Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 35 tsamba 143-146
  • “Chimwemwe Chambiri m’Kupatsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chimwemwe Chambiri m’Kupatsa”
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingakhalire Osangalala
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Muli ndi Mzimu Wopatsa?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 35 tsamba 143-146

Mutu 35

“Chimwemwe Chambiri m’Kupatsa”

INE ndikudziwa chinsinsi china. Kodi inu mungakonde kuchimva icho?—Icho chiri chinsinsi cha chimwemwe.

Pali anthu ochuruka amene sali achimwemwe. Ena amadalira kwambiri pa chimene anthu ena amachita. Ngati munthu wina awapatsa iwo kanthu kena kabwino kwambiri, iwo ali achimwemwe. Ngati palibe munthu wina amene amawachitira iwo kanthu kena kapadera, iwo sali achimwemwe.

Tsopano, nachi chinsinsicho. Mphunzitsi Wamkuruyo anati: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.” Chotero, munthu amene ali wachimwemwe koposa sindiye munthu amene amalandira zinthu, koma munthu amene amapereka kwa anthu ena. Kodi inu munachidziwa chimenecho?— —Machitidwe 20:35, NW.

Tangolingalirani ponena za chimene icho chimatanthauza. Kodi Yesu ananena kuti munthu amene analandira mphatso sakakhala wachimwemwe?—Ai. Inu mumakonda kulandira mphatso, ati?—Ndi inenso, Ife timakhala achimwemwe pamene tilandira zinthu zabwino kwambiri.

Koma Yesu ananena kuti pali chimwemwe chambiridi pamene ife tipatsa. Ndipo Yesu masiku onse anali wolondola, ati?—

Tsopano, kodi nchiani chimene chiripo chimene ife tingathe kupereka kwa anthu ena? Kodi inuyo mukanati nchiani?—

Nthawi zina pamene inu mufuna kupereka mphatso, iyo imadya ndarama. Pafupifupi, ngati iyo iri mphatso imene inu muipeza m’sitoro, inu mudzafunikira kuilipilira iyo. Chotero, ngati inu mufuna kupereka mtundu umenewo wa mphatso, inu mungafunikire kusunga ndarama kufikira mutapeza zokwanira kuigula mphatsoyo.

Koma si mphatso zonse zimene zimachokera m’masitoro. Taimani ndifotokoze. Pa tsiku lotentha palibe kanthu kabwino kofanana ndi tambula ya madzi ozizira. Inu simumatofunikira kupita ku sitoro kaamba ka iwo. Komabe pamene inu muwapereka iwo kwa munthu wina amene ali ndi ludzu, inu mungathe kukhala ndi chimwemwe chimene chimachokera m’kupatsa.

Tsiku lina mwinamwache inu ndi mai wanu mungathe kuphika timakeke. Zimenezo zingathe kukhala zokondweretsa. Ndipo pamene ito choyambilira tituruka mu uvuni, ito timakona bwino kwambiri. Koma kodi nchiani chimene tingachite ndi tina ta timakeke timeneto chimene chikatipanga ife kukhala achimwemwe kwambiridi koposa ndi kumatidya tonseto tokha?—

Inde, chimwemwe chokulirapo chimachokera m’kupatsa. Ife tingathe kukhala ndi nthawi yosangalatsa kumatidya tina tokha. Koma, ngati ife tifuna chimwemwe chambiridi, pamenepo ife tingatikulunge tina ta ito ndi kutipanga ito kukhala mphatso kwa mmodzi wa mabwenzi athu. Kodi inuyo mukakonda kuchita chimenecho nthawi ina?—

Mtumwi Paulo anali mmodzi amene anachidziwa chimwemwe cha kupatsa. Kodi nchiani chimene iye anachipereka kwa anthu ena?—Iye anali ndi chinthu chabwino koposa m’dziko cha kuchipereka. Iye anadziwa choonadi chonena za Mulungu ndi chonena za Yesu. Mokondwa iye anawauza icho ena. Ndipo iye anachichita icho popanda kumamlola munthu ali yense kumpatsa iye ndarama kaamba ka chithandizo chache.

Nthawi ina mtumwi Paulo ndi tsamwali wache Luka anakumana ndi mkazi wina amenenso anafuna kukhala ndi chimwemwe cha kupatsa. Iwo anakumana naye ku mtsinje. Paulo ndi Luka anapita kumeneko chifukwa chakuti iwo anamva kuti iwo anali malo opempherera. Ndipo motsimikizirikadi, iwo anawapeza akazi ena kumeneko.

Paulo anayamba kumawauza akazi amenewa zinthu zabwino zonena za Yehova Mulungu ndi ufumu wache. Mmodzi wa iwo wochedwa Lidiya anamvetsera kwambiri. Iye anazikonda kwambiri zimene iye anazimva. Ndipo iye anafuna kuchita kanthu kena kusonyeza chiyamikiro chache.

Luka amatiuza ife kuti: ‘Iye anatikakamiza ife: “Ngati amuna inu mwandiona ine kukhala wokhulupirika kwa Yehova, lowani m’nyumba mwanga ndi kukhala.” Ndipo iye anangotichititsa ife kudza.’—Machitidwe 16:11-15, NW.

Lidiya anali wokondwa kukhala ndi atumiki a Mulungu amenewa m’nyumba mwache. Iye anawakonda iwo chifukwa chakuti iwo adamthandiza iye kuphunzira ponena za njira ya Mulungu kaamba ka anthu kukhala ndi moyo kosatha. Kunampangitsa iye kukhala wachimwemwe kukhala wokhoza kuwapatsa iwo chakudya kuti adye ndi malo kuti agonepo.

Chotero, Lidiya kupatsa kwache kunampangitsa iye kukhala wachimwemwe chifukwa chakuti iye anafunadi kupatsa. Ndipo chimenecho ndicho kanthu kena kamene ife tiyenera kukakumbukira. Munthu wina angatiuze ife kuti tipereke mphatso. Koma ngati ife kwenikweni sitikufuna kuchichita icho, pamenepo kupatsako sikudzatipangitsa ife kukhala achimwemwe.

Mwachitsanzo, bwanji ngati inuyo munali ndi mtinda wa switi umene inu munafuna kudya? Ngati ine ndinakuuzani kuti inu munayenera kuupereka uwo kwa mwana wina, kodi kukadakupangitsani inu kukhala achimwemwe kuupereka uwo?—Koma inu mungakhale ndi mtinda wa switi pamene mukumana ndi bwenzi lina limene inu mumalikonda kwambiri. Ngati inu munapeza lingaliro lanokha-nokha lakuti kukakhala bwino kwambiri kumbenthulira mtinda wa switiwo bwenzi lanu, pamenepo inu mukakhala achimwemwe kumachichita icho, ati?—

Ndipo, kodi mukudziwa kuti nthawi zina ife timamkonda munthu kwambirimbiri chakuti ife timafuna kumpatsa iye chinthu chiri chonse, ndi kusasiya kanthu kali konse kaamba ka ife ena? Pamene ife tikula m’chikondi, imeneyo ndiyo njira imene ife tiyenera kulingalirira kulinga kwa Mulungu.

Mphunzitsi Wamkuruyo anamdziwa mkazi wina amene analingalira motero. Iye anamuona mkaziyo m’kachisi m’Yerusalemu. Iye anali ndi tindarama tiwiri tokha; timeneto ndito tokha timene iye anali nato. Koma iye anatiika tiwiri tonseto m’bokosi monga chopereka kapena mphatso kaamba ka kachisiyo. Palibe munthu ali yense anamchititsa iye kuchichita icho. Iye anachita icho chifukwa chakuti iye anafuna kutero, chifukwa chakuti iye anamkondadi Mulungu. Kunampangitsa iye kukhala wachimwemwe kukhala wokhoza kupereka.

Chotero, pali njira zambiri m’zimene ife tingathe kuperekera, ati?—Ndipo Mphunzitsi Wamkuruyo amadziwa kuti ngati ife tipereka chifukwa chakuti ife timafuna kutero, ife tidzakhala achimwemwe. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene iye amatiuzira ife kuti: “Yesayesani kupatsa.” Ndiko kuti, kupangeni iko kukhala chizolowezi kuwapatsa anthu ena. Ngati ife tichita chimenecho, ife sitidzakhala okhumudwa chifukwa cha kumyembekezera munthu winanso kutichitira ife kanthu kena kabwino kwambiri. Ife tidzakhala otanganitsidwa kumawapangitsa anthu ena kukhala achimwemwe. Ndipo pamene ife tichichita chimenecho, ife tiri anthu achimwemwe kopambana mwa onse!—Luka 6:38, NW.

(Malingaliro oonjezereka abwino kwambiri onena za mtundu wa kupatsa umene umadzetsa chimwemwe akupezeka pa Mateyu 6:1-4; 2 Akorinto 9:7 ndi Luka 14:12-14.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena