Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g17 No. 4 tsamba 8
  • Mbalame ya Kunyanja Yochititsa Chidwi Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbalame ya Kunyanja Yochititsa Chidwi Kwambiri
  • Galamukani!—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Tinali ndi Cholinga Chapadera Pokaona Chilumba Chotchedwa Christmas Island
    Galamukani!—2007
  • Mbalame Zili ndi Nzeru Zachibadwa Zodabwitsa
    Galamukani!—2007
  • Kufufuza Njira Yolumikiza Nyanja ya Atlantic ndi Pacific Kumpoto kwa Dziko Lapansi
    Galamukani!—2010
  • Ubongo Wodabwitsa wa Gologolo wa ku Arctic
    Kodi Zinangochitika Zokha?
Onani Zambiri
Galamukani!—2017
g17 No. 4 tsamba 8
Mbalame ya kunyanja

Mbalame ya Kunyanja Yochititsa Chidwi Kwambiri

KWA NTHAWI yaitali anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti mbalame zotchedwa Arctic Tern zimauluka pafupifupi mtunda wa makilomita 35,200 pa ulendo wawo wochokera kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi ku Arctic, kukafika kum’mwera kwenikweni ku Antarctica n’kubwereranso. Koma kafukufuku waposachedwapa, wasonyeza kuti mbalamezi zimauluka mtunda wautali kwambiri kuposa pamenepa.

Mbalame ya kunyanja

Chithunzi chosonyeza njira imene mbalame ya Arctic Tern imadutsa

Pofuna kudziwa mtunda umene mbalame za mtunduwu zimauluka, ofufuza anamangirira tizipangizo tating’ono kwambiri toyezera mtunda pa mbalame zina. Tizipangizoti tinasonyeza kuti mbalamezi zimauluka mtunda wa makilomita 90,000 paulendo wochoka ku Arctic komanso kubwerera. Palibe nyama iliyonse imene inayendapo mtunda ngati umenewu. Anapezanso kuti mbalame ina inauluka pafupifupi makilomita 96,000.

Mbalamezi zimauluka mokhotakhota paulendo wawowu. Moti njira imene zimatsatira zikamauluka podutsa panyanja ya Atlantic imaoneka ngati chilembo cha “S.” Zimauluka mokhotakhota potengera mmene mphepo ya panyanjayo imayendera.

Mbalamezi zimakhala ndi moyo pafupifupi zaka 30 ndipo pa nthawiyi zimakhala zitauluka mtunda oposa makilomita 2.4 miliyoni. Mtunda umenewu ndi wofanana ndi kupita ku mwezi n’kubwerako, maulendo atatu kapena 4. Wochita kafukufuku wina anati: “N’zochititsa chidwi kwambiri kuona kuti kambalame kolemera magalamu oposa 100 okha, kamauluka mtunda wautali chonchi.” Buku lina linati: “Chaka chilichonse mbalamezi zimakhala ndi nthawi ya masana yambiri kuposa cholengedwa chilichonse” chifukwa choti pa nyengo yotentha zimapezeka kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi ndipo zikapita kum’mwera zimakapezanso nyengo yomweyo.​—Life on Earth: A Natural History.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena