 5:3, 4.
11. Kodi ndimotani mmene Yakobo akuchitira ndi vuto la kulamulira lirime?
11 Yakobo, mbale wopeza wa Yesu, akutsutsa kalankhulidwe kosalamulirika ndipo akusonyeza mmene kuliri kovuta kulamulira lirime. Iye akuti: ‘Lirimenso liri chiŵalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Tawonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lirime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziŵalo zathu laikika lirime, ndilo lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena. Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam’nyanja, zimazoloŵeretsedwa, ndipo zazoloŵeretsedwa ndi anthu; koma lirime palibe munthu akhoza kulizoloŵeretsa; liri choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha. Timayamika [Yehova, NW] ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu; mochokera mkamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.’—Yakobo 3:5-10.
12, 13. Kodi ndimalemba ena ati amene amasonyeza kufunika kwa kulamulira zochita zathu ndi khalidwe?
12 Ndithudi, kudziletsa kumaphatikizapo zochita zathu. Mbali imodzi imene kudziletsa kwakukulu kuli kofunikira ndiyo unansi wathu ndi osiyana nawo chiŵalo. Akristu akulamulidwa kuti: “Thaŵani chisembwere chakugonana.” (1 Akorinto 6:18, New International Version) Amuna okwatira akuchenjezedwa kulekezera chikondwerero chawo chakugonana kwa akazi awo, akumauzidwa mwapang’ono kuti: ‘Imwa madzi a m’chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m’kasupe mwako.’ (Miyambo 5:15-20) Tikuuzidwa momvekera bwino kuti ‘achigololo adzawaweruza Mulungu.’ (Ahebri 13:4) Kudziletsa kuli kofunika mwapadera kwa awo amene akakulitsa mphatso ya umbeta.—Mateyu 19:11, 12; 1 Akorinto 7:37.
13 Yesu anafotokoza mwachidule nkhani yonse yokhudza zochita zathu kwa anthu anzathu pamene anapereka lomwe mwachisawawa limatchedwa “Lamulo Lamakhalidwe Abwino,” akumati: ‘Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.’ (Mateyu 7:12) Zowonadi, kumafunikira kudziletsa kuti tisalole zilakolako zathu zadyera kapena zitsenderezo zakunja kapena ziyeso kutipangitsa kuchitira ena mosiyana ndi mmene tikafunira kuti atichitire.
14. Kodi Mawu a Mulungu amapereka uphungu wotani ponena za zakudya ndi zakumwa?
14 Ndiyeno pali nkhani ya kudziletsa ponena za chakudya ndi chakumwa. Mawu a Mulungu mwanzeru amapereka uphungu uwu: ‘Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.’ (Miyambo 23:20) Makamaka ponena za tsiku lathu, Yesu anachenjeza kuti: ‘Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.’ (Luka 21:34, 35) Inde, kudziletsa kumaphatikizapo maganizo ndi malingaliro athu, limodzinso ndi mawu athu ndi zochita zathu.
Chifukwa Chake Kudziletsa Kuli Chitokoso Chotero
15. Kodi Malemba amasonyeza motani kutsimikizirika kwa chitsutso cha Satana pa kusonyeza kudziletsa kwa Akristu?
15 Kudziletsa sikuli kosavuta chifukwa chakuti, monga momwe Akristu onse amadziŵira, tiri ndi mphamvu zazikulu zitatu zomwe zimalimbana ndi kusonyeza kwathu kudziletsa. Choyamba, pali Satana ndi ziŵanda zake. Malemba samasiya chikaikiro chirichonse ponena za kukhalapo kwawo. Chotero, timaŵerenga kuti “Satana analowa mwa” Yudase nthaŵi pang’ono asanatuluke kupita kukapereka Yesu. (Yohane 13:27) Mtumwi Petro anamfunsa Hananiya kuti: ‘Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga mzimu woyera?’ (Machitidwe 5:3) Moyenerera kwenikweni, Petro anachenjezanso kuti: ‘Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.’—1 Petro 5:8.
16. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kudziletsa ponena za zinthu zadzikoli?
16 M’zoyesayesa zawo zakusonyeza kudziletsa, Akristu ayeneranso kulimbana ndi dzikoli lomwe ligona “mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. Ponena za ilo, mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.’ Kusiyapo kokha ngati tisonyeza kudziletsa ndi kupeŵa mwamphamvu chikhoterero chirichonse chakukonda dziko, tidzagonjera ku chisonkhezero chake, monga momwe anachitira Dema yemwe kale anali wantchito mnzake wa Paulo.—1 Yohane 2:15-17; 5:19; 2 Timoteo 4:10.
17. Kodi ndivuto lotani limene timabadwa nalo lokhudza kudziletsa?
17 Monga Akristu, timafunikiranso kudziletsa ngati titi tilimbane mwachipambano ndi zifooko ndi zophophonya zathu zakuthupi zobadwa nazo. Sitingapeŵe chenicheni chakuti ‘ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.’ (Genesis 8:21) Mofanana ndi Mfumu Davide, ‘tinabadwa m’mphulupulu, ndipo amayi athu anatilandira m’zoipa.’ (Salmo 51:5) Mwana wongobadwa kumene samadziŵa kalikonse ponena za kudziletsa. Pamene akufuna chinachake, amangopitiriza kulira kufikira atachilandira. Lipoti lina lonena za kuphunzitsa mwana likufotokoza kuti: ‘Ana amalingalira m’njira yosiyana kotheratu ndi achikulire. Ana ali adyera ndipo kaŵirikaŵiri osavomereza kuumirizidwa kwanzeru kwenikweni chifukwa chakuti sali okhoza “kudziika m’malo a munthu wina.”’ Zowonadi, ‘utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.’ Komabe, mwakupereka ‘nthyole yomlangira,’ mwapang’onopang’ono amaphunzira kuti pali malamulo amene ayenera kuwamvera ndikuti dyera liyenera kuthetsedwa.—Miyambo 22:15.
18. (a) Malinga ndi kunena kwa Yesu, kodi ndizikhoterero zotani zimene zimakhala mumtima wophiphiritsira? (b) Kodi ndimawu otani a Paulo amene amasonyeza kuzindikira kwake vuto la kusonyeza kudziletsa?
18 Inde, zikhoterero zathu zadyera zobadwa nazo zimapereka chitokoso kwa ife pamene tiyesa kusonyeza kudziletsa. Zikhoterero zimenezi zimakhala mumtima wophiphiritsira, womwe Yesu ananena za iwo kuti: ‘Mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiŵereŵere, zakuba, za umboni wonama, zamwano.’ (Mateyu 15:19) Ndicho chifukwa chake Paulo analemba kuti: ‘Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe mkati mwanga ndiwo.’ (Aroma 7:19, 20) Komabe, sunali mkhalidwe wopanda chiyembekezo, popeza kuti Paulo analembanso kuti: ‘Ndipumphuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.’ Kupumphuntha thupi lake kunafunikira kusonyeza kudziletsa.—1 Akorinto 9:27.
19. Kodi nchifukwa ninji Paulo anali wokhoza kunena zowonadi kuti anapumphuntha thupi lake?
19 Paulo ananenadi zowona kuti anapumphuntha thupi lake, popeza kuti kusonyeza kudziletsa kuli kocholoŵana ndi zinthu zina zambiri zakuthupi, monga ngati kukwera kwa liŵiro la kuyenda kwa mwazi, mitsempha yodwala, kusoŵa tulo, kupweteka kwa mutu, kudzimbidwa, ndi zina zotero. M’nkhani yotsatira, tidzafotokoza mikhalidwe ndi zothandiza zimene zingatithandize kusonyeza kudziletsa.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kuli kofunika?
◻ Kodi pali zitsanzo zotani za awo amene anataikiridwa chifukwa chosoŵa kudziletsa?
◻ Kodi ndi m’mbali ziti mmene tiyenera kusonyeza kudziletsa?
◻ Kodi ndi adani atatu ati amene amakupanga kukhala kovuta kwa ife kusonyeza kudziletsa?
[Chithunzi patsamba 10]
Akristu afunikira kusonyeza kudziletsa m’zakudya ndi zakumwa
[Chithunzi patsamba 11]
Kudziletsa kudzatithandiza kupeŵa miseche yovulaza
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Historical Pictures Service