Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bw mutu 1 tsamba 4-14
  • Kupanga Chosankha Choyenera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupanga Chosankha Choyenera
  • Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHITHANDIZO M’KUPEZA NJIRA
  • MAPINDU AMENE AMACHOKERA M’MOYO WOTEROWO
  • CHIYEMBEKEZO CHABWINO KOPAMBANA CHA M’TSOGOLO
  • NTHAWI YA KUSANKHA
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Zimene Ubatizo Wanu Umatanthauza
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Chimene Muyenera Kuchita Kuchita kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Khalani ndi Moyo Moyembekezera Kukwaniritsidwa kwa Lonjezo
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
Onani Zambiri
Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
bw mutu 1 tsamba 4-14

Mutu 1

Kupanga Chosankha Choyenera

1. Kodi ndi njira ya moyo yotani imene ikakhala yokhutiritsa kwenikweni?

MOYO wokhala ndi tanthauzo lenileni—ha, ndi wokhutiritsa chotani nanga mmene ungakhalire! Ndipo makamaka ngati uli ndi lonjezo la mtsogolo mosungika ndi mwachimwemwe. Kodi ife enife tingasankhe njira ya moyo yoteroyo? Pali chifukwa chabwino chokhulupiririra kuti tingathe.

2. Ponena za moyo, kodi nchifukwa ninji pali kufulumira ponenza za kupanga chosankha choyenera?

2 Komabe, nkofunika kwambiri, kupanga chosankha chimenecho mosazengereza. Choyamba, utali wa moyo wathu waumunthu kwakukulukulu umangotenga zaka makumi owerengeka, ndipo uli ndi zosatsimikizirika zambiri. Kodi ndani amene angadalire pa kukhala wokhoza kuononga zaka zambiri kuyesa choyamba njira iyi ya moyo ndiyeno kenako iyo, akumayembekezera potsirizira pake kupeza njira yabwino koposa? Zosankha zopangidwa zingaonekere kukhala zabwino—pa nthawiyo. Koma kodi ndi kangati pamene timamva kukunenedwa kuti: ‘Ngati kukanakhala kotheka kuzibwerezanso’? Si zokhazi, koma pali chifukwa chokhulupiririra kuti nthawi ndi yochepera mtundu wa anthu wonse yoti apeze njira ya kupanga chosankha choyenera.

CHITHANDIZO M’KUPEZA NJIRA

3. Kodi ndani amene angatiuze za chimene chimapangitsa moyo kukhala watanthauzo kwenikweni, ndipo chifukwa ninji?

3 Pamenepotu, funso ndiro lakuti, kodi ndani amene angatiuze chimene chingapangitsedi moyo wathu kukhala watanthauzo kweni—kweni? Kodi ndani amene angatisonyeze njira imene sidzachititsa malingaliro a chisoni, iyo imene motsimikizirika idzatsimikiziritsa m’tsogolo mwachimwemwe, mosungika? Moyenerera, kodi sayenera kukhala Uyo amene analenga mtundu wa anthu? Ndithudi Mlengi wathu amadziwa njira ya moyo imene iri yabwino kopambana kwa ife. Ndipo amaibvumbula kwa ife m’Mawu make olembedwa. Koma iye samatikakamiza kuitsatira. M’malo mwake, iye mokondweretsa amapempha anthu a mafuko onse kupanga chosankha chanzeru.

4. Kodi ndi motani mmene Mlengi walimbikitsira anthu kupanga chosankha chanzeru ponena za moyo wao?

4 Zaka mazana ambiri zapitazo, iye anayamba kugwiritsira ntchito amuna ndi akazi odzipereka ndi opanda dyera kupanga chisonkhezero chimenechi. Chitsanzo chake cha iye mwini cha kuolowa manja cha kupereka zonse zimene zikufunika kaamba ka moyo chimaonjeza mphamvu ku kudandaulira kwake. Mulungu alidi wokondweretsedwa nafe—tonsefe-ndipo ali chire kutithandiza. Zimenezi zinamveketsedwa m’mawu ouziridwa awa a mtumwi Paulo onenedwa kwa anthu a mu Atene wakale:

“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja; satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu . . . kuti afunefune. Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuyimba anu ati, Pakuti ifenso tiri mbadwa zake.”—Machitidwe 17:​24-28.

5, 6. Kodi ndi zosankha zotani zimene zaikidwa pamaso pa mtundu wa anthu?

5 Monga “ana” a Mlengi wathu, kodi ife tonse tikuyang’anizana ndi chosankha chotani? Mawu opitirizabe a nkhani youziridwa akuchisonyeza, kuti:

“Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu. Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitisimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.” (Machitidwe 17:29-31)

Mogwirizana ndi zimenezi, pali kwakukulukulu zosankha ziwiri zokha: Anthu angasankhe kutembenukira kwa Wam’mwambamwambayo ndi kugonjera ku chifuniro chake; kapena iwo angathe kusankha kupitirizabe kukhala ndi moyo umene umanyalanyaza iye ndi zitsogozo zake zokhalira ndi moyo wachimwemwe. Kodi kutembenukira kwathu kwa Mulungu kukaphatizikizamo chiyani?

6 Chofunika kopambana, kumaphatikizamo kulandira uyo amene iye ‘anapangiratu kuweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.’ Ameneyu ndiye Mwana wake, amene pa dziko lapansi, anali ndi dzina lakuti Yesu. (Yohane 5:22,27) Chifukwa ninji iye? Chifukwa chakuti anthu mosakanika ali mu ukapolo, mu nsinga ku kupanda ungwiro, uchimo ndi imfa, ndipo uyu anatsimikizira kukhala Mesiya kapena Kristu woyembekezeredwa kwa nthawi yaitaliyo amene Wam’mwambamwambayo akulinganiza kumgwiritsira ntchito kudzetsa chimasuko ku ukapolo umenewo.—Yesaya 53:7-12.

7. Kodi ndi motani m’mene Yesu Kristu akulowetsedwera m’kusankha kwa munthu njira yabwino koposa ya moyo?

7 Nazi zimene cholembedwa cha Baibulo chimasonyeza: M’ngululu ya 33 C.E., Yesu anafera pa mtengo wozunzirapo. Imfa yake inapereka nsembe yofunikayo kuti itetezere machimo athu. (1 Petro 2:24; 1 Yohane 2:2) Masiku makumi anai ataukitsidwa kwa akufa, iye anakwera kumwamba, kumeneko kukapereka mtengo wa nsembe yake kwa Atate. Kuyambira pa nthawi imeneyo kumkabe mtsogolo, mtundu wa anthu kuli konse unafunikira kudziwa kuti chimasuko ku uchimo ndi imfa chingapezedwe kokha mwa kulandira Yesu monga Mpulumutsi woikidwa ndi Mulungu. “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Chifukwa cha chimenecho, njira ya moyo yabwino ndiyo ija imene imatipezetsa mkhalidwe wobvomerezedwa ndi Mulungu monga atsatiri a Mwana wake, inde, monga Akristu oona.

MAPINDU AMENE AMACHOKERA M’MOYO WOTEROWO

8. Kodi nchifukwa ninji kudzitcha kwa munthu kukhala Mkristu sikumatanthauza kwenikweni kuti iye wapeza njira ya moyo yabwino koposa?

8 Mamiliyoni mazana ochuluka lero lino amadzitcha Akristu. Kodi zimenezi zimatanthauza kuti iwo apeza njira yabwino koposa ya moyo? Ayi, pakuti kudzitcha chabe kukhala Mkristu sikumatsimikiziritsa moyo woterowo. Kunena zoona, Yesu anati ambiri adzamcha Mbuye wao koma kuti iye akanena kwa iwo kuti: “Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:23) Ngati tidzitcha Akristu, tiri ndi chifukwa chabwino chopendera kuti tione kaya ngati tikugwirizana moona mtima ndi chitsanzo ndi chiphunzitso cha Mwana wa Mulungu. Zimenezi zikuchititsa kubuka kwa funso lakuti, Kodi nchiyani chimene tiyenera kuyembekezera kuona ponena za njira imene Akristu oona amakhalira ndi moyo imene imaipangitsa kukhala njira ya moyo yabwino koposa ngakhale pa tsopano lino? Yankho la funso limeneli nlofunika kwambiri m’kutsimikizira kuti ndi gulu liti pakati pa ambiri odzitcha kukhala okhulupirira Yesu Kristu limene limaimira mpingo wake woona.

9. Kodi ndi mkhalidwe wotani umene umadziwikitsa mpingo woona Wachikristu, ndipo kodi ndi motani m’mene mkhalidwe umenewu umasonyezedwera?

9 Mwana wa Mulungu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chifukwa cha chimenecho, mpingo woona Wachikristu uyenera kukhala ubale wa m’mitundu yonse, wopanda mipingiridzo yaupfuko, yautundu, yabanja, kutchuka ndi chuma. Mu ubale umenewo, kuli konse kumene tingapite pa dziko lapansi, tiyenera kukhala okhoza kupeza mabwenzi okhulupirika, anthu amene tingathe kuwadalira ndi amene tingawasiyire kuyang’anira zinthu zathu. Ngakhale kuli kwakuti angakhale asanadziwane nafe, iwo akasonyeza chisamaliro chokulirapo kwambiri ndi chikondi kwa ife koposa m’mene akachitira achibale athu ambiri. (Marko 10:29, 30) Kwa odzitcha kukhala Akristu mamiliyoni ochulukawo, kungamveke kukhala kosakhulupiririka kuti pali ubale wa m’mitundu yonse woterowo. Koma zikwi zambiri za Mboni za Yehova zingathe kuchitira umboni chenicheni chakuti izo zakhala ndi chikondi chenicheni chaubale.

10. Kodi ndi motani m’mene kutsanzira chitsanzo cha yesu Kristu kumathandizirira kukhala kwathu ndi maunansi abwino ndi ena?

10 Ndani amene sangabvomereze kuti kusangalala ndi maunansi abwino ndi ziwalo za banja, achinansi ndi ogwira nawo ntchito kumathandizira kwambiri chimwemwe chathu cha ife eni? Yesu Kristu anakhala ndi moyo ndi kuphunzitsa njira ya chikondi. Njira imeneyi imaonjezera maunansi abwino ndi ena, pakuti “chikondano sichichitira mnzake choipa.” (Aroma 13:8-10) Ndiponso, pamene tichitira ena mokoma mtima, mwachifundo ndi mwa chikondi, timakupangitsa kukhala kosabvuta kwa iwo kusonyeza mikhalidwe yabwino imeneyo kwa ife.

11.Kodi ndi motani mmene zitsogozo za Baibulo zimatitetezerera ku kudzibvulaza tokha?

11 Zitsogozo za Baibulo zingatitetezere ku kudzibvulaza. Ndithudi tiyenera kuyembekezera zimenezi kuchokera ku njira yabwino koposa ya moyo. Kutsatira miyezo ya makhalidwe abwino ya Baibulo kumatitetezera ku zopweteka zamalingaliro ndi mantha amene amatsagana mosapeweka ndi kugonana kosaloledwa ndi lamulo. (Miyambo 5:3-11, 18; Mateyu 5:27,28; Ahebri 13:4) Kukhala ndi moyo monga ophunzira odzipereka a Yesu Kristu kumatipatsa nyonga yofunikayo kuti tipewe kumwa mopambanitsa, kudya mopambanitsa, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa maganizo, kuchobva juga ndi zoipa zina. (Miyambo 23:29, 30; Yesaya 65:11; 1 Akorinto 6:9-11; 2 Akorinto 7:1) Ndalama zimene papitapo zinali kuonongeredwa pa zizolowezi zoterozo zingathe kugwiritsiridwa ntchito kupindulitsa nazo ena, kukumachititsa kupezedwa kwa chimwemwe chachikulu kopambana chimene chimachokera ku kupatsa kochokera mu mtima. (Machitidwe 20:35) Kutsatira uphungu wa Baibulo wa kupewa kuipidwa kowawa mtima ndi kaduka kumachititsadi thanzi labwino kwambiri.—Salmo 37:1-5; Miyambo 14:30.

12. Mosasamala kanthu za zofoka zathu, kodi ndimotani mmene tingapitirizire kukhala ndi chikumbu mtima choyera?

12 Ndithudi, tonsefe, pa nthawi ina timalephera kukhala mtundu wa munthu amene ife tikakonda kukhala. Kaya m’mawu Kapena m’zochita, tingakhumudwitse ena. Chenicheni chakuti ife tiri anthu opanda ungwiro chimagogomezeredwa mopweteka kwa ife. Komabe, pamene modzichepetsa tipempha chikhululukiro kwa Mulungu, iye amachipereka kwa ife pa maziko a chisoni chathu chochokera mu mtima ndi kukhulupirira kwathu mapindu a nsembe yotetezera machimo ya Yesu. (1 Yohane 2:1, 2) Ndicho chifukwa chake tingathe kupitirizabe kukhala ndi chikumbu mtima choyera. Sitimaopa kufikira Mulungu kaamba ka chitandizo pa nkhani iri yonse, tiri ndi chidaliro chakuti iye, mwa njira ya mzimu wake, adzatithandiza m’kuchita mwachipambano ndi zobvuta zathu ndi ziyeso.—1 Yohane 3:19-22.

13. Kodi mkhalidwe wa awo amene samalingalira kwambiri Mawu a Mlengi ndi wotani?

13 Bwanji za anthu amene asankha kukhala ndi moyo umene umasonyeza kudera nkhawa kochepa ponena za Mawu a Mlengi? Iwo amasenza okha zobvuta ndi zosautsa zawo. Kuphatikiza pa kuthekera kwa kusangalala ndi zaka zowerengeka za moyo tsopano lino, iwo alibe chiyembekezo chenicheni kaamba ka m’tsogolo. Pamene imfa ikuyandikira, iwo kawirikawiri amakhala ndi chiyembekezo cha kuopa kuthekera kwa chilango chochokera ku mphamvu yoposa yaumunthu.

14. Kodi ophunzira oona a Yesu Kristu akuyang’ana m’tsogolo mwa chiyembekezo chaphamphu ku chochitika chotani?

14 Ha, ndi zosiyana chotani nanga mmene ziriri kwa ophunzira oona a Yesu Kristu! Iwo samaopa tsiku la m’tsogolo la chiweruzo. M’malo mwake, mwa chiyembekezo chaphamphu, iwo amayang’ana m’tsogolo ku kudza kwa Yesu Kristu mu ulemerero monga mfumu yolakika imene idzawamasula ku zisalungamo zonse ndi chitsenderezo ndiyeno nkufutukulira ulamuliro wake ku mbali iri yonse ya dziko lapansi. (2 Atesalonika 1:6-10; Chibvumbulutso 19:11-16; yerekezerani ndi Salmo 72:8.) Inde, m’tsogolo mwabwino kwambiri mukali m’tsogolo. Kodi nchiyani chimene pa nthawiyo chidzasangalatsa?

CHIYEMBEKEZO CHABWINO KOPAMBANA CHA M’TSOGOLO

15, 16. Kodi ndi m’tsogolo mwaulemerero motani mmene mulipo kaamba ka atumiki okhulupirika a Mulungu?

15 Baibulo limayankha kuti: ‘Tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko lapansi latsopano monga mwa lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petro 3:13, NW) “[Mulungu] adzapukuta msozi uli wonse m’maso mwao, ndipo sipadzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kupfuula ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.” (Chibvumbulutso 21:4, NW) Ngakhale imfa yeniyeniyo sidzalepheretsa kukwaniritsidwa kwa m’tsogolo kwa zimenezi, pakuti Mlengi wa moyo angathenso kuukitsa akufa. Ndipo iye adzatero mwa njira ya Mwana wake.—Yohane 5:28, 29.

16 Kodi kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu kudzatanthauzanji kwa inu? Taganizirani za kukhala pansi pa ulamuliro wangwiro wa Yesu Kristu pakati pa anthu amene moona mtima amadera nanu nkhawa, amene mokondwa amaika zabwino zanu poyamba koposa zao za iwo eni. Onse pokhala akumvera lamulo lopambana la chikondi, sipadzakhala upandu, chisalungamo, sipadzakhala chitsenderezo. Inu simudzadzigwiritsa nokha mwala kapena ena. Kubvutika kwa maganizo ndi zosatsimikizirika kapena maupandu akulu zidzakhala kulibe. Kupsinjika, kupanda pake ndi kusukidwa zimene zapangitsa moyo kukhala wosautsa kwa maniliyoni ochuluka sizidzakhalakonso. Kuusa moyo kochititsidwa ndi kupwetekedwa kwambiri kwa thupi sikudzamvedwanso. Misozi ya chisoni sidzakhalanso m’maso mwa ali yense. Ngakhale imfa yeniyeniyo sidzakubvulazani, ikumadukiza ntchito zanu kapena kukuchotserani okondedwa anu.—Yesaya 25:6-8; 65:17.

17. Kodi nchifukwa ninji moyo wa awo amene samapatsa Mlengi malo suli watanthauzo kwenikweni?

17 Yerekezerani zimenezi ndi zimene anthu ali nazo, awo, amene ngakhale kuli kwakuti Sali oipa mwamakhalidwe, samakhala ndi nthawi ya kulingalira Mlengi m’miyoyo yao. Iwo angakhale ndi ulemu ndi chuma cha zinthu zakuthupi zimene iwo amakhumba, mwina mwake kupeza chikhutiro chokulira m’kuthandiza osowa ndi kusangalala ndi ntchito za maphunziro ndi zosangalatsa zabwino. Komabe, iwo ayenera kubvomereza chenicheni chosapeweka chakuti palibe chiri chonse pa dziko pano chimene chiri chokhalitsa kwenikweni. Palibe ali yense amene ali wosati nkugweredwa ngozi, matenda kapena imfa. Chuma sichidzatetezera ku zinthu zimenezi ndiponso sitingamke nacho pamene moyo utha. (Salmo 49:6-20; Mlaliki 5:13-15; 8:8) Zoyesayesa zokhala ndi cholinga choyenera za kuthandiza anthu anzathu zingafike pa kuomba mpeya chifukwa cha mikhalidwe yoipa. Chotero moyenerera kungafunsidwe kuti: Kodi moyo ungakhale watanthauzo motani ngati m’tsogolo motsirizira mmene uwo umapereka muli manda chabe? Kodi ndi motani m’mene ungakhalire wabwino ngati umasemphana kwenikweni ndi m’tsogolo mwamuyaya mwa munthu?—Yerekezerani ndi Mlaliki 1:11, 15, 18; 2:10, 11; 9:11, 12.

NTHAWI YA KUSANKHA

18. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuchedwa mkupanga chosankha choyenera ponena za moyo wathu? (b) Kodi ndi motani m’mene mkhalidwe wathu uliri wofanana ndi uja wa kholo Nowa?

18 Makamaka popeza kuti payenera kukhala tsiku la chiweruzo, nkofunika kwambiri kuti anthu kuli konse asankhe njira ya moyo imene idzapereka mphotho, osati chitsutso. Pali kufulumira ponena za kupanga chosankha chimenechi. Sitikudziwa chimene chidzadza mawa. Ndiponso, kudza kwa Yesu Kristu kudzafutukulira ulamuliro wake wachifumu pa dziko lonse lapansi kukuyandikirayandikirabe. Mkhalidwe wa mtundu wa anthu uli wofanana ndi uja wa kholo Nowa m’masiku a chigumula cha pa dziko lonse chisanadze. lye anali ndi zosakha ziwiri: (1) kutsatira njira zosaweruzika za anthu a m’nthawi yake kapena (2) kugonjera ku chifuniro cha Mulungu. Mwachimwemwe, Nowa anapanga chosankha choyenera. Iye anakhoma chingalawa ndipo, limodzi ndi ziwalo zisanu ndi ziwiri za banja lake, analowamo atalamulidwa ndi Mulungu. Ziwalo zisanu ndi zitatu za banja laumunthu zimenezi zinapulumuka chigumulara, ndipo ndicho chifukwa chake tiri moyo lero lino.—⁠1 Petro 3:20.

19. Kodi 1 Petro 3:21, 22 amabvumbulanji ponena za chipulumutso?

19 Mofananamo, kwa ife, chimodzi cha zofunika zopezera moyo wosatha ndicho lonjezo la kutumikira Yehova Mulungu monga ophunzira a Yesu Kristu. Monga momwe kunaliri kuti kunalibe chipulumutso kunja kwa chingalawa, kwa ife kulibe chipulumutso popanda makonzedwe a Mulungu kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. Atatha kutchula kulanditisidwa kumene anthu asanu ndi atatuwo anakhala nako m’chingalawa, mtumwi Wachikristu Petro analemba kuti:

“Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu mwa kuuka kwa Yesu Kristu; amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.”​—⁠1 Petro 3:21, 22.

20. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ubatizo wa m’madzi wokha si wokwanira kuti munthu apeze moyo wosatha?

20 Sindiwo ubatizo wa m’madzi wokha umene umachititsa chipulumutso. Pamene kuli kwakuti madzi angathe kutsuka litsiro kapena pfumbi, “kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi” mwa kutsuka kotsimikizirika kwa kunja kumene kumapulumutsa. Onani kuti Petro ananti chipulumutso chiri kupyolera “mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” Chotero, munthu amene akubatizidwa afunikira kuzindikira kuti moyo wosatha uli wothekera kokha chifukwa chakuti Mwana wa Mulungu anafa imfa ya nsembe, anaukitsidwa pa tsiku lachitatu ndipo potsirizira pake anakwezedwera ku dzanja lamanja la Mulungu. ​—⁠Aroma 10:9, 10.

21. Kodi ndi motani mmene munthu amapezera “chikumbu mtima chokoma”?

21 Ndiponso, mtumwi Petro anagogomezera pa “funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu.” Kuti akhale ndi chikumbu mtima chabwino chimenecho, onse amene akufuna kubatizidwa afunikira choyamba kulapa zolakwa zao zakale, kusonyeza kukhulupirira makonzedwe a Mulungu a moyo wosatha, kutembenuka ku njira yoipa ndi kudzipatulira kapena kudzipereka iwo eni kotheratu ku kuchita chifuniro cha Mulungu. Ubatizo uli chizindikiro chapoyera cha chitsimikiziro cha mu mtima chimenechi. Atatsatira zonse zimene Yehova Mulungu tsopano amafuna, wophunzira wobatizidwayo amafikira pa kukhala ndi chikumbu mtima chabwino. Kwa utali wonse umene iye asungabe chikumbu mtima choyera chimenecho iye ali mu mkhalidwe wopulumutsidwa. Chiweruzo chachitsutso cha Mulungu sichidzaperekdwa kwa iye.—Yerekezerani ndi Machitidwe 2:38-40; 3:19; 10:34-48.

22. Kodi ndi motani mmene tingapindulire ndi makalata awiri ouziridwawo a mtumwi Petro?

22 Pamene anthu asankha mwamsanga njira yabwino koposa ya moyo imeneyi, ndi pameneso iwo adzayamba mwamsanga kupeza mapindu make. Pamene chosankhacho changopangidwa cha kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndi kudzipereka ku ubatizo wa m’madzi mosonyeza kudzipereka kapena kudzipatulira kwathu, ife ndithudi tifunikira kuumirira mokhulupirika ku chosankha chimenecho. Koma kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupitirizabe kusankha kulondola njira imeneyi ya moyo? Kodi ndi motani mmene tingakanizire zisonkhezero zimene zingachititse kutayikiridwa kwathu madalitso a tsopano lino ndi a m’tsogolo ogwirizanitsidwa ndi kukhala ophunzira enieni a Mwana wa Mulungu amenewa? Kalekale, mtumwi wouziridwa Petro anapereka mayankho abwino kwambiri a mafunso amenewa. Makalata ake awiri akupanga maziko a zimene zikulongosoledwa m’bukhu lino. Tikhulupirira kuti, mwa kupenda kwathu makalata amenewa, tidzalimbikitsidwa kugwiritsa njira yabwino koposa ya moyo monga atumiki a Mulungu ndi kupitirizabe kusangalala ndi njira ya moyo imeneyi mokulira kwambiri.

[Chithunzi chachikulu patsamba 4]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena