Mutu 15
Boma Limene Lidzagonjetsa Mdani wa Munthu Imfa
CHIFUNO choyambirira cha Mulungu kaamba ka munthu chinali chakuti iye angakhale ndi moyo ndi kusangalala ndi moyo pa dziko lapansi laparadaiso. Tingathe kukhala ndi chidaliro chakuti chifuno chimene’chi chidzakwaniritsidwa. Chikuchirikizidwa ndi lonjezo lodalirika la Mulungu lakuti mdani wa munthu imfa adzagonjetsedwa, kuchotsedwa.—1 Akorinto 15:26.
Utali wa moyo wa pafupi-pafupi zaka makumi asanu ndi awiri kapena makumi asanu ndi atatu zokha sindiwo wokha umene ulipo. Ngati umene’wo unali utali wokwanira wa chimene ngakhale okonda Mulungu akanayembekezera, mkhalidwe wao ukanasiyana pang’ono ndi uja wa awo amene samalemekeza Mulungu kapena Mau ake. Koma siziri choncho. Baibulo limati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondi’cho mudachionetsera ku dzina lake.”—Ahebri 6:10; 11:6.
Kodi n’chiani chimene chiri mphotho ya awo amene akutumikira Yehova Mulungu chifukwa cha kum’konda kwao kwambiri ndi njira zake zolungama? Pali mphotho ya tsopano lino ndi ya m’tsogolo momwe. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chipembedzo chipindula zones, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Ngakhale tsopano kumvera lamulo la Mulungu kumatsogolera ku kusangalala ndi moyo wokhutira ndi wachimwemwe. Ponena za moyo “ulinkudza,” Aroma 6:23 amati: “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha.”
Ndithudi, pansi pa mikhalidwe iripo’yi, moyo wosatha ungaonekere kukhala wosafunika. Koma ndiwo moyo wamuyaya pansi pa boma lolungama umene Mulungu walonjeza. Kuti lonjezo limene’lo likwaniritsidwe, anthu choyamba ayenera kumasulidwa ku chochititsa imfa. Kodi chochititsa chimene’cho n’chiani? Mtumwi wouziridwa Paulo akuyankha kuti: “Mbola ya imfa ndiyo uchimo.”—1 Akorinto 15:56.
Kale pa nthawi ya kuperekedwa kwa chiweruzo pa anthu awiri opanduka’wo, Adamu ndi Hava, ndi pa woyambitsa chipanduko, Yehova Mulungu anasonya ku njira ya imene anthu akamasulidwira ku uchimo ndi imfa. Osati kwa njoka yopanda nzeru yogwiritsiriridwa ntchito m’chinyengo’yo, koma kwa Satana iye mwini monga “njoka yakalamba’yo” Mau a Mulungu analunjikitsidwako, kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkazi’yo, ndi pakati pa mbeu yako ndi yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” Chiweruzo chimene’chi, cholembedwa pa Genesis 3:15, chinapereka maziko a chiyembekezo kwa ana am’tsogolo a Adamu ndi Hava. Chinasonyeza kuti mdani wa munthu akagonjetsedwa.—Chibvumbulutso 12:9.
Ndithudi, kuphedwa chabe kwa “njoka yokalamba’yo,” Satana Mdierekezi, sikukakhala kokwanira kuchotsa chibvulazo chonse chimene iye anachititsa mwa kusonkhezera anthu oyambirira’wo kupandukira Mulungu. Koma m’mene kuthetsedwa’ko kukachitikira kunakhalabe chinsinsi kufikira pa nthawi imene Mulungu anasankha kuchibvumbula.—1 Yohane 3:8.
Mothandizidwa ndi Baibulo lathunthu, ife lero lino tingathe kumasula chinsinsi chopatulika chimene’chi. “Mkazi” wochulidwa pa Genesis 3:15 sakanakhala Hava. Hava, mwa njira yake ya chipanduko, anaimira kumodzi ndi “njoka yokalamba’yo,” motero akumadzipangitsa kukhala mbali ya “mbeu” yake. Ndiyeno’nso, palibe mbadwa iri yonse yachikazi ya Adamu ndi Hava ikanakhala mkazi amene’yo. Kulekeranji kutero? Chifukwa chakuti ‘mbeu ya mkazi’ inayenera kukhala ndi mphamvu yaikulu kwambiri koposa ija ya munthu wamba m’malo mwakuti iphwanye “njoka yokalamba’yo,” munthu wauzimu wosaoneka’yo Satana Mdierekezi. Kuti atulutse “mbeu” yamphamvu yotero’yo, “mkazi’yo” akayenera kukhala, osati waumunthu, koma wauzimu.
Pa Agalatiya 4:26 “mkazi” amene’yu akudziwikitsidwa kukhala “Yerusalemu wa kumwamba.” Amene’yu ali wapadera kwambiri. Kodi ziri choncho motani?
Mzinda wakale wa Yerusalemu unali malikulu a ufumu wa Yuda. Chifukwa chakuti mfumu yoyamba Yachiyuda, Davide, inakhazikitsa mpando wake wachifumu kumene’ko, Yerusalemu kuyambira m’nthawi yake kumkabe m’tsogolo anatulutsa mafumu a mtundu’wo. Chifukwa cha chimene’cho kukakhala kokha kwachibadwa kuyembekezera kuti “Yerusalemu wa kumwamba” akatulutsa mfumu. Chinthu chimene’chi chinasonya ku boma lakumwamba, lokhala ndi mfumu yakumwamba, monga chiwiya chothetsera uchimo ndi imfa.
“Yerusalemu wa kumwamba” sindiye mkazi kapena mzinda weni-weni. Ali mzinda wophiphiritsira ndi wauzimu. Pokhala wakumwamba, wapangika ndi anthu auzimu amphamvu, angelo. Chotero, pamenepa, kuti mmodzi wochokera pakati pa anthu auzimu amene’wa achedwe mfumu kukatanthauza kuti “Yerusalemu wa kumwamba” watulutsa wolowa nyumba ku ufumu. Kodi chinthu chotero’cho chinachitika?
MFUMU ITULUTSIDWA
Chimene’cho ndicho cheni-cheni chimene’di chinachitika m’chaka cha 29 C.E. Pa nthawi imene’yo munthu’yo Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kukhala Woyembekezera kukhala Mfumu. Chimene’chi chinachitika pa nthawi imene anadzionetsera kwa Yohane M’batizi m’madzi. Ponena za chimene chinachitika, Baibulo limasimba kuti: “Pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inam’tsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau ochokera ku miyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 3:16, 17.
Miyezi ingapo pambuyo pake Yesu anayamba kulengeza kuti: “Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Inde, ufumu unali utayandikira m’kukhalapo kwa Woyembekezera kukhala Mfumu’yo.
Ngakhale kuli kwakuti anabadwa monga munthu pa dziko lapansi, Yesu analiko asanakhale munthu. Iye mwini anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsika’yo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) Posonyeza chitsanzo chapadera cha kudzichepetsa kwa Yesu, Mtumwi wouziridwa Paulo analemba kuti: “Anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.” (Afilipi 2:5-7) Ponena za m’mene kusamuka kumene’ku kuchokera ku moyo wakumwamba kumka ku moyo wa pa dziko lapansi kunachitikira, tiri ndi kukambitsirana kolembedwa kwa mngelo Gabrieli ndi namwali Mariya:
“Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Mariya; pakuti wapeza chisomo kwa Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nadzachedwa dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzachedwa Mwana wa Wamkulu-kulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.
“Koma Mariya anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna? Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulu-kulu idzakuphimba iwe: chifukwa chake’nso Choyera’cho chikadzabadwa, chidzachedwa Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:30-35.
Motero, monga mmodzi wa ana a Mulungu opanga “Yerusalemu wa kumwamba,” moyo wa Yesu unachititsidwa kusamutsidwa kuchokera kumwamba kumka m’mimba ya namwali Mariya ndipo anabadwa ali khanda langwiro laumunthu. Chozizwitsa chotero’cho chingamveke kukhala chosakhulupiririka kwa ena, komabe chimene’cho sichimapereka chikaikiro cheni-cheni pa kutsimikizirika kwa chochitika’cho. Ndithudi Uyo amene anapangitsa kukhala kothekera kwa munthu wathunthu kukula kuchokera ku selo la dzira limene liri laling’ono kwambiri koposa piriyodi pamapeto a chiganizo chino. Akatha, mwa njira ya mzimu wake kapena mphamvu yogwira ntchito, kusamutsa moyo kuchokera kumwamba kubwera pa dziko lapansi. Ndipo popeza kuti moyo wa Yesu unasamutsidwa m’njira imene’yi m’malo mwakuti iye akhale wolowa nyumba wachikhalire wa Mfumu Davide, iye kweni-kweni anachokera ku “Yerusalemu wa kumwamba.”
Monga momwe kunanedweratu mu ulosi wa Mulungu wa Genesis 3:15, Yesu anadzakhala ndi ‘bala la ku chitende’ lochokera kwa “njoka yokalamba’yo” pamene iye anakhomeredwa ku mtengo wopherapo pa Nisan 14 wa chaka cha 33 C.E. Mosafanana ndi kuphwanyidwa mutu kumene palibe kuchira, ‘bala la ku chitende’ limene’lo linali lakanthawi chabe. Pa tsiku lachitatu Mulungu anaukitsa Yesu kwa akufa, akumam’patsa “mphamvu ya moyo wosaonongeka.” (Machitidwe 10:40; Ahebri 7:16) Monga munthu wauzimu wosakhoza kufa, Mfumu Yesu Kristu ali wokhoza kuphwanya “njoka yakalamba’yo” mutu ndi kuchotsa kuononga konse kumene amene’yo wakuchititsa.
OLAMULIRA ANZAKE
Yesu Kristu ndiye wamkulu wa “mbeu” ya chiungwe imene’yo. Mwa njira ya iye Mulungu Wamphamvuyonse adzaphwanya Satana Mdierekezi pansi pa mapazi a anzake a Yesu mu ufumu wakumwamba. (Chibvumbulutso 20:1-3) Polembera kalata awo okhala mu mzera wa ulamuliro mtumwi Wachikristu Paulo analongosola kuti: “Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.” (Aroma 16:20) Kodi ulamulira anzake amene’wa ndani?
M’bukhu lotsirizira la Baibulo, Chibvumbulutso, chiwerengero chikuperekedwa kukhala 144,000. Polongosola zimene iye anaona m’masomphenya, wolemba Chibvumbulutso’yo mtumwi Yohane, akuti: “Taonani, Mwanawankhosa’yo [Yesu Kristu, amene anafa imfa yonga mwanawankhosa wa nsembe] alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndi pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao. . . . Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kuli konse amukako. Iwowa anangulidwa mwa anthu [osati mtundu umodzi wa anthu monga ngati Aisrayeli], zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chibvumbulutso 14:1-4.
Kuli’di koyenera kuti a 144,000 akusonyezedwa kukhala ali limodzi ndi Mwanawankhosa pa Phiri la Ziyoni. Phiri la Ziyoni la mzinda wakale wa Yerusalemu linali malo kumene mafumu a Yuda analamulirira, malo a mphala yachifumu. Panali’nso pa Phiri la Ziyoni pamene Davide anamangapo chihema cha likasa (bokosi) lopatulika la chipangano m’mene munaikidwa magome awiri a miyala olembedwa Malamulo Khumi. Pambuyo pake likasa’lo linasamutsidwira ku chipinda cha m’kati-kati cha kachisi womangidwa ndi mwana wa Davide Solomo pa malo otalikirapo pang’ono pa Phiri la Moriya. Liu’lo Ziyoni, m’kupita kwa nthawi, linafikira pa kuphatikizamo Moriya. Motero Ziyoni anali ndi chigwirizano chachikulu ndi ufumu kudza’nso unsembe.—2 Samueli 6:12, 17; 1 Mafumu 8:1; Yesaya 8:18.
Chimene’chi chimagwirizana ndi cheni-cheni chakuti Yesu ali ponse pawiri Mfumu ndi Wansembe, akumaphatikiza malo antchito onse’wo monga momwe anachitira Melikiezedeke wa Salemu wakale. Chifukwa cha chimene’cho Ahebri 6:20 amanena za Yesu kukhala “atakhala mkulu wa nsembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.” M’malo antchito a Mfumu ndi Wansembe, Yesu amalamulira ali pa Phiri la Ziyoni wakumwamba.
Olamulira anzake’wo nawo’nso ali ansembe. Monga bungwe iwo akuchedwa “ansembe achifumu.” (1 Petro 2:9) Ponena za ntchito yao, Chibvumbulutso 5:10, NW chimatiuza kuti: “Inu [Kristu] mudawapanga kukhala ufumu wa ansembe kwa Mulungu wathu, ndipo iwo ayenera kulamulira monga mafumu pa dziko lapansi.”
CHIFUNO CHA BOMA’LO
Nkhawa yaikulu ya Mfumu ndi Wansembe Yesu Kristu ndi olamulira anzake aunsembe’wo ndiyo kugwirizanitsa mtundu wonse wa anthu ndi Yehova Mulungu. Kunene’ku kumatanthauza kuchotsedwa kwa zizindikiro zonse za uchimo ndi kupanda ungwiro, pakuti awo okha amene akusonyeza mokwanira chifanizo cha Mulungu angathe kuima mwa kuyenera kwa iwo eni pamaso pake. Chakuti Ufumu wolamulira’wo uli mbali ya kuyendetsedwa kwa zinthu kwa Mulungu kochititsa zimene’zi chikusonyezedwa pa Aefeso 1:9-12:
“[Mulungu] anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunam’komera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengo’zo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko. Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake; kuti ife amene tinakhulupirira Kristu kale tikayamikiritse ulemerero wake.”
Popeza kuti Yesu Kristu ali wopanda chimo ndipo ali wogwirizana kotheratu ndi Yehova Mulungu, kugwirizanitsidwa kwa zinthu zonse ndi iye kunachititsa kugwirizanitsidwa kwa mtundu wa anthu ndi Yehova Mulungu. Zimene’zi ziri zoonekera bwino kuchokera m’cheni-cheni chakuti mbali imene’yi ya ntchitoya Ufumu itatsirizidwa, Baibulo limanena kuti Yesu Kristu ‘akupereka ufumu kwa Mulungu ndi Atate wake.’—1 Akorinto 15:24.
Kuti achite ntchito yaikulu kwambiri’yo ya kupangitsa mtundu wa anthu kukhala wagwiro, olamulira akumwamba’wo adzakhala’nso akugwiritsira ntchito oimira a pa dziko lapansi, amuna okhala ndi kudzipereka kwapadera ku chilungamo. (Salmo 45:16; Yesaya 32:1, 2) Amuna amene’wa adzafunikira kukwaniritsa ziyeneretso zimene Mfumu Yesu Kristu akufuna-funa mwa awo amene iye akuwaikizira thayo. Ziyeneretso ziwiri zazikulu ndizo kudzichepetsa ndi chikondi chodzipereka nsembe. Yesu anati: “Mudziwa kuti mafumu a athu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma amene ali yense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene ali yense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:25-27) Iye anati’nso: “Lamulo langa ndi iri, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.”—Yohane 15:12, 13.
Kodi simukaona kukhala wosungika pansi pa oimira a Ufumu amene amasonyeza chikondi ndi kudzichepetsa kotero’ko, amene akakusamalirani kweni-kweni?
Sipadzakhala zobvuta m’kulankhulana pakati pa boma lakumwamba’lo ndi oimira a pa dziko lapansi a Mfumu Yesu Kristu. M’nthawi zakale Yehova Mulungu anapereka mauthenga kwa atumiki ake pa dziko lapansi mwa njira ya angelo ndi mphamvu yake yogwira ntchito yosaoneka. (Danieli 10:12-14; 2 Petro 1:21) Eya, ngakhale anthu akhala okhoza kutumiza ndi kulandira mauthenga omka ndi ochokera kuzida zolandirira ndi kutumiza mauthenga ndi masiteshoni m’mlengalenga mozungulira kutali kwambiri pamwamba pa dziko lapansi. Ngati anthu opanda ungwiro angachite zinthu zotero’zo, kodi n’chifukwa ninji ali yense ayenera kuganiza kuti zimene’zi zikakhala zobvuta kwambiri kwa olamulira a kumwamba angwiro’wo?
Komabe, boma Laufumu la Yesu Kristu ndi olamulira anzake lisanachite ntchito yogwirizanitsa mtundu wa anthu ndi Mulungu, makamu onse otsutsa ayenera kuchotsedwa. Palibe chisonyezero n’chapang’ono chomwe chakuti awo olamulira mtundu wa anthu lero lino ali ofunitsitsa kupereka ulamuliro wao kwa Yesu Kristu ndi olamulira anzake. Iwo amaseka lingaliro lakuti’lo boma lakumwamba lidzatenga ulamuliro wotheratu wa zochitika za dziko lapansi. Ndicho chifukwa chake iwo adzafunikira kukakamizidwa kuzindikira ulamuliro wa ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mw Kristu wake. Zimene’zi zidzachititsa kutaya kwao malo antchito a ulamuliro kudza’nso miyoyo yao. Monga momwe Baibulo limatiuzira kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Litatha kuchotsa chitsutso chonse, boma Laufumu’lo lidzayamba ntchito ya kumasula mtundu wa anthu ku matenda ndi imfa. Kodi imene’yi idzachitidwa motani?