Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 2 tsamba 3-7
  • Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?
  • Galamukani!—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Makhalidwe Abwino Komanso Kudziwa Mulungu Molondola
  • Baibulo Limafotokoza Mmene Mavuto Anayambira
  • Baibulo Limanena Kuti Mavuto Adzatha
  • Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?
    Galamukani!—2007
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 2 tsamba 3-7
Bambo akuwerenga Baibulo

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?

Baibulo linalembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Kuyambira nthawi imeneyo, mabuku ena ambirimbiri akhala akulembedwa koma pano sapezekanso. Komatu si mmene ziliri ndi Baibulo. Tiyeni tione mfundo zotsatirazi.

  • Olamulira ambiri anayesetsa kuchita zinthu zoti Baibulo lisamafalitsidwenso, koma sizinatheke. Mwachitsanzo, buku lina linanena kuti m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, m’mayiko ena omwe amati ndi achikhristu, “munthu amene anali ndi Baibulo lachinenero cha anthu wamba kapena amene ankaliwerenga, ankamuona kuti ndi wampatuko ndiponso woukira boma.” (An Introduction to the Medieval Bible) Ndipotu anthu ena omwe ankamasulira Baibulo kapenanso amene ankalimbikitsa anthu kuliphunzira, anaika moyo wawo pangozi ndipo ena anaphedwa.

  • Komabe, padziko lonse palibenso buku lina limene limapezeka ndi anthu ambiri kuposa Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti Mabaibulo pafupifupi 5 biliyoni kapena mabuku ake ena, asindikizidwa m’zinenero zoposa 2,800. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi mabuku ena monga olimbikitsa nzeru za anthu, a sayansi ndi ena ambiri chifukwa ndi anthu ochepa chabe amene amapezeka nawo ndipo pakapita nthawi anthu ambiri sawagwiritsanso ntchito.

  • Baibulo lathandiza kuti zinenero zina zisasinthe kwambiri. Mwachitsanzo, chinenero cha ku Germany chinatengera kwambiri Chijeremani cha m’Baibulo limene Martin Luther anamasulira. Anthu amati Baibulo la King James Version lomwe linatuluka koyamba “mwina ndi buku [la Chingelezi] limene lathandiza kwambiri kuti chinenerochi chisasinthe.”

  • Buku lina linanena kuti Baibulo “linathandiza kwambiri anthu a m’mayiko a ku Europe komanso North America osati pa nkhani za kupembedza zokha, komanso za chikhalidwe, luso losiyanasiyana, malamulo, ndale ndiponso zinthu zina zambiri.”—The Oxford Encyclopedia of the Books of the Bible.

Zimenezi ndi zitsanzo zochepa chabe zomwe zimasiyanitsa Baibulo ndi mabuku ena. Koma kodi n’chifukwa chiyani Baibulo limapezeka ndi anthu ambiri? Nanga n’chifukwa chiyani anthu analolera kuika moyo wawo pangozi chifukwa cha Baibulo? Zifukwa zina n’zakuti: Baibulo limathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kudziwa Mulungu molondola. Limawathandizanso kudziwa mmene mavuto anayambira. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti limathandizanso kudziwa kuti mavutowa adzatha komanso limafotokoza mmene adzathere.

MFUNDO ZACHIDULE

Baibulo lotsegula

Baibulo lili ndi mabuku okwana 66, ndipo linatenga zaka pafupifupi 1,600 kuti lilembedwe.

Mulungu anagwiritsa ntchito anthu 40 kuti alembe Baibulo. Ena mwa anthuwa anali alimi, asodzi, oweruza, mafumu ndiponso oimba.

Mfundo yaikulu m’Baibulo ndi yokhudza Ufumu wa Mulungu umene ndi boma lakumwamba lomwe lidzalamulire dziko lapansi. (Danieli 2:44; 7:13, 14) Ufumuwu udzathetsa zoipa zonse kuphatikizapo imfa ndipo udzagwirizanitsa anthu. Mlengi wathu Yehova Mulungu ndi amene adzachita zonsezi.—1 Akorinto 15:24-26.

Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Makhalidwe Abwino Komanso Kudziwa Mulungu Molondola

Maphunziro ndi ofunika ndithu. Koma nyuzipepala ina inanena kuti, “Maphunziro . . . amene amachititsa munthu kupatsidwa mayina aulemu . . . sathandiza munthu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.” (Ottawa Citizen) Ndipotu zimenezi n’zoona chifukwa kafukufuku wina amene bungwe lina linachita anasonyeza kuti anthu ambiri ophunzira kwambiri, kuphatikizaponso akuluakulu a bizinesi komanso a boma amakonda kuchita chinyengo, kunama, ndiponso kuba. Ndipo zimenezi “zimachititsa kuti anthu asamawakhulupirire.”

