Njira Yokha ya Moyo Wosatha
“Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo.”—YOHANE 14:6.
1, 2. Kodi Yesu anayerekezera njira ya kumoyo wosatha ndi chiyani, ndipo kodi fanizo lake likutanthauza chiyani?
MU ULALIKI wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anayerekezera njira ya moyo wosatha ndi msewu umene munthu amaloŵamo kudzera pachipata. Onani kuti Yesu anagogomezera kuti njira imeneyi ya kumoyo n’njovuta. Anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo [wosatha], ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”—Mateyu 7:13, 14.
2 Kodi mukumvetsa tanthauzo la fanizo limeneli? Kodi silikusonyeza kuti pali msewu, kapena njira, imodzi yokha yomuka nayo kumoyo ndi kuti tikufunika kusamala kwambiri kuti tisaphunthwe kuchoka panjira ya kumoyo imeneyo? Nangano kodi njira yokha ya kumoyo wosatha imeneyi ndiyo iti?
Mbali ya Yesu Kristu
3, 4. (a) Kodi Baibulo limasonyeza motani mbali yofunika imene Yesu amachita pa chipulumutso chathu? (b) Kodi ndi liti pamene Mulungu kwa nthaŵi yoyamba ananena kuti anthu angakhale ndi moyo kosatha?
3 Mwachionekere, Yesu ali ndi mbali yofunika kwambiri panjira imeneyo, monga momwe mtumwi wake Petro ananena kuti: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina [kusiyapo la Yesu] pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Mofananamo, mtumwi Paulo anati: “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Yesu mwiniyo anavumbula kuti njira yokha ya kumoyo wosatha ndi yodzera mwa iyeyo, pakuti anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo.”—Yohane 14:6.
4 Chotero ndi kofunika kwambiri kuti tivomereze mbali ya Yesu pa kutheketsa moyo wosatha. Motero tiyeni tipende mbali yake mosamalitsa. Kodi mukudziŵa kuti ndi liti, pambuyo pa kuchimwa kwa Adamu, pamene Yehova Mulungu anasonyeza kuti anthu angakhale ndi moyo kosatha? Anatero Adamu atangochimwa. Tsopano tiyeni tifufuze mmene kwa nthaŵi yoyamba kunaloseredwera kuti Yesu Kristu adzaperekedwa monga Woombola mtundu wa anthu.
Mbewu Yolonjezedwa
5. Kodi njoka imene inanyenga Hava tingaizindikire bwanji?
5 Mwa kugwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa, Yehova Mulungu anatchula Mpulumutsi wolonjezedwa ameneyu. Anachita zimenezi pamene anali kupereka chiweruzo kwa “njoka” imene inalankhula ndi Hava ndi kumunyenga kuti asamvere Mulungu mwa kudya chipatso choletsedwa. (Genesis 3:1-5) Zoonadi, njoka yotchulidwayo sinali njoka yeniyeni. Inali cholengedwa champhamvu chauzimu chimene m’Baibulo chikudziŵikitsidwa kuti ndi “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” (Chivumbulutso 12:9) Satana anagwiritsa ntchito nyama yachabechabe imeneyi monga cholankhuliramo chake ponyenga Hava. Motero, poweruza Satana, Mulungu anati kwa iye: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo [mbewu ya mkazi] idzalalira [“idzazunzunda,” NW] mutu wako, ndipo iwe udzalalira [“udzazunzunda,” NW] chitende chake.”—Genesis 3:15.
6, 7. (a) Kodi mkazi amene akubala “mbewu” ndani? (b) Kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwa, ndipo kodi akukwaniritsanji?
6 Kodi “mkazi” ameneyu, amene ali mdani wa Satana, ndani? Monga momwe “njoka yokalambayo” ikudziŵikitsidwira m’Chivumbulutso chaputala 12, momwemonso mkaziyu amene Satana amamuda. Onani kuti m’vesi 1 akuti ali “wovekedwa dzuŵa, ndi mwezi ku mapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziŵiri.” Mkazi ameneyu akuimira gulu la Mulungu lakumwamba la angelo okhulupirika, ndipo “mwana wamwamuna” amene anabala akuimira Ufumu wa Mulungu, wokhala ndi Yesu Kristu monga Mfumu yolamulira.—Chivumbulutso 12:1-5.
7 Nanga “mbewu,” kapena mbadwa, ya mkazi, yotchulidwa pa Genesis 3:15, imene idzazunzunda “mutu” wa Satana n’kumupha, ndani? Ndiye uja amene anatumidwa ndi Mulungu kuchokera kumwamba kudzabadwa mozizwitsa mwa namwali, inde, munthuyo Yesu. (Mateyu 1:18-23; Yohane 6:38) Chaputala 12 cha Chivumbulutso chikusonyeza kuti pokhala Wolamulira wakumwamba woukitsidwa, Mbewu imeneyi, Yesu Kristu, adzatsogolera kugonjetsa Satana ndipo adzakhazikitsa, malinga ndi kunena kwa Chivumbulutso 12:10, ‘ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake.’
8. (a) Kodi ndi chinthu chatsopano chiti chimene Mulungu anakonza mogwirizana ndi chifuno chake choyamba? (b) Kodi ndani akupanga boma latsopano la Mulungu?
8 Chotero Ufumu umenewu m’manja mwa Yesu Kristu uli chinthu chatsopano chimene Mulungu anakonza mogwirizana ndi chifuno chake choyamba chakuti anthu asangalale ndi moyo wosatha padziko lapansi. Satana atapanduka, Yehova mwamsanga anakonza zochotseratu zotsatira zake zonse za kuipa mwa boma latsopano limeneli la Ufumu. Pamene Yesu anali padziko lapansi anasonyeza kuti sadzakhala yekha polamulira mu Ufumu umenewu. (Luka 22:28-30) Ena adzasankhidwa mwa anthu kukagwirizana naye kumwamba ndi kulamulira limodzi naye, motero akumakhala mbali yachiŵiri ya mbewu ya mkaziyo. (Agalatiya 3:16, 29) Mu Baibulo chiŵerengero cha amene adzakhala olamulira anzake a Yesu—onse otengedwa mwa anthu ochimwa padziko lapansi—chikutchulidwa kuti ndi 144,000.—Chivumbulutso 14:1-3.
9. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anafunika kuonekera padziko lapansi monga munthu? (b) Kodi Yesu anapasula motani ntchito za Mdyerekezi?
9 Komabe Ufumuwo usanayambe kulamulira, panafunikira kuti mbali yoyamba ya mbewuyo, Yesu Kristu, ionekere padziko lapansi. Chifukwa? Chifukwa chakuti anaikidwa ndi Yehova Mulungu kuti “akawononge [kapena, kupasula] ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Ntchito za Satana zinaphatikizapo kuchititsa Adamu kuchimwa, kumene kunadzetsa chiweruzo cha uchimo ndi imfa pa ana onse a Adamu. (Aroma 5:12) Yesu anapasula ntchito ya Mdyerekezi imeneyi mwa kupereka moyo Wake dipo. Motero iye anatheketsa anthu kumasuka pa chiweruzo cha uchimo ndi imfa natsegula njira ya moyo wosatha.—Mateyu 20:28; Aroma 3:24; Aefeso 1:7.
Zimene Dipo Limakwaniritsa
10. Kodi Yesu ndi Adamu anali ofanana motani?
10 Popeza kuti moyo wa Yesu unasamutsidwa kuchoka kumwamba kuloŵa m’mimba ya mkazi, anabadwa munthu wangwiro, wosaipitsidwa ndi tchimo la Adamu. Anali ndi mphamvu yokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Momwemonso, Adamu analengedwa munthu wangwiro ndi chiyembekezo chosangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Mtumwi Paulo anali kuganiza za kufanana kwa amuna aŵiriŵa pamene analemba kuti: “Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo [Yesu Kristu] anakhala mzimu wakulenga moyo. Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiŵiri ali wakumwamba.”—1 Akorinto 15:45, 47.
11. (a) Kodi Adamu ndi Yesu anakhudza motani mtundu wa anthu? (b) Kodi nsembe ya Yesu tiyenera kuiona motani?
11 Kufanana kwa anthu aŵiriŵa—amuna aŵiri okha angwiro amene anakhalako padziko lapansi—kukugogomezeredwa mwa kutchula kwa Baibulo kuti Yesu “anadzipereka yekha dipo lolinganiza kaamba ka onse.” (1 Timoteo 2:6, NW) Kodi Yesu analingana ndi yani? Eya, ndi Adamu pamene anali munthu wangwiro! Tchimo la Adamu woyamba linachititsa banja lonse la anthu kuweruzidwira ku imfa. Nsembe ya “Adamu wotsirizayo” inayala maziko otiombola ku uchimo ndi imfa, kuti tikhale ndi moyo kosatha. Nsembe ya Yesu ili yamtengo wapatali kwambiri! Mtumwi Petro anati: “Simunaomboledwa ndi zovunda, golidi ndi siliva.” M’malo mwake, Petro anafotokoza kuti: “Koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.”—1 Petro 1:18, 19.
12. Kodi Baibulo limafotokoza motani mmene chiweruzo chathu cha ku imfa chidzachotsedwera?
12 Baibulo limafotokoza bwino njira imene chiweruzo cha ku imfa pabanja la anthu chidzachotsedwera. Limati: “Mwa kulakwa kumodzi [kwa Adamu] kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi [njira yonse ya moyo wokhulupirika wa Yesu, yofika pachimake pa imfa yake] chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse. Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi [Adamu] ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi [Yesu] ambiri adzayesedwa olungama.”—Aroma 5:18, 19.
Chiyembekezo Chaulemerero
13. Kodi ndi chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza motero ponena za kukhala ndi moyo wosatha?
13 Makonzedwe ameneŵa a Mulungu ayenera kutisangalatsa kwambiri! Kodi simukukondwa kuti anapereka Mpulumutsi? Atafunsidwa kuti, “Kodi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha chimakusangalatsani?” pakufufuza kwina kumene kunachitidwa ndi nyuzipepala ina mumzinda wina waukulu wa ku United States, modabwitsa 67.4 peresenti ya anthu ofunsidwawo anayankha kuti “Ayi.” Chifukwa chiyani anati safuna kukhala ndi moyo kosatha? Mwachionekere chifukwa chakuti moyo padziko lapansi tsopano uli ndi mavuto ambiri. Munthu wina anati: “Sizindisangalatsa kuganiza za mmene ndingaonekere ndili ndi zaka 200.”
14. Kodi ndi chifukwa chiyani kukhala ndi moyo kosatha kudzakhala kosangalatsa kotheratu?
14 Komabe, Baibulo silikunena za kukhala ndi moyo kosatha m’dziko limene anthu akuvutika ndi matenda, ukalamba, ndi masoka ena. Ayi, chifukwa pokhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachotsa mavuto onse otero ochititsidwa ndi Satana. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha” maboma onse otsendereza a dzikoli. (Danieli 2:44) Panthaŵiyo, poyankha pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake, “chifuno” cha Mulungu ‘chidzachitika padziko lapansi monga zilili kumwamba’. (Mateyu 6:9, 10, Today’s English Version) M’dziko latsopano la Mulungu, dziko litayeretsedwa kuipa konse, mapindu a dipo la Yesu adzagwiritsidwa ntchito mokwanira. Inde, anthu onse amene adzayenerera adzakhalanso ndi thanzi langwiro!
15, 16. Kodi m’dziko latsopano la Mulungu mudzakhala mikhalidwe yotani?
15 Kwa anthu okhala m’dziko latsopano la Mulungu, mawu a m’Baibulo aŵa adzakwaniritsidwa: “Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.” (Yobu 33:25) Lonjezo lina la Baibulo lidzakwaniritsidwanso lakuti: “Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 35:5, 6.
16 Tangoganizani: Mosasamala kanthu za msinkhu wathu panthaŵiyo, kaya tikhale ndi zaka 80, 800, kapena ngakhale kuposa pamenepo, matupi athu adzakhalabe athanzi labwino. Zidzakhala monga momwe Baibulo limalonjezera kuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Panthaŵiyo lonjezo ili nalonso lidzakwaniritsidwa: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.
17. Kodi tingayembekeze kuti anthu adzakwanitsa kuchita zotani m’dziko latsopano la Mulungu?
17 M’dziko latsopano limenelo, tidzatha kugwiritsa ntchito ubongo wathu wodabwitsa mwanjira imene Mlengi wathu anafuna poulenga ndi mphamvu yopanda malire ya kuphunzira. Eya, tangoganizani za zinthu zodabwitsa zimene tidzachita! Ngakhale anthu opanda ungwiro akhala okhoza kupanga zonse zimene tiona kuchokera ku zinthu za padziko lapansi—mafoni a m’manja, mamaikolofoni, mawatchi, pagers [tizipangizo todziŵitsira munthu kuti wina akufuna kulankhula naye pafoni], makompyuta, ndege, inde, zilizonse zomwe munganene. Palibe chimene chinapangidwa ndi zinthu zimene anazitenga kutali mumlengalenga. Pokhala ndi moyo wopanda mapeto patsogolo pathu, mphamvu yopanga zinthu zaluso idzakhala yopanda malire m’Paradaiso wa padziko lapansi amene akudzayo!—Yesaya 65:21-25.
18. Kodi ndi chifukwa chiyani moyo sudzakhala wotopetsa m’dziko latsopano la Mulungu?
18 Ndipo moyo sudzakhala wotopetsa. Ngakhale tsopano lino timalakalaka chakudya chathu chotsatira, ngakhale kuti takhala tili kudya nthaŵi zikwi zambirimbiri. Pokhala anthu angwiro, tidzasangalala kwambiri ndi zakudya zokoma za dziko lapansi la Paradaiso. (Yesaya 25:6) Ndipo tidzasangalala kwamuyaya posamalira nyama zochuluka za dziko lapansi komanso poyang’ana kuloŵa kwa dzuŵa kochititsa chidwi, mapiri, mitsinje, ndi zigwa. Inde, moyo sudzakhala wonyong’onya m’dziko latsopano la Mulungu!—Salmo 145:16.
Kukwaniritsa Zofuna za Mulungu
19. Kodi ndi chifukwa chiyani kuli koyenera kukhulupirira kuti pali zofunika kuchita kuti tilandire mphatso ya Mulungu ya moyo?
19 Kodi mungayembekeze kulandira mphatso yaikulu ya Mulungu ya moyo wosatha m’Paradaiso popanda kuchitapo kanthu kalikonse kuti muipeze? Kodi si kwanzeru kuti Mulungu angafune zinazake kwa ife? Inde. Sitingati Mulungu amangotiponyera mphatsoyo. Amatipatsa, koma tiyenera kuikalimira kuti tiilandire. Inde, tifunika kuchita khama. Mungafunse funso limodzimodzi lija lomwe wolamulira wachinyamata wolemera anafunsa Yesu: “Chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?” Mwina mungafunse funsoli monga momwe mdindo wa m’ndende ya ku Afilipi anafunsira kwa mtumwi Paulo kuti: “Ndichitenji kuti ndipulumuke?”—Mateyu 19:16; Machitidwe 16:30.
20. Kodi chofunika chachikulu kuti tipeze moyo wosatha ndi chiyani?
20 Usiku imfa yake isanafike, Yesu anasonyeza chofunika chachikulu pamene popemphera kwa Atate wake wakumwamba anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamutuma.” (Yohane 17:3) Kodi chimenechi sichofunika choyenera kuti tipeze chidziŵitso cha Yehova, amene anatheketsa moyo wosatha, ndi cha iye amene anatifera, Yesu Kristu? Komatu pakufunika zambiri kuposa kungopeza chidziŵitso chimenecho.
21. Kodi timasonyeza motani kuti tikukwanitsa chofunika cha kusonyeza chikhulupiriro?
21 Baibulo limanenanso kuti: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” Ndiyeno limati: “Iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.” (Yohane 3:36) Mumaonetsa kuti mukukhulupirira Mwanayo mwa kusintha moyo wanu ndi kuugwirizanitsa ndi chifuno cha Mulungu. Muyenera kusiya njira iliyonse yolakwika imene mungakhale mukutsatira ndipo chitani zinthu zimene zidzakondweretsa Mulungu. Muyenera kuchita zimene mtumwi Petro analamula mwakuti: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.”—Machitidwe 3:19.
22. Kodi ndi zochita ziti zimene zikuphatikizidwa pa kutsatira mapazi a Yesu?
22 Tisaiwale kuti kuli kokha mwa kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kuti tingakhale ndi moyo wosatha. (Yohane 6:40; 14:6) Timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro mwa Yesu mwa ‘kulondola mapazi ake [mosamalitsa, NW].’ (1 Petro 2:21) Kodi kuchita zimenezi kumaphatikizapo chiyani? Chabwino, Yesu, m’pemphero kwa Mulungu, anati: “Taonani, ndafika, . . . kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.” (Ahebri 10:7) Kuli kofunika kutsanzira Yesu povomera kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kupatulira moyo wanu kwa Yehova. Pambuyo pake, muyenera kusonyeza kudzipatulira kumeneko mwa ubatizo wa m’madzi; nayenso Yesu anadziperekera kuti abatizidwe. (Luka 3:21, 22) Kuli koyenera kwambiri kutenga masitepe ameneŵa. Mtumwi Paulo ananena kuti “chikondi cha Kristu chitikakamiza.” (2 Akorinto 5:14, 15) M’njira yotani? Chabwino, chikondi chinasonkhezera Yesu kupereka moyo wake m’malo mwa ife. Kodi zimenezi siziyenera kutikakamiza kuti tilabadire mwa kumukhulupirira iyeyo? Inde, chiyenera kutikakamiza kutsanzira chitsanzo chake cha chikondi cha kudzipereka pothandiza ena. Kristu anali kukhala ndi moyo kuti azichita chifuno cha Mulungu; tiyenera kuchita mofananamo, osakhalanso ndi moyo kwa ife tokha.
23. (a) Kodi amene akulandira moyo ayenera kuwonjezedwa kuchiyani? (b) Kodi ndi chiyani chimene chimafunika kwa amene ali mu mpingo wachikristu?
23 Sikuti amenewo ndiwo mapeto ake. Baibulo limati pamene anthu 3,000 anabatizidwa pa Pentekoste wa 33 C.E., iwo “anawonjezedwa.” Kuwonjezedwa kuti? “Anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano,” anafotokoza motero Luka. (Machitidwe 2:41, 42) Inde, anasonkhana pamodzi kuphunzira Baibulo ndi kuyanjana, chotero anawonjezedwa ku mpingo wachikristu, kapena kuti anakhala mbali yake. Akristu oyambirira anali kufika pamisonkhano mokhazikika kuti azilangizidwa mwauzimu. (Ahebri 10:25) Mboni za Yehova lerolino zimachitanso zimenezi, ndipo zikukulimbikitsani kukhala nazo limodzi pamisonkhano imeneyi.
24. Kodi “moyo weniweniwo” ndi chiyani, ndipo ndi motani ndiponso ndi liti pamene udzapezedwa?
24 Anthu mamiliyoni ambiri tsopano akutsata njira yopapatiza ya kumoyo. Kupitiriza panjira imeneyi yopapatiza kumafunadi khama! (Mateyu 7:13, 14) Paulo anasonyeza zimenezi m’pempho lake lochonderera lakuti: “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira.” Kulimbikira nkhondo imeneyi ndi kofunika kuti ‘tigwire [“kugwiritsa,” NW] moyo weniweniwo.’ (1 Timoteo 6:12, 19) Moyo umenewo sindiwo moyo uno wa zoŵaŵa ndi zopweteka ndi mavuto, umene tchimo la Adamu linadzetsa pa ife. M’malo mwake, ndiwo moyo m’dziko latsopano la Mulungu, umene udzakhalako posachedwa pamene nsembe ya dipo ya Kristu idzagwiritsidwa ntchito pa onse okonda Yehova Mulungu ndi Mwana wake pambuyo poti dongosolo ili la zinthu lachoka. Tiyeni tonsefe tisankhe moyo—“moyo weniweniwo”—moyo wosatha m’dziko latsopano laulemerero la Mulungu.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
◻ Kodi ndani amene ali njoka, mkazi, ndi mbewu zotchulidwa pa Genesis 3:15?
◻ Kodi Yesu analingana motani ndi Adamu, ndipo kodi dipo linatheketsa chiyani?
◻ Kodi mukuyembekezera chiyani chimene chidzapangitsa dziko latsopano la Mulungu kukhala losangalatsa kwambiri kwa inu?
◻ Kodi tiyenera kukwaniritsa zofunika ziti kuti tikakhale ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu?
[Chithunzi patsamba 10]
Kwa ana ndi achikulire omwe, Yesu ali njira yokha ya moyo wosatha
[Chithunzi patsamba 11]
Mu nthaŵi yoikika ya Mulungu, nkhalamba zidzakhalanso ndi mphamvu ngati anyamata