Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g19 No. 1 tsamba 12-15
  • Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”
  • Galamukani!—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI UFUMU WA MULUNGU UDZABWERA LITI?
  • MMENE UFUMU WA MULUNGU UDZAYAMBIRE KULAMULIRA
  • KODI ANTHU ADZAPINDULA BWANJI UFUMU UKAMADZALAMULIRA?
  • Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Ufumu wa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ufumu “Woti Sudzawonongeka ku Nthaŵi Zonse”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Galamukani!—2019
g19 No. 1 tsamba 12-15
Anthu akukhala mosangalala m’Paradaiso

MMENE MAVUTO ONSE ADZATHERE

Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”

Posachedwapa Ufumu wa Mulungu womwe takhala tikuyembekezera kwa nthawi yaitali, udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi. Mogwirizana ndi zimene Mulungu anatilonjeza pa Salimo 72:7, padzikoli “padzakhala mtendere wochuluka.” Koma kodi ufumuwu udzayamba liti kulamulira? Kodi padzachitika zotani kuti Ufumuwo uyambe kulamulira? Nanga tidzapindula bwanji ndi ulamuliro umenewo?

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZABWERA LITI?

Baibulo linaneneratu zinthu zingapo zomwe zidzachitike monga “chizindikiro” chosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera. Zinthuzi ndi monga nkhondo za mayiko, njala, matenda, zivomezi komanso kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo.​—Mateyu 24:3, 7, 12; Luka 21:11; Chivumbulutso 6:2-8.

Ulosi wina unanena kuti: “masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) Ndi zoona kuti kwa zaka zambiri anthu ena akhala akusonyeza makhalidwe amenewa. Koma panopa ndi mmene anthu ambiri alili.

Maulosiwa anayamba kukwaniritsidwa m’chaka cha 1914. Ngakhale anthu olemba mbiri, akatswiri a nkhani za ndale komanso olemba mabuku amatsimikiza kuti zinthu zinasintha kwambiri kuyambira m’chakachi. Mwachitsanzo, Peter Munch yemwe ndi katswiri wolemba mbiri ku Denmark analemba kuti: “Kungoyambira pomwe nkhondo yoyamba inamenyedwa mu 1914, zinthu zinasintha kwambiri m’mbiri ya anthu. Zinangokhala ngati tachoka m’nyengo imene chilichonse chinkaoneka kuti chili m’chimake, n’kulowa m’nyengo ya mavuto okhaokha, chidani komanso yomwe kulikonse anthu amangoona kuti si otetezeka.”

Komabe zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti zinthu zikhala bwino kutsogoloku. Zikutithandizanso kudziwa kuti posachedwa Ufumu uyamba kulamulira dziko lapansili. Ndipotu Yesu atafotokoza za mavutowa, ananenanso za chinthu china chosangalatsa chomwe chidzakhale mbali ya chizindikirochi. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14.

Uthenga wabwino umenewu ndi umene a Mboni za Yehova amalalikira. Ndipo magazini yawo yodziwika kwambiri ili ndi mutu wakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Nthawi zambiri magazini ya Nsanja ya Olonda imafotokoza zinthu zochititsa chidwi zomwe Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu padzikoli.

MMENE UFUMU WA MULUNGU UDZAYAMBIRE KULAMULIRA

Mfundo 4 zotsatirazi zikusonyeza zimene zidzachitike:

  1. Ufumuwu sudzalamulira pogwiritsira ntchito anthu andale a padzikoli.

  2. Olamulira andale, pofunitsitsa kukhalabe pa maudindo awo, adzakana ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.​—Salimo 2:2-9.

  3. Ufumu wa Mulungu sudzalekerera koma udzawononga maboma andale omwe amafuna kuti azingolamulirabe anthu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 19:17-21) Mabomawa adzawonongedwa pankhondo yomaliza, yomwe imatchedwa Aramagedo.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

  4. Onse amene amamvera mokhulupirika Ufumu wa Mulungu, adzapulumuka pa nkhondo ya Aramagedo ndipo adzalowa m’dziko latsopano. Iwowa ndi amene adzapange gulu lomwe Baibulo limati “khamu lalikulu.” Ndipo anthuwa alipo mamiliyoni.​—Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14.

    KODI UFUMU WA KHRISTU UDZACHITA ZOTANI?

    Yesu ali padzikoli, anasonyeza anthu zomwe adzachite akadzayamba kulamulira mu Ufumu wa Mulungu. Iye anachiritsa odwala ndi olumala. (Mateyu 4:23) Anadyetsa anthu ambiri. (Maliko 6:35-44) Komanso analamulira mphamvu za m’chilengedwe.​—Maliko 4:37-41.

    Yesu akuphunzitsa anthu

    Koposa zonse, iye anaphunzitsa anthu mmene angakhalire mwamtendere ndi anzawo. Anthu amene panopo amagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsazi, amakhala ndi makhalidwe ofunika omwe adzawathandize kukhala mwamtendere mpaka kalekale Ufumuwo ukadzayamba kulamulira. Palibe maphunziro aliwonse a kusukulu amene angathandize anthu mpaka pamenepa. Zinthu zochititsa chidwi zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wa paphiri, mungathe kuzipeza pa Mateyu chaputala 5 mpaka 7. Bwanji mudziwerengere nokha machaputala amenewa. Muli uthenga wopereka nzeru ndipo unalembedwa ndi mawu osavuta kumva. Mukawerenga muona kuti mfundo zake ndi zogwira mtima kwambiri.

KODI ANTHU ADZAPINDULA BWANJI UFUMU UKAMADZALAMULIRA?

Kuti munthu adzakhale nzika ya Ufumu wa Mulungu ayenera kuphunzitsidwa kaye. N’chifukwa chake Yesu popemphera ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”​—Yohane 17:3.

Anthu akafika podziwa bwino Yehova Mulungu n’kumamuona kuti ndi weniweni, amapindula m’njira zambiri. Tiyeni tingokambiranako njira ziwiri: Yoyamba, amakhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Ndipo chikhulupiriro chimenechi, chomwe chimabwera chifukwa cha umboni womwe apeza, chimawathandiza kutsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni komanso kuti uyamba kulamulira posachedwa. (Aheberi 11:1) Chachiwiri, amayamba kukonda kwambiri Mulungu ndi anthu ena. Kukonda Mulungu kumawachititsa kuti azimumvera ndi mtima wonse. Pomwe kukonda anthu ena, kumawachititsa kutsatira mfundo yofunika kwambiri imene Yesu anaphunzitsa yakuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”​—Luka 6:31.

Monga mmene bambo amene amakonda ana ake amachitira, Mlengi wathu nayenso amatifunira zabwino. Amafuna tidzapeze moyo womwe Baibulo limatchula kuti “moyo weniweniwo.” (1 Timoteyo 6:19) Moyo umene tikukhala panopa si ‘moyo weniweni.’ Tikutero chifukwa anthu ambiri akukumana ndi mavuto aakulu ndipo zimakhalanso zovuta kuti apeze zinthu zofunika. Kuti mudziwe mmene “moyo weniweniwo” udzakhalire, tiyeni tikambirane zinthu zina zosangalatsa zomwe Ufumu wa Mulungu udzachitire nzika zake.

MMENE MOYO WENIWENIWO UDZAKHALIRE

  • “M’masiku ake (Khristu akamadzalamulira), wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka . . . Adzakhala ndi anthu omugonjera . . . kukafika kumalekezero a dziko lapansi.”​—Salimo 72:7, 8, 13, 14.

  • “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.”​—Salimo 46:9.

  • ● “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

  • “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya . . . Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”​—Yesaya 65:21, 22.

  • “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Anthu akukhala mosangalala m’Paradaiso

Ufumu ukadzayamba kulamulira, anthu adzakhala otetezeka komanso adzakhala ndi chakudya chambiri

MFUNDO YAIKULU

ZIMENE YESU ANAPHUNZITSA ZIMATHANDIZA ANTHU KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO KOMANSO KUCHITA ZINTHU ZOYENERA. AMENE AMATSATIRA MFUNDO ZIMENEZI ADZASANGALALA NDI MTENDERE MU UFUMU WA KHRISTU

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena