Mutu 4
M’mene Ufumu wa Mulungu Ukukhalira Boma la Dziko
1, 2. Kodi chionongeko cha “fano” chikudza motani—kuchokera m’kati kapena kuchokera kunja?
“FANO” lophiphiritsira la ulamuliro wa dziko wopangidwa ndi ndale za dziko za anthu—golidi wake, siliva wake, mkuwa wake, chitsulo chake ndi dongo lake-iro lonse lathunthu liri loyenera kuonongedwa! Yehova Mulungu, amene ananeneratu mapeto kuyambira pachiyambi, akunena motero m’Mau ake olosera. Tiyeni tione kuchokera m’Mau amene’wo kuti sindiwo mkhalidwe wogawanika wa mapazi ndi zala umene umachititsa kugwa kwa ‘fano’lo.’ Sindiyo nkhondo ya nyuklea iri yonse ya pa dziko lonse lapansi pakati pa “chitsulo” chophiphiritsira ndi “dongo” lophiphiritsira imene ikudzetsa chionongeko cha “fano” kuchokera kumutu kufikira kuphazi. Loto lolosera’lo monga momwe linakumbutsiridwa Nebukadinezara ndi mneneri wa Yehova Danieli momvekera bwino likusonyeza kuti chionongeko’cho sichikuchokera m’kati mwa “fano’lo,” koma chikuchokera kunja kwake. Nanga, kodi chimachokera kuti? Danieli anasonyeza chimene’chi pamene iye anatsiriza kumasulira kwake, pouza Mfumu Nebukadinezara kuti:
2 “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaononeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire. Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m’phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golidi; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m’tsogolomo; loto’li nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.”—Danieli 2:44, 45.
3. Kodi n’chifukwa ninji nthawi yakuti Mulungu apange masinthidwe iri pafupi?
3 Ife lero lino, amene tingathe kuyang’ana m’mbuyo ku zaka zoposa 2,580 za nthawi’yo kuyambira pa loto la Nebukadinezara, tiri ndi zifukwa zochulukirapo zokhulpirira, zoposa zimene Nebukadinezara anali nazo, zakuti loto’lo liri lodalirika m’tanthauzo ndi kuti kumasuliridwa kwake kochitidwa ndi Danieli n’kodalirika. Chifukwa cha chimene’cho tikuchititsidwa kukhulupirira mau a “Mulungu wamkulu.” Ndipo chotero, kodi chionongeko cha “fano” lophiphiritsira’lo chikuchokera kuti? Chikuchokera kwa “Mulungu wa kumwamba,” Uyo amene amasintha nthawi ndi nyengo ndi amene amatsitsa mafumu ndi kukhazikitsa mafumu ena monga momwe afunira. Nthawi yoikika yoti iye atero iyenera kukhala iri pafupi kwambiri. Kodi n’chifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa chakuti kale’lo kuchiyambi kwa mphakasa ya chaka cha 1914 C.E., chaka chotsirizira cha Nthawi za Akunja, “nthawi zoikidwira za mitundu” chinatha. Malinga ndi kunena kwa mau a Kristu mu Luka 21:20-24, zimene’zi zinatanthauza kuti nthawi inali itafika yakuti Mulungu aletse kupondereza koonjezereka kwa mitundu pa chimene Yerusalemu anachiimira. Motani?
4. Kodi ndi motani m’mene Mulungu anachitira ndi mapemphero a atsogoleri achipembedzo onena za Nkhondo Yoyamba ya Dziko?
4 M’chirimwe cha 1914 nkhondo ya dziko inaulika pakati pa Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri ndi mbali zazikulu zotsala za Ulamuliro wa Dziko wapapitapo Wachisanu ndi Chimodzi, kwa nthawi ina wodziwika kukhala Ufumu Woyera Wachiroma wa Mtundu wa Jeremani. Nkhani yaikulu yokanganiridwa inali ulamuliro wa Dziko lonse pano pa dizko lapansi, limene mbali yake imodzi mwa zinai pa nthawi imene’yo inalamulidwa ndi Ufumu wa Britain. Ufumu wa Mulungu Waumesiya unali wosakondweretsa kapena kunukha kanthu kwa okanganira omenyana’wo. Ndipo komabe iwo anali kumenyanira chija chimene ufumu wa Mulungu Waumesiya (monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi Yerusalemu wa nthawi za Baibulo) unali nacho kuyenera, ndiko kuti, ulamuliro wa dziko lonse. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko anapempherera mbali zonse zokhala ndi phande m’nkhondo ya pa dziko lonse’yo. Koma kodi Yehova Mulungu analabadira mapemphero a kukonda dziko lao ndi autundu a atsogoleri achipembedzo’wo? Kutali-tali! Malinga ndi kunena kwa chithunzi-thunzi cholosera choperekedwa m’Chibvumbulutso 12:1-10, pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914 Yehova Mulungu anachititsa kubadwa kumwamba kwa ufumu wake Waumesiya wolonjezedwa’wo m’manja mwa Mwana wake wolongedwa ufumu, Yesu Kristu.
5, 6. Kodi “mwala” unasemedwa m’phiri lotani? Liti, ndipo motani?
5 M’menemu ndimo m’mene “mwala” wa m’loto la Nebukadinezara unasemedwera m’phiri popanda chithandizo cha manja a munthu. Ufumu Waumesiya wokhala m’manja mwa Yesu Kristu wolemekezedwa’yo ndiwo “mwala wa m’loto’lo. Ufumu wolonjezedwa kwa nthawi yaitali umene’wo ukanatha kudza kokha kuchokera kwa “Mulungu” wa kumwamba,” Yehova, Ambuye Mfumu.
6 Chotero “phiri” m’limene mwala’wo ukusemedwa modabwitsa siliri limodzi la “mapiri asanu ndi awiri” pa amene mkazi wachigololo wachipembedzo’yo, Babulo Wamkulu, wakhala akukhalapo monga mfumu yachikazi. (Chibvumbulutso 17:9; 10) “Phiri” lophiphiritsira’lo siliri phiri la pa dziko lapansi la ulamuliro. Liri “phiri” la ulamuliro wa m’chilengedwe chonse, pakuti uli ulamuliro wa Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, ndiko kuti, Yehova “Mulungu wamkulu.” (Salmo 121:1, 2; Danieli 2:45) “Mwala” wachifumu’wo unasemedwa ndi mphamvu yaumulungu kuchokera ‘m’phiri’ la m’chilengedwe chonse pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914 C.E. kuyambira pa nthawi imene’yo ufumu wa Mulungu Waumesiya uli ndi kuyenera kwa kulowerera m’zochitika za mitundu ndi kuchititsa “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu” kulalikidwam’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu “kaamba ka umboni ku mitundu yonse” mapeto ao asanafike. (Mateyu 24:3-14, NW) Ufumu’wo tsopano ukugwira ntchito!
7. Kodi ndi motani m’mene “mafumu aja” asonyezera chitsimikiziro cha kupitirizabe kulamulira?
7 M’chaka chogwedezeka ndi nkhondo chimene’cho cha 1914 panali olamulira ambiri okhala pa mipando yachifumu monga mafumu koposa pa tsopano lino. Kumene’ko panali mikhalidwe yochititsa mau a Danieli 2:44 kukhala oona: Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka.” “Mafumu” amene’wo, kapena olamulira ali onse a ndale za dziko amene alamulira pa dziko lapansi, akana kumvetsera “mbiri yabwino ya ufumu” imene tsopano yafalitsidwa pa dziko lonse. Iwo, kapena maboma ao, atsutsa kapena kuzunza mwachiwawa olalikira Achikristu a “mbiri yabwino” a ufumu wokhazikitsidwa Waumesiya wa Yehova. Zimene’zi, “mafumu” otero’wo azichita monga chisonyezero cha kukhala kwao otsimikizira kusungabe maulamuliro ao a pa dziko lapansi. Pamenepa, kodi n’chiani, chimene chiyenera kuchitidwa ponena za olamulira otero’wo amene amakana kupereka maulamuliro ao ku ufumu Waumesiya umene Mulungu waukhazikitsa? Danieli 2:44 amatipatsa yankho:
8. Kodi chinthu chochitidwira ku “fano’lo” chimatanthauzanji kaamba ka dongosolo lathu’li?
8 “ Ndi [ufumu] wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.” Chinthu chotero’cho chidzatanthauza mapeto otheratu a dongosolo lino la zinthu. Chidzatanthauza kuzimiririka kwa “fano” lophiphiritsira’lo la maulamuliro a ndale za dziko opangidwa ndi anthu. Zimene’zi ziri patsogolopa, pafupi kwambiri tsopano koposa kale lonse chiyambire 1914 C.E. Kuchotsedwa kwa “fano” lolambiridwa la ulamuliro waumunthu sikudzakhala kwamtendere. Padzakhala kutswanyidwa ndi kuperedwa kwake kukhala ngati ufa. Pamene “mwala” wa Ufumu Waumesiya ulowa, kunena kwake titero, mu mpweya wa dziko lathu lapansi’li pa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu, sudzasweka mofanana ndi miyala ina yochokera kutali m’mlengalenga. Ndi mphamvu yokwanira ya liwiro lonse limene uwo walionjezera chiyambire 1914, “mwala” wosaonongeka umene’wu wolimba mofanana ndi daimondi udzafika pa cholinga chake ndi mphamvu yophwanya. Kuti?
9. Kodi ndi kuombana kotani kumene mbadwo wa pambuyo pa Nthawi za Akunja uno udzakuona?
9 Pa “mapazi” a “fano” lophiphiritsira’lo, “mapazi” a chitsulo ndi dongo lachinyontho amene akali chiriri lero lino. Ife, mbadwo uno wa mtundu wa anthu, tikukhala ndi moyo mu “masiku a mafumu aja,” m’masiku a “mapazi” a mbali ina chitsulo, mbali ina dongo amene’wa. Ife mbadwo uno wa pambuyo pa Nthawi za Akunja, tatsala pang’ono kuona kugundana kwa “mwala” wa Ufumu’wo ndi Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri ndi maboma onse a ndale za dziko m’kati kapena kunja kwa gulu la Mitundu Yogwirizana. Motero, m’kuombana kotsirizira pa nkhani yaikulu ya ulamuliro wa m’chilengedwe chaponse-ponse, “mwala” wa Ufumu’wo udzathetsa kotheratu “maufumu onse.” Kodi zimene’zo zidzatanthauzanji kwa ife amene tiri a mbadwo uno amene tidzapezeka tiri m’kati mweni-mweni mwa kuombana kumene’ku? Kodi tinayamba talingalira za zimene’zo?
10. Kodi n’chifukwa ninji kutha kwa ulamuliro wa anthu sikudzasiya popanda boma?
10 Kuthetsedwa mwachiwawa kwa dongosolo la pa dziko lonse lapansi la ulamuliro wopangidwa ndi anthu wa ndale za dziko sikudzasiya pano popanda kanthu ponena za boma la mtundu wa anthu. Loto lolosera la Nebukadinezara silimasonyeza kuti kupanda boma kotero’ko kudzakhalapo pa dziko lapansi m’limene munthu ali yense wokhalapo adzangochita monga momwe afunire popanda kugonjera ku boma liri lonse. M’malo mwake, boma lalikulu kopambana, lamphamvu kopambana m’mbiri yonse ya anthu lidzatenga ulamuliro wotheratu pa opulumuka ochokera pakati pa mbadwo uno.
11. Kodi Danieli anaona “fano” loperedwa’lo litalowedwa m’malo ndi chiani?
11 Oyanjidwa kopambana adzakhala awo a m’mbadwo uno amene adzakhala ndi mwai wa kuona kukwaniritsidwa kwa zimene mneneri Danieli anaona m’masomphenya, akumatipatsa ife kulongosola uku pamenepo: “Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fano’li pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya. Pamenepo, chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezaka’nso malo ao; ndi mwala udagunda fano’wo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.”—Danieli 2:34, 35.
12. Kodi kudzaza dziko lapansi kwa phiri’lo kumasonyezanji?
12 Kodi zimene’zi zikusonyezanji? Palibe kanthu kena koposa ndi kuti ufumu Waumesiya wa Mulungu monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi “mwala” udzadzaza dziko lonse lapansi, kuli konse kumene ana a anthu akhala.
13. Kodi limene’li lidzakhala boma lokhazikika m’njira yotani, ndipo chifukwa ninji?
13 Malikulu a boma’lo adzakhala kumwamba, kumene Yesu Kristu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu ndi kulongedwa ufumu amakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, koma adzafutukulira mphamvu yake yauzimu ku dziko lapansi, osati tsopano kaamba ka zifuno za kusakaza, koma kaamba ka ulamuliro wangwiro ndi kudalitsidwa kwa omvera okhala pa “dziko lonse lapansi.” Limene’li lidzakhala boma lokhazikika, losati n’kugubuduzidwa ndi zipanduko ziri zones za chiukiro. ‘Silidzaonongeka,’ kapena’nso kukhala ndi wolowa m’malo waumunthu. ‘Silidzasiyidwira mtundu wina wa anthu.’ Mosafanana ndi maufumu a olamulira omafa aumunthu kuyambira ku Babulo wa m’nthawi ya Nimrode kumkabe m’tsogolo, ‘udzakhala chikhale,’ kosatha. (Danieli 2:44, 45) Wolamulira wake wakumwamba, Mfumu Yaumesiya Yesu Kristu, pa amene Yehova Mulungu wapatsa kusafa, sadzalola boma lake kufa. Iye mwiniyo adzakhala ndi moyo “kosatha” kuti asungebe ufumu umene’wo kaamba ka kukwaniritsidwa kotheratu kwa chifuniro cha Mulungu kaamba ka dalitso losatha la mtundu wonse wa anthu womvera pa dziko lapansi lolamulidwa mwangwiro.
14. Kodi ndani amene adzakhala anthu achimwemwe pakati pa mbadwo wa lero lino’wu?
14 Ndipo m’menemu ndimo m’mene ufumu wa Mulungu ukukhalira boma la dziko lonse. Achimwemwe ali awo onse a mbadwo uno lero lino amene adzakhalabe ndi moyo kuuona ukukhala wotero. Iwo angakhale nzika zake zachikondi ndi zomvera kosatha!