Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 36 tsamba 175-181
  • Mawu Omalizira Oyenera ndi Kusunga Nthaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Omalizira Oyenera ndi Kusunga Nthaŵi
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • **********
  • Kusunga Nthaŵi ndi Kuigaŵa Bwino
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mawu Omaliza Ogwira Mtima
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kukonza Autilaini
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 36 tsamba 175-181

Phunziro 36

Mawu Omalizira Oyenera ndi Kusunga Nthaŵi

1-3. Kodi mungagwirizanitse motani mawu omalizira ndi mutu wa nkhani yanu?

1 Kaŵirikaŵiri mawu otsirizira ndiwo amakhala oyamba kukumbukidwa. Choncho mawu omalizira a nkhani yanu afunika kuwakonzekera bwino lomwe. Ayenera kuunika bwino mfundo zazikulu zimene mukufuna kuti anthu akazikumbukire ndi kugogomeza mutu wa nkhani mosaiŵalika. Chifukwa cha kaumbidwe ka nkhani yanuyo ndi kalankhulidwe kake, mawu omalizira ayenera kulimbikitsa omvetsera kuchitapo kanthu. Ndiyo mfundo imene tikukulimbikitsani kuisamala kwambiri pamene mufika pa luso lakuti “Mawu omalizira oyenera, ogwira mtima” pafomu yanu ya Uphungu wa Kulankhula.

2 Mawu omalizira ogwirizana mwachindunji ndi mutu wa nkhani. Ponena za maganizo a mmene mungagwirizanitsire mawu omalizira ndi mutu wa nkhani, onaninso Phunziro 27. Mawu omalizira safunikira kubwereza mutu wa nkhani m’mawu ambiri, ngakhale kuti ophunzira ena, makamaka atsopano, angaone zimenezo kukhala zothandiza; m’malo mwake mawu omalizira ayenera kungogogomezanso mutuwo. Ndiyeno, malinga ndi mutuwo, sonyezani omvetsera zimene ayenera kuchita.

3 Ngati mapeto saali ogwirizana mwachindunji ndi mutu wa nkhani, sadzamanga bwino nkhani yonse pamodzi. Ngakhale ngati mugwiritsa ntchito mawu omalizira ongondandalika mfundo zazikulu, mudzafunikirabe kuwonjeza sentensi imodzi kapena aŵiri otchula mfundo yaikulu ya mutu wa nkhani yanu.

4-9. N’chifukwa chiyani mawu anu omalizira ayenera kusonyeza omvetsera anu chochita?

4 Mawu omalizira osonyeza omvetsera chochita. Popeza kuti kaŵirikaŵiri cholinga chanu polankhula chimakhala kulimbikitsa omvetsera kuchita kanthu kena kapena kuwakhutiritsa palingaliro lina lake, n’kwachionekere kuti malingaliro omalizira a nkhani yanu ayenera kumveketsa mfundo zimenezo. Chotero, cholinga chachikulu cha mawu omalizira ndicho kusonyeza omvetsera chimene ayenera kuchita ndi kuwalimbikitsa choti achite.

5 Pachifukwa chimenecho, komanso pofuna kumveketsa cholinga cha nkhani yanu, mawu omalizira ayenera kukhala ndi mphamvu yokhutiritsa ndi yolimbikitsa omvetsera. Mudzapeza kuti masentensi afupiafupi ndiwo amakhala bwino pofuna kugogomeza mawu omalizira. Komabe, zilibe kanthu kuti mawu anuwo mwaaumba bwino chotani, muyenera kupereka zifukwa zomveka zoti anthuwo achitire zimene mukuwalimbikitsazo, kuphatikizapo mapindu amene angapezepo mwa kutsatira njira imeneyo.

6 Mawu omalizira ayenera kutsatira bwino lomwe zimene zafotokozedwa kale m’nkhaniyo. Choncho, zimene munena m’mawu omalizira zikhale zolimbikitsa omvetsera anu kuti achitepo kanthu pa zimene zanenedwa kale m’thunthu la nkhaniyo. Mawu anu omalizira adzamveketsa ndi kugogomeza zimene anthuwo ayenera kuchita kuti alabadire mwa kutsatira zimene zalankhulidwa m’nkhaniyo ndipo mawu anu omalizira olankhulidwa mwamphamvu adzawalimbikitsa kwambiri kuchita zimenezo.

7 Mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba kaŵirikaŵiri mawu omalizira amakhala ofooka. Zimenezo zimachitika pamene sitisonyeza mwininyumba chimene ayenera kuchita, kaya kugula limodzi la mabuku, kapena kuti avomere kudzam’chezeranso kapena kanthu kena kalikonse.

8 Ngakhalenso mawu omalizira a nkhani za m’sukulu angakhalenso ofooka ngati angolongosola mfundo zazikulu za nkhaniyo popanda kulimbikitsa omvetserawo kuti achitepo kanthu. Matanthauzo a mfundo zina ayenera kuperekedwa, kapena kuti phindu la mfundozo liyenera kumveketsedwa kwa omvetsera.

9 Alankhuli ena amaona kuti n’kothandiza kwambiri kumaliza nkhani ya mutu wa m’Baibulo mwa kubwereza mwachidule mfundo zazikulu za nkhaniyo, akumagwiritsa ntchito malemba ofunika kwambiri ndi mutu wa nkhani monga maziko ake. Mwa kubwereramo mwachidule m’nkhani m’njira imeneyo limodzi ndi kutchulapo malemba oŵerengeka monga mmene mungachitire pakhomo la munthu, mudzamveketsa nkhaniyo bwino lomwe, komanso mudzapatsa omvetsera anu kanthu kena kamene angakagwiritse ntchito pobwereza mfundo zazikulu za nkhaniyo. Chimenecho ndicho cholinga chachikulu cha mawu omalizira, ndipo kachitidwe kameneka ndiko koyenera komanso kamakwaniritsa cholingacho mogwira mtima.

**********

10-14. Perekani malingaliro ponena za utali woyenera wa mawu omalizira.

10 Mawu omalizira autali woyenera. Utali wa mawu omalizira suyenera kudalira koloko, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri n’zimene zimachitika. Mawu omalizira amakhala autali woyenera ngati ali ogwira mtima nakwaniritsa cholinga chake. Choncho kuyenera kwake kumadziŵika mwa zotsatira zake. Izi n’zimene phungu wanu adzachita pamene mukugwirira ntchito paluso lakuti “Mawu omalizira autali woyenera,” pasilipi la Uphungu wa Kulankhula.

11 Pofuna kudziŵa utali woyenera wa mawu omalizira powayerekeza ndi thunthu la nkhani, onani kufupika kwa mawu omalizira a buku lonselo la Mlaliki opezeka pa Mlaliki 12:13, 14, ndipo ayerekezeni ndi Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu ndi mawu ake omalizira pa Mateyu 7:24-27. Pamenepo tikuona mitundu iŵiri ya mawu omalizira ndi utali wosiyana, komabe onsewo akukwaniritsa cholinga chake.

12 Mawu omalizira sayenera kuwafika modzidzimutsa omvetsera anu. Ayenera kusonyeza kuti tsopano mukufika kumtsiriziro kwa nkhani, komanso kamvekedwe ka mawu kayeneranso kusonyeza zimenezo. Zimene munena ndi mmene mukuzinenera ziyenera kumaliza nkhani yanu. Simuyenera kungokokerakokera mawu. Ngati simukhoza kumanga nawo nkhani yanu pamodzi ndi kukopabe chidwi cha omvetsera mpaka kumapeto, akonzeninso mawu omalizirawo. Adakali aatali kwambiri.

13 Ngati ndinu mlankhuli watsopano, ndi bwino nthaŵi zonse kufupikitsa mawu anu omalizira. Akhale osavuta, olunjika ndi olimbikitsa. Musalole kuti azingoyenderera.

14 Ngati mukukamba imodzi mwa nkhani zosiyirana, kapena ngati mukulankhula pamsonkhano wautumiki, pamenepo mawu anu omalizira adzagwirizana ndi mawu oyamba a nkhani yotsatira, chotero ayenera kukhala ofupikirapo ndithu. Komabe, mbali iliyonse payokha iyenera kukhala ndi mawu omalizira okwaniritsa cholinga cha nkhaniyo. Ngati atero, ndiko kuti alidi autali woyenera.

**********

15-18. Ngati nthaŵi siisamalidwa, kodi mapeto ake amakhala chiyani?

15 Kusunga nthaŵi. Si utali wokha wa mawu omalizira umene uli wofunika; m’pofunikanso kusunga nthaŵi ya mbali iliyonse ya nkhani. Kaamba ka chimenecho “Kusunga nthaŵi” kwapatsidwa malo akeake pasilipi la Uphungu wa Kulankhula.

16 Kufunika kwa kusunga nthaŵi pankhani sikuyenera kuchepetsedwa. Ngati nkhani yakonzedwa bwino, nthaŵinso imakhala itasamalidwa bwino, koma ngati wolankhulayo, poyesa kuloŵetsapo mfundo zake zonse adya nthaŵi, pamenepo walephera kukwaniritsa cholinga chake. Tikutero chifukwa omvetserawo adzayamba kutakataka ndi kumayang’ana pamawochi awo ndi kusamvetsera kwenikweni zimene iye akunena. Mawu omalizira, amene ayenera kusonyeza tanthauzo lonse la nkhaniyo ndi cholinga chake, adzatayika. Ngakhale ngati anenedwa, nthaŵi zambiri omvetsera samapindulapo kanthu chifukwa wolankhulayo amakhala atadya nthaŵi.

17 Si omvetsera okha amene amatekeseka pamene mlankhuli adya nthaŵi, ngakhalenso mlankhuli yemwe. Pamene aona kuti nthaŵi ikum’thera ndipo mfundo adakali nazo zochuluka, angayese kufotokoza zambiri panthaŵi imodzi, akumawononga kugwira mtima kwa nkhaniyo. Chotsatirapo chake, iye amakhala wosakhazikika polankhula. Komanso, ngati wokamba nkhani aona kuti alibe mfundo zotsirizira nthaŵi imene wapatsidwayo, nayesa kukokera nkhani yakeyo, idzakhala yosagwirizanika ndi yongopondaponda apa ndi apa.

18 Ngakhale kuti woyang’anira sukulu adzasonyeza kwa wophunzira kuti nthaŵi yake yatha, zimenezo n’zokhumudwitsa, ponse paŵiri kwa wophunzirayo ndi kwa omvetsera omwe, pamene nkhani idukizidwa isanathe. Mlankhuliyo ayenera kukhala ndi chidwi choti alankhule nkhani yakeyo bwino lomwe. Omvetserawo adzamva ngati asiyidwa m’malere ngati samva mawu omalizira. Munthu wokhala ndi chizoloŵezi chomadya nthaŵi m’nkhani zake amasonyeza kuti saganizira ena kapena amapereka umboni wa kusakonzekera.

19, 20. N’chifukwa ninji kusunga nthaŵi kuli kofunika kwenikweni pamsonkhano wautumiki ndi msonkhano wachigawo?

19 Pamene alankhuli angapo ali ndi mbali papologalamu, kusunga nthaŵi kumakhala kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, msonkhano wa utumiki ungakhale ndi mbali zisanu. Ngati mlankhuli aliyense apitirira nthaŵi imene wapatsidwa ndi mphindi imodzi yokha, msonkhanowo udzapitirira nthaŵi yake ndi mphindi zisanu. Chikhalirecho aliyense wangodya nthaŵi yochepa kwambiri. Chotsatirapo chake n’chakuti ena angatuluke msonkhano usanathe kuti akapeze basi yopitira ku nyumba, kapena amuna osakhulupirira amene abwera kudzatenga akazi awo angakwiye poyembekezera. Kungoti zonse sizikhala bwino.

20 Mavuto amakhalaponso ngati mmodzi wa alankhuli pankhani yosiyirana samaliza nthaŵi yake. Mwachitsanzo, ngati mbale wopatsidwa mphindi 30 papologalamu ya msonkhano wachigawo amaliza nkhani yake m’mphindi 20, zingasokoneze pologalamu ngati mlankhuli wotsatira sanakonzekere kuyamba nthaŵi yomweyo.

21-24. Mwachidule fotokozani mavuto ena amene amakhalapo pakusunga nthaŵi ndi zimene zimawachititsa.

21 Ndithudi, chimodzi cha zifukwa zazikulu zochititsa kudya nthaŵi pankhani ndicho kukhala ndi mfundo zochuluka kwambiri. Chimenechi ndi chinthu chofunika kuwongolera pokonza nkhani. Komabe, ngati mfundo zinazo, mfundo zoyambirira pafomu la Uphungu wa Kulankhula mwazizoloŵera bwino lomwe mpaka pa mfundo inoyi, kusunga nthaŵi sikudzakhala vuto. Ngati mwadziŵa kale kulekanitsa mfundo zanu zazikulu ndi kukonza autilaini yoyenera, mudzaona kuti nthaŵi imangosungika yokha. Kusunga nthaŵi kwaikidwa chakumapeto kwa fomuyo chifukwa kumadalira kwambiri maluso oyambirirawo a kulankhula amene mwawaphunzira kale.

22 Kaŵirikaŵiri vuto pa nthaŵi limakhala kudya nthaŵi. Mlankhuli amene wakonzekera bwino lomwe kaŵirikaŵiri amakhala ndi mfundo zambiri, koma afunikira kusamala kuti asagwiritse ntchito nthaŵi yoposa imene wapatsidwa.

23 Komabe, alankhuli atsopano kapena osazoloŵera, vuto lawo limakhala kusiyako nthaŵi. Ayenera kuphunzira kutsiriza nthaŵi yonse imene apatsidwa. Poyamba kungakhale kowavuta pang’ono kuti alinganize nkhani zawo kotero kuti zizitha ndendende panthaŵi yofunikira, koma ayenera kuyesetsa kumaliza pafupifupi nthaŵi yopatsidwayo. Komabe, kusamaliza nthaŵi yakeko sikudzayesedwa chofooka ngati wophunzirayo anaikonzekera bwino nkhani yake ndi kuipereka mokhutiritsa kwambiri, kupatulapo ngati nthaŵi imene wasiyayo n’njaikulu kodetsa nkhaŵa.

24 Kaya kulephera kusunga nthaŵi kwa wokamba nkhani kuyenera kuyesedwa chofooka kapena ayi, kudzadalira kuona mmene omvetsera akulabadirira pamene iye akulankhula. Pamene woyang’anira sukulu asonyeza kuti nthaŵi yatha, wophunzirayo ayenera kukhala womasuka kumaliza sentensi imene alipo. Ngati ndi sentensi imeneyo akhoza kumaliza nkhani yake mogwira mtima moti omvetserawo n’kuona kuti amvetsera nkhani yokwanira, pamenepo kulephera kusunga nthaŵi sikuyenera kuyesedwa chofooka.

25-29. Kodi munthu angatani pofuna kutsimikiza kuti adzasunga bwino nthaŵi pankhani yake?

25 Kodi ndi motani mmene munthu angamasungire bwino nthaŵi? Kwenikweni zimadalira kukonzekera. Kukonzekera n’kofunika kwambiri, osati kusanja mfundo kokha, komanso kalankhulidwe ka nkhaniyo. Ngati mwakonzekera bwino lomwe kalankhulidwe kake, kaŵirikaŵiri nthaŵi idzasungika bwino.

26 Posanja nkhani yanu sonyezani bwino lomwe zimene zili mfundo zanu zazikulu. Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse mungakhale ndi mfundo zazing’ono zingapo zoti mukazifotokoze. Komanso, zina zidzakhala zofunika kwambiri koposa zina. Onani kuti n’ziti zimene zili zofunika kwambiri pa nkhaniyo ndipo n’ziti zimene zingalumphidwe kutakhala kofunika kutero. Ndiyeno ngati, m’kati mwa nkhani yanu, muona kuti nthaŵi ikukutherani, kudzakhala kosavuta kungosankhulapo mfundo zazikulu zokha ndi kusiya zazing’onozo.

27 Zimenezo n’zimene kaŵirikaŵiri tiyenera kumachita mu utumiki wakumunda. Pamene tipita kumakomo a anthu, ngati anthuwo alola kuti amvetsere timalankhula nawo kwa mphindi zochulukirapo. Koma timakhalanso okonzekera kupereka ulaliki umodzimodziwo m’njira yachidule, tikumatenga mwina mphindi imodzi kapena ziŵiri zokha ngati kuli kofunika. Kodi timachita motani zimenezo? Timakumbukira mfundo yathu yaikulu imodzi kapena zingapo ndi mawu ofunikira ochirikiza mfundozo. Timakhalanso ndi mfundo zina zazing’ono zimene zingagwiritsidwe ntchito kufutukula nkhaniyo, koma tikudziŵa kuti ngati mkhalidwe sulola timasiya zimenezo. Tingatsatirenso njira imodzimodziyi pokamba nkhani papulatifomu.

28 Kaŵirikaŵiri kumakhala kothandiza kwa mlankhuli kulemba chizindikiro m’mphepete mwa nkhani yake chosonyeza pamene ayenera kufika atatsiriza theka la nthaŵi yake, kapena ngati nkhani yakeyo ili yaitali, angaigaŵe m’zigawo zinayi. Ndiyeno pamene adutsa zizindikiro za nthaŵizo paautilaini yake, ayenera kuyang’ana pa koloko kuti aone mmene akuchitira. Ngati aona kuti nthaŵi ikum’thaŵa, imeneyo ndiyo nthaŵi yoti ayambe kulumpha mfundo zazing’ono, m’malo moti ayambe kutero nthaŵi itatha kale zimene zingam’pangitse kungophwanyirira mawu omalizira ndi kuwononga kugwira mtima kwake. Komabe, kumakhala kosokoneza kwambiri ngati mlankhuli akungoyang’anayang’ana pawochi nthaŵi zonse kapena ngati akuyang’anapo moonekera kwambiri, kapenanso ngati auza omvetsera ake kuti nthaŵi yam’thera choncho ayenera kufulumiza nkhani yake. Zimenezo ayenera kuzichita m’njira yachibadwa yosadodometsa nayo omvetsera.

29 Kuti musunge bwino nthaŵi yonse ya nkhani m’pofunika kuti mawu oyamba akhale autali woyenera, ndi kuti iliyonse ya mfundo zazikulu ifotokozedwe m’nthaŵi yoyenera, komanso kuti musiye nthaŵi yokwanira ya mawu omalizira. Chimenechi si chinthu chongochiganiza nthaŵi yomweyo mutaona kuti nthaŵi yakutherani. Ngati muyang’ana nthaŵi kuyambira pachiyambi penipeni, mapeto ake adzakhala nkhani yokambidwa bwino komanso yosunga nthaŵi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena