Mutu 5
Kuneneratu Nthawi ya Ulamuliro wa Dziko
1, 2. Cha m’ma-600 B.C.E. kodi Nebukadinezara ananenanji ponena za Mulungu?
TIYENI tiyang’ane pa mapu a dziko lapansi ndi kupeza dziko la Iraq, Turkey wa mu Asiya, Suriya, Lebanon, Yordano ndi Israyeli. Ngati olamuliro a maiko amene’wo anali kukhala pafupi ndi chiyambi cha zaka za zana lachisanu ndi chimodzi Nyengo yathu Ino isanakhale, iwo akanakhala akulamulidwa ndi Ulamuliro wa Dziko Wachitatu ndipo nawu uthenga umene iwo akanaulandira mwaukumu kuchokera ku Babulo:
2 “Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu. Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam’mwamba-mwamba. Ha! Zizindikiro zake n’zazikulu, ndi zozizwa zake n’za mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamuliro kwake ku mibadwo mibadwo.”—Danieli 4:1-3.
3. Kodi ulamuliro wa Nebukadinezara unali wotani poyerekezera ndi wa Mulungu?
3 Ndi mau olowetsamo zambiri amene’wo mfumu ya pa nthawi’yo ya Babulo inasonya, osati ku Ufumu wa iye mwini wa Baibulo, Ulamuliro wa Dziko Wachitatu wa mbiri ya Baibulo, koma ku ufumu ndi ulamuliro wa Mulungu Wam’mwamba-mwamba. Kuwerengera kuchokera pa kukhala ndi phande kwa Mfumu Nebukadinezara m’kuonongedwa kwa malikulu a Asuri Nineve mu 632 B.C.E. mpaka kukafika ku kugubuduzidwa kwa Babulo kochitidwa ndi Koresi Mperisi mu 539 B.C.E., Ufumu wa Babulo wa Nebukadinezara ndi mzera wake wa mafumu unakhala kwa zaka makumi asanu ndi anai mphambu zitatu kapena zoposa, zosakwanira zaka zana limodzi. Koma ufumu ndi ulamuliro wa Mulungu Wam’mwamba-mwamba ziri za ku nthawi yosatha, mbadwo ndi mbadwo, ndiko kunena kuti, kosatha, ku nthawi yopanda mapeto. Ufumu ndi ulamuliro wa Yehova ziri zofutukuka kwambiri, osati kokhal ponena za nthawi, koma’nso m’chigawo chokhala mu ulamuliro’wo. Ufumu wa Nebukadinezara unalowetsamo kokha mbali ya kumwela chakumadzulo kwa Asiya, Middle East ndipo potsirizira pake Igupto, koma chigawo chokhala mu ulamuliro wa Mulungu Wam’mwamba-mwamba n’cha mchilengedwe chonse, chomalowetsamo kumwamba ndi dziko lapansi lomwe. Mulungu Wam’mwamba-mwamba’yo ali Wolamulira wa m’Chilengedwe chonse, ndipo wotero kosatha!
4. Kodi Nebukadinezara motero analengeza mulungu wapamwamba kwambiri loposa Merodaki?
4 India ndi mitundu ndi mafuko ena amakono ali ndi milungu yao ya mtundu ndi ya pfuko, ndipo Babulo wakale anali ndi milungu yake. Koma Nebukadinezara, wolambira wa mulungu wa Babulo Merodaki, anakakamizika kulengeza pa dziko lonse kuti pali Mulungu Wam’mwamba-mwamba, amene amachita zizindikiro ndi zozizwitsa zimene ziri zazikulu ndi zodabwitsa, motsimikizira kukhalapo kwake kweni-kweni. Chilengezo cha Nebukadinezara chimanena zimenezi.
LOTO LA NEBUKADINEZARA LA MTENGO WAUKULU
5, 6. Kodi ife tsopano tikukondweretsedwa ndi chitsa cha mtengo chakale chotani?
5 Ife tonse lero lino tiri okondweretsedwa ndi mitengo. Tingabzale mitengo, koma ife tonse tiyenera kubvomereza kuti mitengo sinalengedwe ndi munthu. Iyo inalipo pano pa dziko lapansi zaka zikwi zambiri munthu asanafikepo mu 4026 B.C.E. Mitengo ina iri yodabwitsa ponse pawiri kaamba ka ukulu wao ndi kukhala kwao kwa nthawi yaitali, mofanana ndi mitengo ya sequoia m’boma la Amereka la California.
6 Mfumu Nebukadinezara akusimba za mtengo wautali kwambiri koposa sequoia wamkulu wamtali kopambana, sempervirens, wautali mapazi 367.8 (mamita 112). Ndi mlikiti waukulu chotani nanga umene uyenera kukhala utakhalapo pamene mtengo umene’wo unalikhidwa! Chitsa ndi mizu yake yochuluka’yo inasiyidwa pansi. Tsopano tiyeni ife eni tichitire chithunzi-thunzi chitsa cha mtengo chimene’cho kukhala chiri ndi mikombero ya chitsulo ndi mkuwa yochikulunga zolimba kuchititsa kuti pasakhala mphukira iri yonse. Kwamuyaya? Ai, koma kwa zaka zikwi ziwiri kudza mazana asanu mphambu makumi awiri. Kodi chitsa chingakhalebe ndi moyo kwa utali wotero’wo? Chitsa chimene tikunena’chi chinatero. Ndipo, zitawerengedwa kuyambira pa nthawi ya kupanga kwa Nebukadinezara chilengezo chake chonena za chitsa cha mtengo umene’wuwo, zaka zikwi ziwiri kudza mazana asanu mphambu makumi awiri zimene’zo zikatha pa nthawi ina m’zaka zathu za zana la makumi awiri zino. Chabwino, pamenepa, kodi chitsa cha mtengo chimene’cho chamasulidwa m’nthawi yathu? Kodi kumene’ku kukatanthauza kanthu kali konse kwa ife lero lino? Tingathe kuona!
KULONGOSOLA KWA MFUMU MWINI’YO MONGA MOMWE KWASUNGIDWIRA
7, 8. Kodi n’chifukwa ninji Nebukadinezara anaumirizika kuuza Danieli loto lake?
7 Tiyeni choyamba tione m’mene chitsa cha mtengo chimene’cho chinaonedwera ndi wolamulira wa Ufumu wa Babulo, Ulamuliro wa Dziko Wachitatu wa ulosi wa Baibulo. Mu chilengezo chake chachifumu tikuuzidwa kuti: “Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m’nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m’chinyumba changa. Ndinaona loto lakundiopsya, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m’mtima mwanga, zinandibvuta ine. Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babulo, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa loto’li.” Ndiyeno chiani?
8 “Pamenepo anafika alembi, openda, Akasidi, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera loto’li, koma sanandidziwitsa kumasulira kwake. Koma potsirizira pake analowa pamaso panga Danieli, dzina lake ndiye Belitsazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amene’nso muli mzimu wa milungu yoyera m’mtima mwake; ndipo ndinam’fotokozera loto’li pamaso pake.”—Danieli 4:4-8.
9. M’malo mwa Danieli, kodi tiri n’chiani chotithandiza molosera?
9 Chokumana nacho cha Nebukadinezara chimasonyeza m’mene kuliri kopanda pake ndi kopusa kwa olamulira a mitundu ndi atsogoleri a ndale za dziko onse kutembenukira kwa openda nyenyezi ndi alauli ndi olankhula ndi mizimu ena kuyesa kupeza molondola chimene chiri m’tsogolo. Olamulira Sali naye lero lino mneneri Danieli koti apiteko, koma tiri ndi bukhu lolosera la Danieli. M’menemo tingaphunziremo zinthu zimene zasonyeza kale zaka zathu za zana la makumi awiri zino ndi chimene chiri m’tsogolo muno posachedwapa kaamba ka mbadwo uno. Loto la Nebukadinezara ndi kulimasulira kwa Danieli ndi m’mene linakwaniritsidwira m’njira ya fanizo monga chidindo kapena chitsimikiziritso cha phindu lake lolosera, zonse’zo m’zokondweretsa kwa ife tsopano. Chotero tiyeni tsopano timvetsere pamene Nebukadinezara akusimbira Danieli loto lake lokhala ndi kufunika kwa pa dziko lonse’lo. Iye anati:
10, 11. Kodi n’chiani chimene chinachitikira mtengo umene mfumu inauona m’loto?
10 “Masomphenya a m’mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu. Mtengo’wo unakula nulimba,ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi. Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m’menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m’mlengalenga zinafatsa m’nthambi zake, ndi nyama zonse zinadya’ko.
11 Ndinaona [Ine Mfumu Nebukadinezara] m’masomphenya a m’mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Anapfuulitsa, natero, Likhani mtengo’wo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwanzani zipatso zake, nyama zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake. Koma siyani chitsa ndi mizu yake m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; m’chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama ziri m’machire a m’dziko. Mtima wake usandulike, usakhale’nso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizim’pitire nthawi zisanu ndi ziwiri. Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyera’wo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam’mwamba-mwamba alamula mu ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.”—Danieli 4:10-17.
12. Kodi ndi mafunso otani amene akubuka ponena za kulikhidwa kwa mtengo umene’wo?
12 Malinga ndi kunena kwa kalongosoledwe kamene’ka ka loto’lo monga momwe kanaperekedwera ndi Mfumu Nebukadinezara kwa Danieli mtengo’wo unatalika kuposa mitengo ina yonse. Uwo unali kuonekera kwa onse okhala pa dziko lapansi, kotero kuti palibe ali yense amene anali wokhoza kuunyalanyaza. Uwo unali mtengo wabwino. Ngakhale kuli kwakkuti sunali kuchedwa “mtengo wa moyo,” unali mtengo wochirikiza moyo, pakuti unabala zipatso zochuluka, zokwanira kudyetsa zamoyo zonse pa dziko lapansi. Nangano, kodi n’chifukwa ninji, unayenera kukhala ngati mtengo woposa wofotokozedwa m’masomphenya a Ezekieli, chaputala cha makumi atatu mphambu chimodzi, vesi lachitatu kufikira la khumi ndi chiani, m’kulikhidwa? Kodi ndi motani m’mene thunthu la mtengo wolikhidwa’wo likanakhalira ndi “mtima” wa munthu ndipo umene’wu ndi kusinthidwira ku “mtima wonga wa nyama”? Kodi ndi motani m’mene kulikhidwa kwa mtengo’wo ndi kusiyidwa kwa thunthu lake logwetsedwa’lo kugona tantha pansi mu msipu kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri” kukatsimikizirira kuti “Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu”? Malinga ndi kunena kwa “mthenga” waungelo kapena mlonda kapena kalinde, chimene’cho ndicho chimene chinali chifuno cha kachitidwe kosonyezedwa m’loto la mfumu’lo.
KUMASULIRA KWA LOTO’LO
13, 14. (a) Kodi ndi mafunso otani amene ayenera kuyankhidwa ponena za Mulungu monga wolikha? (b) Kodi mtengo wautali’wo unaphiphiritsira yani, ndipo chifukwa ninji?
13 Kodi Wam’mwamba-mwamba’yo monga Wolamulira Wamkulu angatulutse malamulo akuti ufumu, boma, ulamuliro wa dziko, ulikhidwe ngati mtengo wautali kwambiri,ndipo kodi angakhazikitse mfumu ina ndi kuipatsa ufumu, ngakhale kuli kwakuti akuchokera mu mkhalidwe wotsika kopambana wa mtundu wa anthu?
14 Amene’wa ndiwo mafunso amene anaperekedwa kweni-kweni kwa Danieli kuti ayankhe, monga momwe Mfumu Nebukadinezara anam’funsira tsopano kaamba ka kumasulira loto la mtengo. (Danieli 4:18) Koma kodi n’chifukwa ninji Danieli anabvutika maganizo pamene Mulungu Wam’mwamba-mwamba’yo anam’bvumbulira tanthauzo la loto la mfumu, ndipo kodi n’chifukwa ninji Nebukadinezara anam’tsimikiziritsa Danieli kotero kuti asachite mantha m’kulongosola loto’lo? Chinali chifukwa chakuti, choyamba, kulikhidwa kwa mtengo waukulu’wo kunali ndi tanthauzo lachindunji kwa Nebukadinezara iye mwini. Chifukwa cha chimene’cho Danieli anafuna kuti loto lolaula limene’li likakwaniritsidwa motero pa munthu wina’nso, pa adani amene anadana ndi mfumu’yo. (Danieli 4:19) Danieli akuyankha mafunso athu’wo pamene tikumumva akunena kuti:
15-17. (a) Kodi ndi mtima wa yani umene ukanasinthidwa kuchoka ku wa munthu kukhala ngati wa nyama? (b) Kodi ndi motani m’mene Nebukadinezara akanabvutikira ndi kululuzika kotero’ko?
15 “Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera pa dziko lonse lapansi, . . . ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.”—Danieli 4:20-22.
16 Chotero mtengo wautali kufikira kumwamba umene’wo unaimira ulamuliro, ulamuliro wa pa dziko lonse monga momwe unaperekedwera kwa munthu wina monga wolamulira. Anali wolamulira amene’yu amene anali ndi “mtima” umene ukasinthidwa kuchoka ku uja wa munthu kukhala uja wa nyama. Kusintha kotero’ko kukatanthauza kugwa, kululuzika, kodi si choncho? Kululuzika kumene’ku kunali kogwirizana ndi chifuniro ndi chifuno cha Mulungu Wam’mwamba-mwamba, ‘Wolamulira mu ufumu wa anthu,’ pakuti Danieli anapitirizabe kunena ndi Nebukadinezara kuti:
17 “Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengo’wo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nichikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitam’pitirira nthawi zisanu ndi ziwiri; kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam’mwamba-mwamba chadzera mbuye wanga mfumu: kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng’ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mum’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.”—Danieli 4:23-25.
18. Kodi ndi m’tsogolo mowala motani m’mene Danieli anapereka ku loto’lo?
18 Komabe, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zitapitira mfumu mu mkhalidwe woluluzika umene’wo, ndiyeno chiani? Loto la nebukadinezara silinayankhe mwachindunji funso limene’li, koma kumasulira kwa Danieli kunayankha. Posonyeza mbali yokondweretsa ya loto’lo, Danieli anati kwa mfumu: “Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphamwi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.”—Danieli 4:26, 27.
19. (a) Kodi ndi motani ndipo ndi liti pamene loto’lo linayamba kukwaniritsidwa pa mfumu’yo? (b) Kodi n’chifukwa ninji mpando wachifumu’wo unasungidwa kuti iye adzaukhale’nso?
19 Mosasamala kanthu za uphungu wolimba mtima wa Danieli, Nebukadinezara anapitirizabe kukhala wonyada chifukwa cha kukhala mfumu yokha ya Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, Ulamuliro wa Dziko Wachitatu wa ulosi wa Baibulo. Chotero, chaka cha mwezi wokhala chotsatirapo chinam’peza akuyenda pa chindwi pa nyumba yake yachifumu pa Babulo. Ndiyeno, monga momwe Danieli iye mwini akutiuzira, “Mfumu inanena, niti, Suyu Babulo wamkulu ndinam’manga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uonekere ulemerero wa chifumu changa? Akali m’kamwa mwa mfumu mau awa, anam’gwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe ufumu wakuchokera. Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng’ombe; nizidzakupitirira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.”—Danieli 4:28-32.
CHITSANZO CHOLOSERA CHA CHENI-CHENI
20-22. Kodi ndi motani m’mene wolamulira wa dziko’yo anasandukira kuchoka ku kukhala munthu kumka ku kukhala ngati nyama?
20 Chimene chinachitika tsopano chinali chitsanzo cholosera cha cheni-cheni chachikulu kopambana. Chotero loto la Nebukadinezara linayamba kukwaniritsidwa kwake mwa munthu wokhala ndi ulamuliro wa pa dziko lonse.
21 Ndiko kuti, “mtengo” waukulu kwambiri wophiphiritsira’wo unakhapidwa ndi kugwa tantha pa dziko lapansi. Chitsa chokha, ‘tsinde,’ chinasiyidwa chiripo, koma chinamangidwa ndi mikombero ya chitsulo ndi mkuwa kuuletsa kumera mphukira kwa utali wa “nthawi zisanu ndi ziwiri” zolengezedwa’zo. Kweni-kweni, Nebukadinezara wamphamvu’yo anatsika pa mpando wake wachifumu wa ulamuliro. “Wolamulira m’ufumu wa anthu” anaumiriza zimene’zi mwa kuchititsa misala mfumu ya Babulo, kusintha mtima wake kuchoka ku uja wa munthu wamphamvu mu ulamuliro kukhala uja wa nyama, nkhunzi yodya udzu m’chire. Mwina mwake akulu-akulu a mphala ya Mfumu Nebukadinezara anakumbukira loto ndi kumasulira kwa Danieli ndipo anaopa kulowetsa wina wake m’malo mwake pa mpando wachifumu. Koma Mulungu Wam’mwamba-mwamba anali kweni-kweni uyo amene anali kusunga mpando wachifumu wa ulamuliro’wo kaamba ka Nebukadinezara kuti adzabwezeretsedwepo pa mapeto a “nthawi zisanu ndi ziwiri” zoikidwiratu.—Danieli 5:18-21.
22 Zinthu zinayenda monga momwe’di mau amene anachokera kumwamba anali atanenera kwa wolamulira wa dziko wonyada’yo kuti: “Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kum’chotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng’ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame.”—Danieli 4:33; yerekezerani ndi Machitidwe 12:21-23.
23. Kodi n’chifukwa ninji kudwala kwa mfumu sikunatanthauze kugwa kwa Babulo?
23 Kodi kululuzidwa kwa Mfumu Nebukadinezara kumene’ku kunatanthauza kugwa kwa Ufumu wa Babulo? Kutali-tali! Malinga ndi kunena kwa chilengezo cha Mulungu Wam’mwamba-mwamba ufumu umene’wu unayenera kupitirizabe kwa zaka zina makumi ochuluka monga Ulamuliro wa Dziko Wachitatu, umene tsopano unalingana ndi tsinde lomangidwa ndi mkombero la mtengo waukulu kwambiri woonedwa m’loto la Nebukadinezara. Mneneri Danieli anapitirizabe monga mtumiki wa mfumu yopenga’yo, iye anatumikira monga “wolamuliro chigawo chonse cha ulamuliro wa Babulo ndi kazembe wamkulu pa amuna anzeru a Babulo.” Ndipo’nso, atsamwali a Danieli atatu Achihebri, Hananiya, Misaeli ndi Azariya, anapitirizabe kukhala ndi mbali m’kuyendetsedwa kwa zinthu za chigawo cha ulamuliro umene’wo. (Danieli 1:11-19; 2:48, 49; 3:30) Ndithudi andende Achiyuda ochuka anai amene’wa m’Babulo anali kuwerengera nthawi ya kudwala kwa mfumu ndipo anali kuyembekezera nthawi ya kulandira’nso kwake mpando wachifumu atachira misala monga mfumu ya Amitundu imene yaphunzira bwino phunziro lakuti “Wam’mwamba-mwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.” Pa mapeto a “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimene’zi zinachitika.
24. Itachira kodi mfumu’yo idanenanji ponena za Wam’mwamba-mwamba?
24 Mfumu’yo ikutiuza yokha zimene zinachitika: “Atatha masiku awa tsono, Ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam’mwamba-mwamba, ndi kum’yamika ndi kum’chitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwo mibadwo; ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m’khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye Muchitanji?”—Danieli 4:34, 35.
25. Chotero kodi ndi chimasuko chotani chimene chitsa cha mtengo’wo chinakhala nacho pa nthawi imene’yo?
25 Pa nthawi imene’yo, monga momwe loto lolosera’lo likunenera za Nebukadinezara iye mwini, mikombero ya chitsulo ndi mkuwa yomangidwa pa tsinde la mtengo waukulu kwambiri’wo inadulidwa ndi kuchotsedwa. “Nthawi zisanu ndi ziwiri” zeni-zeni zinakwanira, ndipo panali kukwanira kwa nthawi ya kubwezeretsedwa ku ulamuliro kwa mfumu ya misala’yo. Nebukadinezara akusimba zimene’zi, pamene iye akupitiriza kunena kuti: “Nthawi yomweyo nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uoneke’nso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika mu ufumu wanga, Iye nandionjezera’nso ukulu wochuluka.” (Danieli 4:36) Ha, ndi “chizindikiro cha kuchiritsa” chotani nanga chimene motero chinachitidwa ndi Mulungu Wam’mwamba-mwamba’yo!—Danieli 4:2; Machitidwe 4:22.
26. Kodi ndi Ahebri ati mosakaikira anagwirizana nawo m’kufuna-funa mfumu, ndipo chifukwa ninji?
26 Kukaonekera kukhala koyenera kwambiri kuti Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya monga “mandoda” ayenera kukhala anali pakati pa awo amene anafuna-funa mfumu yobwezeretsedwa’yo monga chizindikiro cha kukhulupirika kwao kwa iye ndi cha kukhala kwao atatezera zabwino za ufumu wake m’kati mwa kudwala kwake misala. (Yerekezerani ndi 2 Samueli 19:11-15.) Alambiri anai a Yehova Mulungu amene’wa akakhala kweni-kweni okondweretsedwa ndi chiyambukiro cha chokumana nacho cha mfumu choluluza pa iye chochititsidwa ndi Mulungu wao. Koposa ena onse ogwirira ntchito mfumu, iwo anazindikira kubvomereza kwa Nebukadinezara Ulamuliro wa m’Chilengedwe chonse wa “Wolamulira” Wam’mwamba-mwamba amene Nebukadinezara anam’cha “Mfumu ya kumwamba,” yolamulira kosatha. Iwo anaona m’mene Mfumu yakumwamba imene’yi inabwezerera ufumu kwa munthu amene kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri” anali ‘wotsika kopambana wa anthu’ m’kutsitsidwa koposa mkhalidwe wa anthu kufika pa uja wa nyama ya kuthengo. (Danieli 4:17) Iwo anazindikira zimene Yehova anali kuchita!
“NTHAWI ZISANU NDI ZIWIRI”
27. Kodi “nthawi zisanu ndi ziwiri” kwa nthawi yaitali zalingaliridwa kukhala nthawi yaitali motani?
27 Kodi kweni-kweni “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimene’zo m’kati mwa zimene Nebukadinezara anali wosonkonezeka maganizo ndi wopangitsidwa kukhala wopanda mphamvu kaamba ka ulamuliro wachifumu zikakhala za utali wotani? M’bukhu la mbiri lochedwa “Antiquities of the Jews,” lotulutsidwa m’Chigriki cha m’zaka za zana loyamba ndi Myuda. Flavius Josephus, iye analingalira “nthawi zisanu ndi ziwiri” kukhala “zaka zisanu ndi ziwiri.” (Bukhu X, Chaputala X, ndime 6) M’zaka za zana lotsatirapo wotembenuza Wachigriki wa bukhu la Danieli, ndiko kuti, Theodotion, wa ku Ponto, Asia Minor, pakati pa chaka cha 180 ndi 182 C.E., anatembenuza mau Achihebri’wo kukhala “zaka zisanu ndi ziwiri” (hepta ete). Ochitira ndemanga ena Achiyuda amamva “nthawi” pano kukhala zikutanthauza “zaka.” Kunena zoona, otembenuza angapo amakono amawatembenuza motere. The New American Bible (Lachiroma Katolika) limati: “Kufikira zitatha zaka zisanu ndi ziwiri.” (Danieli 4:13, 20, 22, 29, NA) Mofananamo, A New World Translation lolembedwa ndi James Moffatt ndi The Complete Bible-An American Translation limati “zaka zisanu ndi ziwiri.” (Ndipo’nso Good News Bible, la 1976)
28. Ponena za mfumu’yo kodi zaka’zo zinali za kuwerengera kwa yani?
28 Chotero, zaka za mwezi wokhala za Baibulo zikakhala zikutanthauzidwa, popeza kuti lamulo la nthawi’lo linali lochokera kwa Woyambitsa Baibulo Loyera, Yehova Mulungu. Zolembedwa zakale zikusimbidwa kukhala zikusonyeza kuti panali zaka zingapo m’zimene Nebukadinezara sanachite kanthu kali konse. Zaka zimene’zi zingachitikire pamodzi bwino lomwe ndi “nthawi zisanu ndi ziwiri” za kukhala kwake wosagwira ntchito monga munthu wosonkonezeka maganizo.
29. Kodi chifuno chokwanira cha loto’lo chinakwaniritsidwa ponena za mfumu’yo?
29 Komabe, kodi ndi zokha’zo zimene ziripo ku nkhani’yo? Palibe maziko a chikaikiro ponena za kuti loto la Nebukadinezara limene’lo lonena za mtengo wautali kufikira kumwmba linali lolosera, iro pokhala louziridwa ndi Yehova Mulungu. Koma kodi kukwaniritsidwa kwa loto’lo kuli kolekezara ku kukwaniritsidwa kwakale kokha kumene’ko pa munthu mmodzi yekha, Mfumu nebukadinezara, kuti aphunzire phunziro lonena za ulamuliro? Kodi ndiko kupyolera mwa chokumana nacho cha iye mwini kuti chifuno cha kachitidwe ka Yehova ndi iye chimachitidwa, ndiko kuti, “kuti amoyo adziwe kuti Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu”? (Danieli 4:17) Mwa kukhazikitsa pa ufumu wa anthu “wolubukira anthu” kodi Mulungu Wam’mwamba-mwamba’yo akukhazikitsa pa anthu ulamuliro wotsika kopambana? Mwachionekere ai! (Danieli 4:36, 37) Kwa “amoyo” m’zaka zathu za zana la makumi awiri zoopsya zino, loto la Nebukadinezara liyenera kukhala ndi kukwaniritsidwa kwina ndi kokhala ndi zambiri zolowetsedwamo. Liri nako’di!
30. Kodi ndi motani m’mene mtengo’wo ukuphiphiritsirira ulamuliro wa m’chilengedwe chonse wa Yehova?
30 Maumboni akale akutsimikizira kukwaniritsidwa koyambirira kwa loto la mfumu ya Babulo. Kodi ndi motani m’mene maumboni a pambuyo pake akutsimikizirira kukwaniritsidwa kokulira ndi kotheratu kwa loto limodzi-modzi’lo? Eya, Nebukadinezara, amene pa nthawi imene’yo kale’lo anaphiphiritsiridwa ndi mtengo waukulu kwambiri, anali wolamulira wa Ufumu wa Babulo. Chotero iye anaphiphiritsira ulamuliro wa pa dziko lonse, wokhala ndi kudziwidwa kwa pa dziko lonse. Mofananamo, “mtengo” umene unasonyezedwa ndi iye unaimira ulamuliro waukulu kwambiri koposa uja umene unali ndi mfumu ya Babulo. Pa nthawi imene’yo, kodi ndi ulamuliro kapena ufumu uti umene unali waukulu kwambiri koposa uja wa Mfumu Nebukadinezara, umene unalibe wopikitsana nawo pa dziko lapansi? Ulamuliro wokha wa uyo amene Nebukadinezara anam’bvomereza kukhala “Wam’mwamba-mwamba,” “Mfumu ya kumwamba.” (Danieli 4:34, 37) Chifukwa cha chimene’cho, mtengo wautali kufikira kumwamba wochirikiza moyo wa loto la Nebukadinezara umene’wo unali kuimira ULAMULIRO WA M’CHILENGEDWE CHAPONSE-PONSE wa Wam’mwamba-mwamba, Yehova Mulungu, maka-maka m’kugwirizana kwake ndi dziko lathu lapansi’li. Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chaponse-ponse umene’wu uli wamuyaya, “wokhala chikhalire,” kwa mibadwo yonse.
31. Kodi tanthauzo lotero’lo loperekedwa ku mtengo’wo limadzutsa mafunso otani?
31 Tanthauzo lotero’lo logwirizanitsidwa ndi “mtengo” limadzutsa mafunso m’maganizo mwathu, kodi si choncho? Inde. Mwa chitsanzo, kodi ndi motani m’mene “mtengo” wotero’wo ukalikhidwira? Ndipo kumene’ku molamulidwa ndi Mfumu ya m’Chilengedwe Chaponse-ponse, Mulungu Wam’mwamba-mwamba iye mwini? Kodi ndi motani m’mene ukukhazikitsidwira kachiwiri’nso? Mau olembedwa a Mulungu, Baibulo Loyera, amalongosola.
32, 33. Kodi ndi motani m’mene ufumu wa Davide unaimirira ulamuliro wa Mulungu?
32 Kwa nyengo ya nthawi yaitali Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse wa Yehova unali kuimiridwa pano pa dziko lapansi. Motani? Kuti? Liti? Kumene’ku kunali mwa njira ya ufumu umene iye anakhazikitsa pa anthu ake osankhidwa, mafuko khumi ndi awiri a Israyeli. Maka-maka zimene’zi zinali choncho pamene wodzozedwa wa Yehova, Mfumu Davide, anapangidwa kukhala mfumu pa mafuko onse khumi ndi awiri a Israyeli, amene pambuyo pake anasamutsira mzinda wake wa malikulu pa Yerusalemu, umene iye anaulanda kuchokera kwa Ayebusi achikunja. M’menemotu munali mu 1070 B.C.E.
33 M’chaka chimodzi-modzi’cho Mfumu Davide anachititsa kuti Likasa lopatulika la Chipangano cha Yehova lisamutsidwire ku mzinda’wo ndi kuikidwa m’hema wokhomedwa pafupi ndi nyumba yake yachifumu. Motero, kunena kwake titero, Yehova anayamba kulamulira mu Israyeli pa maliklu a Israyeli Yerusalemu, ndipo mfumu ya Israyeli inanenedwa kukhala ikukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova.” (1 Mbiri 29:23; 16:1-31) Mobwereza-bwereza Mfumu Davide anabvomereza Yehova kukhala Mfumu yake yakumwamba, Wolamulira weni-weni wa Israyeli. (Salmo 5:2; 24:7-10; 68:24; 145:1) Pamenepa, ndithudi, ufumu wokhazikika pa Yerusalemu wokhala ndi Davide ndi mbadwa zake zachifumu zokhala pamenepo pa “mpando wachifumu unaimira Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse wa Yehova ponena za dziko lathu lapansi’li.—2 Mbiri 13:5, 8.
34. Kodi ndi liti pamene mtengo wophiphiritsira umene’wo unalikhidwa, ndipo motani?
34 Moyenerera kusonyezedwa kwa Ulamuliro wa Yehova wa m‘Chilengedwe Chonse kumene’ko monga momwe kunachitidwira kupyolera mwa Mfumu Davide ndi olowa m’malo ake achifumu pa Yerusalemu kunali kumene kunaphiphiritsiridwa ndi mtengo waukulu kwambiri’wo woonedwa m’loto la Nebukadinezara. M’loto’lo, mtengo woposa yonse umene’wo unalikhidwa. Mogwirizana ndi loto’lo, Ulamuliro wa Mulungu monga momwe unasonyezedwera mwa mzera wa mafumu a Davide pa Yerusalemu unalikhidwa, kugwetsedwa, kusiyitsidwa kugwira ntchito. Liti? Mu 607 B.C.E., pamene Nebukadinezara wa ku Babulo anadzetsa chionongeko pa Yerusalemu ndi kachisi wake ndi kutenga mfumu yake yotsirizira yokhazikitsidwa pa mpando wachifumu, Zedekiya wa banja la Davide, kumka ku ukapolo kukafera kumene’ko. Yehova iye mwini anachititsa kuti mtengo wophiphiritsira’wo ulikhidwe, pakuti iye mwini anagwiritsira ntchito Nebukadinezara monga “mtumiki” wake kuchititsa kugubuduzidwa kumene’ku. Yehova iye mwini anachititsa kusintha kusonyezedwa kwa ulamuliro wake kumene’ku kulinga ku dziko lathu lapansi’li.—Yeremiya 25:8-11, 17-29; Ezekieli 21:22-27.
35. Kodi chitsa cha mtengo’wo chinamangidwa ndi mikombero ya chitsulo kaamba ka chifuno chotani?
35 Pa nthawi imene’yo mikombero ya kuletsa kwaumulungu monga momwe inaphiphiritsiridwira ndi mikombero yachitsulo ndi ya mkuwa inakulungidwa pa tsinde la ulamuliro waumulungu monga momwe umasonyezedwera kupyolera mwa mbadwa yachifumu ya Mfumu Davide. Palibe mphukira yachifumu imene ikaphuka kuchokera patsinde limene’li kaamba ka kuphuka’nso kwa ulamuliro waumulungu wochitidwa kupyolera mwa mfumu Yaudavide. Kodi mkhalidwe woluluzika wa Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse wa Yehova umene’wu ukapitirizabe kwa utali wotani? Kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri,” zimene zinasonyezedwa molosera ndi “zaka zisanu ndi ziwiri” za kuchotsedwa pa mpando wachifumu kwa Nebukadinezara kuti iye akakhale ngati nyama yakuthengo. Chotero, kodi “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimalowetsamo nthawi yochuluka motani?
36. Kodi n’chifukwa ninji “nthawi zisanu ndi ziwiri’zo” sizikatanthauza masiku 2,520 eni-eni?
36 “Nthawi” kapena “chaka” cha mwezi wokhala yogwiritsiridwa ntchito mogwirizana ndi ulosi wa Baibulo imakhala ndi masiku okwanira 360, ndiko kuti, miyezi khumi ndi iwiri ya mwezi wokhala wa masiku okwanira 30 uli wonse. (Yerekezerani ndi Genesis 7:11 mpaka 8:4.) “Nthawi zisanu ndi ziwiri” kapena “zaka zisanu ndi ziwiri” chifukwa cha chimene’cho zikakhala masiku 360 kuchulukitsa ndi 7, kapena masiku 2,520. Kodi masiku 2,520 amene’wo ayenera kungomvedwa monga momwe alirimu m’nkhani imene’yi? Eya, zaka zisanu ndi ziwiri za mwezi wokhala kapena masiku 2,520 pambuyo pa chionongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. ndi kusiyidwa kwa dziko lake lolamulidwa naye m’dziko la Yuda liri labwinja, Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse wa Yehova ponena za dziko lapansi sunakhazikitsidwe’nso, kodi si choncho? Ai! M’chaka cha 600 B.C.E. Aisrayeli opulumuka anali chikhalirebe mu ukapolo m’Babulo, Yerusalemu ndi dziko la Yuda anali chikhalirebe bwinja, ndipo Ufumu wa Babulo unali chikhalirebe ulamuliro wa dziko lonse m’nthawi’yo. Sizinachitike mpaka zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zitatu pambuyo pake, kapena mu 537 B.C.E., kuti Aisrayeli okhalitsidwa akapolo’wo anapatsidwa ufulu ndi wogonjetsa Babulo kuchoka, ndi kukakhala’nso m’dziko lakwao lokondedwa’lo. Komabe, ngakhale zinali choncho, ufumu waumulungu wa banja la Davide sunakhazikitsidwe’nso pa Yerusalemu.
37. Kodi ndi kutsatana-tsatana kotani kwa maulamuliro a dziko kumene kukuyambirira ufumu wa Mulungu?
37 Ufumu wa Amedi ndi Aperisi tsopano unatenga ulamuliro wa dziko lonse monga Ulamuliro wa Dziko Wachinai wa ulosi wa Baibulo, ndipo Koresi Wamkulu, Mperisi, anali mfumu. Chotero Zerubabele, wolowa nyumba walamulo ndi wachibadwidwe wa mpando wachifumu wa Davide, anangopangidwa kukhala bwanamkubwa wa chigawo cha Perisiya cha Yuda. Amedi ndi Aperisi anafanana ndi zifuwa ndi mikono ya siliva ya fano lachitsulo loonedwa m’loto louziridwa limene mneneri Danieli anayenera kukumbutsa Nebukadinezara ndi kum’masulira. (Danieli 2:31, 32, 39) Malinga ndi kunena kwa loto lofanana’lo ndi kumasulira kwake, ulamuliro wa dziko wa Amitundu unayenera kuchitidwa kena’ko ndi Ulamuliro wa Dziko wonga mkuwa wa Grisi ndiyeno kenako ndi Ufumu Wachiroma wonga chitsulo limodzi ndi mphukira yake yochokera pamenepo mu mpangidwe wa Ulamuliro Wauwiri wa Britain ndi Amereka wa zaka za mazana a makono. Choyamba, pambuyo pake, Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse wa Yehova (monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi phiri) ndi ufumu (wophiphiritsiridwa ndi mwala wosemedwa) ukadodometsa mzera wa maulamuliro a dziko a Amitundu. (Danieli 2:32-35, 44, 45) Zimene’zi zikutifikitsa ku zaka zathu za zana la makumi awiri!
38. Kodi ndi liti pamene masiku 2,520, onedwa mophiphiritsira’wo, akatha?
38 Chifukwa cha chimene’cho, kuli koonekera bwino kwambiri, kuti “nthawi zisanu ndi ziwiri” za masiku 2,520, poyerekezeredwa ndi “fano” la maulamuliro a dziko, kuchokera kumutu kufikira ku mapazi, ziyenera kuimira kanthu kena kotalikirapo koposa zaka zeni-zeni zisanu ndi ziwiri za mkhalidwe wonga chinyama wa Nebukadinezara, kuthengo. Chotero liri lonse la masiku 2,520 amene’wa liyenera kuonedwa mogwirizana ndi lamulo la Baibulo lochitira zinthu lakuti: “Tsiku limodzi kuliyesa chaka, tsiku limodzi kuliyesa chaka, ndiko kumene ndakupatsa.” (Ezekieli 4:6, NW; yerekezerani ndi Numeri 14:34.) Chimene’chi chikatanthauza kuti “nthawi zisanu ndi ziwiri” za kulamuliridwa kwa dziko lapansi ndi maulamuliro a dziko a Akunja popanda chidodometso chochokera ku ufumu wa Mulungu zikakhala za utali wa zaka 2,520 kuyambira pa kupasulidwa kwa dziko la Yuda (kuphatikizapo Yerusalemu ) kochitidwa ndi Ababulo. Chiwerengero cha zaka chimene’cho choyambira pakati—kati pa mwezi wokhala wachisanu ndi chiwiri (kapena Tishri 15) wa 607 B.C.E. chikutifikitsa ife pati? Ku Tishri 15, kapena October 4/5, wa 1914. C.E.
39. Kodi n’chiani chimene chinatsatira kuchotsedwa kwa mikombero pa chitsa cha mtengo’wo?
39 Pa nthawi imene Yehova Mulungu Wamphamvuyonse akamasula mikombero ya chitsulo ndi mkuwa yozengenezedwa pa chitsa chokhala ndi mitsitsi chophiphiritsira’cho cha Ulamuliro wa m’Chilengedwe Chonse. Motero iye akalola “mphukira’ yaufumu kuphuka kuchokera mu icho kaamba ka kukhazikitsidwa kwa Ulamuliro Wake wa m’Chilengedwe Chonse kulinga ku dziko lonse lapansi. (Yobu 14:7-9; Yesaya 11:1, 2) Zimene’zi zinachitika m’kubadwa kwa “mwana wa boma la mwamuna, lonenedweratu m’Chibvumbulutso 12:5-10 (AV; NW), boma limene linayenera “kuweta mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.” M’loto la Nebukadinezara la “fano” la maulamuliro a dziko, chochitika chimene’chi chinaphiphiritsidwa ndi kusemedwa kwa “mwala” m’phiri ndi cholinga cha kuononga “fano” la maulamuliro a dziko. (Danieli 2:34, 35) Ha, ndi njira yatanthauzo yotani nanga m’mene imene’yo inaliri yosonyezera mapeto a “nthawi zoikidwiratu za amitundu,” mapeto a “nthawi za Akunja,” monga momwe zinanenedweratu ndi Yesu Kristu mu Luka 21:24!—NW; AV.
40. Kodi ndi kupondereza kochitidwa ndi maulamuliro a dziko a Akunja kotani kumene kunayenera kulekeka pa nthawi’yo?
40 Kuyambira pa nthawi imene’yo kumkbe m’tsogolo, boma laufumu limene linaimiridwa ndi Yerusalemu wakale pansi pa ufumu wa banja lachifumu la Davide silinayenera “kuponderezedwa,” “kutsenderezedwa,” ndi maulamuliro a dziko Achikunja. Uwo unayenera kuwapondereza!
41. Kodi ndi kubwezeretsedwa koposa kwa Nebukadinezara kotani kumene Mulungu anakuneneratu?
41 Polingalira zonse zapita’zo, Wolamulira wa m’Chilengedwe chonse, amene amadziwa mapeto kuyambira pa chiyambi, ananeneneratu yoposa nthawi ya Nebukadinezara chabe kuti idzabwezeretsedwa ku mpando wachifumu wa Ulamuliro wa Dziko wa Ababulo. Yehova Mulungu ananeneneratu, pa nthawi imodzi-modzi’yo, nthawi ya kulimbikitsa ulamuliro wa dziko wa iye mwini mwa kutsimikizira’nso Ulamuliro wake woyenerera wa m’Chilengedwe cha Ponse-ponse kulinga ku dziko lathu lapansi. Pokhala atatsimikizira nthawi ya umene’wu, tsopano tiri mu mkhalidwe wabwino wolingalira Woimira Wamkulu amene Mfumu ya m’Chilengedwe Chonse Yehova akum’gwiritsira ntchito kaamba ka zimene’zi. Kodi titero?