NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUKHALA NDI BANJA LOSANGALALA?
Kodi Mungatani KutiMuzigwirizana Ndi Anthu a M’banja Lanu?
KODI mukuganiza kuti Baibulo lingatithandize kuti tizigwirizana ndi anthu a m’banja lathu? Tiyeni tione zimene anthu ena ananena komanso mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.
MFUNDO ZA M’BAIBULO ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA MWAMTENDERE M’BANJA
MUZICHITA ZINTHU MOGANIZIRANA.
“Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:3, 4.
“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akolose 3:13.
Anthu amene atchulidwa pamwambawa ndi ena mwa anthu amene Baibulo lawathandiza kuti azikhala mwamtendere ndi anthu a m’banja lawo.a Anthuwa amayesetsa kuchita mbali yawo ngakhale kuti anthu ena a m’banja lawo ndi ovuta. Zimenezi zimawathandiza kuti azikhala osangalala chifukwa Baibulo limati: “Olimbikitsa mtendere amasangalala.”—Miyambo 12:20.
a Kuti mudziwe mfundo zina zomwe zingathandize kuti banja lanu lizikhala losangalala, werengani mutu 14 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka pa webusaiti ya www.pr418.com/ny. Pa webusaitiyi palinso nkhani zina zothandiza mabanja. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MALANGIZO OTHANDIZA BANJA LONSE.