Koma Baibulo limatithandiza kwambiri pa nkhani za makhalidwe abwino komanso kuti tidziwe Mulungu. Limatithandizanso kuzindikira zinthu “zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.” (Miyambo 2:9) Mwachitsanzo, bambo wina wazaka 23, dzina lake Stephen, nthawi ina anamangidwa ku Poland. Ali m’ndende anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kutsatira zimene ankaphunzirazo. Iye ananena kuti: “Panopa ndikumvetsa bwino zimene amatanthauza akamati, ‘Uzilemekeza atate ako ndi amayi ako.’ Ndaphunziranso kumaugwira mtima makamaka ndikakwiya kwambiri.”—Aefeso 4:31; 6:2.

Stephen anasangalala kwambiri ndi mfundo ya pa Miyambo 19:11, yakuti: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” Panopa akakumana ndi vuto linalake lalikulu amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kupeza njira yabwino yothetsera vutolo. Iye ananenanso kuti: “Ndaona kuti Baibulo ndi buku lomwe lili ndi malangizo abwino kwambiri.”

Chitsanzo china ndi Maria, yemwe ndi wa Mboni za Yehova. Tsiku lina iye ananyozedwa ndi mayi wina yemwe amadana ndi a Mboni, anthu ambiri akuona. Ngakhale kuti anamulalatira kwambiri, Maria sanabwezere ndipo anangopitiriza ulendo wake. Mayi wachipongweyo anachita manyazi kwambiri ndi zimene anachitazi ndipo kenako anayamba kufunafuna a Mboni za Yehova. Patapita mwezi umodzi mayiyu anakumana ndi Maria ndipo anamukumbatira n’kumupepesa. Mayiyu anazindikira kuti Maria sanabwezere zachipongwe zija chifukwa cha zimene amakhulupirira. Zimenezi zinachititsa kuti iye ndi anthu 5 a m’banja lake, ayambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Yesu ananena kuti nzeru imatsimikiziridwa ndi ntchito zake. (Luka 7:35) Choncho palibe amene angatsutse kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza. Baibulo limatithandiza kukhala anthu abwino. Ndipo mfundo zake “zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu,” ‘zimasangalatsa mtima’ ndiponso zimathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukonda Mulungu.—Salimo 19:7, 8.

Baibulo Limafotokoza Mmene Mavuto Anayambira

Anthu ofufuza akafuna kudziwa zambiri za mliri wa matenda enaake, amafufuza chimene chayambitsa mliriwo. Mofananamo, kuti timvetse chifukwa chake anthu amavutika, tiyenera kudziwa chomwe chinayambitsa mavutowo. Baibulo ndi lothandiza kwambiri chifukwa limatiuza mmene mavuto anayambira komanso mmene tinalengedwera.

Buku la Genesis limanena kuti mavuto a anthu anayamba pamene Adamu ndi Hava anakana kumvera Mulungu. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti iwo anafuna kuti azisankha okha zabwino kapena zoipa m’malo modalira Mulungu yemwe anawalenga. (Genesis 3:1-7) N’zomvetsa chisoni kuti kungochokera nthawi imeneyo, anthu anayamba kukhala ndi mtima wosafuna kuuzidwa zochita. Zimenezi zinachititsa kuti anthu asakhale ndi ufulu weniweni, azikangana, aziponderezana ndiponso kuti makhalidwe aipe kwambiri. (Mlaliki 8:9) Izi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu . . . alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Koma n’zosangalatsa kuti mavuto onse atha posachedwapa.

Baibulo Limanena Kuti Mavuto Adzatha

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amakonda anthu omwe amalemekeza ulamuliro komanso mfundo zake. Limatitsimikiziranso kuti Iye sadzalekerera anthu oipa kuti apitirize kubweretsa mavuto padzikoli ndipo limanena kuti, oipa “adzadya zipatso za njira yawo.” (Miyambo 1:30, 31) Koma limanenanso kuti “anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.

Baibulo lotsegula lili pambali pa kapu ya khofi

“Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:3, 4.

Mulungu adzagwiritsa ntchito ‘Ufumu wake’ kuti akwaniritse zimene ankafuna zoti anthu azikhala mwamtendere padzikoli. (Luka 4:43) Ufumu umenewu udzakhala boma lolamulira dziko lonse ndipo udzasonyeza kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira anthu. M’pemphero lachitsanzo, Yesu anasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli. Iye anati: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”—Mateyu 6:10.

Mu Ufumu umenewu, anthu onse azidzachita zimene Mulungu akufuna podziwa kuti ndi Mlengi wawo komanso kuti ndiye woyenera kulamulira. Mavuto monga katangale, dyera, umphawi, kusankhana mitundu ndiponso nkhondo adzatha. Padziko lonse padzakhala boma limodzi, ndipo anthu onse azidzatsatira mfundo zofanana za makhalidwe abwino komanso azidzapembedza Mulungu m’njira yofanana.—Chivumbulutso 11:15.

Kuti mudzakhale nawo m’dziko latsopanoli, muyenera kuphunzira zimene Mulungu amafuna. Lemba la 1 Timoteyo 2:3, 4 limati: “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” Muyenera kudziwa malamulo ndiponso mfundo zimene Ufumu wa Mulungu uzidzayendera. Zina mwa mfundo zimenezi ndi zomwe Yesu Khristu ananena pa ulaliki wa paphiri. (Mateyu, chaputala 5 mpaka 7) Mukamawerenga machaputala amenewa muziganizira mmene moyo udzakhalire munthu aliyense akamadzatsatira malangizo anzeru omwe Yesu anaperekawa.

Malinga ndi mfundo zimene zafotokozedwa m’nkhaniyi, kodi n’zodabwitsa kuti Baibulo lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse? Ayi. Tikutero chifukwa uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu. Ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amafunitsitsa kuti anthu amitundu ndiponso zinenero zonse aphunzire za Iye n’kudzasangalala ndi madalitso amene Ufumu wake udzabweretse.—Machitidwe 10:34, 35.

Nyenyezi zikuonekera kuthambo

Baibulo limanena kuti pali malamulo omwe amatsogolera zinthu zakuthambo

BUKU LIMENE LIMALETSA KUCHITA ZAMIZIMU

Buku lina limanena kuti: “Anthu akale ankaganiza kuti chilengedwe chonse chimayendetsedwa ndi milungu inayake yosadziwa chilichonse.” (Encyclopedia of Science and Religion) Koma Baibulo limanena kuti chilengedwechi chimayendetsedwa ndi malamulo. Mwachitsanzo, zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, linanena kuti pali malamulo amene amayendetsa zinthu zakuthambo ndi zapadziko lapansili. (Yobu 38:33) Lemba la Yeremiya 31:35, limanenanso za malamulo a “mwezi” ndiponso a “nyenyezi.” Choncho anthu amene anazindikira zimenezi ankapewa kulambira mafano komanso kuchita zamizimu.—Yobu 31:26-28; Yesaya 47:1, 13.

BUKU LIMENE LIMANENA ZINTHU MOSABISA

Chosangalatsa kwambiri n’choti anthu omwe analemba Baibulo analemba zinthu mosabisa moti ankalemba ngakhale zomwe iwowo ankalakwitsa. Mwachitsanzo, Mfumu Davide inachita chigololo ndi Batiseba. Davide sanabise tchimo lakeli ndipo ananena kuti: “Ndachita chinthu choipa pamaso panu.” (Salimo 51:4) Nayenso mtumwi Yohane ananena kuti anagwadirapo mngelo kawiri konse pofuna kumulambira. Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Samala! Usatero ayi! . . . Lambira Mulungu.” (Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9) Mosiyana ndi anthu akale omwe analemba mabuku, olemba Baibulo okha ndi amene analemba zinthu mosabisa.

BUKU LOTHANDIZA KUTI TISAMAVUTIKE MAGANIZO

Baibulo limatilimbikitsa kukhala ndi makhalidwe monga chikondi ndiponso kukhululukira ena. Makhalidwewa angatithandize kuti tisamavutike maganizo. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 4:32 limati: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”

Kabuku kena komwe kanafalitsidwa ndi achipatala cha Mayo, ku United States kanati: “Ngati simukhululukira ena, inuyo ndi amene mumavutika kwambiri.” Kabukuka kananenanso kuti kukhululukira ena “kungathandize kuti munthu azikhala bwino ndi ena, akhale wokonda Mulungu komanso woganiza bwino. Munthu wotereyu sakhala ndi nkhawa kwambiri, sapanikizika, amakhala wodekha, magazi amayenda bwino m’thupi mwake, savutika maganizo ndiponso sakhala ndi vuto lomwa mowa kapena mankhwala osokoneza bongo pofuna kuthetsa mavuto.”

BUKU LIMENE LIMAYANKHA MAFUNSO AKULUAKULU OKHUDZA MOYO

Mwana wosabadwa

Mwana wosabadwa

Sayansi ingatithandize kupeza mayankho a mafunso ambiri, koma singayankhe onse. Buku lina linanena kuti: “Asayansi ambiri, madokotala ndiponso akatswiri ena amavomereza kuti sayansi singayankhe mafunso okhudza makhalidwe ndiponso chipembedzo.”—Biotechnology—Changing Life Through Science.

  • SAYANSI INGAFOTOKOZE malamulo amene chilengedwe chimayendera pogwiritsa ntchito masamu, koma siingatiuze chifukwa chimene zinthu zinalengedwera komanso chifukwa chimene chilengedwecho chimagwiritsira ntchito malamulo.

  • SAYANSI INGAFOTOKOZE mmene ziwalo zoberekera zimagwirira ntchito koma siingatithandize kuchita zinthu mwanzeru pa nkhani ya kugonana.

  • SAYANSI INGAFOTOKOZE mmene mwana wosabadwa amakulira m’mimba mwa mayi ake, koma siingakuthandizeni kudziwa kuti kuchotsa mimba n’kulakwa.

Baibulo limayankha mafunso okhudza nkhani zimenezi ndi zina zambiri. Choncho, limatithandiza kumvetsa “zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”​—Miyambo 2:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena