Mutu 1
Kodi Mbiri Yabwino Ingapezeke Kuti Lero Lino?
1. Kodi n’chiani chimene inu mukachilingalira kukhala mbiri yabwino?
IFE tonse timakondwera ndi mbiri yabwino, kodi si choncho? Eya, chifuno cha bukhu lino ndicho kusimba mbiri yabwino imene imakondweretsa mwamuna, mkazi ndi mwana ali yense pa dziko lino lapansi lero lino. Limasonyeza m’tsogolo mosangalatsa ndi mosungika kwa anthu onse. Kunena zoona, pamene muzindikira chimene mbiri yabwino imene’yi ikunena, tiri otsimikiza kuti mudzabvomereza kuti iri mbiri yabwino yabwino kopambana.
2. Kodi mbiri yabwino iyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa ife? (Miyambo 12:25; 25:25)
2 Kuti ikhale mbiri yabwino kwa ife, mbiri imene’yi ikafunikira kukhudza miyoyo yathu. Iyenera kutisangalatsa, ndi kutilimbikitsa kukhala ndi lingaliro lotsimikizira ponena za m’tsogolo. Iyenera kutithandiza pamene tikukumana mwachidaliro ndi zeni-zeni za moyo. Chiyambukiro chake chiyenera kukhala kupepuza akatundu amene akulemera anthu ochuluka m’kati mwa nyengo ino ya kusatsimikizira. Iyenera kuthandizira kuchotsa mantha athu, ndi kupangitsa moyo kukhala watanthauzo ndi woyenera kukhala nao.
3. Kodi ndi mbiri za m’nyuzi zotani zimene zikakusangalatsani?
3 Tiyene timene kuti m’mawa uli wonse pamene titenga nyuzipepa tikuwerenga mitu ya nkhani yonga iyi:
“Palibe Kusowa kwa Nyumba—Ntchito Zosungika kwa Ali yense”
“Zokolola Zochuluka Kopambana—Zakudya Zabwino Zochuluka”
“Mipingiridzo Yaupfuko Yatha”
“Upandu Wafafafanizidwa”
“Mtendere wa pa Dziko Lonse Lapansi Wotheratu”
“Matenda ndi Ukalamba Zachotsedwa—Zipatala ndi Nyumba Zolinganiza Maliro Zatsekedwa”
“Olamulira a Dziko Lapansi Ali Ogwirizana Kotheratu—Maprogramu Osangalalira Mokwanira ndi Moyo Akupangidwa”
4. (a) Kodi mukalingalira kukwaniritsidwa kwa mbiri yabwino imene’yo kukhala chozizwitsa? (b) Kodi mungalingalire zochitika zina za tsiku ndi tsiku zimene ziri’di zozizwitsa? (Luka 12:27) (c) Moyenerera, kodi ndani amene ali wochititsa zinthu zimene’zi? (Machitidwe 14:15, 17) (d) Kodi mbiri yabwino’yo imalongosola’nso chiani?
4 Ndithudi mbiri zonga zimene’zo zikatisangalatsa! Komabe, mwina mwake inu mukunena kuti, ‘Zimene’zo n’zosatheka! Sizingachitike konse! Zimene’zo zikakhala chozizwitsa!’ Koma kodi chozizwitsa n’chiani? Chimafotokozedwa kukhala “chochitika chodabwitsa chochititsidwa ndi chochititsa china chauzimu.” Ndipo ndithudi tazingidwa nthawi zonse ndi zodabwitsa zimene palibe chochititsa chaumunthu chikazichititsa kapena kuzipanga. Eya, moyo weni-weni’wo n’chozizwitsa! Ndipo pakati pa zinthu zamoyo pa dziko lapansi, zozizwitsa miyandamiyanda zikuchitika tsiku liri lonse. Kubadwa kwa chamoyo chiri chonse n’chozizwitsa, chimodzi-modzi’nso kumasula kwa duwa liri lonse. Kukongola kumene kwakuta dziko lapansi’li, ndi kuchuluka kwa makonzedwe ochirikiza moyo pa iro, zimasonyeza kuti Mlengi wanzeru zonse ndi wachikondi chonse anachita chozizwitsa m’kupanga zonse. Mbiri yabwino yolongosoledwa muno ikusimba zinthu zina zobdabwitsa zimene iye ali pafupi kuchita m’kubwezeretsa umodzi, mtendere ndi chimwemwe pakati pa zolengedwa zake zonse.
5. Kodi ndi uthenga wotani umene mumauona m’chilengedwe?
5 Ngakhale tsopano, kumene anthu adyera sanaipitse dziko lapansi’li, zolengedwa zonse zimachitira umboni kwa ife kuti Uyo amene anazilinganiza nazipanga ali ndi mikhalidwe yodabwitsa ya chikondi, kukoma mtima, nzeru ndi kuzindikira. Maulemerero a chilengedwe chake ali mbali ya uthenga wake kwa ife. Ha, ndi kotonthoza ndi kokondweretsa chotani nanga m’mene kuliri ku maso athu kukongola kwa chidikha cha udzu wobiriwira! Komabe kubiriwira kumodzi-modzi’ko kwa zomera ndiko chinthu chimene chimasandutsa mphamvu yochokera ku dzuwa kukhala chakudya chochirikiza matupi athu. Nkhope ya munthu iri ndi mfuno yonunkhizira, makutu omvera, maso oonera, ndi pakamva, mano ndi lirime zodyera ndi kulankhulira. Koma pamene ziwalo zonse’zi ziphatikizidwa pamodzi, ha ndi yokongola chotani nanga m’mene nkhope imene’yo ingaonekere m’kusonyeza umunthu umene umasonyeza mikhalidwe yonga ya Mulungu!
6. (a)Kodi ndi m’Mabukhu awiri ati amene Mlengi Wamkulu’yo akuperekamo uthenga wake kwa anthu? (b) Kodi ndichiyembekezo chotani chimene ulosi wa Baibulo umapereka kaamba ka: (1) Nyumba ndi ntchito zosatha kwa onse? (2) Zakudya zochuluka? (3) Kuchotsedwa kwa mipingiridzo yaupfuko? (4) Kufafanizidwakwa upandu? (5) Kuthetsedwa kwa nkhondo? (6) Kuchotsedwakwa matenda, ukalamba ndi imfa? (7) Kulamuliridwa kwa dziko lapansi m’chilungamo?
6 Inde, zinthu zodabwitsa zimene timaziona m’chilengedwe, kuphatikizapo kupangidwa kwa munthu mwiniyo, zimapereka kwa ife uthenga wakuti Mlengi Wamkulu aliko ndipo ali ndi chifuno kulinga kwa anthufe. Komabe, iye akulemba uthenga umene’wu, osati kokha m’Bukhu la chilengedwe chake, koma’nso m’zilembo zolembedwa m’Bukhu lina losindikizidwa limene ife lero lino tingaliwerenge. M’Bukhu limene’li iye amasonyeza zimene iye angachite m’kuthetsa mabvuto ndi kuchiritsa matenda amene amayang’anizana ndi anthufe lero lino. Chonde, talingalirano, zitsanzo zina za zimene Mlengi wa dziko lathu lapansi amanena kuti adzachitira anthu ake.
Nyumba ndi Ntchito Zosatha kwa Ali Yense:
“Adzamanga’nso . . . nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.” “Koma wondimvera ine [nzeru] adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Amosi 9:14; Miyambo 1:33.
Zipatso ndi Zakudya Zochuluka kwa Onse:
“Dziko lapansi l[idz] apereka zipatso zake.” “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.” Ndidzakukwezani Mulungu wanga . . . Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chao.”—Salmo 67:6; 72:16; 145:1, 16.
Mipingiridzo Yaupfuko Ikulowedwa m’Malo ndi Ubale wa Anthu:
“Taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe . . . sadzamva’nso njala, kapena ludzu.” “Inu nonse muli abale.” – Chibvumbulutso 7:9, 16; Mateyu 23:8.
Upandu, Chiwawa ndi Kuipa Zifafanizidwa:
“Ochita zoipa adzadulidwa: . . . Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psyiti.” “Pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.”—Salmo 37:9, 10; 92:7.
Kupezedwa kwa Mtendere wa Pa Dziko Lonse Lapansi—Kulibe’nso Nkhondo:
“Mtendere pa dziko lapansi pakati pa anthu oyanjidwa.” “Iwo . . . sadzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunzira’nso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsya.”—Luka 2:14, NW; Mika 4:3, 4.
Kuchotsedwa kwa Matenda, Ukalamba ndi Imfa:
“Sipadzakhala’nso imfa; ndipo sipadzakhala’nso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” “Panali mitengo ya moyo . . . Ndipo masamba a mitengo’yo anali ochiritsira mitundu [ya anthu]. Ndipo sipadzakhala’nso themberero liri lonse.”—Chibvumbulutso 21:4; 22:2, 3, NW.
Boma Limodzi Lolungama kaamba ka Anthu Onse:
“Taonani, mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.” “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu . . . kufikira malekezero a dziko lapansi.”— Yesaya 32:1; Salmo 72:7, 8.
7. (a) Kodi mbiri yabwino ikulengedzedwa kwa anthu angati monga “uthenga wosangalatsa”? (b) Kodi n’chifukwa ninji imene’yi ingachedwe mbiri yabwino “yosatha”? (Yesaya 40:8)
7 Zimene’zi zikumveka ngati mbiri yabwino yodabwitsa, kodi si choncho? Zoona, anthu ena amaseka mbiri yabwino imene’yi, koma alibe chiri chonse chopereka m’malo mwake. Inu simufunikira kukhala ngati iwo. Inu ndi banja lanu simudzataya kanthu kali konse-ndipo mungapeza zochuluka—mwa kupenda malonjezo abwino kwambiri amene’wa. Mbiri yabwino imene tiri pafupi kuipenda posachedwapa yachedwa “mbiri yabwino yosatha” imene ikulengezedwa “montha uthenga wosangalatsa kwa awo amene akukhala pa dziko lapansi, ndi kwa mtundu uli wonse ndi pfuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chibvumbulutso 14:6, NW) Imasimba za mapindu achikhalire ndi osatha amene alinkudza kwa anthu onse.
[Chithunzi chachikulu patsamba 4]