Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 8 tsamba 11
  • Mafanizo Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafanizo Abwino
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Mafanizo Oyenerera
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • “Nthawi Zonse Iye Ankalankhula Nawo Pogwiritsa Ntchito Mafanizo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • “Kopanda Fanizo Sanalankhula Kanthu kwa Iwo”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Phunzitsani Mwanzeru Ndi Mosonkhezera
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 8 tsamba 11

PHUNZIRO 8

Mafanizo Abwino

Lemba

Mateyu 13:34, 35

MFUNDO YAIKULU: Munkhani yanu muziikamo mafanizo ochititsa chidwi komanso othandiza anthu kumvetsa mfundo zikuluzikulu.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Mafanizo azikhala osavuta kumva. Mofanana ndi Yesu, muzigwiritsa ntchito zinthu zing’onozing’ono pofotokoza zikuluzikulu komanso zinthu zosavuta pofotokoza zinthu zovuta. Musamatchule mfundo zambirimbiri zomwe zikhoza kusokoneza anthu. Zimene mukutchula mufanizo zizigwirizanadi ndi mfundo yamunkhani yanu kuti anthu asamachite kudzifunsa kuti, ‘Kodi pamenepa ndiye zikugwirizana bwanji?’

    Mfundo yothandiza

    Muzichita chidwi ndi zinthu. Muziyang’ana zinthu m’dera lanu, muziwerenga mabuku athu komanso muzimvetsera nkhani za anthu aluso. Ndiye muzitolera zitsanzo zimene mungadzagwiritsire ntchito pophunzitsa. Muzilemba penapake mafanizowo n’kuwasunga.

  • Muziganizira mfundo zothandiza kwa anthu. Zitsanzo zanu zizikhala zodziwika komanso zochititsa chidwi kwa anthu amene mukulankhula nawo. Musamagwiritse ntchito mafanizo amene angakhumudwitse kapena kuchititsa manyazi anthu.

  • Muzithandiza anthu kudziwa mfundo yaikulu. Zitsanzo zanu zizikhala pa mfundo zikuluzikulu osati zing’onozing’ono. Anthu azikumbukira mfundo yaikuluyo osati fanizo lokhalo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena