Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g25 No. 1 tsamba 14-15
  • Muziyembekezera Kuti Zinthu Zidzasintha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziyembekezera Kuti Zinthu Zidzasintha
  • Galamukani!—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
  • ZIMENE MUNGACHITE
  • KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI, NANGA UDZACHITA CHIYANI?
  • Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Baibulo Limatithandiza Kuti Tikhale Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
  • Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Galamukani!—2025
g25 No. 1 tsamba 14-15
Banja lakhala pansi ndipo likuyang’ana malo okongola.

ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU

Muziyembekezera Kuti Zinthu Zidzasintha

Kodi mitengo ya zinthu ikukwera kwambiri m’dziko lanu, koma ndalama zimene mumapeza sizikuwonjezereka? Kodi mumadera nkhawa mmene mungapezere zinthu zofunika pa moyo wanu komanso za anthu am’banja lanu? Ngati ndi choncho, mukhoza kumada nkhawa mukaganizira zam’tsogolo. Koma kukhala ndi chiyembekezo pa nthawi ngati imeneyi n’kothandiza kwambiri.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Munthu amene ali ndi chiyembekezo sikuti amangolakalaka zinthu zabwino zitachitika. Chiyembekezo chimatipatsa mphamvu ndipo chimatithandiza kuti tichite zinthu zimene zingatithandize pa mavuto athu. Mwachitsanzo, kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene ali ndi chiyembekezo . . .

  • amatha kupirira mavuto

  • savutika kusintha

  • amasankha zinthu mwanzeru zomwe zimathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino komanso wathanzi

ZIMENE MUNGACHITE

Choyamba, muziganizira mmene Baibulo lingakuthandizireni masiku ano. M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kudziwa zochita pa vuto la kukwera mitengo kwa zinthu. Malangizowa angakuthandizeni kuona kuti sikuti palibiretu mtengo wogwira. Koma pali zimene mungachite panopa komanso zimene mungadzachite m’tsogolo ngati mavutowo atafika poipa kwambiri.

“Kuganiza bwino kudzakuyangʼanira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.”—Miyambo 2:11.


Chachiwiri, muziganizira zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo. Mukazindikira kuti nzeru zopezeka m’Baibulo n’zothandiza kwambiri, mudzafufuza zimene bukuli limanena zokhudza m’tsogolo. Mwachitsanzo, mudzazindikira kuti Mulungu amafuna kuti mukhale ndi “tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino” ndipo wayala kale maziko oti zimenezi zitheke. (Yeremiya 29:11) Maziko amene tikunenawa ndi Ufumu wa Mulungu.

KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI, NANGA UDZACHITA CHIYANI?

Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lidzalamulire dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Ufumuwu uzidzalamulira kuchokera kumwamba ndipo udzathetsa umphawi ndi mavuto ena onse. Moti padzikoli padzakhala mtendere komanso zinthu zambiri, ngati mmene malemba ali m’munsiwa akusonyezera.

“Udzakhala wosangalala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.”—Salimo 128:2.

“[Anthu amene adzakhale mu Ufumuwo] sadzagwira ntchito mwakhama pachabe.”—Yesaya 65:23.

“Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.”—Salimo 72:16.

Anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira malonjezo amenewa podziwa kuti Mulungu “sanganame.” (Tito 1:2) Tikukulimbikitsani kuti inunso muwerenge zimene Baibulo limanena. Chiyembekezo chimene Baibulo limapereka chingakuthandizeni kupirira mavuto azachuma n’kumayembekezera kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino.

Ramaz.

“Chiyembekezo chimene ndapeza chifukwa chophunzira Baibulo, chandithandiza kuti ndiziona kuti mavuto am’dzikoli ndi akanthawi. Kuganizira zimenezi kwandithandiza kuti ndizipirira mavuto azachuma omwe akungowonjezereka.”—Ramaz, Georgia.

DZIWANI ZAMBIRI

Kodi zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo, mungazikhulupirire? Onerani pa jw.org vidiyo yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena zoona? komanso yakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Mzimayi akutenga Baibulo pashelefu.
    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena