Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 37 tsamba 151-154
  • Mtumwi Amene Anafikira Kukhala Mbala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtumwi Amene Anafikira Kukhala Mbala
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Usakhale Wakuba!
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Umene Ena Amati Uthenga Wabwino wa Yudasi N’chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 37 tsamba 151-154

Mutu 37

Mtumwi Amene Anafikira Kukhala Mbala

KODI munthu wina ali yense anayamba wakuberani kanthu kena?—

Kodi inu munamva bwanji ponena za icho?—Amene anachibayo anali mbala, ndipo palibe munthu ali yense amene amaikonda mbala.

Kodi inu munadziwa kuti mmodzi wa atumwi a Yesu anafikira kukhala mbala?—Dzina lache linali Yudase Isikariote.

Yudase anazidziwa zinthu zimene zinali zoyenera kuzichita. Ngakhale pamene iye anali mnyamata wamng’ono iye analimva lamulo la Mulungu. Iye anadziwa kuti nthawi ina Mulungu analankhuladi kuchokera kumwamba ndi mau akuru ndi kuwauza anthu ache kuti: “Usabe.” Yudase anadziwa kuti lamulo la Mulungu linali loyenera.—Eksodo 20:15.

Pamene iye anakula anakumana ndi Mphunzitsi Wamkuruyo. Yudase anazikonda zinthu zimene Yesu anazinena. Yudase anafikira zinthu zimene Yesu anazinena. Yudase anafikira kukhala wophunzira wa Yesu. Pambuyo pache, Yesu anamsankhadi Yudase kukhala mmodzi wa atumwi ache khumi ndi awiri.

Yesu ndi atumwi ache anaononga nthawi yochuruka limodzi. Iwo anayendera limodzi. Iwo anadyera limodzi. Ndipo ndarama za kaguluko zinasungidwa pamodzi m’bokosi. Yesu analipereka bokosi limenelo kwa Yudase kuti alisamalire.

Ndithudi, ndaramazo sizinali za Yudase. Yesu anali uyo amene akadamuuza iye kuzigwiritsira nchito kwache. Koma kodi mukuchidziwa chimene Yudase anachichita patapita kanthawi? Iye anayamba kuzitenga ndarama m’bokosimo pamene iye sanayembekezeredwe kutero. Iye ankazitenga izo pamene ena sanali kuona. Iye anafikira mbala. Tsopano iye anayamba kumaganiza za ndarama nthawi zonse. Iye anayesayesa kuzipeza njira zopezera zochuruka za izo.

Tsiku lina mkazi wina anatenga mafuta abwino kwambiri ndi kuwadzoza iwo mapazi a Yesu kumpangitsa iye kumva bwino. Koma Yudase anadandaula. Iye ananena kuti mafutawo anayenera kukhala atagulitsidwa kotero kuti iwo akadakhala ndi ndarama zochuruka za kuwapatsa anthu osauka. Kwenikweni iye anafuna kupeza ndarama zochuruka m’bokosimo kotero kuti iye akadatha kuziba. Kodi inu mumaganiza chiani ponena za munthu wonga ameneyo?—Yohane 12:1-6.

Yesu sanamuuze Yudase nthawi yomweyo kuti iye anali mbala. Koma iye anamuuza iye kuti asambvutitse mkazi amene anali wokoma mtima kwambiriyo. Yudase sanazikonde zimenezo. Kodi nchiani chimene iye akachichita?

Iye akadakhala atamva chisoni. Iye akadayenera kukhala atamuuza Yesu kuti iye anali kumaba, ndipo iye akadayenera kukhala atazibwezera ndaramazo. Koma m’malo mwache, iye anachita kanthu kena koopsya.

Iye anapita kwa akulu ansembe, amene anali adani a Yesu. Iwo anafuna kumgwira Yesu. Koma iwo anafuna kuchichita icho usiku chotero anthu sakadawaona iwo. Yudase anawauza iwo kuti: ‘Ndidzakuuzani mmene mungampezere Yesu ngati mundipatsa ndarama. Kodi mudzandipatsa zingati?’ Ansembewo anati: ‘Tidzakupatsa ndarama za siliva makumi atatu!’ Zimenezo zinali ndarama zambiri.—Mateyu 26:14-16.

Yudase woipayo anazitenga ndaramazo. Kunali ngati kuti iye anali kumamgulitsa Mphunzitsi Wamkuruyo kwa anthu amenewo. Kodi mungamganizire munthu ali yense akumachichita chinthu choopsya choterocho?—Eya, chimenecho ndicho mtundu wa chinthu chimene chimachitika pamene munthu amafikira kukhala mbala. Iye amazikonda ndarama kwambiri koposa ndi mmene iye amamkondera Mulungu.

Tsopano, tiyeni titsimikizire kuti tikuimvetsetsa nkhani imeneyi bwino lomwe. Kuti tizindikire chimene mbala iri, tifunikira kudziwa chimene chimatanthauza kukhala ndi kanthu kena. Anthu amakhala ndi zinthu chifukwa chakuti iwo anazigwilira izo nchito. Kapena iwo anazigula izo ndi ndarama. Kapena mwinamwache izo zinaperekedwa kwa iwo monga mphatso.

Pamene atate wanu amagwira nchito iwo amalipidwa ndarama kaamba ka iyo. Kodi ndaramazo zimakhala zao?—Inde, chifukwa chakuti iwo anazigwilira izo nchito. Izo siziri zanu; izo ziri zao.

Iwo amagula zinthu zimene ziri m’nyumba mwanu ndi ndarama zimenezo. Izo zimakhala zao. Chifukwa chakuti izo zimakhala zao, iwo ali ndi kuyenera kwa kunena amene angazigwiritsire izo nchito. Iwo amakuuzani inu ngati inu mungathe kusewera nazo kapena ai. Ndipo iwo mwinamwache amawalola mai wanu kukuuzani chimenechinso.

Nthawi zina inu mumapita kukasewera ndi ana ena m’nyumba zao, eti?—Zinthu zimene ziri m’nyumba mwao ndizo za atate wao. Kodi kukakhala koyenera kutenga kanthu kena kuchokera m’nyumba yao ndi kunka nako ku nyumba kwanu?—Ai kusiyapo ngati atate wao kapena mai akuuzani inu kuti mungatenge. Ngati mutenga kanthu kena kunka nako kwanu popanda kumawapempha iwo, kumeneko kukakhala kuba.

Kodi nchifukwa ninji munthu amaba?—Eya, iye angaone kanthu kena kamene kali ka munthu wina. Mwinamwache icho ndicho njinga. Pamene iye amaiyang’ana njinga imeneyo ndi kumanganizira za iyo, ndi pamenenso iye amaikonda iyo. Ngati iye sali munthu wachikondi, iye samasamala mmene munthu winayo akulingalilira. Chotero iye angammenye munthu winayo ndi kuyesayesa kumlanda iye njingayo. Kapena iye angayembekezere kufikira pamene munthu winayo sali kuona. Ndiyeno iye amaithawitsa njingayo. Kodi nchiani chimene iye kwenikweni ali kumachichita?—Iye ali kuba.

Mwinamwache munthu winayo sakumuona iye akuba njingayo. Koma munthu wina amamuona iye akuba. Kodi mukumdziwa ameneyo?—Yehova Mulungu amamuona iye akuba. Mulungu amaona kuti iye ali mbala.

Sikumapanga kusiyana kuli konse ngati munthu winayo ali ndi zinthu zambiri kapena zapang’ono chabe. Anthu ena amapita ku sitoro ndi kuona zinthu zosawerengeka kumeneko. Iwo amaona kanthu kena kamene iwo amakafuna kwambiri. Iwo amadziuza okha kuti palibe munthu ali yense amene adzachiphonya chimodzi chokha. Chotero iwo amachitenga icho, koma iwo samachilipilira. Kodi kumeneko kuli koyenera?—Ai, ndiko kuba.

Pamene anthu amachita chimenecho, iwo ali kumafanana ndi Yudase. Chifukwa chakuti Yudase anali mbala! Tiyeni titsimikizire kuti tisafane naye konse.

(Kuli kolakwa kuba. Baibulo limachimveketsa bwino lomwe chimenechi pa Marko 10:17-19; Aroma 13:9; Aefeso 4:28.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena