Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 62 tsamba 148-tsamba 149 ndime 1
  • Ufumu Wofanana ndi Mtengo Waukulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu Wofanana ndi Mtengo Waukulu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kuvumbula Chinsinsi cha Mtengo Waukulu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Kuneneratu Nthawi ya Ulamuliro wa Dziko
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Pamene Yehova Anaphunzitsa Mafumu Maphunziro
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 62 tsamba 148-tsamba 149 ndime 1
Mtengo umene Nebukadinezara analota ukugwetsedwa

MUTU 62

Ufumu Wofanana ndi Mtengo Waukulu

Tsiku lina Nebukadinezara analota maloto oopsa. Ndiyeno anaitana anthu anzeru a mu ufumu wake kuti amuuze tanthauzo lake. Koma palibe amene anakwanitsa kumasulira malotowo. Kenako Nebukadinezara anauza Danieli maloto akewo.

Anamufotokozera kuti: ‘Ndinalota mtengo womwe unakula kwambiri n’kufika kumwamba. Umaoneka padziko lonse ndipo unali ndi masamba okongola komanso zipatso zambiri. Nyama zakutchire zimakhala mumthunzi wake komanso mbalame zimamanga zisa munthambi zake. Kenako mngelo anabwera kuchokera kumwamba n’kufuula kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo mudule nthambi zake. Koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo komanso wakopa. Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu nʼkukhala mtima wa nyama ndipo padutse nthawi zokwana 7. Anthu adziwe kuti Mulungu ndi Wolamulira ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.”’

Yehova anathandiza Danieli kuti adziwe zimene malotowa ankatanthauza. Danieli anachita mantha ndi tanthauzo la malotowo. Anauza Nebukadinezara kuti: ‘Mfumu, malotowa akunena za inu. Koma zikanakhala bwino akanakhala kuti akunena za adani anu. Mtengo waukulu umene unadulidwawo ukuimira inuyo. Mudzasiya kukhala mfumu ndipo mudzapita kutchire n’kumakadya msipu ngati nyama yakutchire. Koma popeza mngelo ananena kuti chitsa cha mtengowo chisazulidwe, ndiye kuti mudzabwereranso n’kukhala mfumu.’

Patatha chaka, tsiku lina Nebukadinezara ankayenda padenga la nyumba yake n’kumaona zinthu zikuluzikulu zimene anachita mu ufumu wake. Iye anati: ‘Koma ndiye zinthu zikundiyendera bwino. Taonani mmene mzinda wa Babulo ukukongolera!’ Koma mawu ake adakali m’kamwa, anamva mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Nebukadinezara! Ufumu wachoka m’manja mwako.’

Nthawi yomweyo Nebukadinezara anachita misala ndipo anakhala ngati nyama yakutchire. Anachoka kunyumba yake yachifumu n’kumakakhala kutchire ndi nyama. Tsitsi lake linatalika ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.

Patatha zaka 7, Nebukadinezara anachira ndipo Yehova anamuikanso kukhala mfumu ya Babulo. Kenako iye anati: ‘Ndikutamanda Yehova, Mfumu yakumwamba. Panopa ndadziwa kuti iye ndi Wolamulira. Amatsitsa anthu odzikweza ndipo angathe kupereka ufumu kwa aliyense amene akufuna.’

“Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke, ndipo mtima wodzikuza umachititsa kuti munthu apunthwe.”​—Miyambo 16:18

Mafunso: Kodi maloto a Nebukadinezara ankatanthauza chiyani? Kodi Nebukadinezara ananena kuti waphunzira chiyani zokhudza Yehova?

Danieli 4:1-37

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena