Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 83
  • Kucherezedwa ndi Mfarisi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kucherezedwa ndi Mfarisi
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Asangalatsidwa ndi Mfarisi Wotchuka
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kuitanira Anthu ku Chakudya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Awo Amene Anasankha Malo Abwino Kwambiri
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Fanizo la Phwando la Ukwati
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 83

Mutu 83

Kucherezedwa ndi Mfarisi

YESU akali chikhalirebe m’nyumba ya Mfarisi wotchuka ndipo wangochiritsa kumene mwamuna wodwala mbulu. Pamene akuwona alendo anzake akusankha malo aulemu pachakudya, iye akuphunzitsa phunziro la kudzichepetsa.

“Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu kuchakudya cha ukwati,” pamenepo Yesu akufotokoza motero, “usaseyama pampando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye, ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pampando wa kuthungo.”

Chotero Yesu akupereka uphungu wakuti: “Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pamalo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemelero pamaso pa onse akuseyama pachakudya pamodzi ndi iwe.” Pomaliza, Yesu akuti: “Aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndi wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”

Kenako, Yesu akulankhula kwa Mfarisi amene anamuitana nafotokoza mmene angalinganizire phwando lokhaladi ndi chiyamikiro cha Mulungu. “Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena chamadzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena afuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphaŵi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho.”

Kulinganizira chakudya kotero kwa osauka kudzabweretsa chimwemwe kwa wogaŵirayo chifukwa chakuti, monga momwe Yesu akufotokozera kwa womchereza wakeyo, “pakuti idzabwezedwa mphotho pakuuka kwa olungama.” Mafotokozedwe a Yesu a chakudya choyamikiridwa chimenechi akumbutsa mlendo mnzakeyo mtundu wina wa chakudya. “Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu,” mlendo ameneyu akutero. Komabe, sionse amene amaŵerengera mtengo moyenerera chiyembekezo cha chimwemwe chimenecho, monga momwe Yesu akupitiriza kusonyeza mwa fanizo.

“Munthu wina anakonza phwando lalikulu; naitana ambiri; ndipo anatumiza kapolo wake . . . kukanena kwa oitanidwawo, Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano. Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke kukauwona; ndikupempha undilole ine. Ndipo anati wina, ndagula ng’ombe zamagoli asanu, ndipo ndimka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika. Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.”

Nzodzikhululukira zopanda pake chotani nanga! Mozoloŵereka munda kapena ziŵeto zimapendedwa zisanagulidwe, chotero palibe kufulumira kwenikweni kumene kulipo kukaziwona pambuyo pake. Mofananamo, ukwati wa munthu suyenera kumlepheretsa kuvomereza chiitano chofunika chotero. Chotero pambuyo pa kumva zodzikhululukira zimenezi, mbuyeyo akukwiya ndi kulamulira kapolo wake kuti:

“Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nawo muno aumphaŵi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina. Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamula chachitika, ndipo malo atsalapo. Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumisewu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu aloŵe, kuti nyumba yanga idzale. . . . Kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalaŵa phwando langa.”

Kodi fanizoli likufotokoza mkhalidwe wotani? Eya, “mbuye” wokonza phwandolo amaimira Yehova Mulungu; “kapolo” wopereka chiitano, Yesu Kristu; ndipo “phwando lalikulu,” ndiwo mwaŵi wa kukhala mumzera wa Ufumu wakumwamba.

Awo olandira chiitano choyamba chakudza mumzera wa Ufumu, koposa ena onse anali atsogoleri achipembedzo Achiyuda, a m’tsiku la Yesu. Komabe, iwo anakana chiitanocho. Motero, makamaka kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., chiitano chachiŵiri chinaperekedwa kwa onyozedwa ndi odzichepetsa a mtundu Wachiyuda. Koma siokwanira amene analabadira kudzadza malo 144,000 mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Chotero mu 36 C.E., zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, chiitano chachitatu ndi chomalizira chinaperekedwa kwa osakhala Ayuda osadulidwa, ndipo kusonkhanitsidwa kwa amenewa kwapitirizabe kufikira m’tsiku lathu. Luka 14:1-24.

▪ Kodi ndiphunziro la kudzichepetsa lotani limene Yesu akuphunzitsa?

▪ Kodi ndimotani mmene munthu angalinganizire phwando lokhala ndi dalitso la Mulungu, ndipo kodi nchifukwa ninji lidzambweretsera chimwemwe?

▪ Kodi nchifukwa ninji zodzikhululukira za alendo oitanidwa ziri zopanda pake?

▪ Kodi nchiyani chimene chikuimiriridwa ndi “phwando lalikulu” la fanizo la Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena