Mutu 9
Pali Wina Wokulirapo
KODI munayamba mwamumva munthu wina akumati, “Ndikufuna ndikanakhala wamkuru kotero kuti ndikadatha kuchita chinthu chiri chonse chimene ndinachifuna”?—Kodi inu munayamba mwafuna zimenezo?—
Nzoona kuti achikulire angathe kuchita zinthu zina zimene ana sangathe. Koma palibe ali yense wa ife amene angathe kuwapanga malamulo athu onse kaamba ka moyo. Pali wina wokulirapo koposa ife. Kodi mukumdziwa ameneyo?—
Anthu ochuruka amabvomereza kuti Mulungu alidi wokulirapo koposa ife. Koma sikuli kokwanira kunena chimenecho. Ife tifunikira kusonyeza kuti timachikhulupilira icho mwa njira ya zinthu zimene ife timazichita.
Ichi chikusonyezedwa ndi chimene chinamchitikira Adamu ndi Hava. Iwo anali mwamuna ndi mkazi oyambilira. Anthu ena amanena kuti nkhani yonena za Adamu ndi Hava iri kokha yoyerekezera. Koma Mphunzitsi Wamkuruyo sananene zimenezo. Iye anadziwa kuti iyo inali yoona. Mvetserani, ndipo ndidzakuuzani chimene chinachitika.
Pamene Mulungu anampanga Adamu ndi Hava, iye anawaika iwo m’munda wokongola m’malo ochedwa Edene. Uwo unali munda wa maluwa, paradaiso. Iwo akadatha kukhala ndi moyo pamenepo kosatha. Koma panali phunziro limene iwo anafunikira kuliphunzira. Ndipo liri phunziro limene ife tifunikira kuliphunziranso. Ilo siliri lobvuta. Ilo liri lapafupi ngati ife kwenikweni tikufuna kuliphunzira ilo.
Yehova anamuuza Adamu ndi Hava kuti iwo akadatha kudya zipatso zonse ndi miteza zimene iwo anazifuna kuchokera m’mitengoyo mu Edene. Koma panali mtengo umodzi wokha umene iwo sanayenera kudya. Yehova anati kwa Adamu. “Koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:17.
Kodi nchiani chimene chikachitika ngati iwo akanadya zochokera ku mtengo umenewo?—Iwo akafa. Moyo wao unadalira pa kumumvera Yehova Mulungu. Sikunali kokwanira kungonena kuti iwo anamkhulupilira Mulungu. Iwo anafunikira kukusonyeza uko mwa njira ya zinthu zimene iwo anazichita. Limenelo linali phunzirolo. Silinali kwenikweni lobvuta, eti?—Koma linali lofunika kwambiri.
Ngati Adamu ndi Hava akanamumvera Mulungu, iwo akanamasonyeza kuti iwo anamkonda iye ndipo anamfuna iye kukhala wolamulira wao. Koma ngati iwo akadya zochokera ku mtengo umenewo, kodi kukasonyeanji?—Kukasonyeza kuti iwo sanali kwenikweni oyamika kaamba ka zinthu zonse zimene Mulungu anali atawapatsa iwo. Iwo akakhala akumanena kuti: “Palibe munthu ali yense amene angathe kutiuza ife cha kuchichita. Tidzachita monga momwe ife tikufunira.”
Kodi inuyo mukadachitanji ngati mukadakhalapo? Kodi inuyo mukadakhala mutamumvera Yehova? Kapena kodi inu mukadakhala mutadya zochokera mu mtengo umenewo?—
Poyamba Adamu ndi Hava anamumvera Mulungu. Koma kenaka chinjoka kapena njoka inalankhula ndi Hava tsiku lina. Ndithudi, njoka singathe kulankhula mwa iyo yokha. Anali mngelo amene anachipanga icho kuonekera ngati kuti chinjokacho chinali kulankhula. Mngelo ameneyo anali atayamba kuganizira zinthu zoipa. Iye anafuna kuti Adamu ndi Hava azilambira iye. Iye anafuna kuti iwo azichita zinthu zimene iye anazinena. Iye anafuna kuwatenga malo a Mulungu.
Chotero mngelo woipa ameneyo anaika malingaliro olakwa m’maganizo mwa Hava. Iye anati kwa mkaziyo: ‘Mulungu sanakuuzeni zoona. Inu simudzafa ngati mudya zochokera ku mtengo umenewo. Inu mudzakhala anzeru ngati Mulungu.’ Kodi inu mukanachikhulupilira chimene mau amenewo anachinena?—
Hava analibe kuyenera kuli konse kwa kuchikulupilira chimene chinjokacho chinanena. Chinthu chiri chonse chimene iye anali nacho chinali chochokera kwa Mulungu. Koma tsopano iye anayamba kufuna kanthu kena kamene Mulungu sanampatse iye. Iye anadya zochokera ku mtengowo. Ndiyeno iye anapereka zina kwa Adamu.
Adamu sanachikhulupilire chimene chinjokacho chinanena. Koma kufuna kwache kukhala limodzi ndi Hava kunali kwamphamvu kwambiri koposa chikondi chache kaamba ka Mulungu. Chotero nayenso anadya za mtengowo.—Genesis 3:1-6.
Kodi choturukapo chache chinali chotani?—Mulungu sananame. Moyo umadaliradi pa kumumvera iye. Chotero Adamu ndi Hava anafa. Ndipo iwo anabweretsa imfa ku mtundu wonse wa anthu.
Baibulo limatiuza ife kuti mngelo amene adanama kwa Hava amachedwa Satana Mdierekezi. Iye ali mdani wa Mulungu. Ndipo iye ali mdani wathunso.—Chibvumbulutso 12:9.
Iye amafuna kumpangitsa munthu ali yense kusamumvera Yehova. Chotero iye amayesayesa kuika malingaliro oipa m’maganizo mwathu. Iye amanena kuti palibe munthu ali yense amene amamkondadi Yehova. Iye amanena kuti inu ndi ine sitimamkonda Mulungu ndi kuti ife sitimafunadi kuchita chimene Mulungu amachinena. Koma kodi iye akunena zoona? Kodi ife tiri otero?—
Mdierekezi amanena kuti ife tidzaleka kumamtumikira Yehova ngati munthu wina akupangitsa iko kukhala kobvuta pang’ono kaamba ka ife. Iye amanena kuti ife timamumvera. Yehova kokha pamene chinthu chiri chonse chikuyenda m’njira imene ife tikuchifunira icho. Iye amanena kuti munthu ali yense ali wotero. Kodi iye akunena zoona?—
Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti Mdierekeziyo ali wabodza! Iye anasonyeza kuti pali anthu amene amamkondadi Yehova. Iye sananena kuti: ‘Palibe munthu ali yense amene angathe kundiuza ine chimene ndingachichite.’ M’malo mwache, iye anati: “Atate ali wamkuru ndi Ine.” Iye anamumvera Yehova. Ndipo iye sanakuchita iko nthawi zonse, ngakhale pamene anthu ena anakupangitsa kukhala kobvuta kaamba ka iye. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova kufikira iye atafa. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Mulungu anamuukitsira iye, kuti akhale ndi moyo kosatha.—Yohane 14:28.
Chimenecho ndicho chimene Mphunzitsi Wamkuruyo anachichita. Koma kodi nchiani chimene ife tidzachichita?—Ngati ife sitimumvera Yehova, pamenepo ife tiri kumachita chimene Mdierekezi amafuna kuti ife tichite. Koma ngati ife timamkondadi Mulungu wathu, ife tidzawamvera malamulo ache. Tidzawachita iwo tsiku liri lonse. Ndipo tidzawachita iwo chifukwa chakuti ife timafunadi kuwachita.
(Kodi ndani amene ife tidzamtumikira—Yehova kapena Mdierekezi? Werengani chimene Baibulo limachinena ponena za nkhani imeneyi pa Yobu 1:8-12; 2:1-5; 27:5; Miyambo 27:11.)