Mutu 14
Mphamvu pa Mphepo ndi Mafunde
KODI INU munayamba mwakhala mu mkuntho pamene mphepo inali kumaomba zolimba kwambiri?—Kodi munaopa?—Kuli bwino kukhala wosamala pa nthawi yonga imeneyo. Pakuti inu mukatha kubvulazidwa mu mkuntho woipa.
Chotero kodi nchiani chimene inu muyenera kuchichita pamene mphepo iyamba kuomba zolimba, kapena pamene inu muona mphezi ikung’anima kumwamba? Kodi inu mukuganiza chiani?—Chinthu chanzeru kuchichita ndicho kulowa m’nyumba. Ngati inu simutero, mphepoyo ikatha kukugwetserani nthambi ya mtengo. Kapena mphezi ingakumenyeni. Anthu mazana ambiri amaphedwa chaka ndi chaka ndi mikuntho.
Inu ndi ine sitingathe kuziletsa mphepo zamphamvu kuti zisaombe. Ndipo ife sitingathe kuwachititsa bata mafunde a nyanja. Kunena zoona, palibe munthu ali yense wamoyo amene angathe kuchichita chimenechi. Koma kodi inu mukudziwa kuti munthu wina anakhala pa dziko lapansi pa nthawi ina amene anali ndi mphamvu pa mphepo ndi mafunde?—Anali Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo. Kodi mungafune kumva chimene iye anachichita?—
Madzulo tsiku lina iye atatha kuphunzitsa m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya, iye anati kwa ophunzira ache: “Tiolokere tsidya lina.” Chotero iwo ananyamuka m’bwato nayamba kuoloka nyanjayo.
Yesu anali wotopa kwambiri. Iye anali atagwira nchito zolimba tsiku lonse. Chotero iye anapita ku mbuyo kwa bwatolo nagona pansi pa mtsamilo. Mwamsanga iye anagona tulo tatapatapa.
Ophunzirawo anakhalabe maso kuliyendetsabe bwatolo. Chiri chonse chinali bwino lomwe kwa kanthawi, koma kenaka mphepo yamphamvu inabuka. Iyo inaomba zolimba moonjezereka-onjezereka, ndipo mafundewo anapitirizabe kumakula-kula. Mafundewo anayamba kumagabvikira m’bwatolo, ndipo bwatolo linayamba kudzaza madzi. Ophunzirawo anachita mantha kuti iwo adzamira.
Koma Yesu sanachite mantha. Iye anali m’tulobe kumbuyo kwa bwatolo. Potsirizira pache, ophunzirawo anamdzutsa, nati: ‘Mphunzitsi, Mphunzitsi, tipulumutseni; ife tiri pafupi kufa mu mkuntho uwu.’
Atatero, Yesu anadzuka nalankhula ndi mphepo ndi mafundewo. “Tonthola, khala bata!” iye anatero. Pomwepo mphepoyo inaleka kuomba. Nyanjayo inakhala bata.
Ophunzirawo anadabwa. Iwo anali asanachione chiri chonse chonga chimenecho ndi kale lonse. Iwo anayamba kumalankhula wina ndi mnzache kuti: “Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?”—Marko 4:35-41; Luka 8:22-25.
Kodi inu mukumdziwa Yesu?—Kodi inu mukukudziwa kumene iye amalandirako mphamvu yache yaikuruyo?—Ophunzirawo sanayenere kukhala ndi mantha pamene Yesu anali momwemo limodzi ndi iwo, chifukwa chakuti Yesu sanali munthu wamba. Iye ankatha kuchita zinthu zodabwitsa zimene palibe munthu wina akanatha kuchita. Tandiloleni ndikuuzeni kanthu kenanso kamene iye pa nthawi ina anakachita pa nyanja yanamondwe.
Kunali nthawi ina pambuyo pache, pa tsiku lina. Pamene kunali kutada Yesu anawauza ophunzira ache kukwera bwato ndi kutsogola kunka ku tsidya lina la nyanjayo. Pamenepo Yesu anakwera kulowa m’phiri yekha. Anali malo opanda phokoso kumene iye akadatha kupemphera kwa Atate wache, Yehova Mulungu.
Ophunzirawo analowa m’bwatolo, nayamba kuoloka nyanjayo. Koma posakhalitsa mphepo inayamba kuomba. Iyo inaomba zolimba moonjezeraka-onjezereka. Tsopano inali nthawi ya usiku.
Amunawo anachotsa thanga nayamba kupalasa. Koma iwo sanali kumapita patali kwambiri, chifukwa chakuti mphepo yamphamvuyo inali kumamenyana nawo. Bwatolo linali kumandenguma cha m’mbuyo ndi cha patsogolo m’mafunde akuruwo, ndipo madzi anali kumagabvikiramo. Amunawo analimbika zolimba kumayesayesa kufika ku gombe, koma iwo sanathe.
Yesu anali chikhalirebe yekha m’phirimo. Iye anakhala momwemo nthawi yaitali. Koma tsopano adatha kuona kuti ophunzira ache anali m’ngozi m’mafunde akuruwo. Chotero iye anatsika m’phirimo kunka m’mphepete mwa nyanjayo. Iye sanalumphiremo ndi kuyamba kusambira, ndipo iye sanayende kubvu-kubvu m’madziwo. Ai, koma Yesu anayamba kuyenda pamwamba pa nyanja yanamondweyo monga momwe ife tikanayendera pa kapinga!
Kodi nchiani chimene chikachitika ngati inu mutayesa kuyenda pa madzi? Kodi mukuchidziwa?—Inu mukanamira, ndipo mungafe ndi madzi. Koma Yesu anali wosiyana. Iye anali ndi mphamvu zapadera.
Yesu anali ndi ulendo wautali wa pafupifupi mamailo atatu kapena anai kuti alipeze bwatolo. Chotero kunali pafupifupi mbanda kucha pamene ophunzirawo anamuona Yesu akumadza kwa iwo pa madzi. Koma iwo sadachikhulupilire chimene iwo anachiona. Iwo anaopsyedwa kwambiri, ndipo iwo anapfuula mwa mantha ao.
Pamenepo Yesu analankhula nawo: “Limbani mtima, ndine pano; musakhale ndi mantha.”
Mwamsanga Yesu atakwera m’bwatolo, namodweyo analeka. Ophunzirawo anadabwanso. Iwo anagwa pamaso pa Yesu, nati: “Inu mulidi Mwana wa Mulungu.”—Mat. 14:23-33; Yoh. 6:16-21, NW.
Kodi sikukadakhala kodabwitsa kukhala ndi moyo kale pa nthawi imeneyo ndi kumuona Yesu akumazichita zinthu ngati zimenezo?—Eya, ife tingathe kukhala ndi moyo pa nthawi imene Yesu adzazichita zinthu zimene ziri zodabwitsa mofananamo.
Baibulo limanena kuti Mulungu wampanga Yesu kukhala Wolamulira mu ufumu wa Mulungu, ndipo posachedwapa boma lache lokha lidzalamulira pa dziko lapansi ili. Palibe munthu ali yense amene ali kukhala ndi moyo pa nthawi imeneyo adzafunikira kukhala ndi mantha a namondwe. Yesu adzaigwiritsira nchito mphamvu yache pa mphepo ndi mafunde kaamba ka dalitso la onse amene amamumvera iye. Kodi imeneyo sidzakhala nthawi yodabwitsa mu imene mungakhalemo?—
(Malemba ena omasonyeza mphamvu yaikuru ya Yesu monga uyo amene Mulungu akumpanga kukhala wolamulira mu ufumu wa Mulungu ndiwo: Mateyu 28:18; Dan. 7:13, 14; Aefeso 1:20-22.)