Mutu 3
Kodi Mulungu Ndani?
1. Kodi ncifukwa ninji pali cosokonezeko cacikuru ponena za amene ali Mulungu?
KUFUNIKIRA Mulungu kwa munthu ndi cithandizo cace sikunakhale kwakukuru ndi kale lonse mofanana ndi tsopano lino. Miyoyo yathu imadalira pa kumdziwa iye. Koma, mwacilendo kwambiri, pali cisokonekero cacikuru ponena za amene iye ali, pakuti lerolino, mofanana ndi kale, pali milungu yambiri imene ikulambiridwa m’maiko ambiri. Komabe Baibulo limalongosola momvekera bwino kuti pali Mulungu woona mmodzi yekha.—1 Akorinto 8:5, 6.
2. (a) Kodi “Mulungu” liri dzina laumwini la Mulungu woona? (b) Kodi dzina lace laumwini ndi lotani?
2 Kuti adzilekanitse yekha ndi milungu yocuruka yonama, Mulungu woonayo wadzipatsa iye mwini dzina laumwini. Ililo limamlekanitsa ndi yina yonse. Ena angafunse kuti “Kodi dzina lace sindilo ‘Mulungu?’” Ai, pakuti “Mulungu” langokhala dzina laulemu cabe, monga ngati “Prezidenti,” “Mfumu” ndi “Woweruza” angokhala maina aulemu cabe. Dzina laumwini la Mulungu ladziwikitsidwa kwa ife kupyolera m’Mau ace, Baibulo, ndipo dzina limenelo ndilo YEHOVA. M’matembenuzidwe ambiri a Baibulo dzina limeneli likupezeka pa Salmo 83:18, pamene mu (AV) timawerenga kuti: “Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu lokha liri Yehova, ndinu wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Ndipo cifupifupi m’matembenuzidwe onse dzinalo likupezeka pa Cibvumulutso 19:1-6 monga mbali ya mau akuti “Aleluya” kapena “Haleluya.” Mau amenewa amatanthauza “tamandani Ya” (cidule ca Yehova). The Catholic Encyclopedia (1910, Voliyamu VIII, tsamba 329) limati ponena za Dzina Laumulungu limeneli: “Yehova, dzina lenileni la Mulungu m’Cipangano Cakale.” Komabe, The Jerusalem Bible, matembenuzidwe aposacedwapa Acikatolika, limaligwiritsira nchito kawirikawiri dzina lakuti “Yahweh,” monga momwenso amacitira matembenuzidwe ena ambiri. Kodi ncifukwa ninji kuli conco?
3. (a) Kodi dzina la Mulungu likusonyezedwa motani m’Malemba Achihebri? (b) Kodi ncifukwa ninji kuli kosathekera kudziwa kwenikweni za mmene dzina la Mulungu linali kuchulidwira mu Cihebri mu nthawi zakale?
3 Mu Cihebri, cinenero mu cimene mabukhu oyambirira makumi atatu kudza asanu ndi anai a Baibulo (AV) analembedweramo, dzina la Mulungu likusonyezedwa kwa nthawi zikwi zikwi ndi malemba anai Acihebri, YHWH. Mu nthawi zakale cinenero Cacihebri cinali kulembedwa popanda mavaulo, wowerengayo anali kulowetsamo mavaulo pamene anali kuwerenga. Cotero, cothetsa nzeru cace ndico cakuti lerolino tiribe njira ya kuwadziwira mavaulo enieni amene Ahebriwo anali kuwagwiritsira nchito limodzi ndi makonsonanti akutiwo YHWH. Asikolara ambiri amalingalira kuti dzinalo linali kuchulidwa motere “Yahweh,” koma kachulidwe kakuti “Jehovah” (“Yehova”) kakhala kakugwiritsidwa nchito kwa zaka zambiri ndipo kali kodziwika kwakukuru
4. (a) Kodi ndi motani mmene akulu a mpingo amene amanena kuti sitinayenera kugwiritsira nchito dzina la Mulungu cifukwa cakuti sitimadziwa kachuledwe kace kenikeni ali osatsimikizira? (b) Kodi cimene ciri cofunika kwambiri nciani koposa ndi mmene timalichulira dzina la Mulungulo? (c) Kodi ncifukwa ninji kuli kofunika kugwiritsira nchito dzina la Mulungu, pomalingalira za Macitidwe 15:14?
4 Popeza kuti pali kukaikira ponena za kachulidwe kenikeni ka dzina la Mulungulo, akulu a mpingo ena amanena kuti musamaligwiritsira ilo nchito konse, koma m’malo mwace kumangoti “Mulungu” kapena “Ambuye.” Komabe, iwo samaumiliza kuti musamawagwiristira nchito maina akuti “Yesu” ndi “Yeremiya.” Komabe machulidwe ofala amenewa ali osiyana kwambiri ndi machulidwe Acihebri akuti “Yesh’ua” ndi “Yirmeiah’.” Cinthu cofunika ndico osati machulidwe amene mungawagiritsire nchito pa Dzina Laumulungulo, kaya muti “Yahweh,” “Yehova,” kapena machulidwe ena, malinga ngati machulidwewo ali ofala mu cinenero canu. Cimene ciri colakwika ndico kulephera kuligwiritsira nchito dzinalo. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti awo amene samaligwiritsira ilo nchito sangadziwikitsidwe limodzi ndi awo amene Mulungu akuwatenga kuti akhale “anthu a dzina lace.” (Macitidwe 15:14) sitinayenera kungolidziwa kokha dzina la Mulungu komanso kulilemekeza ilo ndi kulitamanda pamaso pa ena, monga momwe Mwana wa Mulungu anacitira pamene anali pa dziko lapansi.—Mateyu 6:9; Yohane 17:6, 26.
MIKHALIDWE YA MULUNGU NDI CIFUKWA CACE TINAYENERA KUMLAMBIRA IYE
5. Ncifukwa ninji palibe munthu amene anamuona Mulungu ndi kale lonse?
5 Kodi nciani cimene Baibulo limatiuza ife ponena za Mulungu? Ilo limatiuza kuti “Mulungu ndiye mzimu.” (Yohane 4:24) Mzimu suli wopangidwa ndi mnofu ndi mwazi, kapena zinthu zina zimene zingaonedwe ndi kukhudzidwa ndi ziwalo zaumunthu. (1 Akorinto 15:44, 50) Cotero, maso aumunthu sanamuone konse Mulungu. (Yohane 1:18) Iye ali wapamwambamwamba koposa ciriconse cimene maso athu angathe kuciona. Ulemerero wa mapiri, kunyezimira kwa dzuwa, ngakhale ulemerero wa thambo lodzaza ndi nyenyezi siziri kanthu poyerekezedwa ndi iye.—Yesaya 40:25, 26.
6. (a) Kodi ndi motani mmene Baibulo pa Cibvumbulutso 15:3, 4 limailongosolera mikhalidwe ya Mulungu? (b) Kodi Mulungu anali ndi ciyambi?
6 Mposadabwitsa kuti m’miyamba yonse nyimbo imayimbidwa yakuti: “Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa inu nokha muli woyera.” (Cibvumbulutso 15:3, 4) Monga Mlengi wa zinthu zonse, Yehova Mulungu, “Mfumu yosatha,” anakhalako pasanakhale ena onse. Iye ali “woyambira ku nthawi yosayamba kufikira ku nthawi yosatha,” kumatanthauza kuti iye analibe ciyambi ndipo sadzakhala ndi mapeto.—1 Timoteo 1:17; Salmo 90:2, AV [89:2, Dy].
7. (a) Malinga ndi kunena kwa Cibvumbulutso 4:11, kodi ncifukwa ninji kuli koyenera kuti kulambira kwathu kumapita kokha kwa Yehova? (b) Kodi ndi mwa njira ya ciani Mulungu anacicita cilengedwe ca zinthu zonse?
7 Pamenepo, ndi koyenera cotani nanga kuti kulambira kwathu kuyenera kupita kwa iye kokha! Pamene tizilingalira nchito zace zakulenga, ifenso tinganene kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphambu; cifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa cifuniro canu zinakhala, nizinalengedwa.” (Cibvumbulutso 4:11) Iye anacitsiriza cilengedwe, osati ndi zipangizo zonga ngati zimene anthu amazigwiritsira nchito, koma mwanjira ya mzimu wace woyera, umene uli mphamvu yace yogwira nchito yosaoneka. (Genesis 1:2; Salmo 104:30 [103;30, Dy]) Uli mzimu woyera umodzimodziwo mwa umene pambuyo pace unalipangitsa Baibulo kulembedwa kotero kuti ife ticidziwe cifuniro cace ndi zifuno kaamba ka anthu pa dziko lapansi.—2 Petro 1:21.
8. (a) Ncifukwa ninji ife tiri a thayo kwa Mulungu? (b) Cotero, kodi ndi funso lotani limene tifunikira kulilingalira mosamalitsa?
8 Popeza kuti zinthu zonse zinalengedwa ‘cifukwa ca cifuniro cace,’ izo zonse ziyenera kutumikira cifuno ca Mulungu. Yehova anamlangiza mwamuna ndi mkazi oyambawo, Adamu ndi Hava, za cifuno cace kaamba ka iwo, ndipo iye anawapangitsa iwo kucita mogwirizana ndi ico. Kodi ifenso tiri ndi thayo pamaso pa Mulungu? Inde, cifukwa cakuti Mulungu ndiye Magwero a moyo wathu. Ici ciri coona, osati kokha cifukwa tacokera kwa anthu awiri oyambirira amenewo amene Mulungu anawapatsa moyo, komanso cifukwa cakuti moyo wathu womapitirizawu tsiku lirilonse umadalira pa dzuwa, mvula, mpweya ndi cakudya zimene Yehova amapitirizabe kutipatsa ife. (Salmo 36:9 [35:10, Dy]; Mateyu 5:45) Pamenepo, kodi ndi ku ukulu wotani ife timakhala ndi moyo mogwirizana ndi cifuniro ca Mulungu kaamba ka ife? Tifunikira kulingalira mosamalitsa ponena za ici, cifukwa cakuti mwai wathu kaamba ka moyo wamuyaya uli paupandu.
9. (a) Kodi tinayenera kumuopa Mulungu mu njira yotani? (b) Kodi ncifukwa ninji tingakhalire okondwa kuti Yehova ali wamphamvuyonse?
9 Kodi ife tiyeneradi kumuopa Mulungu? Inde, koma mwa mantha omaopa kucipandukira cifuniro cace, cifukwa cakuti cifuniro cace ciri coyenera. Ngakhale mu zinthu wamba, kodi sitimaopa kuzicita zinthu zina zoopsa zimene zingacititse cibvulazo kapena kutayika kwa moyo? Nanga tinayenera kuopa mokulira cotani za kusamkondweretsa “Yehova Mulungu, Wamphamvuyonseyo.” Komabe tingakhale okondwa kuti iye ali wamphamvuyonse, pakuti, “maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera waphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi iye.” (2 Mbiri 16:9;a onaninso Yesaya 40:29-31.) Ndipo tingatsimikizire kuti Yehova nthawi zonse amaigwiritsira nchito mphamvu yace ndi colinga coyenera ndiponso kaamba ka ubwino wa awo amene amacikonda cimene ciri coyenera. Pakuti “Mulungu ndiye cikondi.”—1 Yohane 4:8.
10. Kodi ndi mikhalidwe yotani ya Yehova imene imatipangitsa ife kukhala acimwemwe kuti tikhale naye monga Mulungu wathu?
10 Cifukwa ca cimeneco, Yehova sali Mulungu wotsendereza. “Njira zace zonse ndi ciweruzo.” (Deuteronomo 32:4) Zoonadi, iye ali “Mulungu wansanje,” komanso iye ali “Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wa coonadi.” (Eksodo 20:5; 34:6) “Popeza adziwa mapangidwe athu akumbukira kuti ife ndife pfumbi.” (Salmo 103:14 [102:14, Dy]) Tingakhale okondwa pokhala ndi Mulungu woteroyo amene ali wolungama komanso womvera cifundo monga Woweruza wathu Wamkuru, Wopereka Lamulo ndi Mfumu.—Yesaya 33:22.
11. Ngakhale ngati tisacizindikire cifukwa cace ca lamulo lina la Mulungu, kodi nciani cimene cidzatisonkhezera ife kulimvera ilo?
11 Yehova ali ndi “nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi luntha ali nazo.” (Yobu 12:13) Umboni wa nzeru yace ukuonekera mu nchito zace zonse za kulenga, kumwamba ndi pa dziko lapansi pomwe. Pamenepo, ife tingafunse kuti: “kodi ncifukwa ninji munthu wina aliyense angaikaikire nzeru ya Mulungu?” Baibulo limasonyeza kuti zofuna zace ziri kaamba ka ubwino wathu, limodzi ndi colinga ca ubwino wathu wosatha. Kungakhale koona kuti pangakhale nthawi zina pamene ife, monga anthu okhala ndi nzeru zokhala ndi polekezera ndi luntha, sitimazindikira mokwanira cifukwa cace lamulo lina loperekedwa ndi Mulungu liri lofunika kwambiri, kapena mmene limagwirira nchito kaamba ka ubwino wathu. Komabe cikhulupiriro cathu camphamvu cakuti Mulungu amadziwa zocuruka kopambana koposa ifeyo, kuti zimene akuzidziwa ndi zazikuru kwambiri koposa zathu, ndi kuti cimene amacicita ciri kaamba ka ubwino wathu wosatha, cidzatisonkhezera ife kumumvera iye ndi mtima wofunitsitsa.—Salmo 19:7-11 [18:8-12, Dy]; Mika 6:8.
KODI MULUNGU ALI “UTATU”?
12. (a) Kodi nciani cimene ziphunzitso za carici, monga ngati Ciphunzitso ca Athanasia, zimaphunzitsa ponena za Mulungu? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tinayenera kuwafunsa ponena za ciphunzitso cimeneci?
12 Zipembedzo zocuruka za Cikristu ca Dziko zimaphunzitsa kuti Mulungu ali “Utatu,” ngakhale kuli kwakuti liu lakutilo “Utatu” silimaonekera m’Baibulo. The World Council of Churches posacedwapa inanena kuti zipembedzo zonse zimene ziri mbali ya Bungwe limenelo ziyenera kucibvomereza ciphunzitso cakuti pali “Mulungu mmodzi, Atate, Mwana ndi mzimu Woyera,” amene ali anthu atatu mwa Mulungu mmodzi. Awo amene amaphunzitsa ciphunzitso cimeneci amabvomereza kuti ico ciri “cinsinsi.” Ciphunzitso ca Athanasia, ca mu zaka za zana lacisanu ndi citatu mu Nyengo Yathu Yino, cimanena kuti Atateyo, Mwana ndi Mzukwa Woyera (Mzimu) onse atatuwo ali opangidwa ndi cinthu cimodzi, onse atatuwo ali amuyaya (ndipo motero analibe ciyambi), ndipo onse atatuwo ali amphamvuyonse. Cotero ciphunzitsoco cimanena kuti mu “Utatu palibe amene anayamba kukhalapo kapena kudza pambuyo pa mnzace; palibe wokulira kapena wocepera kwa mnzace.”b Kodi kunena kumeneko kuli kwanzeru? Mofunika kwambiri, kodi iko kuli kogwirizana ndi Baibulo?
13. Malinga ndi kunena kwa New Catholic Encyclopedia, kodi aneneri Acihebri ndi Akristu oyambirira anakhulupirira mu “Utatu”?
13 Ciphunzitso cimeneci sicinadziwidwe ndi aneneri Acihebri ndi atumwi Acikristu. New Catholic Encyclopedia (kusindikiza kwa mu 1967, Voliyamu XIV, tsamba 306) imabvomereza kuti “ciphunzitso ca Utatu Woyera sicinaphunzitsidwe mu OT [Cipangano Cakale].” Imabvomerezanso kuti ciphunzitsoco ciyenera kunenedwa kuti cinayambira patapita zaka mazana atatu kudza makumi asanu kuyambira pa imfa ya Yesu Kristu. Cotero Akristu oyambirira amene anaphunzitsidwa mwacindunji ndi Yesu Kristu sanakhulupirire kuti Mulungu ali “Utatu.”
14. Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera kuti iye sanali wofanana ndi Mulungu Atate wace?
14 Pamene Yesu anali pa dziko lapansi iye ndithudi sanali wofanana ndi Atate wace, pakuti iye ananena kuti panali zinthu zina zimene iye ngakhale angelo sanazidziwe koma Mulungu yekha anazidziwa. (Marko 13:32) Kuonjezerapo, iye anapemphera kwa Atate wace kuti amuthandize pamene anakumana ndi ciyeso. (Luka 22:41, 42) Ndiponso, iye mwiniyo ananena kuti: “Atate ali wamkuru ndi Ine.” (Yohane 14:28) Cifukwa ca cimeneci, Yesu analankhula za Atate wace kukhala “Mulungu wanga” ndiponso kukhala “Mulungu woona yekha.”—Yohane 20:17; 17:3.
15. Kodi ndi motani mmene tikudziwira kuti Yesu sanali wofanana ndi Mulungu ngakhale pambuyo pa kuukitsidwa kwace kucokera kwa akufa?
15 Pambuyo pa imfa ya Yesu, Mulungu anamuukitsa iye kuti akhalenso ndi moyo ndipo iye anampatsa ulemerero woposa umene anali nawo poyamba. Komabe, iye anali cikhalirebe wosafanana ndi Atate wace. Kodi tikudziwa bwanji? Cifukwa cakuti pambuyo pace Malemba ouziridwa amalongosola kuti Mulungu ali cikhalirebe “mutu wa Kristu.” (1 Akorinto 11:3) Baibulo limanenanso kuti Yesu ayenera kulamulira monga mfumu yosankhidwa ndi Mulungu kufikira iye atawaika adani ace onse pansi pa mapazi ace, ndi kuti pa nthawi imeneyo “Mwanayo adzagonjera kwa iye amene anampatsa zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:28, AV) Moonekera bwino, ngakhale kuyambira pamene iye anaukitsidwa Yesu Kristu sali wofanana ndi Atate wace.
16. (a) Kodi kalongosoledwe ka Yesu, kakuti “Ine ndi Atate ndife amodzi,” kamaphunzitsa za “Utatu”? (b) Kodi nciani cimene Yesu amatanthauza ponena za kalongosoledwe kameneko?
16 Koma kodi pa nthawi yina Yesu sananene kuti, “Ine ndi Atate ndife amodzi”? (Yohane 10:30) Inde, iye anatero. Komabe, kanenedwe kameneko sikamapereka lingaliro lirilonse la “Utatu,” popeza kuti iye anangonena kokha za anthu awiri kukhala amodzi, osati atatu. Motsimikizirikadi Yesu sanali kuwaombanitsa malemba amene tawawerenga kalewo. Cimene iye anacitanthauza mwa kanenedwe kameneka iye mwiniyo anacimveketsa bwino pambuyo pace pamene iye anapemphera ponena za atsatiri ace kuti “akhale amodzi, monga Ife tiri mmodzi.” (Yohane 17:22) Yesu ndi Atate wace ali “mmodzi” pa cifukwa cakuti Yesu ali wogwirizana kotheratu ndi Atate wace. Ndipo iye anapemphera kuti atsatiri ace akhalenso ogwirizana ndi Atate wace, ndi Yesu ndiponso wina ndi mnzace.
17.Kodi ncifukwa ninji kalongosoledwe ka pa Yohane 1:1 sikamaphunzitsa za “Utatu”?
17 Bwanji ponena za mau a pa Yohane 1:1 (AV), amene amamunena Yesu kukhala “Mauyo,” kumati: “Paciyambi panali Mau, ndipo Mauyo anali ndi Mulungu, ndipo Mauyo ndiye Mulungu”? Kodi cimeneco sicimatsimikizira za “Utatu”? Ai. Coyamba, taonani kuti ali anthu awiri okha amene aculidwa, osati atatu. Ndiponso, m’mutu wace wokhawokhawo, vesi 2 limanena kuti Mauyo “paciyambi anali ndi Mulungu,” ndipo vesi 18 limanena kuti “palibe munthu anamuona Mulungu nthawi iriyonse,” komabe anthu anamuona Yesu Kristu. Pa zifukwa izi, ndiponso mogwirizana kotheratu ndi malemba Acigriki, matembenuzidwe ena a vesi 1 amati: “Mauyo anali ndi Mulungu, ndipo Mauyo anali waumulungu,” kapena anali “mulungu,” ndiko kuti, Mauyo anali munthu wamphamvu wonga Mulungu. (AT; NW) Cotero mbali iyi ya Baibulo iri yogwirizana ndi mbali zina zonsezo; iyo simaphunzitsa “Utatu.”c
18. Kodi ndi motani mmene colembedwa ca Baibulo conena za cimene cinacitika pa Penekoste wa mu 33 C.E. cimasonyezera kuti mzimu woyera sungakhale munthu?
18 Ponena za “Mzimu Woyera,” wochedwawo “Munthu Wacitatu wa Utatu,” taona kale kuti uwo suli munthu, koma mphamvu yogwira nchito ya mulungu. (Oweruza 14:6) Yohane Mbatizi ananena kuti Yesu adzabatiza ndi mzimu woyera monga momwe Yohane anali kubatizira ndi madzi. Madzi sali munthu monga momwe wakhalira mzimu woyera kuti suli munthu. (Mateyu 3:11) Cimene Yohane anacineneratu cinakwaniritsidwa pamene Mulungu anamcititsa Mwana wace Yesu Kristu kuutsanulira mzimu woyera pa atumwi ndi ophunzira mkati mwa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E., kotero kuti “anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera.” Kodi iwo “anadzazidwa” ndi munthu? Ai, koma iwo anadzazidwa ndi mphamvu yogwira nchito ya Mulungu.—Macitidwe 2:4, 33.
19. (a) Cotero, kodi “Utatu” uli ciphunzitso ca Baibulo? (b) Kodi ndi mu dziko lakale liti akunja anali kukhulupirira m’mautatu a milungu?
19 Pamenepo, kodi nciani cimene zenizenizo zimasonyeza ponena za “Utatu”? Liulo ngakhale lingaliro lacelo silikupezeka m’Mau a Mulungu, Baibulo. Ciphunzitsoco sicinayambike ndi Mulungu. Koma, mudzakondweretsedwa kudziwa kuti, malinga ndi kulongosola kwa bukhu lakuti Babylonian Life and History (Lolembedwa ndi Sir E. A. Wallis Budge, kusindikiza kwa 1925, tsamba 146, 147), mu Babulo wakale, akunja anali kukhulupirira cinthu coteroco; ponena zoona, iwo anali kulambira milungu ya mautatu osiyanasiyana.
KUMAMLAMBIRA MULUNGU “MUMZIMU NDI M’COONADI”
20. Malinga ndi kunena kwa aroma 12:2, kodi teyenera kucita ciani kuti timpatse Mulungu kudzipereka kosagawanika?
20 Kuti mumkonde ndi kumlemekeza munthu, wolemekezayo amafunikira kumdziwa iye monga momwedi iye wakhalira. Kuti mupereke kwa Mulungu kudzipereka kosagawanika kumene iye amakufuna, mufunikira kuphunzira Mau ace ndi kuti ‘mukadzitsimikizire inu mwini za cifuniro cabwino ndi cobvomerezeka ndi cangwiro ca Mulungu.’ (Aroma 12:2) Cinthu cofunika tsopano sindico ca mmene anthu akufunira kumlambira Mulungu, koma za mmene Mulungu amafunira kulambiridwa.
21. M’Mau a Mwana wa Mulungu, kodi ndi motani mmene Mulungu amafunira kulambiridwa?
21 Madzoma acipembedzo ndi ‘zothandizira kudzipereka’ zingaonekere kukhala zokongola m’maso mwa awo amene amazigwiritsira izo nchito, koma kodi ndi motani mmene Mulungu amazionera izo? Ndithudi inu mufuna kudziwa, cifukwa cakuti mukufuna kukhala ndi cibvomerezo ca Mulungu. Mwana wa Mulungu mwiniyo amatiuza ife kuti “olambira oona adzamlambira Atate mumzimu ndi m’coonadi.” (Yohane 4:23) Mwacitsanzo, kodi kugwiritsira nchito mafano kuli kulambira “mumzimu ndi m’cooandi”? Kodi kumamkondweretsa Mulungu?
22. (a) Kodi nciani cimene Baibulo, pa Eksodo 20:4, 5, limanena ponena za mafano acipembedzo? (b) Kodi nciani cimene Mau a Mulungu amanena kusonyeza kuti kagwiritsiridwe ka nchito ka zifaniziro monga “cithandizo” mu kulambira sikuli mbali ya kulambira koona?
22 Pa Eksodo 20:4, 5, mu limodzi la Malamulo Khumi, Mulungu mwiniyo amanena kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciriconse . . . usazipembedzere izo, usazitumikire izo.” (The Catholic Jerusalem Bible) Anthu ena amalilingalira fano lacipembedzo kukhala “cothandizira” pa kumulambira Mulungu cifukwa cakuti angalione ndi kulikhudza fanolo. Koma Mulungu anamuuzira mtumwi Paulo kulemba kuti: “Tiyenda mwa cikhulupiriro si mwa cionekedwe.” (2 Akorinto 5:7) Mulungu amanena mwacimvekere pa nkhaniyo. Iye amatiuza ife kuti kugwiritsira nchito mafano sikuli mbali ya kulambira koona, koma kuti mafano amenewo ali “Cinyengo.” (Yesaya 44:14-20; Salmo 115:4-8 [113:4-8, cigawo caciwiri ca manambarawo, Dy]) Ngakhale kukhale kwakuti wina anganene kuti ulemu umene umaperekedwa ku fano lacipembedzo uli wocepera koposa uja umene umaperekedwa kwa Mulungu, Mulungu mwiniyo amanena kuti iye sadzagawana konse ulemerero wace wonse ndi ulemu ndi mafano oterowo.—Yesaya 42:8.
23. Pamene tiunguzaunguza panyumba pathu, kodi ndi mau otani a mtumwi Yohane amene tinayenera kuwakumbukira?
23 Mwacikondi, mtumwi Yohane amaticenjeza ife kuti: “Dzisungireni nokha kupewa mafano.” (1 Yohane 5:21) Bwanji osaunguzaunguza panyumba panu ndi kudzifunsa nokha kuti kodi ndikucicita cinthu ici? (Deuteronomo 7:25) Pakumaupangitsa moyo wanu ndi njira ya kalambiridwe kanu kukhala zogwirizana ndi cifuniro ca Yehova cacikondi inu mungalipeze dalitso lace losatha.—1 Akorinto 10:14.
24. Ngati tifunadi kuyandikira kwa Mulungu, kodi nciani cimene tinayenera kucicita?
24 Pitirizanibe kuphunzira za kulemekezeka kwa Yehova ndi zifuno zace zacikondi, ndipo mudzakula m’cikondi ca pa iye. Musalilole tsiku kupita osamthokoza iye kaamba ka zinthu zabwino zimene mwasangalala nazo cifukwa ca kukoma mtima kwace kwacikondi. Pamene muphunzira zoculuka ponena za iye, tsimikizirani mumtima mwanu za kufunika kwace kwa kukhala wokhulupirika kwa iye monga Mulungu wamkuru wa cilengedwe caponseponse. Mwa kumvera kwacikondi kwa iye, inu mudzadziika mu njira imene imatsogolera ku moyo wamuyaya.—Aefeso 4:23, 24; Salmo 104:33-35 [103:33-35, Dy].
[Mawu a M’munsi]
a 2 Paralipomenon 16:9, Dy.
b Cyclopœdia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yolembedwa ndi J. M’Clintock ndi J. Strong, Voliyamu II, tsamba 561.
c Okhulupirira mu Utatu asiyiratu kuwagwira mau akuti “Atate, Mau, ndi Mzukwa Woyera: ndipo atatuwa ali mmodzi” amene amaonekera m’matembenuzidwe ena a Baibulo pa 1 Yohane 5:7. Asikolara a malemba akubvomerezana kuti mau amenewa ali ongophatikizidwapo mwa pambuyo pace ku malemba ouziridwawo.