Phunziro 34
Mafanizo Oyenerera
1, 2. Fotokozani mwachidule mmene mafanizo amathandizira nkhani.
1 Pamene mlankhuli agwiritsa ntchito mafanizo, kwenikweni amakhala akupereka zithunzi zatanthauzo m’maganizo mwa omvetsera. Mafanizo amadzutsa chidwi ndipo amagogomeza mfundo zofunika kwambiri. Amayambitsa munthu kuganiza ndipo kumakhala kosavuta kumvetsa malingaliro atsopano. Mafanizo osankhidwa bwino amakopa maganizo ndiponso amakhudza mtima. Chotsatirapo chimakhala chakuti uthengawo umaloŵa m’maganizo ndi mphamvu imene kaŵirikaŵiri mawu chabe satha kuipereka. Komatu zimenezo zimatheka pokhapokha ngati mafanizowo ali oyenerera. M’pofunika kuti akhale oyenerana ndi nkhaniyo.
2 Nthaŵi zina, mutha kugwiritsa ntchito fanizo pofuna kuchotsa maganizo olakwika kapena okondera. Fanizo likhoza kukankhira pambali maganizo otsutsa musanayambe kufotokoza chiphunzitso chinachake chochititsa mkangano. Mwachitsanzo, munganene kuti, “Palibe tate angaike pamoto dzanja la mwana wake pofuna kum’langa.” Fanizo loterolo pofuna kulankhula za chiphunzitso cha “helo,” mwamsanga lingapangitse chikhulupiriro chonama cha “helo” kukhala chonyansa moti chitha kutsutsika mosavuta.
3-6. Kodi mafanizo angatengedwe ku magwero otani?
3 Mafanizo amagwa m’mitundu yambiri. Atha kukhala ofanizira zinthu, oyerekeza zinthu, osiyanitsa zinthu, mikuluŵiko, zokumana nazo, ndi zitsanzo. Ndipo tikhoza kuwatenga ku magwero ambiri. Atha kunena za zinthu za chilengedwe, zamoyo ndi zopanda moyo. Akhoza kunena za ntchito za omvetsera, makhalidwe a anthu kapena zochita zawo, zinthu za m’nyumba, kapena zinthu zopangidwa ndi anthu monga nyumba, ngalaŵa, ndi zina zotero. Komabe, fanizo lililonse limene mlankhuli angaligwiritse ntchito, ayenera kulisankha chifukwa cha chochitikacho ndi nkhaniyo, osati chabe chifukwa chakuti ndi fanizo lake lapamtima.
4 Chenjezo pang’ono. Musakoleretse nkhani yanu mopambanitsa ndi mafanizo ambirimbiri. Agwiritseni ntchito, koma musapyole muyezo.
5 Kugwiritsa ntchito mafanizo koyenera ndiko luso. Kumafuna luso ndi kuzoloŵera. Komanso n’kofunika kwambiri kuti mafanizowo akhale ogwira mtima. Kuti muphunzire kugwiritsa ntchito mafanizo muyenera kuphunzira kukonda mafanizo. Pamene mukuŵerenga, onani mafanizo amene amagwiritsidwa ntchito. Pamene muyang’ana zinthu, ziganizireni mogwirizana ndi moyo wachikristu ndi utumiki wathu. Mwachitsanzo, mutaona duŵa limene likufoota, mungaganize kuti, “Ubwenzi uli ngati chomera. Kuti chikule ndi mphamvu chimafuna kuchithirira.” Anthu ena lerolino akayang’ana mwezi amangoganiza za maulendo akuthambo. Akristu amauona kukhala ntchito ya manja a Mulungu, chinthu cha kuthambo chozungulira dziko lapansi, chokhalako kwamuyaya, chimene chimakhudza miyoyo yathu tsiku ndi tsiku, chopangitsa mafunde kutundumuka ndi kusefukira panyanja.
6 Pokonza nkhani, ngati mafanizo osavuta safika msanga m’maganizo, onani nkhani yofananako ndi yanuyo m’zofalitsa za Watch Tower Society. Onani ngati muli mafanizo alionse. Ganizirani mawu ofunika kwambiri m’nkhaniyo ndi zithunzi zimene mawu akupereka m’maganizo mwanu. Gwirizanitsani zimenezo ndi nkhani yanu. Koma kumbukirani, kusapereka fanizo lililonse kumakhalapo bwino koposa kupereka fanizo losayenerera. Poganizira mfundo yakuti “Mafanizo oyenerana ndi nkhani,” imene yaikidwanso pafomu ya Uphungu wa kulankhula, pali mbali zina zingapo zofunika kuzikumbukira.
7-9. N’chifukwa ninji mafanizo osavuta ali ogwira mtima kwambiri?
7 Osavuta. Fanizo losavuta limakumbukika msanga. Limathandizira kumveketsa mfundo imene ikuperekedwa m’malo moiphimba chifukwa cha kucholoŵana kwake. Mafanizo a Yesu kaŵirikaŵiri sanali a mawu ambiri. (Mwachitsanzo, onani Mateyu 13:31-33; 24:32, 33.) Kuti fanizo likhale losavuta, mawu ake ayenera kukhala osavuta kumva. Ngati fanizo lifunikira kulongosola kwambiri, limenelo ndi katundu wolemetsa. Lisiyeni kapena lifeŵetseni.
8 Yesu anagwiritsa ntchito zinthu zazing’ono kulongosolera zinthu zazikulu, zinthu zosavuta kulongosolera zinthu zovuta. Fanizo liyenera kuonekera bwino m’maganizo, losapereka mbali zambirimbiri panthaŵi imodzi. Liyenera kukhala lolunjika ndi lotsimikizika. Si kaŵirikaŵiri pamene mafanizo oterowo amagwiritsidwa ntchito mosayenera.
9 Fanizo limakhala labwino kwambiri ngati lili logwirizana kwathunthu ndi nkhani. Ngati pali mbali ina ya fanizo imene ili yosayenera kwenikweni, kungakhale bwino kungoichotsa mbaliyo. Chifukwa munthu wina adzangoganizira za mbali yosayenerayo ndipo nkhani yonse idzaipa.
10, 11. Sonyezani chifukwa chake tanthauzo la mafanizo liyenera kumveketsedwa bwino.
10 Kumveketsa bwino tanthauzo lake. Ngati simutanthauzira fanizo, ena angazindikire tanthauzo lake koma ambiri sangathe. Mlankhuliyo ayenera kulimvetsa bwino fanizolo ndi kudziŵa cholinga chake. Ayenera kufotokoza momveka bwino pamene pagona phindu la fanizolo. (Onani Mateyu 12:10-12.)
11 Fanizo mungalitanthauzire m’njira zambiri. Mungaligwiritse ntchito kumveketsa bwino mfundo imene mwatchula musananene fanizolo kapena pambuyo pake. Kapena mwakugogomeza zotsatirapo za mfundo imene yaperekedwa ndi fanizolo. Kapenanso mwa kungosonyeza mfundo zogwirizana za m’fanizolo ndi nkhani yanu.
12-14. N’chiyani chingathandize kudziŵa fanizo loyenerera?
12 Kugogomeza mfundo zofunika kwambiri. Musagwiritse ntchito fanizo chabe chifukwa chakuti lafika m’maganizo mwanu. Pendani nkhaniyo kuti muone mfundo zazikulu ndiyeno sankhani mafanizo amene angathandize kumveketsa mfundozo. Ngati mafanizo amphamvu kwambiri agwiritsidwa ntchito pa mfundo zazing’ono kwambiri, omvetsera angakumbukire mfundo zazing’ono koposa zazikulu. (Onani Mateyu 18:21-35; 7:24-27.)
13 Fanizo siliyenera kuphimba mfundo yanu. Likhale limene omvetsera atha kulikumbukira. Koma likhale loti polikumbukira fanizolo, azilikumbukira limodzi ndi mfundo yake. Ngati mfundo yakeyo sangaikumbukire, ndiye kuti fanizolo lapambanitsa.
14 Pokonza nkhani ndi posankha mafanizo, yerekezani phindu la fanizolo ndi mfundo zofunika kuzigogomeza. Kodi likugogomeza mfundo zimenezo? Kodi likuzipangitsa kuonekera? Kodi likupangitsa mfundozo kumveka ndi kukumbukika mosavuta? Ngati silitero, si fanizo loyenerera.
**********
15, 16. Fotokozani chifukwa chake mafanizo ayenera kuyenerana ndi omvetsera.
15 Mafanizo safunikira kuyenerana ndi nkhani yokha, koma ayeneranenso ndi omvetsera. Mfundo imeneyi yaikidwa payokha pa fomu ya uphungu monga “Mafanizo oyenerana ndi omvetsera.” Pamene Natani anauzidwa kukadzudzula Davide patchimo lake ndi Bateseba, anasankha fanizo la munthu wosauka ndi kamwana ka nkhosa kake kamodzi. (2 Sam. 12:1-6) Fanizo limenelo linasankhidwa mwaluso, komanso linali lomuyenera Davide chifukwa anali atakhalapo mbusa. Mwamsanga iye anazindikira mfundo ya fanizolo.
16 Ngati pakati pa omvetserawo pali achikulire kwambiri, musagwiritse ntchito mafanizo okondweretsa achinyamata okha. Koma polankhula ku gulu la ophunzira a kukoleji, mafanizo oterowo angakhale oyenerera kwambiri. Nthaŵi zina mungasankhe mafanizo oyenera ogunda mbali zonse ziŵiri, monga achikulire ndi achinyamata, komanso amuna ndi akazi.
17-19. Kuti mafanizo agwire mitima ya omvetsera anu, kodi ayenera kutengedwa ku zinthu zotani?
17 Onena za zinthu zodziŵika bwino. Ngati mugwiritsa ntchito zinthu zapafupi m’mafanizo, zidzakhala zodziŵika bwino kwa omvetsera anu. Ndi mmene Yesu anachitira. Kwa mkazi wa pachitsime uja iye anayerekeza mikhalidwe yake yopatsa moyo ndi madzi. Anagwiritsa ntchito zinthu zazing’ono m’moyo, osati zapadera. Mafanizo ake anaperekadi zithunzi zosavuta m’maganizo mwa omvetsera, kapena anawakumbutsa msanga zochitika za m’miyoyo yawo. Iye anagwiritsa ntchito mafanizo ndi cholinga choŵaphunzitsa.
18 Leronso n’chimodzimodzi. Akazi a panyumba angadziŵe za bizinesi, koma polankhula nawo mungachite bwino kwambiri ngati mugwiritsa ntchito mafanizo okhudzana ndi zinthu zimene amachita nazo tsiku ndi tsiku, ana awo, ntchito zapanyumba, ndi zinthu zimene amagwiritsa ntchito panyumba.
19 Mafanizo ogwiranso mtima ndi aja onena za chinthu cha kumaloko, mwinamwake chodziŵika kudera lokhalo. Zochitika zapanthaŵiyo zodziŵika kumaloko, monga nkhani zapanyuzi, zimakhalanso zoyenerera ngati zili zabwino.
20-22. Tchulani mbuna zoyenera kupeŵa pogwiritsa ntchito mafanizo.
20 Abwino. Fanizo lililonse logwiritsidwa ntchito liyenera kukhala logwirizana bwino ndi makambirano a m’Baibulo amene alipowo. Mwachionekere, mafanizo sayenera kukhala onyazitsa. Peŵani mawu otanthauzanso zinthu zina ngati muona kuti angamvedwe molakwa. Nali langizo labwino lofunika kulitsata: Ngati mukukayikira fanizo, lisiyeni.
21 Mafanizo sayenera kukhumudwitsa munthu aliyense mwa omvetserawo ngati mungapeŵe zimenezo, makamaka aja ongoyamba kumene kusonkhana nafe. Pachifukwa chimenecho, si bwino kubutsa nkhani ya chiphunzitso kapena ya mkangano imene si mfundo yaikulu m’nkhani yanuyo. Mwachitsanzo, simungagwiritse ntchito chitsanzo monga cha kuika magazi m’thupi kapena kupanga suluti ku mbendera ngati zimenezo sizinali mfundo zazikulu za m’nkhani yanu. Zingangoputa wina ndi kum’khumudwitsa. Koma ngati nkhani yanu ikunena zimenezo, imeneyo tsopano ndi nkhani ina. Umenewo umakhala mwayi wanu wakuti muwafotokozere tsatanetsatane wake ndi kuwakhutiritsa. Koma musafooketse cholinga chanu mwa kulola mafanizo anu kutchinga maganizo a omvetsera anu ku choonadi chofunika kwambiri chimene mukufotokoza.
22 Choncho sankhani bwino mafanizo anu. Onetsetsani kuti ndi oyenerera. Adzakhaladi oyenerera ngati ayenerana ndi nkhani yanu komanso omvetsera anu.