Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 3 tsamba 12-14
  • Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUMENE TINGAPEZE MALANGIZO ODALIRIKA
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Galamukani!—2017
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 3 tsamba 12-14
Munthu akuwerenga Baibulo.

Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?

Monga mmene taonera munkhani zapitazi, anthu akhala akuganiza kuti zinthu monga kukhulupirira mwayi, maphunziro, chuma komanso kungokhala munthu wabwino n’zimene zingawathandize kukhala ndi tsogolo labwino. Kugwiritsa ntchito njira zimenezi kuli ngati kupita kumalo amene sitikuwadziwa pogwiritsa ntchito mapu olakwika. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe malangizo odalirika otithandiza kudziwa za tsogolo lathu? Tiyeni tione.

KUMENE TINGAPEZE MALANGIZO ODALIRIKA

Tikamafuna kusankha zochita pa nkhani inayake, nthawi zambiri timafunsira nzeru kwa munthu wamkulu komanso wanzeru kuposa ifeyo. Mofananamo, tingapeze malangizo odalirika okhudza tsogolo lathu kuchokera kwa winawake yemwe ndi wamkulu komanso wanzeru kuposa ifeyo. Malangizo amenewa tingawapeze m’buku lomwe linayamba kulembedwa zaka 3,500 zapitazo. Buku limeneli limatchedwa Baibulo.

Kodi Baibulo ndi lodalirika chifukwa chiyani? Baibulo ndi buku lodalirika chifukwa amene analilemba ndi wamkulu komanso wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse. Iye amatchedwa “Wamasiku Ambiri” ndipo wakhalapo “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Danieli 7:9; Salimo 90:2) Iye ndi “Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi.” (Yesaya 45:18) Kudzera m’buku lakeli, amatiuza kuti dzina lake ndi Yehova.​—Salimo 83:18.

Baibulo silinena kuti chikhalidwe kapena mtundu winawake wa anthu ndi wabwino kuposa mitundu ina. Zili choncho chifukwa tinalengedwa ndi Mulungu yemwe analenga anthu onse. Malangizo ake ndi othandiza nthawi zonse ndipo athandiza kwambiri anthu m’mayiko onse. Baibulo limapezeka m’zinenero zambiri ndipo lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse.a Choncho munthu wina aliyense akhoza kuliwerenga n’kupindula ndi malangizo ake. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Limati:

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mofanana ndi kholo limene limakonda komanso kupereka malangizo kwa ana ake, Yehova Mulungu yemwe ndi atate wachikondi amatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Choncho mungakhulupirire Mawu ake chifukwa chakuti iyeyo ndi amene anatilenga ndipo amadziwa bwino zinthu zimene zingatithandize kuti tizisangalala.

BAIBULO NDI LODALIRIKA

Zithunzi: 1. Munthu ali musitima ndipo akuwerenga Baibulo pafoni yake. 2. Pafoni ya munthuyo pakuoneka Baibulo.

Baibulo ndi buku lodalirika ponena zam’tsogolo chifukwa zaka 2,000 zapitazo, linaneneratu zomwe zikuchitika padzikoli komanso makhalidwe oipa amene anthu akusonyeza masiku ano.

ZOCHITIKA PADZIKOLI

“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.”​—LUKA 21:10, 11.

MAKHALIDWE A ANTHU

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”​—2 TIMOTEYO 3:1-4.

Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinatheka bwanji kuti Baibulo lilosere zinthu zimene zikuchitika masiku ano molondola chonchi? Sitikukayikira kuti mukugwirizana ndi zimene Leung, wa ku Hong Kong, ananena. Iye anati: “Maulosi a m’Baibulo analembedwa kale kwambiri. Palibe munthu aliyense amene akanatha kulosera zinthu zimenezi molondola chonchi. Baibulo liyenera kuti linalembedwa ndi winawake wanzeru kwambiri kuposa anthufe.”

M’Baibulo muli maulosi ambirimbiri omwe anakwaniritsidwa kale.b Zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi mawudi ochokera kwa Mulungu. Yehova anati: “Ine ndine Mulungu ndipo palibenso . . . aliyense wofanana ndi ine. Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.” (Yesaya 46:9, 10) Choncho m’pomveka kukhulupirira kuti zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo lathu, zidzachitikadi.

BAIBULO LILI NDI MALANGIZO OMWE ANGAKUTHANDIZENI MPAKA KALEKALE

Makolo akuyenda ndi ana awo atagwirana manja.

Zinthu zikhoza kumakuyenderani bwino mukamagwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba Opatulika pa moyo wanu. Onani zitsanzo zotsatirazi.

MALANGIZO OTHANDIZA PA NKHANI YA NDALAMA NDI NTCHITO

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—MLALIKI 4:6.

MALANGIZO OTHANDIZA M’BANJA

“Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.

MALANGIZO OTHANDIZA KUKHALA BWINO NDI ENA

“Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungachite choipa.”—SALIMO 37:8.

Mukamatsatira malangizo a m’Baibulo, mungakhale ndi moyo wabwino panopa komanso mungadzakhale ndi tsogolo labwino. M’Baibulo timapezamo malonjezo a Mulungu okhudza zinthu zabwino zimene zidzachitike m’tsogolo monga

MTENDERE NDI CHITETEZO

“Adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.

NYUMBA NDI CHAKUDYA CHOKWANIRA

“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—YESAYA 65:21.

SIKUDZAKHALANSO MATENDA NDI IMFA

“Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.

Kodi mungatani kuti mudzalandire nawo madalitso amenewa? Werengani nkhani yotsatira kuti muone zimene mungachite.

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kumasulira komanso kufalitsidwa kwa Baibulo, pitani pa www.jw.org pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MBIRI KOMANSO BAIBULO.

b Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 9 wa buku lakuti, Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezeka pawebusaiti yathu ya www.jw.org pamene alemba kuti LAIBULALE > MABUKU.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena