Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 5 tsamba 14-15
  • Aristotle

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aristotle
  • Galamukani!—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Aristotle Analemba Mabuku a Nkhani Zosiyanasiyana
  • Akatolika Anayamba Kuphunzitsa Mfundo za Aristotle
  • Kodi Ndani Anakhazikitsa Malamulo a Zinthu Zakuthambo?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimatsutsanadi?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Sayansi Yapangitsa Baibulo Kukhala Lachikale?
    Galamukani!—1990
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 5 tsamba 14-15

TIONE ZAKALE

Aristotle

Aristotle

ZAKA zoposa 2,300 zapitazo, Aristotle analemba mfundo zambiri zokhudza sayansi komanso nzeru za anthu. Anthu akhala akuphunzira ndiponso kuchita chidwi ndi zimene analembazo ndipo zinamasuliridwa m’zilankhulo zambiri. Pulofesa wina wa mbiri yakale dzina lake James MacLachlan analemba kuti: “Anthu a ku Europe ankakhulupirira mfundo za Aristotle zokhudza chilengedwe kwa zaka pafupifupi 2,000.” Nawonso Akatolika, Asilamu komanso anthu a matchalitchi ena akhala akuphunzitsa mfundo zina za Aristotle.

Aristotle Analemba Mabuku a Nkhani Zosiyanasiyana

Aristotle analemba nkhani zosiyanasiyana zokhudza zinthu monga makhalidwe, zilankhulo, malamulo, mphamvu yokoka, kayendedwe ka zinthu, zosangalatsa, ndakatulo, ndale, luso lolankhula ndi kulemba, sayansi ya zakuthambo, ya zinthu zamoyo komanso sayansi ya kaganizidwe ka anthu. Iye analembanso za mzimu wa munthu, womwe ankakhulupirira kuti umafa. Koma amadziwika kwambiri chifukwa cha zimene analemba zokhudza sayansi ya zamoyo ndiponso mfundo zimene munthu ayenera kutsatira kuti atsimikizire zinthu zinazake.

Kale akatswiri amaphunziro a ku Greece ankayang’anitsitsa zinthu za m’chilengedwe, kuziganizira mofatsa, kenako ankapeza njira imene angazifotokozere. Iwo ankaona kuti ngati ataganizira kwambiri mfundo zimene akuzidziwa kale akhoza kumvetsa zinthu zambiri zokhudza chilengedwe.

Zimenezi zinathandiza akatswiriwo kumvetsa zinthu zina zolondola, monga zoti zinthu za m’chilengedwe zimayenda mwadongosolo. Koma vuto n’lakuti analibe zipangizo zowathandiza kuona zinthu zakutali komanso zing’onozing’ono kwambiri. Choncho anthu anzeruwo, kuphatikizapo Aristotle, nthawi zina sankatulukira zolondola. Mwachitsanzo, ankakhulupirira kuti mapulaneti ndiponso nyenyezi zimayenda mozungulira dziko lapansi. Pa nthawi imeneyo, anthu ankaona kuti mfundoyi ndi yosatsutsika. Buku lina linati: “Zimene anthu ankaona komanso kuganiza zinkachititsa kuti azikhulupirira maganizo a anthu a ku Greece oti zinthu zakuthambo zimayenda mozungulira dziko lapansi.”—The Closing of the Western Mind.

Maganizo olakwikawa anakhudza moyo wa anthu ambiri chifukwa si asayansi okha amene ankaphunzitsa zimenezi.

Akatolika Anayamba Kuphunzitsa Mfundo za Aristotle

Kale ku Europe anthu ambiri omwe ankati ndi Akhristu ankaona kuti zimene Aristotle ankaphunzitsa ndi zoona. Atsogoleri a tchalitchi cha Katolika ankaphatikiza mfundo za Aristotle m’zimene ankaphunzitsa. Munthu wina wodziwika kwambiri amene ankachita zimenezi anali Thomas Aquinas. (Anabadwa cha m’ma 1224 ndipo anakhala ndi moyo pafupifupi zaka 50.) Patapita nthawi, mfundo yoti zinthu zakuthambo zimayenda mozungulira dziko lapansi inakhala mbali ya zikhulupiriro za Akatolika. Atsogoleri a matchalitchi ena monga Calvin ndiponso Luther anayambanso kuphunzitsa zimenezi ndipo ankanena kuti ndi mfundo yochokera m’Baibulo.—Onani bokosi lakuti, “Sankamvetsa Bwino Malemba.”

Anthu ambiri ankaona kuti zimene Aristotle ankaphunzitsa ndi zoona

Wolemba mabuku wina dzina lake Charles Freeman anati: “Zinali zovuta kusiyanitsa zikhulupiriro zina za Akatolika ndi zimene Aristotle ankaphunzitsa chifukwa zinkafanana kwambiri.” Choncho anthu ankanena kuti zinali ngati Aquinas “anabatiza” Aristotle kuti akhale Mkatolika. Komabe Freeman analembanso kuti zoona zake n’zakuti “Aquinas ndi amene anakhala wotsatira wa Aristotle.” Zinali ngati tchalitchi chonse cha Katolika chinkatsatira Aristotle. N’chifukwa chake atsogoleri a tchalitchi cha Katolika anakakamiza katswiri wina wa sayansi ya zakuthambo ndiponso ya masamu dzina lake Galileo kuti asiye kuphunzitsa zoti dziko limayenda mozungulira dzuwa.a Anachita zimenezi ngakhale kuti Galileo anali atapeza umboni wotsimikizira zomwe ankaphunzitsazo. Koma n’zochititsa chidwi kuti Aristotle ankadziwa kuti mfundo zasayansi zimatha kusintha asayansi akatulukira mfundo zina zatsopano. Matchalitchi akanachita bwino kuzindikiranso mfundoyi.

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani nkhani yakuti, “Galileo’s Clash With the Church” mu Galamukani! yachingelezi ya April 22, 2003.

DZIWANI IZI

  • Aristotle ankakonda kuphunzira zinthu zatsopano, “ankamvetsa kufunika kwa zinthu za m’chilengedwe ndipo ankaona kuti zinapangidwa mochititsa chidwi kwambiri.”—Aristotle—A Very Short Introduction.

  • Iye ankakhulupirira kuti zinthu zinapangidwa ndi winawake wabwino yemwe alibe chiyambi ndipo amakhala kutali kwambiri ndi chilengedwechi.

  • Aristotle ndi amene anali woyamba kulemba za sayansi ya zamoyo komanso zokhudza mfundo zimene anthu amatsatira kuti atsimikizire zinthu zinazake.

  • Aristotle anaphunzitsa mnyamata wina wa ku Makedoniya yemwe anadzakhala Alexander Wamkulu.

Chithunzi chosonyeza zinthu zakuthambo zikuyenda mozungulira dziko

Anthu ambiri akale ankakhulupirira kuti zinthu zakuthambo zimayenda mozungulira dziko lapansi

Sankamvetsa Bwino Malemba

Atsogoleri ena a matchalitchi ankakakamira mfundo ya Aristotle yoti zinthu zakuthambo zimayenda mozungulira dziko lapansi. Iwo ankachita zimenezi chifukwa chakuti sankamvetsa bwino malemba ena a m’Baibulo monga Salimo 104:5. Lembali limati: “[Mulungu anakhazikitsa] dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale.” Sikuti wolemba salimoli ankafotokoza za malo amene dziko lili m’chilengedwe. Koma anagwiritsa ntchito mawu andakatulo pofuna kusonyeza kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti dziko lapansi lidzakhalepo mpaka muyaya.—Mlaliki 1:4.

Baibulo likanena zinthu zokhudza sayansi zimakhala zolondola. Mwachitsanzo, lemba la Yobu 26:7, lomwe linalembedwa zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, limanena kuti Mulungu “anakoloweka dziko lapansi m’malere.” Komanso lemba la Yobu 38:33 limasonyeza kuti pali malamulo amene amatsogolera zinthu zakuthambo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena