Mawu Oyamba
Simukufunika kukhala katswiri wa sayansi kuti muzindikire kuti dzikoli lawonongeka kwambiri. Madzi abwino, nyanja zikuluzikulu, nkhalango ngakhalenso mpweya zawonongekeratu. Kodi dzikoli lidzakhalanso bwino? Onani zifukwa zimene zingakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo.