Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 3 tsamba 14-tsamba 15 ndime 3
  • Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Anataya Malo Ao
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mulungu ndi Wamkulu Kuposa Aliyense
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Pali Wina Wokulirapo
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 3 tsamba 14-tsamba 15 ndime 3
Adamu ndi Hava akutuluka m’munda wa Edeni

MUTU 3

Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu

Adamu wagwira chipatso cha mtengo woletsedwa chimene Hava wamupatsa

Tsiku lina Hava ali yekha, njoka inabwera n’kuyamba kulankhula naye. Inamufunsa kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anakuletsani kuti musamadye zipatso za mtengo uliwonse m’mundamu?’ Hava anayankha kuti: ‘Ayi. Anangotiletsa zipatso za mtengo umodzi wokha, ndipo anati tikadzadya zipatso zimenezo tidzafa.’ Ndiyeno njokayo inati: ‘Inutu simudzafa. Ndipo mukadya zipatso zimenezi mudzafanana ndi Mulungu.’ Kodi zimenezi zinali zoona? Ayi, linali bodza. Koma Hava anakhulupirira zimene njokayi inanena. Atayamba kuyang’anitsitsa zipatsozo, anayamba kuzisirira. Ndiyeno anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya kenako anakapatsa Adamu. Adamu ankadziwa kuti akapanda kumvera Mulungu adzafa. Komabe nayenso anadya chipatsocho.

Adamu ndi Hava akutuluka m’munda wa Edeni ndipo angelo ndi lupanga lozungulira akulondera khomo lolowera m’mundawo

Madzulo a tsiku lomwelo Yehova analankhula ndi Adamu ndi Hava. Anawafunsa chifukwa chake sanamvere. Hava anati njoka ndi imene yamuchititsa, ndipo Adamu anati Hava ndi amene wamuchititsa. Chifukwa cha kusamverako, Yehova anawathamangitsa m’munda wa Edeni. Kuti asabwereremonso, Yehova anaika angelo komanso lupanga loyaka moto pamalo olowera m’mundawo.

Yehova ananena kuti njoka nayonso idzalangidwa. Komatu sinali njoka yeniyeni imene inalankhula ndi Hava. Yehova sanalenge njoka zoti zizitha kulankhula. Choncho mngelo woipa ndi amene anachititsa kuti njokayo ilankhule. Anachita izi pofuna kunamiza Hava. Mngelo ameneyo amadziwika kuti Satana Mdyerekezi. M’tsogolomu, Yehova adzamuwononga kuti asamadzanamizenso anthu.

“Mdyerekezi . . . ndi wopha anthu kuchokera pachiyambi ndipo sanapitirize kukhala mʼchoonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi.”​—Yohane 8:44

Mafunso: N’chifukwa chiyani Hava anadya chipatso? Kodi chinachitika n’chiyani Adamu ndi Hava atalephera kumvera Yehova? Kodi Satana Mdyerekezi ndi ndani?

Genesis 3:1-24; Yohane 8:44; 1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 12:9

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena