Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 23 tsamba 95-98
  • Dalitso la Nchito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dalitso la Nchito
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 23 tsamba 95-98

Mutu 23

Dalitso la Nchito

KODI inu mukadakonda kuchita chiti, kugwira nchito kapena kusewera?—Nzoona kuti ife tonse timasangalala ndi kusewera.—Koma kodi kukanakhaladi kwabwino ngati ife tikanasewera nthawi zonse?—Kodi munayamba mwaganizira chimene chikanachitika ngati panalibe munthu ali yense amene anagwira nchito?—

Taganizirani chakudya chimene inu mumadya. Kodi mukudziwa kumene icho chimachokera?—Chochuruka cha icho chimachokera pa zomera ndi mitengo. Koma ngati panalibe munthu ali yense amene anazisamalira izo ndi kuchera zipatso ndi ndiwo zamasamba, kodi inuyo mukanadyanji? Kodi sikuli kwabwino kuti anthu amagwira nchito kotero kuti inu mumakhala ndi chakudya cha kuchidya?—

Taunguza—ungazani m’nyumba m’mene inu mumakhala. Kodi inu muli ndi kama wogonapo?—Kodi muli mipando pa imene mungakhalepo ndipo thebulo?—Kodi inu simuli okondwa kuti munthu wina angwira nchito kuzipanga zinthu zimenezi?—

Kodi ndi motani mmene Mphunzitsi Wamkuruyo analingalirira ponena za nchito? Tiyeni tione.

Ngakhale pamene anali mnyamata iye anagwira nchito mu shopo yaukalipentala. Iye anapanga zinthu za mitengo. Yosefe anali kalipentala, ndipo iye anamlera Yesu monga mwana wache wa iye mwini. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Baibulo limamchera Yesu “mwana wa mmisiri wa mitengo.” M’masiku amenewo mnyamata ankaphunzira kuchita nchito zimodzimodzizo zimene atate wache anazichita.—Mateyu 13:55.

Ingakhale inali yomkhwimira Yesu poyamba. Koma limodzi ndi kuchitachita, iye anaphunzira kuichita nchitoyo bwino lomwe. Yesu anakhalanso kalipentala.—Marko 6:3.

Kodi inu mukuganizira kuti nchito imeneyi inapatsa Yesu chikondwelero?—Kodi inuyo mukanakhala wachimwemwe ngati inuyo mukadapanga matebulo ndi mipando zabwino kwambiri ndi zinthu zina kaamba ka anthu kuzigwiritsira nchito?—Baibulo limanena kuti kuli bwino kwa munthu kukondwera ndi nchito zache.’ Nchito imapereka mtundu wina wachikondwelero chimene inu simungachipeze kuchokera m’kusewera. Sikuli kolakwa kusewera, koma sikuli bwino kusewera nthawi zonse.—Mlaliki 3:22.

Yesu sanagwire nchito monga kalipentala moyo wache wonse. Yehova Mulungu anali ndi nchito yapadera kaamba ka iye kuichita pa dziko lapansi. Kodi inu mukuidziwa nchito imeneyo?—Yesu anati: “Ndiyenera ndilengeze mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu, chifukwa chakuti ine ndinatumidwira imeneyi.” Inde, Mulungu anali ndi nchito yolalikira kuti Yesu aichite.—Luka 4:43, NW.

Kodi ndi motani mmene Yesu analingalirira ponena za kuichita nchito imeneyi? Kodi iye anafuna kuichita iyo?—

Yesu anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yache.” Kodi ndi kwakukuru motani mmene inuyo mumakondera kudya chakudya chanu chokondedwa?—Chimenechi chimakupatsani inu lingaliro la ukuru umene Yesu anaikondera nchito imene Mulungu anampatsa iye.—Yohane 4:34.

Mulungu anatipanga ife kotero kuti ife timakhala achimwemwe pamene ife tiphunzira kugwira nchito. Iye amanena kuti iyo iri mphatso yache kwa munthu kuti iye ayenera “kukondwera ndi nchito yache yokhwima.” Chotero, ngati inu muphunzira kugwira nchito pamene inu muli ang’ono, moyo wanu wonse udzakhala wosangalatsa kwambiri.—Mlaliki 5:19, NW.

Chimenecho sichimatanthauza kuti mwana wamng’ono angathe kuichita nchito ya munthu wamkuru, koma ife tonse tingathe kuchita nchito zina. Atate wanu amagwira nchito tsiku ndi tsiku kotero kuti ife tidzakhala ndi chakudya kuti tidye ndi nyumba mu imene tingakhalemo. Kodi mukuudziwa mtundu wa nchito imene atate wanu amaichita?—Iwo samangodzigwilira okha nchito. Iwo amagwira nchito kaamba ka ubwino wa banja lonse. Ndipo mai wanu amagwira nchito kukonza zakudya zathu. Iwo amapasamalira pa nyumba pathu ndi zobvala zathu kukhala zoyera.

Kodi pali nchito yanji imene inu mungathe kuchita imene idzakhala dalitso ku banja lonselo?—Inu mungathandize kuyala thebulo, kupukuta mbale, kusamalira chipinda chanu ndi kutolera zidole zanu. Mwinamwache inu mukuzichita kale zina za zinthu zimenezo. Kodi nchito imeneyo iridi dalitso?—

Tiyeni tione mmene nchito yonga ngati imeneyo iliri dalitso. Zidole ziyenera kuchotsedwa mutatha kusewera nazo. Kodi nchifukwa ninji inu mukanena kuti chimenecho chiri chofunika?—Zimathandiza kuipangitsa nyumbayo kukhala yaudongo. Kulinso kofunika chifukwa chakuti kungathe kuletsa ngozi. Ngati inu simuzitolera zidole zanu, mai wanu angafike tsiku lina mikono yao itadzaza zinthu ndi kuponda chimodzi cha izo. Iwo angaphunthwe ndi kugwa ndi kupweteka mutu wao. Iwo angafunikiredi kupita ku chipatala. Kodi chimenecho sichikakhala choopsya?— Chotero, pamene inu muzichotsa zidole zanu mutatha kusewera, kumeneko ndiko dalitso kwa ife tonse.

Palinso nchito ina imene ana ali nayo. Ine ndiri kumanganizira za nchito ya ku sukulu. Pa sukulu inu mumaphunzira kuwerenga. Ana ena amakuona kuwerenga kukhala kokondweretsa, koma ena amanena kuti iko kuli kobvuta. Ngakhale ngati iko kumaonekera ngati kobvuta poyamba, inu mudzakhala okondwa ngati muphunzira kuwerenga bwino. Pamene inu mudziwa kuwerenga, pali zinthu zambirimbiri zokondweretsa zimene inu mungathe kuziphunzira. Inu mudzakhala okhoza kudziwerengera nokha, ngakhale bukhu la Mulungu, Baibulo. Chotero, pamene inu muichita nchito yanu ya ku sukulu bwino lomwe, iyo iridi dalitso, ati?—

Pali anthu ena amene amayesayesa kupewa nchito. Mwinamwache inu mukumdziwa wina amene amachita chimenecho. Koma popeza kuti Mulungu anatipanga ife kuti tizigwira nchito, ife tifunikira kuphunzira kusangalala ndi nchito.

Nazi zinthu zina zimene zingathe kuthandiza. Pamene inu muli ndi nchito yakuti muichite, dzifunseni nokha kuti: Tsopano, kodi nchifukwa ninji imeneyi ifunikira kuchitidwa? Pamene inu mudziwa chifukwa chache chimene kanthu kena kali kofunika, kuli kwapafupi kwambiri kuichita iyo. Ndipo kaya nchitoyo iri yaikiru kapena yaing’ono, ichiteni nchitoyo bwino lomwe. Ngati inuyo muchita chimenecho, inu mungathe kukondwera ndi nchito ya manja anu. Pamenepo inu mudzadzidziwira nokha kuti nchito iridi dalitso.

(Baibulo lingathe kumthandiza munthu kukhala wogwira nchito bwino. Werengani chimene ilo limachinena pa Akolose 3:23; Miyambo 10:4; 22:29, Mlaliki 3:12, 13, 22.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena