Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g17 No. 1 tsamba 16
  • Nyerere Yokhala ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyerere Yokhala ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa
  • Galamukani!—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2017
  • Khosi la Nyerere
    Galamukani!—2016
  • Luso la Nyerere Lopukuta Tinyanga Take
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • “Pita ku Nyerere”
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—2017
g17 No. 1 tsamba 16
Nyerere ya siliva ya m’chipululu cha Sahara

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nyerere Yokhala Ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa

M’CHIPULULU cha Sahara mumapezeka nyerere zamtundu winawake zomwe zimatha kukhala m’malo otentha kwambiri omwe nyama zina sizingakhale. Masana, nyama zina zimene zimadya nyerere zamtunduwu zikabisala chifukwa cha dzuwa loswa mtengo, nyererezi zimapeza mwayi wotuluka ku una n’kumakafufuza zakudya. Zina mwa zakudyazi zimakhala tizilombo tomwe tafa ndi kutentha.

Nyerereyi ili ndi cheya pathupi lake chomwe chimaithandiza kukhala yotetezeka kudzuwa

[50] μm

Taganizirani izi: Nyerereyi imatha kukhala pamalo otentha kwambiri chifukwa ili ndi cheya pamwamba komanso m’mbali mwa thupi lake koma kumimba kwake n’kopanda cheya. Cheyachi (1, 2), chimapangitsa kuti nyerereyi izioneka ya siliva. Cheya chilichonse chinapangidwa ngati kachubu kakang’ono kwambiri kokhala ndi mbali zitatu (3). Mbali ziwiri zam’mwamba zimakhala ndi timizere tating’ono kwambiri pomwe mbali yam’munsi imakhala yosalala. Izi zimathandiza nyerereyi m’njira ziwiri. Choyamba, cheyachi chimaiteteza ku cheza cha dzuwa. Chachiwiri, chimathandiza kuti isamatenthedwe kwambiri ndi zinthu zotentha zimene zaizungulira. Komanso popeza kumimba kwake n’kopanda cheya, khungu lakumimbako limatha kubweza kutentha kumene kukuchokera mumchenga.a

Cheya cha nyerereyi achikulitsa pofuna kusonyeza kuti chinapangidwa ngati timachubu ting’onoting’ono

[10] μm

Nyerereyi singathe kukhala ndi moyo ngati thupi lake litatentha madigiri oposa 53.6. Koma chifukwa cha mmene inapangidwira, thupi lakeli silitentha kuposa pamenepa ngakhale kunja kutatentha kwambiri. Akatswiri akuyesetsa kuti apange zinthu zoziziritsira nyumba komanso zinthu zina popanda kugwiritsa ntchito mafani kapena zipangizo zina potengera mmene thupi lanyerereyi linapangidwira.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyerereyi ikhale ndi zinthu zoiteteza ku dzuwa, kapena pali winawake amene anailenga chonchi?

a Pali zinthu zinanso zimene zimathandiza nyerereyi kukhala m’malo otentha kwambiri. Ili ndi mapulotini apadera m’thupi mwake amene sasungunuka akatenthedwa kwambiri. Ilinso ndi miyendo yaitali yomwe imaithandiza kuti isamayandikane ndi mchenga wotentha komanso kuti izithamanga kwambiri. Chinthu chinanso chimene chimaithandiza n’chakuti imatha kulondola una wake mosavuta ndiponso mwamsanga isanapserere ndi dzuwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena