Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 4 tsamba 4
  • 1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero
  • Galamukani!—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Pindulani ndi Zomwe Munazoloŵera Kuchita
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mawu Oyamba
    Galamukani!—2016
  • Kodi n’zotheka Kusiya Zizoloŵezi Zoipa?
    Galamukani!—2004
  • 2 Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kukwaniritsa Zolinga Zanu
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 4 tsamba 4
Mzimayi akulemba

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUSINTHA ZOMWE MUNAZOLOWERA?

1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero

Nthawi zina munthu angamafune kusiya makhalidwe oipa nthawi imodzi. Mwina anganene kuti, ‘Mlungu uno ndikufuna kusiya kusuta, kutukwana komanso kugona mochedwa. Ndipo ndikufuna ndiyambe kuchita masewera olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi ndiponso kuimbira foni achibale anga.’ Komatu ngati munthu atayeseradi kuchita zinthu zonsezi nthawi imodzi, palibe chomwe angakwanitse.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”—Miyambo 11:2.

Munthu wodzichepetsa amangochita zimene angakwanitse. Amadziwa kuti sangakwanitse kuchita chilichonse chifukwa chosowa nthawi, mphamvu komanso zinthu zina. Munthu wotereyu amasintha zinthu pang’onopang’ono.

Munthu akamayesera kusintha zinthu zonse nthawi imodzi, palibe chomwe angakwanitse

ZIMENE MUNGACHITE

Muziyesa kaye kukwaniritsa chinthu chimodzi kapena ziwiri. Kuti zimenezi zitheke tayesani kuchita izi:

  1. Lembani zinthu zabwino zimene mukufuna kuzolowera kumachita komanso zinthu zoipa zomwe munazolowera ndipo mukufuna kuzisiya. Yesetsani kulemba zinthu zambiri ndithu.

  2. Polembapo muyambe ndi zinthu zomwe mukuona kuti ndi zofunika kwambiri.

  3. Ndiyeno pa zinthu zabwino ndi zoipa zimene munalemba zija, musankhepo chinthu chimodzi kapena ziwiri ndipo muziyesetsa kumachita zabwinozo komanso kusiya zoipazo. Zikatheka, yeserani zina mpaka zitathekanso.

Kuti musavutike kuzolowera, muzichita zinthu zabwino pa nthawi yomwe munkachita zinthu zoipa. Mwachitsanzo, ngati pa zinthu zomwe mukufuna kusiya munalembapo vuto loonera kwambiri TV, ndipo pa zinthu zomwe mukufuna mutamachita munalembapo kuti muziimbira foni achibale, mungalembe izi: ‘M’malo mongofikira kuyatsa TV ndikafika pakhomo, ndiziyamba kuimbira foni achibale.’

MALEMBA ENA AMENE ANGAKUTHANDIZENI

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

“Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.”—Mlaliki 7:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena