Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 1 tsamba 4-5
  • Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amuna, Muzikonda Akazi Anu
  • Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu
  • Muzikhala Okhulupirika Kwa Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
  • Makolo, Muziphunzitsa Ana Anu
  • Ananu, Muzimvera Makolo Anu
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Moyo wa Banja Umene Umakondweretsa Mulungu
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 1 tsamba 4-5
Banja losangalala lili limodzi kumsika.

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala

Kukhala pabanja komanso kukhala ndi ana ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu. Iye amafuna kuti tikhale ndi banja losangalala. Choncho pogwiritsa ntchito buku lakale lopatulika iye amatipatsa malangizo amene angathandize banja lathu kukhala labwino komanso losangalala. Taganizirani malangizo anzeru otsatirawa:

Amuna, Muzikonda Akazi Anu

“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”​—AEFESO 5:28, 29.

Mwamuna ndiye mutu wa banja. (Aefeso 5:23) Koma mwamuna wabwino sakhala waukali kapena wongolamula zilizonse. Iye amalemekeza mkazi wake ndipo amamupezera zinthu zofunika pa moyo komanso amamukonda. Amayesetsanso kuchita zinthu zosangalatsa mkazi wake, m’malo mongokakamira zofuna zake. (Afilipi 2:4) Amafotokoza zamumtima mwake momasuka ndiponso mkaziyo akamalankhula amamumvetsera. Iye ‘sapsera mtima kwambiri’ mkazi wake, kumuchitira nkhanza ngakhalenso kumulankhula mwachipongwe.—Akolose 3:19.

Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu

“Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”​—AEFESO 5:33.

Mkazi akamalemekeza mwamuna wake komanso kugwirizana ndi zimene mwamunayo wasankha, zimathandiza kuti m’banjamo mukhale mtendere. Ngati mwamunayo walakwitsa zinazake mkaziyo sachita zinthu momupeputsa koma amakhalabe wodekha komanso waulemu. (1 Petulo 3:4) Pakakhala nkhani yoti akambirane ndi mwamuna wake amasankha nthawi yabwino komanso amalankhula naye mwaulemu.​—Mlaliki 3:7.

Muzikhala Okhulupirika Kwa Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

‘Mwamuna adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’​—GENESIS 2:24.

Mwamuna ndi mkazi akakwatirana amapanga ubwenzi wolimba kwambiri. Choncho anthu okwatirana ayenera kumayesetsa kuti banja lawo likhale lolimba. Iwo angamachite zimenezi pouzana zakukhosi komanso kusonyezana kukoma mtima mu zinthu zing’onozing’ono. Ayenera kukhala okhulupirika m’banja mwawo ndipo sayenera kugona ndi mkazi kapena mwamuna wina. Kuchita zimenezi ndi nkhanza ndipo anthu amasiya kukhulupirirana komanso banja likhoza kutha.​—Aheberi 13:4.

Makolo, Muziphunzitsa Ana Anu

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—MIYAMBO 22:6.

Mulungu anapatsa makolo udindo wophunzitsa ana awo. Zimenezi zikuphatikizapo kuwaphunzitsa makhalidwe abwino komanso kuwapatsa chitsanzo chabwino. (Deuteronomo 6:6, 7) Mwana akamapanda kumvera, kholo lanzeru limachita zinthu modekha. Khololo ‘limakhala lofulumira kumva, lodekha polankhula, losafulumira kukwiya.’ (Yakobo 1:19) Ngati laona kuti mwanayo akufunika kulandira chilango limachita zimenezo mwachikondi, osati mwaukali.

Ananu, Muzimvera Makolo Anu

“Ananu, muzimvera makolo anu . . . ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”—AEFESO 6:1, 2.

Ana ayenera kumvera makolo awo komanso kuwalemekeza kwambiri. Ana akamalemekeza makolo awo amathandiza kuti banja likhale losangalala, lamtendere komanso logwirizana. Ana akuluakulu amalemekeza makolo awo akamaonetsetsa kuti makolowo akusamaliridwa bwino. Zimenezi zingaphatikizepo kuonetsetsa kuti akusamalira pakhomo pawo kapena kuwapatsa thandizo la ndalama.​—1 Timoteyo 5:3, 4.

Ndinakhala Mwamuna Wabwino

“Chifukwa cha m’banja limene ndinakulira, ndinkangolamula zilizonse. Koma ndinaphunzira kuti monga mutu wa banja, sindiyenera kukhala wodzikonda kapena kumachita zinthu ngati bwana, koma ndiyenera kumamvetsera mkazi wanga. Kwa Mulungu ndife thupi limodzi ndipo ndiyenera kumamusamalira ngati thupi langa. Ndimathokoza malangizo anzeru amenewa, chifukwa panopa ndine mwamuna wabwino kwambiri ndipo ndili ndi banja losangalala.”​—Rahul.

Rahul ndi mkazi wake.

Dziwani zambiri:

Kuti mupeze malangizo amene angakuthandizeni kuti banja lanu likhale lolimba, pitani pa jw.org ndipo pitani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU OKWATIRANA KOMANSO MABANJA.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena