Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 84 tsamba 196-tsamba 197 ndime 4
  • Yesu Anayenda Panyanja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anayenda Panyanja
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mphamvu pa Mphepo ndi Mafunde
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Yesu Angatiteteze
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu Analetsa Mphepo Yamphamvu Panyanja
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Wolamulira Amene Akhoza Kulamulira Mphepo Yamphamvu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 84 tsamba 196-tsamba 197 ndime 4
Yesu akuyenda pamadzi ndipo akuuza Petulo kuti apite kumene iye ali

MUTU 84

Yesu Anayenda Panyanja

Kuwonjezera pa kuchiritsa odwala ndi kuukitsa akufa, Yesu ankathanso kulamulira mphepo komanso mvula. Tsiku lina, Yesu anapita kuphiri kukapemphera, ndiye atamaliza anaona kuti panyanja ya Galileya panali chimphepo ndi mafunde. Atumwi ake anali m’boti ndipo ankalimbana ndi mphepo panyanjapo. Ndiyeno iye anatsika m’phirimo n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali boti la atumwi akewo. Atumwiwo ataona munthu akuyenda pamadzi, anachita mantha. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Musachite mantha, ndine.’

Yesu akuyenda pamadzi ndipo akuuza Petulo kuti apite kumene iye ali

Petulo anati: ‘Ambuye ngati ndinuyo, ndiuzeni ndibwere kumene muliko.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Bwera.’ Choncho Petulo anatuluka m’boti muja n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. Koma atayandikira, anayang’ana chimphepo chija. Atatero anachita mantha ndipo anayamba kumira. Iye anafuula kuti: ‘Ambuye, ndithandizeni!’ Yesu anamugwira dzanja n’kumufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani unayamba kukayikira? Chikhulupiriro chako chili kuti?’

Yesu ndi Petulo anakwera m’boti muja ndipo nthawi yomweyo mphepo ija inasiya. Kodi ukuganiza kuti atumwiwo anamva bwanji? Iwo anati: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”

Si nthawi yokhayi pamene Yesu anachita zodabwitsa ngati zimenezi. Pa nthawi ina ali ndi atumwi ake muboti, Yesu anapita chakumbuyo kwa botilo n’kugona. Iye ali m’tulo, panyanjapo panayambika chimphepo. Mafunde ankamenya botilo ndipo mubotimo munalowa madzi. Atumwi anamudzutsa n’kumuuza kuti: ‘Mphunzitsi tifatu, chonde tithandizeni.’ Yesu anadzuka n’kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo chimphepo chija chinatha ndipo panyanjapo panali bata. Ndiyeno Yesu anafunsa atumwiwo kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Atumwiwo anayamba kuuzana kuti: “Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.” Iwo anaphunzirapo kuti ngati amakhulupirira kwambiri Yesu, sayenera kuopa chilichonse.

“Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriro choti ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo?”​—Salimo 27:13

Mafunso: N’chifukwa chiyani Petulo anayamba kumira? Kodi atumwi anaphunzira mfundo iti?

Mateyu 8:23-27; 14:23-34; Maliko 4:35-41; 6:45-52; Luka 8:22-25; Yohane 6:16-21

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena