Zimene Ena Amakhulupirira
Ahindu
amakhulupirira kuti munthu amavutika chifukwa cha zinthu zomwe wachita m’moyo uno, kapena zomwe anachita m’moyo wina m’mbuyomu. Amakhulupiriranso kuti munthu amasiya kuvutika akafika pa nthawi imene imatchedwa kuti moksha, kutanthauza kuti wasiya kubadwanso akafa, chifukwa pa nthawiyi amasiya kuganizira zinthu zosagwirizana ndi zachipembedzo.
Asilamu
amakhulupirira kuti mavuto ndi chilango cha machimo a munthu, kapena njira yoyesera chikhulupiriro chake. Dr. Sayyid Syeed, yemwe ndi pulezidenti wa Islamic Society of North America, ananena kuti mavuto amatikumbutsa kuti “nthawi zonse tiziyamikira Mulungu chifukwa cha madalitso omwe amatipatsa komanso kuti tizikumbukira kuthandiza anthu osauka.”
Chiphunzitso chachiyuda
chimati munthu aliyense amavutika chifukwa cha zochita zake. Ayuda ena amanena kuti anthu akufa adzauka ndipo kenako anthu abwino omwe anakumana ndi mavuto adzachitiridwa zinthu mwachilungamo. Chiphunzitso china cha Ayuda chotchedwa Kabbalah, chimanena kuti munthu akafa amabadwanso ndipo zimenezi zimapereka mwayi kwa munthuyo woti alape machimo ake.
Abuda
amakhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso ndipo amapitiriza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana mpaka pamene adzasiye kuchita, kuganiza, komanso kulakalaka zinthu zoipa. Ndiye akasiya zinthu zimenezi n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino, kuchita zinthu zabwino komanso kukhala wodziletsa, amafika pa nthawi yomwe amaitchula kuti nirvana, kutanthauza kuti mavuto ake onse amatheratu.
Anthu okhulupirira zomwe Confucius ankaphunzitsa
amati mavuto ambiri amachitika chifukwa cha “kulephera komanso zolakwa za anthu.” (A Dictionary of Comparative Religion). Iye ankaphunzitsa kuti ngakhale kuti mavuto akhoza kuchepa ngati munthu atakhala ndi makhalidwe abwino, mavuto ambiri amayambitsidwa ndi “zolengedwa zauzimu zomwe n’zamphamvu kwambiri kuposa anthu. Choncho munthu amangofunika kuvomereza zimene zolengedwa zauzimuzo zasankha.”
Anthu ena okhulupirira zamizimu
amanena kuti anthu amavutika chifukwa cha zaufiti. Iwo amakhulupirira kuti mfiti zikhoza kubweretsa mwayi kapena tsoka ndipo mavuto omwe mfiti zimayambitsa akhoza kuchepa pochita miyambo yosiyanasiyana. Amakhulupiriranso kuti ngati munthu akudwala chifukwa cholodzedwa, miyambo komanso mankhwala a asing’anga zimathandiza kuti munthuyo achire.
Akhristu
amakhulupirira kuti mavuto anayamba chifukwa cha tchimo la anthu awiri oyambirira, monga mmene buku la m’Baibulo la Genesis limafotokozera. Komabe, matchalitchi ambiri awonjezera maganizo awo pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, Akatolika ena amanena kuti mavuto a munthu akhoza ‘kuperekedwa kwa Mulungu’ ngati pempho kuti Mulunguyo adalitse tchalitchi chawo, kapena agwiritse ntchito mavutowo kuti apulumutse munthu winawake.
KUTI MUDZIWE ZAMBIRI
[Chithunzi patsamba 5]
Onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse? pa jw.org.