Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/15 tsamba 3-6
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Akusiya Zipembedzo Zawo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Anthu Akusiya Zipembedzo Zawo?
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Vuto Lagona Pati?
  • Baibulo Linaneneratu Kuti Anthu Ambiri Adzasiya Kupemphera
  • “Tulukani Mwa Iye”
  • Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Babulo Wamkulu Wakugwa Ndipo Woweruzidwa
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Turukani Pakati Pao”
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 11/15 tsamba 3-6

NKHANI YA PACHIKUTO

Nkhani Ya Pachikuto N’chifukwa Chiyani Anthu Akusiya Zipembedzo Zawo?

Banja lina laima panja pa tchalitchi chotsekedwa

Bambo ena a ku Turkey, dzina lawo a Gaffar, ankadabwa ndi zimene ankaphunzira kuchipembedzo chawo zoti Mulungu adzawotcha anthu kumoto. Nawonso akazi awo, dzina lawo a Hediye, anayamba kukayikira chipembedzo chawo ali ndi zaka 9. Mayiwa anati: “Kutchalitchi kwathu ankatiphunzitsa kuti Mulungu analemberatu chilichonse chimene chimachitika pa moyo wa munthu. Ndiye popeza ndinali wamasiye, ndinkaona kuti Mulungu si wachilungamo moti ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndinamulakwira chiyani Mulungu?’ Zimenezi zinkandipweteka kwambiri moti nthawi zambiri ndinkalira usiku wonse. Pamene ndinkakwanitsa zaka 15, ndinkangopita kutchalitchi mwamwambo chabe.”

KODI nanunso munakhumudwa ndi chipembedzo chanu ndipo munasiya kupemphera? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. M’mayiko ambiri chiwerengero cha anthu opemphera chayamba kuchepa moti tsogolo la zipembedzo likukayikitsa. Mwachitsanzo taonani mmene zinthu zasinthira m’mayiko otsatirawa.

AUSTRALIA

Pafupifupi hafu ya chiwerengero cha anthu a m’dziko la Australia, sapita kuchipembedzo chilichonse. Ndipo anthu 10 pa 100 alionse amati sakhulupirira n’komwe zoti kuli Mulungu. Mu 2010, m’busa wina anadandaula kuti, “pa zaka 40 zapitazi, anthu ambirimbiri asiya kupita ku zipembedzo zachikhristu.”

FRANCE

Pa anthu 100 alionse a m’dziko la France, ndi anthu 37 okha amene amapita ku zipembedzo zawo. Ena ananena kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu kapena sapita kuchipembedzo chilichonse. Komanso magazini ina inanena kuti, m’madera amene poyamba tchalitchi cha Katolika chinali champhamvu kwambiri, panopa kwangotsala Akatolika owerengeka.—The Economist.

IRELAND

Zikuoneka kuti dzikoli ndi limene lili ndi anthu ambiri amene asiya kupita ku zipembedzo zawo. Mwachitsanzo, pa anthu 100 alionse amene anafunsidwa, anthu pafupifupi 45 ananena kuti sapita ku chipembedzo chilichonse, ndipo anthu 10 pa 100 alionse, ananena kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu. Dzikoli ndi limodzi mwa mayiko 10 amene ali ndi anthu ambiri omwe sakhulupirira zoti kuli Mulungu. Panopa nkhani imene ili m’kamwam’kamwa m’dzikoli, ndi ya kulowa pansi kwa chipembedzo cha Katolika.

JAPAN

M’dziko la Japan, anthu 16 okha pa anthu 100 alionse ndi amene amapita ku zipembedzo zawo. Pomwe anthu 62 pa 100 alionse sapita kuchipembedzo chilichonse kapena sakhulupirira zoti kuli Mulungu.

SOUTH AFRICA

Ku South Africa, anapeza kuti m’chaka cha 2005, anthu 83 pa 100 alionse ankapita kuzipembedzo zawo. Koma pofika chaka cha 2012, chiwerengerochi chinatsika moti ndi anthu 64 okha pa 100 alionse amene ankapitabe kuzipembedzo zawo.

TUNISIA

Mu 2013, anthu 60 pa 100 alionse m’dziko la Tunisia ananena kuti anasiya kupita ku mzikiti. M’malomwake amangopemphera kunyumba kwawo. Ananena kuti amachita zimenezi poopa kuphedwa ndi zigawenga.

UNITED STATES

Chiwerengero cha anthu amene amapita kuchipembedzo chawo ku United States chatsika. Mwachitsanzo mu 2005, anthu 73 pa 100 alionse ankapita kuzipembedzo zawo. Koma pofika mu 2012, ndi anthu 60 okha pa 100 alionse amene ankapitabe kuzipembedzo zawo ndipo mmodzi pa 5 alionse anati sakonda zopemphera. Komanso atafunsa anthu omwe sanakwanitse zaka 30, anapeza kuti mmodzi pa anthu atatu alionse sakonda zopemphera. Zikuoneka kuti chaka chilichonse matchalitchi ambiri akumatsekedwa chifukwa chosowa anthu.

VIETNAM

Kuyambira mu 2005 kufika mu 2012, chiwerengero cha anthu amene amapita kuchipembedzo chawo ku Vietnam chatsika kuchokera pa anthu 53 kufika pa anthu 30 pa 100 alionse.

Ziwerengero za mayikowa, kupatulapo dziko la Tunisia, zatengedwa kuchokera pa lipoti la kafukufuku amene bungwe lina linachita. Kafukufukuyu anachitika m’mayiko 57, ndipo anthu amene amakhala m’mayikowa ndi oposa 73 peresenti ya anthu omwe ali padziko lonse. —2012 Global Index of Religion and Atheism.

Mapu osonyeza dziko la Australia, France, Ireland, Japan, South Africa, Tunisia, United States ndi Vietnam

Kodi Vuto Lagona Pati?

Anthu ambiri akumaona kuti zipembedzo zawagwiritsa fuwa la moto. Akumati akaganizira zimene anthu opemphera akuchita, akumakhumudwa kwambiri. Mwachitsanzo, anthu opemphera ndi amene akumakhala patsogolo kuchita zachiwawa komanso kupha anzawo. M’malo moti akhale zitsanzo zabwino, akuluakulu a zipembedzo akumachita khalidwe la chiwerewere mopanda manyazi m’pang’ono pomwe. Ndiyeno anthu akaona zimenezi, akumaganiza zongodula phazi. Koma panopa tiyeni tione zifukwa zinanso zimene zikuchititsa kuti anthu asiye kupita ku zipembedzo zawo.

  • Mayiko ambiri akutukuka: Lipoti la bungwe lina linanena kuti, “Munthu akayamba kulemera amaiwala Mulungu.” (Global Index of Religion and Atheism) Zimenezi n’zoona chifukwa m’mayiko ambiri omwe zinthu zikuyenda bwino, anthu ambiri akusiya kupemphera. Pulofesa wina wa zachuma, dzina lake John V. C. Nye, anati: “M’mayiko ena anthu ndi olemera kwambiri moti chuma chawo chikumaposa cha mafumu omwe anali olemera kwambiri zaka 200 zapitazo.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza,’ anthu adzakhala okonda ndalama ndiponso okonda zosangalatsa kuposa Mulungu komanso anthu anzawo. (2 Timoteyo 3:1-5) Munthu wina wolemba Baibulo ankadziwa kuti nthawi zina kukhala ndi chuma kumapangitsa munthu kuiwala Mulungu. Choncho anapempha Yehova Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma . . . kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani.”—Miyambo 30:8, 9.

  • Anthu sakusangalala ndi makhalidwe komanso miyambo ya zipembedzo zawo: Anthu ambiri, makamaka achinyamata, akumaona kuti kupemphera n’kutaya nthawi. Koma pali anthu enanso omwe ayamba kukayikira zipembedzo zawo. Munthu wina wa ku Scotland, dzina lake Tim Maguire, anati: “Anthu ambiri asiya kupemphera chifukwa akhumudwa ndi zimene zipembedzo zawo zikuchita. Akuona kuti atsogoleri a zipembedzo zawo, omwe amayenera kukhala zitsanzo zabwino, ndi amenenso ali atambwali otheratu.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti m’masiku otsiriza kudzabwera aneneri onyenga. Koma kodi aneneri onyengawa akanawadziwa bwanji? Anawauza kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.” (Mateyu 7:15-18) “Zipatso zopanda pake” zimenezi ndi monga kulowerera ndale komanso kulimbikitsa makhalidwe oipa monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Yohane 15:19; Aroma 1:25-27) M’malo mophunzitsa Mawu a Mulungu, aneneri onyengawa amangokhalira kuphunzitsa zinthu za m’mutu mwawo komanso kuchita miyambo yachikunja. (Mateyu 15:3, 9) Komatu Yesu anawauza kuti adyetse nkhosa zake. (Yohane 21:17) Ndiye m’malo mophunzitsa anthu mawu a Mulungu, akumangowamata phula m’maso.

  • Atsogoleri ambiri a zipembedzo ndi adyera: Lipoti lina linanenanso kuti, anthu ambiri akusiya kupemphera chifukwa akuona kuti nkhani yaikulu m’zipembedzomu ikumangokhala perekaniperekani. (Pew Research Center) Kuwonjezera pamenepa, atsogoleri ambiri a zipembedzo akukhala moyo wofewa kwambiri, chonsecho nkhosa zawo zili mu umphawi wadzaoneni. Mwachitsanzo, mumzinda wina ku Germany muli Akatolika ambiri osauka. Koma Bishopu wawo ndi wolemera kwambiri moti anthu akumudzudzula chifukwa akuona kuti amawadyera masuku pamutu. Lipoti linanso linanena kuti ku Nigeria, “kuli anthu 100 miliyoni omwe amasowa ndi ya mchere yomwe, koma abusa a matchalitchi awo amachita kusambira mu ndalama.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu sitichita nawo malonda.” (2 Akorinto 2:17) Pa nthawi imene Paulo ankalemba mawu amenewa, n’kuti ali ndi udindo waukulu kwambiri mumpingo. Koma m’malo momangodikira kuti anthu azimupatsa ndalama, Paulo ankagwira ntchito mwakhama. Ankachita zimenezi kuti asapatse ena chintchito choti azimusamalira. (Machitidwe 20:34) Zimene ankachitazi zikusonyeza kuti ankamvera zimene Yesu ananena zoti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:7, 8.

Zimenezi n’zimenenso a Mboni za Yehova amachita. Amagawira anthu mabuku, magazini, timapepala komanso zinthu zina zofotokoza mfundo za m’Baibulo kwaulere. Komanso samatolera chakhumi kapena kuyendetsa mbale ya chopereka. Ndalama zimene amayendetsera ntchito yawo zimakhala zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.—Mateyu 6:2, 3.

Baibulo Linaneneratu Kuti Anthu Ambiri Adzasiya Kupemphera

Zaka zapitazo, palibe amene ankalota kuti zimenezi zingachitike. Komatu Mulungu ananeneratu m’Baibulo kuti anthu adzasiya kupita kuzipembedzo zawo. Anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa ponena za zipembedzo zonse zabodza. Ananena kuti zipembedzozi zili ngati “hule” ndipo anazitchula ndi dzina lakuti, “Babulo Wamkulu.”—Chivumbulutso 17:1, 5.

M’pake kuti anazitchula kuti “hule,” chifukwa hule sakhala ndi mwamuna mmodzi. Nazonso zipembedzozi zimanena kuti zimalambira Mulungu yekha basi, chonsecho zimagwirizana kwambiri ndi atsogoleri andale kuti zikhale ndi mphamvu komanso kuti zipeze chuma. N’chifukwa chake lemba la Chivumbulutso 18:9 limanena kuti: ‘Mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.’ Dzina lakuti “Babulo Wamkulu” ndi loyenereranso, chifukwa linachokera ku dzina la mzinda wakale wa Babulo. Anthu a mumzindawu ankakhulupirira zinthu zabodza komanso ankachita zamizimu. Nazonso zipembedzozi zimatchedwa Babulo Wamkulu chifukwa zimaphunzitsa zinthu zabodza monga Utatu, kukhulupirira mizimu komanso zoti mzimu umapitirizabe kukhala ndi moyo munthu akafa.a—Yesaya 47:1, 8-11.

Mzinda wakale wa Babulo unali wotetezeka kwambiri chifukwa unazunguliridwa ndi mtsinje wa Firate. Ndiye Amedi ndi Aperisi anaphwetsa mtsinjewu ndipo anadutsa bwinobwino n’kulanda mzindawu popanda wolimbana naye. (Yeremiya 50:1, 2, 38) Tangoganizani, asilikaliwa analanda mzindawo usiku umodzi wokha basi.—Danieli 5:7, 28, 30.

Zipembedzo zabodza zomwe ndi Babulo Wamkulu zilinso “pamadzi ambiri.” Baibulo limanena kuti madzi amenewa ‘akuimira mitundu ya anthu komanso makamu.’ (Chivumbulutso 17:1, 15) Ndiyeno linaneneratu kuti madziwa adzauma ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti Babulo Wamkulu watsala pang’ono kuwonongedwa. (Chivumbulutso 16:12; 18:8) Koma kodi Babulo Wamkuluyu adzawonongedwa ndi ndani? Adzawonongedwa ndi olamulira a dzikoli. Zimenezi zingaoneke zosatheka chifukwa panopa a zipembedzo ndi olamulira a dzikoli, ali khethekhethe. Koma mofanana ndi Babulo wakale, yemwe ankaoneka ngati wosagonjetseka, Babulo Wamkuluyu adzawonongedwa ndithu, ndipo olamulirawa adzamutembenukira poyerayera n’kumuwononga.—Chivumbulutso 17:16, 17.b

Bambo akuwerenga Baibulo ndipo akuganizira za kuphwa kwa madzi a mtsinje womwe unazungulira mzinda wa Babulo komanso anthu akuchoka m’Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zabodza

Kuphwa kwa madzi komwe kunachitika ku Babulo wakale, kukuimira kuchoka kwa anthu m’Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza

“Tulukani Mwa Iye”

Monga taonera, Babulo Wamkulu yemwe akuimira zipembedzo zonse zabodza, awonongedwa posachedwapa. Choncho Mulungu akuchenjeza anthu kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4) Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu akufuna kuthandiza anthu a mitima yabwino omwe akupusitsidwa ndi zipembedzo zabodza kuti asakumane ndi tsoka limeneli.

A Gaffar komanso a Hediye, omwe tawatchula kumayambiriro aja, anamvera chenjezo limeneli. A Gaffar asanaphunzire Baibulo, ankalambira Mulungu chifukwa choopa kuti adzawawotcha kumoto. Koma ataphunzira Baibulo ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri nditazindikira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi komanso kuti amafuna tizimumvera chifukwa chomukonda, osati chifukwa cha mantha.” (1 Yohane 4:8; 5:3) Nawonso a Hediye, mtima unakhala pansi atadziwa kuti si Mulungu amene anapangitsa kuti akhale amasiye komanso kuti sanalemberetu zonse zimene zidzachitike pa moyo wawo. Anasangalalanso kwambiri atawerenga lemba la Yakobo 1:13, lomwe limanena kuti Mulungu sayesa munthu ndi zinthu zoipa. Choncho a Gaffar komanso a Hediye, atazindikira kuti ali m’chipembedzo chabodza, anathawa m’Babulo Wamkulu n’kulowa m’chipembedzo choona.—Yohane 17:17.

Ndiyetu anthu onse amene akutuluka m’Babulo Wamkulu, n’kuyamba ‘kulambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi,’ akuchita zinthu mwanzeru kwambiri. (Yohane 4:23) Posachedwapa, anthu amenewa adzasangalala kukhala ‘m’dziko lapansi lodzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.’—Yesaya 11:9.

Popeza Mulungu “sanganame,” sitikukayikira kuti zipembedzo zonse zabodza zidzawonongedwa. (Tito 1:2) Koma chipembedzo choona chidzakhalapo mpaka kalekale.

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yonena za Babulo Wamkulu, zomwe zimachitika munthu akamwalira, kukhulupirira mizimu komanso nkhani zina, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.

b Onani nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena—Kodi Dzikoli Lidzathadi?” patsamba 14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena