Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bw mutu 2 tsamba 15-28
  • Chithandizo Cholimbikitsa Kumamatira ku Chosankha Chathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chithandizo Cholimbikitsa Kumamatira ku Chosankha Chathu
  • Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NKHANI YOKONDWERETSA KWAMBIRI KWA ANENERI
  • CHIFUKWA CHAKE ANGELO ALI OKONDWERETSEDWA
  • KULIMBIKITSA MAGANIZO ATHU KAAMBA KA NTCHITO
  • KUDZITSIMIKIZIRA IFE ENI KUKHALA ANA OMVERA A MULUNGU
  • “DZISUNGIERNI MWAMANTHA”
  • MTENGO WAPATALI UNALIPIRIDWA
  • Khalanibe ndi “Chiyembekezo cha Chipulumutso” Choŵala!
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Chotandizira Kupirira Pobvutika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Tetezerani Chiyembekezo Chanu Chachikristu
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Chiyembekezo Chokhala ndi Chitsimikiziritso Chotsimikizirika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
Onani Zambiri
Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
bw mutu 2 tsamba 15-28

Mutu 2

Chithandizo Cholimbikitsa Kumamatira ku Chosankha Chathu

1, 2. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera mwafanizo kufunika kwa kuumirira ku chosankha chathu cha kutumikira Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kopanda nzeru kunyalanyaza uphungu wa Yesu?

“PALIBE munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:62) kuti alime bwino lomwe, kuti apangitse mizera kukhala yoongoka, munthu wogwira chikhasuyo ayenera kusumika maso ake pa chikhomo chozikidwa kumapeto ena a mundawo. Ha, ndi kofunika kwambiri chotani nanga m’mene kuliri kusimika maso athu pa chonulirapo cha moyo wathu! Pamenepo masiku ndi zaka zamtengo wapatali za utali wa moyo wathu zidzasonyeza mkhalidwe umene uli wogwirizana ndi chonulirapo chimene ife talingako.

2 Mawu a Mwana wa Mulungu ogwidwa pamwambapowo akusonyeza kuti, pamene tangopanga lonjezo la kutumikira Mlengi wathu, tiyenera kukhala otsimikizira kumamatira ku chosankha chimenecho, mosasamala kanthu za chiri chonse chimene chingatigwere. Dziko lingapereke chimene chimaonekera kukhala njira yosangalatsa kwambiri-kulondola zosangalatsa, kutchuka kapena chuma chakuthupi. Koma kuyang’ana m’mbuyo molakalaka ku zinthu zimenezi-zoipa kwambiri, kuzilola kukhala chinthu chachikulu choyang’anako m’miyoyo yathu-kungathanthauze kutayika kwa mfupo imene tikufunafuna. Kungachititse kutayika kwa moyo.

3. Kodi nchiyani chimene chiri cholinga chachikulu cha chikhulupiriro chathu?

3 “Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake,” akutero Mlaliki 7:8. Chotero, pamene kuli kwakuti kuyamba njira yathu yosankhidwa kuli kofunika kwambiri, ndiko kumaliza kumene kuli kanthu kwenikweni. Ndicho chifukwa chake, m’Mawu a Mulungu, chigogomezero chokulira chikuikidwa pa kutsimikizira kukhala okhulupirika kufikira mapeto. (Mateyu 24:13) Chikhulupiriro chathu chiri nacho monga cholinga chachiklu, chifuno kapena chonulirapo, kupezedwa kwa chipulumutso kapena moyo wosatha.—1 Petro 1:9.

4. (a) Kuti tikhalebe okhulupirika, kodi ndi lingaliro lotani la chipulumutso limene liri lofunika? (b) Kodi 1 Petro 1:10-12 amatiuzanji ponena za chikondwerero cha anereri m’makonzedwe a Mulungu kaamba ka chipulumutso?

4 Kodi nchiyani chimene chingatithandize kuchita khama monga ophunzira okhulupirika a Mwana wa Mulungu? Choyamba, tifunikira kuona bwino lomwe, kulingalira mwamphamvu kwambiri, mtengo waukulu kwambiri wa chipulumutso chimene tikufunafuna. Mawu ouziridwa a mtumwi Petro, bwenzi lapamtima la yesu Kristu, angatithandize kwambiri m’nkhani imeneyi. Chilangizo chake chingatithandize kuona kuti chipulumutso chathu chotsirizira ndicho kanthu kena kamene tiyenera kukapiririra chitsenderezo chiri chonse cha chitsutso, muli monse m’mene chingakhalire chowawa kwambiri. Ndicho kanthu kena kamene tiyenera kukhala ofunitsitsa kukagwirira ntchito, kudzimana, inde, kukafera ngati kutakhala kofunika. (Luka 14:26-33) Pa 1 Petro 1:10-12, mtumwiyo akulemba kuti:

“Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani; ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero wotsatana nao. Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba.”

NKHANI YOKONDWERETSA KWAMBIRI KWA ANENERI

5. Kodi aneneri ananeneratu chiyani ponena za masautso a Mesiya?

5 Zaka mazana ambiri masiku a pa dziko lapansi a Yesu asanakhale, aneneri Achihebri anauziridwa kuneneratu kubvutika kumene kukagwera Mesiya kapena Kristu wolonjezedwayo. Ulosi wa Danieli unasonyeza nthawi ya kufika kwa Kristu ndipo unasonyeza kuti iye akadulidwa mu imfa pambuyo pa utumiki wa zaka zitatu ndi theka. (Danieli 9:24-27) Kuchokera mu ulosi wa Yesaya tikuphunzira kuti Mesiya akakanidwa ndi kukhala mwala wophunthwitsa. (Yesaya 8:14, 15; 28:16; 53:3) Ulosi umenewo unasonyezanso kuti iye akanyamula zowawa za anthu, akayesedwa ndi kutsutsidwa koma nakhala du pamaso pa otsutsa ake, akathiridwa malobvu, kuwerengeredwa pakati pa ochimwa, akalasidwa, kufa imfa ya nsembe ndi kuchotsa machimo kuti atsegulire ambiri njira yopezera mkhalidwe wolungama kwa Mulungu. (Yesaya 50:6; 53:4-12) Ulosi wa Zekariya unasonyeza kuperekedwa kwa Mesiya kaamba ka ndalama zasiliva 30. (Zekariya 11:12) Ndipo mneneri Mika ananeneratu kuti Kristu, “woweruza wa Israyeli,” akapandidwa patsaya.—Mika 5:1.

6. Kodi ndi mfundo zotani zonena za masautso a Mesiya zimene zikufotokozedwa m’Masalmo?

6 Pakati pa mawu a m’Salmo onena za Yesu Kristu pali otsatirapowa: Iye akaperekedwa ndi bwenzi lapatima. (Salmo 41:9) Olamulira, mochirikizidwa ndi nzika zao, akatsutsana naye. (Salmo 2:1, 2) Omanga achipembedzo Achiyuda akamkana. (Salmo 118:22) Mboni zonama zikanamizira Mesiya. (Salmo 27:12) Atafika pa malo ophedwera, iye akapatsidwa chakumwa choledzeretsa. (Salmo 69:21a) Awo omkhomera pa mtengo akakhala ‘kumanja ndi kumapazi kwake’ ngati zirombo. (Salmo 22:16) Akachita maere pa Malaya ake. (Salmo 22:18) Adani ake adamnyodola ndi mawu akuti: “Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.” (Salmo 22:8) Atamva ludzu kwambiri, akapempha madzi ndi kupatsidwa vinyo wosasa. (Salmo 22:15; 69:21b) Imfa yake isanachitke, iye akapfuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” –Salmo 22:1.

7. Kodi maulosi amabvumbulanji ponena za “ulemerero wotsatana” ndi masautso a Kristu?

7 Monga momwe Petro akusonyezera, aneneri anauziridwanso kunena za ‘maulemerero amene akadza pambuyo’ pa kubvutika kwa Mesiya. Mwa mphamvu yaikulu ya Mulungu, Mwana wokhulupirika ameneyu akaukitsidwa kwa akufa. (Salmo 16:8-10) Pa kukwera kwake kumwamba, iye akakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, akuyembekezera kufikira adani ake onse ataikidwa kukhala chopondapo mapazi ake. (Salmo 110:1) Iye akakhala ndi udindo wa wansembe wosatha mofanana ndi dongosolo la Melikizedeke. (Salmo 110:4) Atate wake, “Nkhalamba ya Kale lomwe,” akampatsa ulamuliro waufumu. (Daniel 7:13, 14) Potsirizira pake nthawi idzakwana yakuti wodzozedwa wa Mulungu aphwanye mitundu yonse yotsutsa ulamuliro wake. (Salmo 2:9) Pamenepo iye adzachita ulamuliro pa dziko lonse lapansi.—Salmo 72:7, 8; Zekariya 9:9, 10.

8. Kodi ndi motani m’mene aneneri anasonyezera chikondwerero chachikulu m’zimene iwo analemba, ndipo kodi nchifukwa ninji iwo anatero?

8 Inde, maulosi anapereka kuoneratu kwabwino kwambiri ponena za ntchito ya Mesiya m’kakonzedwe ka Mulungu kaamba ka chipulumutso kapena chilanditso ku uchimo ndi imfa. Kukhulupirika kwake pobvutika, imfa yake, chiukiriro ndi kukwera kumwamba monga munthu wauzimu waulemerero-zonsezi zinali zofunika kuti anthu alandire “Kukoma mtima kwapadera,” kuphatikizapo kukhululukidwa kwa machimo ndi kuyanjanitsidwanso kotheratu ndi Yehova Mulungu monga ana ake. Aneneri iwo eniwo sanali kumvetsetsa mokwanira m’mene chipulumutso chikadzera kupyolera mwa Mesiya. Komatu, monga momwe mtumwi Petro akusonyezera, iwo anali okondweretsedwa ndi zinthu zimene iwo analemba. Iwo anapenda mwakhama mawu olosera, akumaphunzira mobwerezabwereza maulosi ao a iwo eni kuti atumbe tanthauzo la zimene iwo anauziridwa kulemba. Pozindikira kuti munali chowonadi chodabwitsa chophatikizidwa m’zibvumbulutso zimene iwo analandira, aneneriwo anagwiritsira ntchito mphamvu zao zu kulingalira mokwanira mkuyesayesa kupeza phindu lalikulu kwambiri m’zoneneratu zao zoperekedwa ndi Mulunguzo. Zimenezi zinali mosasamala kanthu za chenicheni chakuti sikunachitike kufikira pa kudza kwa Mesiya kuti anthu akanatha kukhala olandira kukoma mtima kosakuyenerera konendweratuko. Komabe, zimene anereri anazimvetsetsa zinali zokwanira kuwalimbikitsa ndipo zinawasonkhezeranso kufuna kudziwa zina zoonjezereka. Iwo anali okondweretsedwa kwenikweni ndi kudziwa za mikhalidwe imene idzakhalapo pa nthawi ya kuonekera kwa Mesiya, inde, “nthawi” yiti imene iye akakumana ndi kubvutika konenedweratuko ndiyeno nkukhala ndi kukwezedwako.

9. Kodi ndani kwenikweni amene anapindula ndi maulosi onena za Mesiya?

9 Monga momwe Petro analongosolera momvekera bwino, anereri Achihebri anafikira pa kumvetsetsa kuti maulosi a Mesiya sanalembedwe kwakukulukulu kaamba ka phindu lao koma kaamba ka phindu la awo amene akakhala akukhala ndi moyo pa nthawi ya kuonekera kwa Mesiya. (1 Petro 1:12) Ponena za zibvumbulutso zimene iye analandira, mmeneri Danieli anabvomereza kuti: “ndinachimva ichi, koma osachizindikira.” (Danieli 12:8) Komabe, anthu amene analandira “mbiri yabwino” imene inalengezedwa m’zaka za zana loyamba C.E. anali anthu amene anapindula mokwanira ndi mawu ouziridwa onena za kudza koyamba kwa Mesiya. Kunali kwa iwo kumene aneneriwo anali kutumikira kwenikweni. –Mateyu 13:16, 17.

10. Kodi ife tiyenera kuyambukiridwa motani ndi chikondwerero chimene aneneri Achihebri anasonyeza m’chipulumutso, ndipo chifukwa ninji?

10 Pamenepa, kodi kudziwa kwathu chikondwerero chachikulu cha anereri kuyenera kutiyambukira motani? Kuyenera kutipangitsa kudzipenda ife eni kuti tione kaya ngati tiri ndi nkhawa yofananayo ponena za chipulumutso. Kodi kukhalabe kwathu atumiki obvomerezeka a Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndiko chinthu chachikulu m’moyo? Kodi ife tiri otenthedwa maganizo kwenikweni ndi nkhani imeneyi? Ndithudi, tiri ndi chifukwa chabwino chokhalira omwerekera kotheratu m’kudzitsimikizira ife eni kukhala ophunzira okhulupirika a Mwana wa Mulungu. Mesiya anadza zaka mazana ambiri zapitazo. Imfa yake ya nsembe inapereka maziko enieni a chipulumutso ndipo inatsimikiziritsa kukwaniritsidwa kwa lonjezo liri lonse la Mulungu. (2 Akorinto 1:20) Kupita kwa nthawi sikunafooketse m’njira iri yonse kutsimikizirika kwa kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. M’malo mwake, kumatsimikiziritsa kuti chikhumbo cha Mulungu nchakuti anthu ochuluka monga momwe kungathekere apeze chipulumutso. (1 Timoteo 2:3, 4; 2 Petro 3:9) Chotero, mwachidaliro, tingathe kuyembekezera kulandira madalitso amene Wam’mwambamwambayo wasungira okhulupirika.

CHIFUKWA CHAKE ANGELO ALI OKONDWERETSEDWA

11. Malinga ndi kunena kwa 1 Petro 1:12, kodi chikondwerero cha angelo nchachikulu kwambiri motani m’makonzedwe a Mulungu kaamba ka chipulumutso?

11 Chitsanzo cha angelo chiyeneranso kutilimbikitsa kuchita zimene tingathe kukhalabe m’chiyanjo cha Mulungu. Ngakhale kuli kwakuti alibe chosowa cha iwo eni cha makonzedwe a chipulumutso, angelo okhulupirika amakhala ndi chikondwerero chenicheni m’kuchitika kwa chifuno chachikulu cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Zinthu izi [zimene zinatanganitsa maganizo a anereri Achihebri] angelo alakalaka kusuzumiramo.” (1 Petro 1:12) Inde, Yesu Kristu asanadze pa dziko lapansi pano, angelo anafuna kudziwa zochuluka ponena za zobvuta za Kristu, “maulemerero amene amatsatirapo” ndi chiyambukiro cha “mbiri yabwino” pa mtundu wa anthu. Mtumwi Petro akanatha kulankhula za iwo kukhala ‘atalakalaka kusuzumiramo’ m’zinthu zimenezi. M’Chigiriki choyambirira, mawuwo ‘kuzumiramo’ amapereka lingaliro la kuweramira pansi ndi cholinga cha kupenda chinthu mosamalitsa kwambiri. Koma kodi nchifukwa ninji angelo anali okondweretsedwa kwambiri m’kupanga kupenda kosamalitsa chibvumbulutso cha Yehova Mulungu chonena za chipulumutso? Monga anthu angwiro auzimu, kodi nchifukwa ninji makonzedwe kaamba ka anthu ochimwa a padziko lapansi akawakondweretsa kwenikweni

12, 13. Kodi ndi motani mmene tingalongosolere chikondwerero chachikulu cha angelo m’chipulumutso cha mtundu wa anthu?

12 Popeza kuti angelo si odziwa zonse, iwo mosakaikira amaonjezera chidziwitso chawo mwa kulingalira mosamalittsa machitidwe a Mulungu ndi zibvumbulutso zake. Makonzedwe a kuomboledwa kwa mtundu wa anthu ndithudi anapereka chitsanzo chodabwitsa cha chikondi cha Mulungu, chiweruzo cholungama, chifundo ndi nzeru. Chotero, mwa kudzitanganitsa iwo eni ndi kupeza chidziwitso chokulirapo chonena za malinganizidwe a Yehova opulumutsira mtundu wa anthu wochimwa, angelo akafikira pa kuzindikira Atate wao wakumwamba moonjezerekadi kwambiri. Iwo akaphunzira zinthu zonena za umunthu wake ndi njira zimene sizikanatha kuzindikiridwa mwa kuphunzira kapena kupenda chochitika chiri chonse cha m’chilengedwe chonse. –Yerekezerani ndi Aefeso 3:8-10.

13 Ndiponso, angelo ali ndi “kukondwera” ndi mtundu wa anthu. (Yerekezerani ndi Miyambo 8:22-31.) Iwo amafuna kuona mtundu wa anthu ukuyanjanitsidwanso ndi Atate wakumwamba, Yehova. Ndicho chifukwa chake Yesu Kristu anati: “Kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”-Luka 15:10

14. (a) Kodi mkhalidwe wa angelo kulinga ku chipulumutso chathu uyenera kutithandiza kuchitanji? (b) Kodi ndi uphungu wotani wa mtumwi Petro umene tiyenera kuukumbukira kuti tikhalebe atumiki okhulupirika a Mulungu?

14 Inde, angelo mamiliyoni ochulukawo anasangalala pamene ife enife tinalapa. Iwo amakhala okondwera kwambiri kutiona tikusunga kukhulupirika mpaka kufikira mapeto. Chotero, iwo ‘amatisonkhezera kupitirizabe.’ Tiyenitu tisalole kuona mwa maganizo athu gulu lalikulu lakumwamba limene liri ndi nkhawa kwambiri ndi chikondi kwa ife kukhala koziya. Ndithudi ife timafuna kuti chisangalalo chao ponena za ife chipitirizebe. Zimenezi zimafuna kuti ife tilabadire chilangizo cha Petro chakuti: “Chotero limbitsani maganizo anu kaamba ka ntchito, sungani malingaliro anu kotheratu; ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwapadera kumene kudzaperekedwa kwa inu pa bvumbulutso la Yesu Kristu.—1 Petro 1:13, NW.

KULIMBIKITSA MAGANIZO ATHU KAAMBA KA NTCHITO

15. Kodi ndi motani mmene tiyenera kumvera chilangizo cha Petro cha ‘kulimbikitsa maganizo athu kaamba ka ntchito’?

15 Kodi kumatanthauzanji kwa ife ‘kulimbikitsa maganizo athu kaamba ka ntchito’? Kumasuliridwa kwa liwu ndi liwu kwa mawu a mtumwi Petrowo kukakhala kwakuti: “Mangani lamba m’zuuno za maganizo anu.” “M’masiku a atumwi, amuna anali kubvala mikanjo. Pogwira ntchito kapena kuchita ntchito ina yamphamvu monga ngati kuthamanga, mwamuna ankakwinda mkanjowo modzeretsa pakati pa miyendo ndi kuumanga zolimba ndi lamba. ‘Kumanga lamba m’zuuno’ kunantanthauza kukhala wokonzekera kaamba ka ntchito. Chifukwa cha chimenecho, kwa ife ‘kumanga ndi lamba m’zuuno za maganizo’ kukatanthauza kuchititsa mphamvu zathu za kulingalira kukhala mu mkhalidwe wokonzekera kuchita mathayo Achikrustu ndi kupirira mu chiyeso chiri chonse chimene chingatigwere.

16. Kodi ndi motani mmene tingasonyezere kuti ‘tikusunga malingaliro athu kotheratu’?

16 Mphamvu zathu za kulingalira pokhala ziri mu mkhalidwe wokonzekera kupitirizabe mu utumiki wokhulupirika kwa Mulungu, ife ndithudi tidzakhala ‘tikusunga malingaliro athu kotheratu.’ Tidzakhala achikatikati m’kuganiza kwathu, okhoza kutsimikizira moyenera kupindulitsa kwa zinthu. Moyo wathu ukasonyeza kuti tikulamulira mphamvu zathu za kulingalira ndipo sitikugonjera ku zonyengerera za dziko lotalikirana ndi Yehova Mulunguli. (1 Yohane 2:16) Chopambana m’miyoyo yathu chikakhala kuchita chimene chiri chokondweretsa kwa Atate wathu wakumvamba ndi Mwana wake.

17. (a) Kodi nchiyani chimene chiri “kukoma mtima kwapadera” kumene kudzaperekedwa kwa okhulupirira? (b) Kodi ndi motani m’mene ‘timaikira chiyembekezo chathu pa kukoma mtima kwapadera kumene kuyenera kuperekedwa kwa ife pa bvumbulutso la Yesu Kristu’?

17 Kuti ‘tilimbikitse maganizo athu kaamba ka ntchito ndi kusunga malingaliro athu kotheratu,’ tiyenera ‘kuika chiyembekezo chathu pa kukoma mtima kwapadera kumene kudzaperekedwa kwa ife pa bvumbulutso la Yesu Kristu.’Pa nthawi imene Ambuye Yesu Khristu akudza mu ulemerero, awo onse okhala ndi chiyembekezo chakumwamba amene akhalabe ophunzira ake odzipereka adzakhala ogawana naye m’kokoma mtima kwapadera kwa Mulungu. (1 Akorinto 1:4-9) Si kokha kuti ophunzira obadwa ndi mzimu anemewa adzakhala ndi mpumulo wotonthoza ku kubvutika kumene iwo akhala akukumana nako kuchokera kwa anthu oipa; komanso Akristu awo okhalandi chiyembekezo cha paradaiso wa pa dziko lapansi adzasungidwa amoyo kupyola “chisautso chachikulu” chimene chikudza pambuyo pa kudza kwa Kristu ndi kukhala nacho patsogolo pao chiyembekezo cha moyo wa pa dziko lapansi wopanda mapeto. Ndithudi, tiri ndi chifukwa chabwino chokumbukirira nthawi zonse kukwaniritsidwa kwa ziyembekezo zathu Zachikrstu, tikumayang’ana patsogolo mwaphamphu ku kukhala kwathu olandira chiyanjo cha Mulungu. Chidaliro chathu m’kukwaniritsidwa kotsimikizirika kwa ziyembekezo zimenezi chingatisonkhezere kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba ndi Mwana wake. Tiyenitu tisumike maso athu mwamphamvu pa madalitso amene kudza kwa Kristu mu ulemerero kudzadzetsa kwa atsatiri make okhulupirika.—Mateyu 25:31-46.

KUDZITSIMIKIZIRA IFE ENI KUKHALA ANA OMVERA A MULUNGU

18. Kodi ndi motani m’mene timadzisonyezera ife eni kukhala “ana omvera”?

18 Mogwirizana ndi ziyembekezo zimenezi, mkhalidwe wathu uyenera kukhala uja wa “ana omvera.” Mtumwi Petro akupitirizabe kuti: “Monga ana omvera, lekani kudzifanizitsa ndi zilakolako zimene munali nazo kale m’kusadziwa kwanu.” (1 Petro 1:14, NW) Monga ana amene amalemekeza ndi kukonda Atate wao wakumwamba, tiyenera kufuna kudzigonjetsera ife eni mosangalala ku zofunika zake, tikumazindikira kuti chimenechi ndicho chinthu choyenera kuchichita. Sitimafunanso kuchita zinthu zathu za moyo mu mkhalidwe umene tinazolowera kale tisanakhale ophunzira a Yesu Kristu. M’kusadziwa kwathu malamulo a Mulungu, tingakhale tinali kugonjera ku zilakolako zathu zochimwa, mwadyera tikumaika zabwino za ife eni poyamba mobvulaza ena, kapena tinasumika miyoyo yathu pa kupeza chuma chakuthupi, kutchuka kapena ulamuliro. Mokulira, tinachititsa miyoyo yathu kukhala yogwirizana ndi mikhalidwe, mawu ndi machitidwe a awo otizungulira. Ife tsopano tikudziwa kuti njira yoteroyo ya moyo imene imanyalanyaza Mulungu iri yopanda pake, yopanda tanthauzo.

19. Monga momwe kwasonyezedwera ndi chilamulo cha Mose, kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kukhala “woyera”?

19 Kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri, tifunikira kutsanzira Yehova Mulungu, amene ali woyera, wopanda uchisi kapena wangwiro. Kodi kutsanzira kwathu Atate wakumwamba kuli kolekezera pa kulambira kwa nthawi zonse? Onani kuti mtumwi Petro akuti: “Mogwirizana ndi Woyerayo amene anakuitanani nanunso khalani oyera mu khalidwe lanu lonse.” (1 Petro 1:15, NW) Kenako iye anagwira mawu mu Levitiko 19:2, amene amati: “Muzikhala oyera; pakuti Ine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.” (1 Petro 1:16) Mawu a m’Levitiko amenewa anatuluka m’kulongosola kumene kumasonyeza zimene Yehova Mulungu anafuna kwa Aisrayeli m’kuchita zonse ziwiri kulambira kwao kwa nthawi zonse ndi zochita zao za nthawi zonse za tsiku ndi tsiku. Zophatikizidwa pakati pa zofunika zimenezi kaamba ka khalidwe loyera ndizo: Kulemekeza makolo, kuona mtima, kulingalira ogontha, akhungu ndi ena obvutika, osasunga nkhani kukhosi koma kukonda munthu mnzathu, kupewa ugogodi ndi kuchita umboni wonama, ndi kupereka chiweruzo cholungama. (Levitiko 19:3, 9-18) Kunena zoona, pamenepa, palibe mbali iri yonse ya moyo imene ikusiyidwa m’chofunika chimenechi cha kukhala woyera kapena wangwiro m’lingaliro la Yehova.

“DZISUNGIERNI MWAMANTHA”

20. Kodi nchiyani chimene tiyenera kukumbukira ponena za chiweruzo, ndipo kodi ndi motani m’mene chimenechi chiyenera kuyambukirira khalidwe lathu?

20 Chifukwa china chachikulu chokhalira ndi moyo mogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu chikupezeka m’mawu otsatirapo a mtumwi Petro: “Ndiponso, ngati mukuitana pa Atate amene amaweruza mopanda tsankho mogwirizana ndi ntchito ya aliyense, dzisungireni mwamantha m’kati mwa nthawi ya kukhala kwanu alendo.” (1 Petro 1:17, NW) Sitiyenera kutaya kapenyedwe ka chenicheni chakuti Atate wathu wakumwamba, mwa njira ya Mwana wake, adzatiweruza. Chiweruzo chimenecho sichidzasonkhezeredwa ndi maonekedwe a kunja koma chidzakhala chopanda tsankho, mogwirizana ndi chimene ife tiri kwenikweni monga anthu. (Yesaya 11:2-4) Chotero, ngati tibvomereza Wammwambamwamba kukhala Atate wathu, tidzafuna kudzisungira ife eni m’njira yakuti iye angayang’ane pa ife mwachibvomerezo, akumapereka chiweruzo chabwino kwa ife. Ife moyenerera tikapitirizabe kulondola njira imene imasonyeza mantha oyenera ndi aulemu kwa Yehova Mulungu.

21. Kodi ndi motani m’mene timasonyezera kuti timaona kukhala kwathu m’dziko lino kukhala nthawi ya “kukhalamo monga alendo”?

21 Ndiponso, tifunikira kuzindikira kuti dziko ndi zimene limapereka nzakanthawi. Tiyenera kudziganizira kukhala tiri “alendo.” Nkofunika kwambiri kwa ife kupewa kudzigwirizanitsa ife eni ndi kanthu kali konse ka m’dziko lino monga ngati kuti tikapitirizabe kosatha. Ngakhale mphala za mwanaalilenji za mafumu a Asuri wakale, Babulo, ndi Perisiya sizikuperekanso malo okhala abwino kwa ali yense; izo ziri mabwinja. Palibe ntchito iri yonse ya kumanga nyumba, palibe chiri chonse chopangidwa chamakono chochitidwa ndi luso la ntchito za manja ndi luso la zopangapanga, palibe chojambulidwa, palibe chozokotedwa, palibe kanthu kali konse kopangidwa ndi munthu kamene kangakhalebe kosasinthika kwamuyaya. Zoona, tiyenera kukhala ndi moyo m’dziko lino limene liri lotalikirana ndi Mulungu, ndipo ‘Sitingasamukepo.’ (1 Akorinto 5:9, 10) Koma sitikufuna kumva kwenikweni kukhala ‘titakhala mwakunja kulinji’ m’dongosolo la zinthu liripoli. Ayi, pakuti ife tikuyembekezera kanthu kena kabwino kwambiri, ku kudza kwa “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zopangidwa ndi Mulungu. (2 Petro 3:13) Ulendo wathu wa kukhala ndi moyo m’dziko uli ‘nthawi ya kukhala alendo,’ ndipo makhalidwe athu, mawu ndi zochita ziyenera kusonyeza kuti ziridi choncho.—Yerekezerani ndi Ahebri 11:13-16.

MTENGO WAPATALI UNALIPIRIDWA

22, 23. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuona kosatha kukhala amangawa kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu?

22 Pogogomezera moonjezereka kufunika kwa kupitirizabe kwathu kukhala oyera, atumiki odzipereka a Yehova Mulungu, mtumwi Petro akulemba kuti: Podziwa kuti simunaomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu; koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.” (1 Petro 1:18, 19) Pokhala titaomboledwa ku chitsutso cha uchimo ndi imfa, ife tiri ndi thayo kwa Yehova Mulungu amene anapanga malinganizidwe akuti tiomboledwe. Tiyeni tiyerekezere monga ngati kuti chiwerengero chachikulu cha siliva kapena golidi chinalipiridwa kutiombola ku imfa. Kodi ife sitikanaona kukhala amangawa kwambiri kwa uyo amene anapanga kudzimana chuma chakuthupi chochuluka choterocho kaamba ka ife?

23 Pamenepa, mangawa athu ndi akulu kwambiri chotani nanga, kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu! Mtengo wa dipo umene unalipiridwa unali wamtengo wapatali kopambana koposa chuma chiri chonse chakuthupi chimene chingathe kutayika, kubedwa kapena kuonongedwa. Mtengo wake uli waukulu kwambiri koposa siliva ndi golidi yense amene ali pa dziko lapansi lero lino. Mwazi wamtengo wapatali wa Mwana wa Mulungu wopanda chimoyo ndiwo mtengo wa dipo ‘wamtengo wapatali’ umene unalipiridwa. Ndiwo mwazi wa moyo wa munthu wina amene anali ndi kuyenera kwa kukhala ndi moyo kosatha ndipo, chotero, wa munthu amene anachita zochuluka koposa kungopereka moyo wake kuchiyambiyambi komwe m’moyo, monga momwe ena achitira kaamba ka chimene iwo anachilingalira kukhala chifukwa cholemekezeka. Kuperekedwa kwa mtengo wa dipo umenewu kunaperekanso maziko, monga momwe Petro akunenera, a ‘kusiyanira ndi makhalidwe athu achabe ochokera kwa makolo athu.’ Kodi ziri choncho motani?

24. Tisanakhale ophunzira a Yesu Kristu, kodi khalidwe lathu lingakhale litakhala “lachabe” motani”?

24 Pamene tinalandira chenicheni cha kukhala kwathu titaomboledwa kapena kugulidwa ndi mwazi wa mtengo wapatali wa Yesu Kristu, tinasiya njira yathu yakale ya moyo. Popanda kudziwa Yehova Mulungu kapena zifuno zake, moyo wathu unakhala “wachabe,” wosaphula kanthu, wopanda pake, m’chakuti unazikidwa kotheratu pa kupezedwa kwa zinthu zimene zinali zosakhalitsa. Njira imene tinadzisungira nayo ingakhaledi itatibvulaza mwamaganizo, mwakuthupi ndi mwamalingaliro. Ndiponso, makolo athu ndi agogo athu angakhale asanadziwe bwino Malemba Oyera. Chifukwa cha chimenecho, miyezo ndi malamulo a khalidwe labwino amene iwo anachitira nawo zinthu zao za moyo ingakhale isanali yogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Iwo angakhale anali kuchita machitachita achipembedzo onyoza Mulungu. Chotero, ngakhale “mwambo” umene tingakhale titalandira kuchokera kwa makolo athu ponena za khalidwe sunachititse kukhala kwathu ndi moyo wokhala ndi chifuno. –Yerekezerani ndi Mateyu 15:3-9.

25. Kodi ndi motani m’mene mawu a 1 Petro 1:10-19 angaperekere chilimbikitso champhamvu kwa ife kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova Mulungu ndi Ambuye wathu Yesu Kristu?

25 Ndithudi, mawu a mtumwi Petro alidi chilimbikitso kwa ife choumiririra ku chosankha chathu cha kutumikira Yehova Mulungu monga ophunzira odzipereka a Yesu Kristu. Sitiyenera konse kulola kudzilola ife eni kuiwala za chikondwerero chaphamphu chimene aneneri Achihebri ndi angelo anasonyeza m’zibvumbulutso zaumulungu zonena za chipulumutso. Tiyenitu nthawi zonse tikumbukire kutsimikizirika kwa chiweruzo cha Mulungu, kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chathu pa bvumbulutso la Yesu Kristu, kufunika kwa kukhala oyera mu khalidwe lathu lonse chifukwa chakuti chiyero cha Yehova chimakufuna, ndi chenicheni chakuti nyengo ya kukhala kwathu ndi moyo m’dziko lino iri nthawi ya kukhala alendo chabe. Koposa zonse, tiyenitu tisasiye konse, inde osasiya konse, kuyang’ana pa chenicheni chakuti taomboledwa ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu Kristu!

26. Kodi ndi motani m’mene zinthu zimene dziko lino lingapereke zingakhalire poyerekezera ndi zimene timapeza kuchokera m’kutumikira Yehova?

26 Zikayerekezeredwa ndi madalitso amene amachokera m’kutumikira Wammwambamwambayo, zinthu zodzionetsera za dziko lino ziri kwenikweni zapadzala. (1 Akorinto 7:29-31; Afilipi 3:7, 8) Palibe kuchuluka kuli konse kwa ndalama kumene kungathe kugula chikumbu mtima choyera, moyo watanthauzo pa tsopano lino ndi m’tsogolo mosatha mwa kukhalandi moyo kwachimwemwe. Komatu utumiki wokhulupirika kwa Mulungu umadzetsa madalitso oterowo. Ha, ndi chifukwa champhamvu chotani nanga chimene tiri nacho chopangira umenewu kukhala nkhawa yathu yaikulu m’moyo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena