Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lr mutu 42 tsamba 217-221
  • Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito
  • Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Nkhani Yofanana
  • Dalitso la Nchito
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • “Mmisiri wa Matabwa”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
lr mutu 42 tsamba 217-221

Mutu 42

Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito

KODI ndi chiyani chimene umakonda kwambiri? Kugwira ntchito kapena kuseŵera?— Kunena zoona, kuseŵera si koipa. Baibulo limanena kuti Yerusalemu ‘adzakhala ndi ana aamuna ndi aakazi akuseŵera m’misewu yake.’—Zekariya 8:5.

Mphunzitsi Waluso anali kusangalala kuona ana akuseŵera. Asanabwere padziko lapansi pano, anati: “Ndinali pa mbali [pa Mulungu] ngati mmisiri . . . ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse.” Mfundo imeneyi yakuti Yesu anali “mmisiri” ikutanthauza kuti anagwira ntchito limodzi ndi Yehova kumwamba. Ndipo ali kumwambako, Yesu anati: ‘Ndinasekerera ndi ana a anthu.’ Inde, monga momwe taphunzirira kale, Mphunzitsi Waluso anali kukonda kwambiri aliyense, ndi ana omwe.—Miyambo 8:30, 31.

Anthu akumanga mitolo ya tirigu

Kodi Mphunzitsi Waluso anali kusangalala ndi chiyani asanabwere padziko lapansi?

Kodi ukuganiza kuti Yesu anali kuseŵera ali mwana?— Ayenera kuti anali kuseŵera ndithu. Koma popeza kuti anali “mmisiri” kumwamba, kodi anagwiranso ntchito padziko lapansi pano?— Eya, Yesu anali kutchedwa ‘mwana wa mmisiri wa matabwa.’ Komanso anali kutchedwa ‘mmisiri wa matabwa.’ Kodi zimenezi zikutiuza chiyani?— Zikutiuza kuti Yosefe, amene analera Yesu monga mwana wake, ayenera kuti anaphunzitsa Yesu ntchitoyo. Ndipo nayenso Yesu anakhala mmisiri wa matabwa.—Mateyu 13:55; Marko 6:3.

Kodi Yesu anali munthu wotani monga mmisiri wa matabwa?— Popeza kuti anatchedwa “mmisiri,” zikutanthauza kuti iye anali waluso pochita ntchito yake kumwamba. Ndiye chifukwa chake ngakhale padziko lapansi pano iye anakhalanso mmisiri wa matabwa popeza anali waluso, si choncho?— Komatu ntchito yopala matabwa inali yovuta kwambiri kalelo. Taona tsono kuvuta kwake. Yesu ayenera kuti anali kupita kutchire kukadula mitengo. Ndiye amati akagwetsa mtengo, anali kuuduladula ndi kunyamula kupita nawo kunyumba. Kenako anali kupala mitengoyo kukhala matabwa amene anali kupangira matebulo, mipando, ndi zinthu zina.

Kodi ukuganiza kuti Yesu anasangalala ndi ntchito imeneyi?— Kodi iwe ungasangalale ngati ungapangire anthu matebulo ndi mipando yabwino komanso zinthu zina zabwino?— Baibulo limanena kuti ndi bwino ‘munthu kukondwera ndi ntchito yake.’ Kusangalala kumene umakhala nako chifukwa chogwira ntchito kumaposa kusangalala kumene ungakupeze poseŵera.—Mlaliki 3:22.

Ndipotu, ntchito imatithandiza kwambiri kuti tiziganiza bwino ndi kukhala athanzi. Ana ambiri amakonda kungokhala, kucheza, ndi kuseŵera ndi anzawo basi. Chifukwa cha zimenezi amakhala aulesi ndi aliuma, ndipo sasangalala ngakhale pang’ono. Ndiponso sasangalatsa anthu ena. Kodi ukuganiza kuti tifunika kuchita chiyani kuti tizisangalala?—

Mu Mutu 17 wa buku lino tinaphunzira kuti kupatsa komanso kuchita zinthu zothandiza ena kumasangalatsa. (Machitidwe 20:35) Baibulo limanena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wosangalala.’ (1 Timoteo 1:11, NW) Ndipo, malinga ndi zija zimene taŵerenga m’buku la Miyambo, Yesu anali “kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse.” Ndi chifukwa chiyani Yesu anali wosangalala?— Eya, mwa zifukwa zina, iye mwini wake ananena kuti: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.”—Yohane 5:17.

Pamene Yesu anali padziko lapansi pano, sanagwire ntchito yopala matabwa moyo wake wonse. Yehova Mulungu anamupatsa ntchito yapadera yoti achite padziko lapansi pano. Kodi ntchito imeneyo ukuidziŵa?— Yesu anati: ‘Ndiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu chifukwa ndinatumidwa kudzatero.’ (Luka 4:43) Nthaŵi zina pamene Yesu analalikira anthu, iwo anamukhulupirira ndipo anauzanso ena zimene iye ananena, ngati mmene anachitira mkazi uyu Msamariya amene ukumuona apa.—Yohane 4:7-15, 27-30.

Yesu akulankhula ndi mzimayi wachisamariya pachitsime; Yesu akugwira ntchito ya ukalipentala

Kodi ndi ntchito ziŵiri ziti zimene Yesu anachita atabwera padziko lapansi?

Kodi Yesu anamva bwanji kuchita ntchito imeneyi? Kodi ukuganiza kuti iye anali kufuna kuchita ntchitoyo?— Yesu anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kodi umakonda kwambiri kudya chakudya chako cha pamtima?— Zimenezi zikungosonyeza mmene Yesu anakondera ntchito imene Mulungu anamupatsa kuti achite.

Mulungu anatipanga m’njira yakuti tizisangalala chifukwa chodziŵa kugwira ntchito. Iye amanena kuti mphatso Yake imene wapatsa munthu ndi yakuti munthuyo ‘azikondwera ndi ntchito yake.’ Choncho ukadziŵa kugwira ntchito uli mwana, moyo wako wonse udzakhala wosangalatsa kwambiri.—Mlaliki 5:19.

Zimenezi sizikutanthauza kuti mwana azichita ntchito ya munthu wamkulu ayi, koma kuti pali ntchito imene ife tonse tingachite. Mwina makolo ako amapita kuntchito masiku onse kuti akapeze ndalama zogulira chakudya cha banja lanu ndi zolipirira nyumba imene mukukhala. Ndipotu ukudziŵa kuti panyumba pamakhala ntchito yambiri yofunika kuchita kuti pakhale poyera ndiponso pooneka bwino.

Kodi ndi ntchito iti imene ungachite kuthandiza banja lonse?— Ungathandize kukonza pathebulo, kutsuka mbale, kutaya zinyalala, kusesa kumene umagona, ndi kutola zimene umaseŵeretsa ndi kuziika m’malo mwake. Mwina wakhala ukuchita zina mwa zimenezi. Ntchito imeneyo imathandiza banja kwambiri.

Amayi akufuna kugwa ndi zoseweretsa za ana

Kodi ndi chifukwa chiyani ufunika kuika zoseŵeretsa zako pamalo abwino ukamaliza kuseŵera nazo?

Tiye tione mmene ntchitoyo imathandizira. Zoseŵeretsa zifunika kuziika pamalo abwino ukamaliza kuseŵera nazo. Kodi ufunikadi kuchita zimenezi? Ukuganiza bwanji?— Zimathandiza kuti panyumba pazioneka bwino, ndipo zimapewetsa ngozi. Ngati sutola zoseŵeretsa zakozo, tsiku lina amayi ako angafike atanyamula zinazake kumanja, ndipo angaponde chimodzi mwa zoseŵeretsazo. Iwo angaterereke kenako ndi kugwa ndi kudzipweteka. Mwina angapweteke mpaka kupita kuchipatala. Kodi zimenezo zingakhale zabwino?— Waonatu nanga, ukamaika zoseŵeretsa zako pamalo abwino utamaliza kuseŵera nazo, zimathandiza onse m’banja.

Iliponso ntchito ina imene ana afunika kuchita. Mwachitsanzo, ntchito ya kusukulu. Kusukulu mumaphunzira kuŵerenga. Ana ena amakonda kuŵerenga, koma ena amanena kuti ndi kovuta. Ngakhale kuti poyamba kuŵerenga kumaoneka kovuta, udzasangalala ukadziŵa kuŵerenga bwino. Ndipo ukadziŵa kuŵerenga, ungadziŵenso zinthu zambiri zosangalatsa. Udzakhoza ngakhale kuŵerenga wekha buku la Mulungu, Baibulo. Ndiye ngati ukuchita ntchito ya kusukulu bwinobwino, zidzakuthandiza kwambiri, kodi si choncho?—

Alipo anthu ena amene safuna kugwira ntchito. Mwina ukudziŵapo munthu wotero. Koma popeza kuti Mulungu anatipanga kuti tizigwira ntchito, tifunika kudziŵa zimene tingachite kuti ntchitoyo izitisangalatsa. Kodi Mphunzitsi Waluso anaikonda motani ntchito yake?— Kwa iye ntchitoyo inali ngati kudya chakudya chake cha pamtima. Nanga ndi ntchito iti imene iye anali kunena?— Anali kunena za ntchito youza ena za Yehova Mulungu ndi mmene iwo angapezere moyo wosatha.

Ndiye pano pali zimene zingatithandize kusangalala ndi ntchito. Iwe uzidzifunsa mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndi chifukwa chiyani ntchito imeneyi ili yofunika?’ Ngati ukudziŵa chifukwa chake ntchitoyo ili yofunika, sivuta kuchita. Ndipo kaya ntchitoyo ili yaikulu kapena yochepa, uichite ndi mtima wonse. Ukatero, udzasangalala ndi ntchito ya manja ako, mofanana ndi Mphunzitsi wathu Waluso.

aibulo lingathandize munthu kukhala wakhama pantchito. Ŵerengani zimene akunena pa Miyambo 10:4; 22:29; Mlaliki 3:​12, 13; ndi Akolose 3:⁠23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena