Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp24 No. 1 tsamba 6-9
  • Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • TIMAFUNIKIRA MALANGIZO OCHOKERA KWA MULUNGU
  • BAIBULO LIMATIUZA ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI TIZICHITA
  • Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Kutsogoleredwa ndi Nzeru Zapamwamba Kuposa Zachibadwa
    Galamukani!—2007
  • Mungapeze Thandizo
    Galamukani!—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
wp24 No. 1 tsamba 6-9

Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera

Tikamasankha zoyenera kuchita pa nkhani ya makhalidwe abwino, sitingakhale otsimikiza kuti zimene tasankhazo zidzatiyenderadi bwino ngati tikungotsatira maganizo athu komanso a anthu ena. Tikutero chifukwa cha zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi nkhani zinanso zambiri. Baibulo lili ndi malangizo othandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera ndipo timakhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala tikamatsatira malangizo amenewa.

TIMAFUNIKIRA MALANGIZO OCHOKERA KWA MULUNGU

Baibulo limasonyeza kuti Yehovaa Mulungu analenga anthu n’cholinga choti azipatsidwa malangizo ndi iyeyo, osati kuti azidzitsogolera okha. (Yeremiya 10:23) N’chifukwa chake iye anapereka malangizo okhudza makhalidwe abwino ndipo malangizowa amapezeka m’Baibulo. Iye amatikonda kwambiri ndipo amafuna kutiteteza kuti tisakumane ndi mavuto chifukwa chosankha zinthu molakwika. (Deuteronomo 5:29; 1 Yohane 4:8) Koposa zonse, monga Mlengi wathu, iye ali ndi nzeru komanso amadziwa malangizo abwino kwambiri omwe angatithandize pa moyo wathu. (Salimo 100:3; 104:24) Komabe, Mulungu sakakamiza anthu kuti aziyendera mfundo zake.

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava, omwe anali anthu oyambirira, zinthu zonse zofunikira kuti azikhala moyo wosangalala. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 15) Anawapatsanso malangizo osavuta ndipo ankayembekezera kuti savutika kuwamvera. Komabe, iye anawapatsa ufulu woti akhoza kusankha kutsatira malangizo ake kapena ayi. (Genesis 2:9, 16, 17) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kuyendera mfundo zawo m’malo moyendera mfundo za Mulungu. (Genesis 3:6) Ndiye kodi zinthu zinawayendera bwanji? Kodi anthu padzikoli zinthu zikuwayendera bwino chifukwa choti akusankha okha zoyenera ndi zosayenera? Ayi ndithu. Anthu akhala akukana kutsatira mfundo za Mulungu kwa zaka zambiri, ndipo zotsatira zake ndi zakuti alibe mtendere komanso sakukhala mosangalala.—Mlaliki 8:9.

Baibulo lili ndi malangizo omwe timafunikira kuti tizitha kusankha zinthu mwanzeru posatengera mmene tilili kapena komwe timachokera. (2 Timoteyo 3:16, 17; onani bokosi lakuti “Buku la Anthu Onse.”) Taonani mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Onani chifukwa chake Baibulo ndi loyeneradi kutchedwa kuti “Mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13. Onerani vidiyo yakuti, Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani? pa jw.org.

BUKU LA ANTHU ONSE

Tonsefe tingayembekezere kuti Mlengi wanzeru komanso wachikondi atipatse mfundo za makhalidwe abwino zimene amafuna kuti aliyense aziyendera. Taonani maumboni otsatirawa:

Anthu amitundu yosiyanasiyana akuwerenga Baibulo. Mabaibulo osindikizidwa komanso apazipangizo zamakono akuoneka m’munsi mwa chithunzi cha anthu.
  • Zinenero zoposa 3,500 Baibulo lathunthu kapena mbali zake zina likupezeka mu zinenero zimenezi ndipo ndi buku limene lamasuliridwa mu zinenero zambiri kuposa buku lina lililonse.

  • Mabaibulo opitirira 5,000,000,000 asindikizidwa ndipo ndi buku limene likupezeka ndi anthu ambiri padzikoli kuposa buku lina lililonse.

Baibulo ndi buku la anthu onsedi chifukwa silimakondera anthu a mtundu, dziko kapenanso chikhalidwe chinachake.

Werengani Baibulo pa jw.org lomwe likupezeka mu zinenero zoposa 250

Bambo akuwerenga Baibulo ndipo akuloza pomwe akuwerenga ndi chala chake.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA BAIBULO?

Anthu ena amanena kuti m’Baibulo simungapezeke malangizo abwino pa nkhani ya makhalidwe abwino. Iwo amapereka zifukwa zotsatirazi:

Zimene amanena: “Baibulo limadzitsutsa.”

Zoona zake: Tikhoza kumvetsa mfundo zomwe zimaoneka ngati zimatsutsana powerenga nkhani yonse, kufufuza mfundo zolondola zokhudza mbiri ndi chikhalidwe cha pa nthawiyo komanso kuganizira zinthu zimene wolemba anaona.

Kuti muone zitsanzo zina pa nkhaniyi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Nkhani za M’Baibulo Zimatsutsana?” pa jw.org.

Zimene amanena: “Anthu amene amanena kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo amachita zinthu zoipa, choncho si buku lomwe lingatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino.”

Zoona zake: Si bwino kuimba mlandu Baibulo chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu omwe amakana kutsatira malangizo opezeka m’Baibulo. Ndipo Baibulo linaneneratu kuti anthu ambiri kuphatikizapo atsogoleri a chipembedzo omwe amanena kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo, azidzachita zinthu zosemphana ndi zimene limanena. Limanenanso kuti chifukwa cha zimenezi, “anthu azidzalankhula monyoza” zimene Baibulo limaphunzitsa.—2 Petulo 2:1, 2.

Kuti muone chitsanzo chosonyeza kuti atsogoleri ambiri achipembedzo sachita zimene Baibulo limaphunzitsa, werengani nkhani yakuti, “Kodi Chipembedzo Chasanduka Bizinezi Yotentha?” pa jw.org.

Zimene amanena: “Anthu amene amayendera mfundo za m’Baibulo salemekeza anthu amene amakhulupirira zosiyana ndi iwowo.”

Zoona zake: Baibulo limalimbikitsa anthu kuti azilemekezana. Silimalimbikitsa kuti anthu. . .

  • azidziona kuti ndi apamwamba kuposa ena.—Afilipi 2:3.

  • asamalemekeze anthu amene amakhulupirira zosiyana ndi iwowo.—1 Petulo 2:17.

  • azikakamiza anthu ena kuti aziyendera maganizo awo.—Mateyu 10:14.

Baibulo limanena kuti nthawi zonse Mulungu amachitira anthu zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi ndipo amafuna kuti nafenso tizichitira ena zomwezo.—Aroma 9:14.

Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi onani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limathandiza Bwanji Anthu Kukhala Ololera?” pa jw.org.

BAIBULO LIMATIUZA ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI TIZICHITA

Baibulo lili ndi nkhani zolondola zofotokoza zimene Yehova wakhala akuchitira anthu kungoyambira pamene anawalenga. Zimene limanena zimatithandiza kuzindikira zinthu zimene Mulungu amaona kuti ndi zoyenera ndi zosayenera, zothandiza kapenanso zimene zingatibweretsere mavuto. (Salimo 19:7, 11) Mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo zimakhala zolondola nthawi zonse ndipo zimatithandiza kusankha mwanzeru pa nkhani ya makhalidwe abwino.

Mwachitsanzo, taonani malangizo opezeka pa Miyambo 13:​20, omwe amati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mfundo imeneyi si yachikale ndipo ikugwirabe ntchito mpaka pano, mofanana ndi mmene zinaliri pa nthawi imene inalembedwa. Baibulo lili ndi mfundo zothandiza zambiri. Onani bokosi lakuti, “Nzeru za M’Baibulo Ndi Zothandiza Mpaka Kalekale.”

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingadziwe bwanji kuti malangizo a m’Baibulo okhudza makhalidwe abwino ndi othandizadi masiku ano? Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene linathandizira anthu ena.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.

NZERU ZA M’BAIBULO NDI ZOTHANDIZA MPAKA KALEKALE

Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, mfundo zake ndi zothandizabe mpaka pano. Anthu analengedwa kuti azifuna kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala ndipo zimenezi sizinasinthe. (Mlaliki 1:9) Tikamatsatira nzeru zopezeka m’Baibulo tikhoza kukwanitsa kukhala ndi moyo woterewu.

Kuchita Zinthu Moona Mtima

  • “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

  • “Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira.”—Aefeso 4:28.

Kukhala Bwino Ndi Ena

  • “Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.” —1 Akorinto 10:24.

  • “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”—Akolose 3:13.

Kusankha Zochita

  • “Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—Miyambo 14:15.

  • “Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala, koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.”—Miyambo 22:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena