Mutu 25
Awo Amene Anasankha Malo Abwino Kwambiri
ANTHU ena masiku onse amafuna zinthu zabwino kwambiri kaamba ka iwo eni. Iwo adzazitenga zinthu zimenezi munthu wina ali yense asanathe kuzipeza izo. Kodi inu mwachiona chimenechi?—Ine ndachiona.
Mwachitsanzo, pa chakudya ine ndaona mbale yaikuru ikumaperekedwa. Iyo inadzazidwa ndi zidutswa za keke wokoma kwambiri. Pamene mbaleyo inafika, munthu ali yense mosamalitsa anayang’anayang’ana zidutswazo kuti atsimikizire kuti iye anatenga chachikuru kwambiri. Kodi inu mukuganiza kuti kuli koyenera kuchita chimenecho?—
Pali kanthu kenanso kamene ine ndakaona kakuchitika. Atate ndi mai awatenga ana ao limodzi ndi iwo kukalichezera bwenzi lina. Pamene iwo analowa m’nyumba ya bwenzilo, anawo anafulumira kukapeza mipando yofewa kwambiri. Kodi chimenechi chiri choyenera?—
Pamene Mphunzitsi Wamkuruyo anali pa dziko lapansi kanthu kena konga kameneko kanachitika. Iye anaitanidwa ku phwando ku nyumba ya Mfarisi wina wochuka. Kunali alendo ambiri amene anaitanidwa. Pamene alendowo analowa kaamba ka chakudyacho, Yesu anaona kuti iwo ankasankha malo abwino kwambiri pafupi ndi mwini phwandolo. Iwo anafuna malo a ulemu. Kodi inuyo mungafune kumva chimene Yesu ananena kwa iwo?—
Iye anawauza iwo fanizo. Ilo linali ndi chilangizo chabwino kaamba ka alendo amenewo, ndipo ilo liri ndi chilangizo china chabwino kaamba ka ife lero lino.
Yesu anati: ‘Munthu wina angakuitaneni inu ku phwando lalikuru laukwati. Pamene inu mupita, musasankhe malo olemekezeka kwambiri kuti mukhalepo. Pakuti munthu wina wolemekezeka koposa inu angakhale ataitanidwanso. Pamenepo uyo wochita phwandoyo angafike kwa iwe nati, “Mpatseni munthu uyu malo anu.” Pamenepo iwe udzakhala ndi manyazi pamene ena onsewo akuyang’ana iwe ukupita ku malo apansi kwambiri.’
Yesu anafuna kuwasonyeza alendowo chinthu choyenera kuchita. Chotero iye anapitirizabe kunena kwa iwo kuti:
‘Pamene inu mwaitanidwa ku phwando la ukwati pita nukhale pansi pa malo apansi kwambiri. Pamenepo uyo amene wakuitanani angafike nati, “Bwenzi, ife tiri ndi malo abwino kwambiri koposa amenewa kaamba ka inu!” Pamenepo iwe udzakhala ndi ulemu pamaso pa ena onse pamene inuyo mukusuntha kunka ku malo abwino kwambiriwo.’—Luka 14:1-11, NW.
Kodi inuyo munaimvetsetsa nsonga ya fanizo la Yesu?—Tiyeni titenge chitsanzo, ndi kuona ngati inu munaimvetsetsa. Tiyeni tinene kuti tinali kupita kukadya chakudya cha madzulo ku nyumba ya munthu wina. Kodi inuyo mukasankha malo abwino kwambiri pamene inuyo munali okonzekera kukhala pansi? Kapena kodi inu mukanawasiyira malo abwino kwambiri munthu wina wache?—Kodi nchiani chimene mukuganiza kuti Yesu akakufunani inu kuchita?—
Tengani chitsanzo china. Yerekezerani kuti inu muli kukwera basi lodzaza anthu. Kodi inuyo muyenera kufulumira kuti mupeze pokhala, ndi kumlola munthu wokalamba kuimilira?—Kodi Yesu akanafuna kuti inu muchite chimenecho?—
Munthu wina anganene kuti sichimapanga kusiyana kuli konse kwa Yesu chimene ife timachichita. Koma kodi inuyo mumachikhulupilira chimenecho?—Pamene Yesu anali pa phwando lalikuru limenelo pa nyumba ya Mfarisiyo, iye anawayang’anitsitsa anthu pamene iwo anaisankha mipando yao. Ndipo kodi inu simuganiza kuti iye ali wokondweretsedwa mofananamo ndi zimene ife timazichita lero lino?—Tsopano popeza kuti Yesu ali kumwamba iye ndithudi ali pa malo abwino kwambiri kutiyang’ana ife.
Pamene munthu ali yense amayesayesa kupeza malo abwino kwambiri, iko kungathe kuchititsa bvuto. Nthawi zina chimenechi chimachitika pamene ana amapita kukakwera galimoto pamodzi. Mwamsanga pamene chitseko cha galimoto chatsegulidwa, iwo amathamanga kuti akapeze malo abwino kwambiri, aja apafupi ndi zenera. Ndipo pomwepo pamakhala kukangana. Iwo amakhala okwiyirana wina ndi mnzache chifukwa chakuti iwo onse amafuna malo abwino kwambiri.
Chimenechinso chingathe kuchitika pamene ana apita kukasewera sewero la mpira. Iwo asanayambe nkuyamba komwe kusewera iwo angakanganirane amene adzakhala woyamba. Kodi siziri zoipa kwambiri kuti zinthu zimenezi zimachitika?—
Nthawi zonse kumafuna kukhala woyamba kungathe kuchititsa bvuto lalikuru. Iko kunachititsadi bvuto pakati pa atumwi a Yesu. Kodi mukuchidziwa chimenecho?—
Yesu anafunikira kuwapatsa iwo onse chilangizo china chabwino. Yesu anawauza iwo kuti olamulira a mitundu amakonda kukhala akuru ndi olemekezeka. Iwo amafuna munthu ali yense kuwamvera iwo. Koma Yesu anawauza atsatiri ache kuti iwo sayenera kukhala otero. Makamaka, Yesu anati: “Amene ali yense amafuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wa onse.” Taganizirani chimenecho!—Marko 10:35-45, NW.
Kodi mumachidziwa chimene kapolo amachichita?—Iye amawatumikira anthu ena, koposa ndi kuwalola ena amtumikire iye. Iye amatenga malo apansi kwambiri, osati malo oyamba. Iye amachita monga wonyozeka kwambiri, osati wolekemezeka kopambana. Ndipo kumbukirani kuti Yesu ananena kuti munthu amene amafuna kukhala woyamba ayenera kuchita ngati kapolo kwa ena.
Tsopano, kodi nchiani chimene inu mukuganiza kuti chimenecho chimatanthauza kwa ife?—Kodi kapolo akakangana ndi mbuye wache ponena za amene adzapeza malo abwino kwambiri?—Kapena kodi iye adzatsutsa ponena za amene adzadya choyamba?—Yesu anasonyeza kuti masiku onse kapolo amamuika mbuye wache patsogolo pa iye mwini. Kodi imeneyo sindiyo njira imene ife tiyenera kuchitanso?— —Luka 17:7-10.
Inde, iyo iri njira Yachikristu kuwaika ena patsogolo pa ife eni. Ichi ndicho chimene Mphunzitsi Wamkuruyo anachichita. Ndipo ngati ife tichitsatira chitsanzo chache ife tidzakhala okondweretsa kwa Mulungu.
(Malemba ambiri omatilimbikitsa ife kuwaika ena patsogolo pa ife eni akupezeka pa Aroma 12:3; ndi Afilipi 2:3, 4.)