Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 41 tsamba 167-170
  • Chakudya cha Kutithandiza Kukumbukira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chakudya cha Kutithandiza Kukumbukira
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kukumbukira Yehova ndi Mwana Wake
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • M’chipinda Chapamwamba
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 41 tsamba 167-170

Mutu 41

Chakudya cha Kutithandiza Kukumbukira

TAYEREKEZERANI kuti munthu wina anakupatsani mphatso yodabwitsa. Kodi inuyo mukamva bwanji ponena za iyo?—Kodi inuyo mukanangonena kokha kuti, “Zikomo,” ndipo kenako kuiwaliratu zonse ponena za uyo amene anaipereka iyo kwa inu? Kapena kodi inu mukafuna kukumbukira chimene iye anachichita?—

Yehova wapereka mphatso yodabwitsa kwambiri kwa ife. Iye anamtumiza Mwana wache wa iye mwini ku dziko lapansi kudzatifera ife. Chifukwa cha chimenechi ife tingathe kumasuka kuchokera ku matenda ndi imfa. Ha, ndi chinthu chachikondi chotani nanga kaamba ka iwo kuchichita! Ndithudi ife sitikufuna kuiwala chimene Mulungu ndi Mwana wache atichitira ife, ati?—

Kodi inu mukudziwa kuti Mwana wa Mulungu anatipatsa ife njira yapadera ya kukumbukilira chimene iye anachichita?—Kodi inu mungafune kumva za iyo?—

Tangodziyerekezerani ngati kuti muli m’chipinda cha m’mwamba cha nyumba ina m’Yerusalemu. Iyo ndi nthawi ya usiku. Tiyeni tione amene ali m’chipindacho. Mphunzitsi Wamkuruyo ali momwemo. Ndi atumwi ache omwe. Iwo ali kumaseyama pa mipando mozungulira thebulo. Pa thebulopo pali nkhosa yoochedwa, mitanda yaphanthipanthi ya mikate ndi vinyo wofiira. Koma ichi sichiri chakudya cha masiku onse. Iwo ali kumakhala ndi chakudya chapadera Kodi inu mukudziwa chifukwa chache?—

Chakudya ichi chiyenera kuwakumbutsa iwo za kanthu kena kofunika kwambiri kamene kanachitika zaka mazana ambirimbiri apitawo. Panali pa usikuwo pamene Yehova anawamasula anthu ache Aisrayeli mu ukapolo mu Igupto.

Yehova anawauza anthu ache kuti: ‘Iphani mwanawankhosa kaamba ka banja liri lonse ndi kuthira mwazi wache pa mphuthu za nyumba zanu.’ Ndiyeno iye anati: ‘Lowani m’kati mwa nyumba zanu nimudye mwanawankhosayo.’

Iwo anachita chimenecho. Ndipo usiku umodzimodzi umenewo mngelo wa Mulungu anadutsa m’dziko la Igupto. M’nyumba zochuruka mngeloyo anapha mwana wachisamba. Koma pamene mngeloyo anaona mwazi pa mphuthuzo, iye anailumpha nyumba imeneyo. M’nyumba zimenezo palibe ana amene anafa. Ngati inuyo mukadakhala kumeneko, kodi ndi m’ziti za nyumbazo inuyo mukadafuna kukhalamo?—

Mfumu ya Igupto inaopsyedwa ndi chimene mngelo wa Yehova anachichita. Iye anawauza Aisrayeli kuti: ‘Inu mwamasuka. Turukani m’Igupto!’ Chotero iwo ananyamulitsa katundu ngamila ndi aburu ao nachoka.

Koma Yehova sanafune anthu ache kuiwala mmene iye anawamasulira iwo. Chotero iye anati: ‘Kamodzi pa chaka inu muyenera kudya chakudya chonga chakudya chimene inu mwadya usiku uno. Ndipo inu muyenera kuwauza ana anu ponena za chimene chinachitika usiku uno mu Igupto.’

Iwo anachicha chakudya chapadera chimenechi Paskha. Kodi inu mukuchidziwa chifukwa chache?—Chifukwa chakuti usiku umenewo mngelo wa Mulungu ‘anazilumpha’ nyumba zao zopakidwa mwazizo. Mukukumbukira?

Yesu ndi atumwi ache ali kumaganizira ponena za chimenechi pamene iwo akudya chakudya cha Paskhacho. Pambuyo pa chimenecho Yesu akuchita kanthu kena kofunika kwambiri. Yang’anitsitsani.

Iye akutenga umodzi wa mitanda yotsalayo ya mkate. Atatha kuupemphelera uwo, iye akuunyema uwo. Iye akuupereka uwo kwa ophunzira ache ndipo akuti: “Tengani, idyani.” Ndiyeno iye akuwauza iwo kuti: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene ndidzalipereka pamene ine ndikuferani inu.’

Kenako Yesu akutenga chikho cha vinyo wofiira. Pambuyo pa pemphero lina la zithokozo, iye akuchipatsira icho mozungulira. Iye akuti: “Mwerani m’menemo, nonsenu.” Ndipo iye akuwauza iwo kuti: ‘Vinyo uyu akuimira mwazi wanga. Posachedwapa ndidzautsanula mwazi wanga kukumasulani inu ku machimo anu. Pitirizanibe kumachita ichi kundikumbukira ine.’—Mateyu 26:26-28, NW; 1 Akorinto 11:23-26.

Kodi mwaona kuti Yesu ananena kuti iwo ayenera kupitirizabe kumachichita chimenechi kumkumbukira iye?—Iwo sakanadzakhalanso ndi chakudya cha Paskha. M’malo mwache, kamodzi pa chaka iwo akanadzakhala ndi chakudya chapadera chimenechi kuikumbukira imfa ya Yesu. Chimenechi chikuchedwa mgonero wa Ambuye. Lero lino ife timauchanso uwo Chikumbutso. Chifukwa ninji?—Chifukwa chakuti uwo umatikumbutsa ife chimene Yesu ndi Atate wache atichitira ife.

Kodi inu mudzatsagana nane ku Chikumbutso nthawi ina pamene icho chichitidwa?—Ngati inu mutero, inu mudzaona mkate waphanthiphanthi ndi vinyo wofiira zikumayendetsedwa. Kodi mkatewo ndi vinyoyo zidzakupangitsani inu kuganizira chiani?—

Mkatewo uyenera kutipangitsa ife kuganiza za thupi la Yesu. Iye anali wofunitsitsa kulipereka thupi limenelo kotero kuti ife tikakhale ndi moyo wosatha. Nanga bwanji ponena za vinyo wofiirayo?—Ameneyo ayenera kutikumbutsa ife za mwazi wa Yesu umene unatsanulidwa pamene anthu anamkhomera iye ku mtengo kuti afe.

Mwazi wa Yesu uli wamtengo wapatali kwambiri koposa mwazi wa mwanawankhosa wa paskhayo mu Igupto. Kodi mukudziwa chifukwa chache?—Mwazi wa Yesu ungatidzetsere ife chikhululukiro cha machimo.

Kodi mukudziwa chimene chidzatanthauza kuchotseredwa machimo athu onse?—Pamenepo ife sitidzachitanso konse kanthu kali konse kolakwa. Ndipo ife sitidzadwala konse, kukalamba ndi kufa! Ife tiyenera kuganizira zimenezo pamene ife tipita ku Chikumbutso.

Kodi munthu ali yense ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso?—Ai, Yesu anawauza awo amene anatero kuti: ‘Inu mudzakhala ndi mbali mu ufumu wanga ndi kukhala pansi pa mipando yachifumu kumwamba limodzi ndi ine.’ Chimenecho chinatanthauza kuti iwo akapita kumwamba kukhala mafumu limodzi ndi Yesu. Awo okha amene akupita kukachita chimenecho ayenera kudya mkate ndi vinyo.

Koma ngakhale ngati ife sitidya mkatewo kapena kumwa vinyoyo, ife tiyenera kufika pa Chikumbutso. Kodi inu mukuchidziwa chifukwa chache?—Chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wache kaamba ka ifenso. Pamene ife tipita ku Chikumbutso ife timasonyeza kuti ife sitinaiwale. Ife timaikumbukira mphatso yodabwitsa ya Mulungu kupyolera mwa Yesu.

(Malemba ena owawerenga kusonyeza kufunika kwa kumafika pa Chikumbutso ndiwo Luka 22:19, 20, 28-30; 1 Akorinto 11:27.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena