Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bw mutu 5 tsamba 50-60
  • Chitsanzo Changwiro—Kristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Changwiro—Kristu
  • Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MMENE YEHOVA AMAWONERA MWANA WAKE
  • ZOTULUKAPO ZOCHOKERA ‘M’KUMKA KU MWALA WAMOYO’
  • Mpingo Wodzozedwera Kulengeza Ufumu
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Chiyembekezo Chokhala ndi Chitsimikiziritso Chotsimikizirika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Kodi Yesu Analidi Mwana wa Mulungu?
    Galamukani!—2006
  • “Njira Choonadi ndi Moyo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
bw mutu 5 tsamba 50-60

Mutu 5

Chitsanzo Changwiro—Kristu

1. Kod nchiyani chimene chikufunika kuti ife tifune kutsanzira Yesu Kristu?

KUTI ife tisonkhezeredwe kutsatira munthu wina mwamtima wonse, tiyenera kukhulupirira kuti chitsanzo chake nchoyenera kutsanziridwa. Pamene tilemekeza kwambiri ndi pamene tikonda kwambiri munthu ameneyo, ndi pamenenso chikhumbo chathu cha kukhala ngati iye chimakhala chachikulu kwambiri. Chotero ukulu wa m’mene tikutsanzirira Yesu Kristu monga chitsanzo chathu umadalira kwakukulukulu pa kumkonda ndi kumyamikira kwathu kwambiri. Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kukula m’kukonda kwathu Mwana wa Mulungu?

2, 3. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti kufika kwathu pa kudziwa Yesu Kristu sikuli kodalira pa kumuona kwathu kwenikweni? (b) Kodi nchifukwa ninji Ayuda ambiri amene anaona kwenikweni Mwana wa Mulungu sanafike pa kumzindikira iye?

2 Mofanana ndi ambiri amene anakhala Akristu pambuyo pa imfa ya yesu m’zaka za zana loyamba, ife enife sitinaone Mwana wa Mulungu. (1 Petro 1:8) Koma kusamuona kwathu ndi maso athu enieniwa sindiko chopinga kufika kwathu pa kumkonda mokulira kwambiri moonjezereka. Ambiri amene anaona kwenikweni Yesu Kristu m’thupi sanafike pa kum’dziwa. Iwo anamlingalira monga momwe iwo analingalirira kuti Mesiya nayenera kukhala, ndipo anakhumudwa. Mwa chitsanzo, anthu a m’dera la kwao anati: “Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi? Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Mariya? ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?”—Mateyu 13:54-57.

3 Zowonadi, maso ndi makutu a awo amene ananena mwa njira yopanda chikhulupiriro imeneyi sanapereke chidziwitso cholondola ku maganizo ndi mitima yao. Chifukwa chakuti iwo anamtsimikizira ndi kaonekedwe ka kunja, kukhala monga wochokera m’banja lonyozeka la mmisiri wopala matabwa, iwo analephera kuzindikira Yesu kukhala Mesiya wolonjezedwayo, Mwana wa Mulungu. Tanthauzo la zozizwitsa za Yesu linali losadziwika m’maganizo mwao. Iwo ananona mikhalidwe yake yabwino kwambiri koma anailingalira molakwa.

4. Kodi ndi motani mmene tingafikire pa kudziwa Mwana wa Mulungu bwino kwambiri, ndipo kodi ndi ziti zimene ziri zina za zinthu zimene tingaphunzire kuchokera ku magwere amenewa?

4 Ife, ku mbali ina, tingathe kufika pa kudziwa ndi kukonda Yesu Kristu mokulira kwambiri mwa kulingalira mosamalitsa ndi mwapemphero zimene Malemba amatiuza ponena za iye. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 1:1-4.) Baibulo limapereka chithunzi chosangalatsa kopambana cha Mwana wa Mulungu. Ngakhale kuli kwakuti iye anali wangwiro, Yesu Kristu sanali wosuliza kwambiri kapena wochita umbuye m’machitidwe ake ndi anthu obvutika. (Mateyu 9:10-13) Nzeru zake zapamwamba kwambirizo sizinapangitse ena kuona kukhala osadziwa kanthu kapena osapeza bwino pamaso pake, popeza kuti iye anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” (Mateyu 11:29) Ngakhale ana sanali kumuopa. (Mateyu 19:13-15) Yesu Kristu analingalira zofooka za ophunzira ake ndipo modekha anabwereza maphunziro ofunika kwambiri. (Yohane 16:12) Poona odwala ndi osowa mauzimu, iye anasonkhezeredwa ndi chisoni ndipo mokondwa anawathandiza. (Mateyu 9:36; Marko 6:34) Kukondweretsedwa kwake ndi osauka kukusonyezedwa ndi chenicheni chakuti iye ndi atumwi anali ndi thumba limodzi la ndalama m’limene iwo akanatapamo zina kuthandiza nazo osowa. (Yohane 12:4-6; 13:29) Mwamphamphu Mwana wa Mulungu anadzigwiritsira ntchito iye mwini mokwanira kaamba ka ena, ndipo molimba mtima anasonyeza poyera chinyengo ndi cholakwa. (Mateyu 23:2-35) Potsirizira pake, motsimikizira chikondi chake chachikulu kaamba ka mtundu wonse wa anthu, iye anapereka moyo wake. (Yohane 15:13) Ha, ndi chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga cha kulimba mtima, kudzichepetsa ndi chikondi chimene Mwana wa Mulunguyo anapereka kwa ife!

MMENE YEHOVA AMAWONERA MWANA WAKE

5. Kodi ndi chidziwitso chofunika chotani ponena za Yesu Kistu chimene, sichingathe kupezedwa mwa mphamvu zakuthupi za kuona, kumva ndi kukhudza?

5 Ndiponso, Malemba okha amatiphunzitsa m’mene Yehova Mulungu amaonera Mwana wake. Chidziwitso choterocho ponena za Yesu Kristu sichingathe kupezedwa mwa kuona kwa maso akuthupi chabe, kumva ndi kukhudza. Mwa chitsanzo, lingalirani, mawu a mtumwi Petro kwa okhulupirira anzake onena za udindo wolemekezeka wa Mwana wa Mulungu ndi mapindu amene amachokera mkupita kwa iye. Mtumwiyo analemba kuti:

“Amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu, inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba yauzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu. Chifukwa kwalembedwa m’lembo, Tanonani, ndiika m’Ziyoni mwala wotsiriza wa pangondya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.” (1 Petro 2:4-6)

Kodi amenewa anatanthauzanji kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba?

6. (a) M’zaka za zana loyamba, kodi ndi motani mmene okhulupirira anali kudzera kwa Mwana wa Mulungu “monga mwala wamoyo”? (b) Kodi nchifukwa ninji moyenerera Yesu akutchedwa “mwala wamoyo”?

6 Mwa kubvomereza Yesu Kristu kukhala Mbuye wao ndi munthu mwa amene iwo akanatha kupeza chipulumutso, iwo anadza kwa iye “monga kwa mwala wamoyo.” Mawu’wo mwala wamoyo” ali oyenerera kwambiri. Yesu Kristu Sali ngati mwala wamba, wozizira, wopanda moyo ku umene palibe zinthu zochirikiza moyo zingatengedweko. Mwana wa Mulungu ali ngati thanthwe pa limene Aisrayeli analandirako madzi mozizwitsa m’chipululu. Malinga ndi kunena kwa mtumwi wouziridwa Paulo, “thanthwe limenelo linatanthauza Kristu.” Linali chizindikiro kapena phiphiritso la Mwana wa Mulungu. (1 Akorinto 10:4) Yesu iye mwini anati:

“Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.” (Yohane 7:37) “Iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:14)

Motero Mwana wa Mulungu anasonyeza kuti chiphunzitso chake, ngati chitamwedwa ngati madzi otsitsimutsa, chikatsogolera ku chipulumutso-ku moyo wopanda mapeto. Ndiponso, Yesu Kristu anali atapatsidwanso mphamvu yopatsa moyo. Chifukwa cha chimenecho, mofanana ndi Atete wake, iye angathe kupatsa ena moyo pa maziko a nsembe yake yotetezera machimo, akumawaukitsa kuchokera kwa akufa.—Yohane 5:28,29.

7. Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu anakanidwira monga “mwalawamoyo”?

7 Monga momwe Petro anasonyezera, Yesu ‘anakanidwa, zowonadi, ndi anthu.’ Makamaka atsogoleri achipembedzo onyadawo sanaone kanthu mwa Mwana wa Mulungu kamene anakalingalira kukhala koyenerera kukatsanzira. Iwo sanayamikire kumvera chifundo ndi kukonda kwake mtundu wa anthu kopereka chitsanzoko. Pamene Yesu anapereka chithandizo chauzimu kwa anthu odziwika kukhala ochimwa, atsogoleri achimpembedzowo anatsutsa kuti: “Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nawo.” (Luka 15:2) Iwo anaona m’mene Mwanayo mwachifundo anagwiritsirira ntchito Sabata kutsegula maso a akhungu, kuchiritsa odwala ndi kumasula opunduka ku zopweteka zao. Koma m’malo mwa kusangalala ndi kutamanda Mulungu, atsogoleri achipembedzo anadzazidwa ndi mkwiyo nalinganiza kumupha. (Mateyu 12:9-14; Marko 3:1-6; Luka 6:7-11; 14:1-6) Iwo anauza munthu wakhungu amene anabwerezeretsedwa kuona kwake kuti: “Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.” (Yohane 9:16) Potsirizira pake bwalo lalikulu la mirandu la Ayuda, Sanhedrin, linagamula kuti yesu aphedwe pa mlandu wonamizira wa kuchitira mwano. (Mateyu 26:63-66) Ali ndi cholinga chakuti chilangochi chichitike, olamulira Achiyuda anasintha mlandu wa Yesuwo kuchoka pa kuchitira mwano kukhala kuukira boma. Mosonkhezeredwa ndi iwowo, bwanamkubwa Wachiroma, Pilato, analamula kuti iye aphedwere pa mtengo mofanana ndi waupandu woipa kopambana wa ndale za dziko.—Luka 23:1-24.

8. Kodi Yehova amalingalira Motani Mwana wake?

8 Kachitidiwe ka anthu m’kukana Yesu Kristu monga maziko sikanasinthe kuwerengera Mwana wake kwa Yehova Mulungu mwiniyo. Popeza kuti Wam’mwambamwambayo anamuikiratu kukhala munthuyo mwa amene mtundu wonse wa anthu ukaomboledwa ndi monga “mwala wamoyo” pa umene mpingo Wachikristu ukamangidwapo, Yesu, monga momwe Petro akufotokozera, anali “wosankhika” ndipo anapitirizabe kukhala wotero. Panalibe chikaikiro chiri chonse m’maganizo mwa Atate ponena za kutchita kwa Mwanayo chifuno cha Mulungu popanda cholakwitsa ndi chimodzi chomwe. Yehova anadziwa kuti Mwana wake anali wangwiro m’kudzipereka ndi chikondi. Pa dziko lapansi, Yesu Kristu anatsimikizira chikondi chake chachikulu kwambiri kwa Atate wake mwa kuchita chifuniro cha Atate wake bwino lomwe pamene anali kubvutika kwambiri. Kukhulupirika kwa Mwanayo poyesedwa mowawa kwambiri kunampangitsa kukhala wamtengo wapatali kwambiri m’maso mwa Wam’mwambamwambayo. Chotero mpingo Wachikristu uli wodalitsidwa mwa kukhala naye mong maziko ake uyo amene Yehova Mulungu amamlingalira kukhala Mwana wowerengeredwa kopambana. (Aefeso 2:20-22) Ndipo ziwalo zodzipereka za mpingo umenewu zimayesayesa mwamphamvu kutsanzira njira yokhulupirika ya Yesu Kristu.

9. Kodi nchifukwa ninji okhulupirira a m’zaka za zana loyamba akanakhalira otsimikizira kuti chikhulupiriro chao sichikafika pa kuwagwiritsa mwala?

9 Awo amene mtumwi Petro anawalembera kalata anali ndi lingaliro la Mulungu ponena za Mwana wake. Monga momwe mtumwiyo analongosolera kuti: “Kwa inu tsono akukhulupira, ali wa mtengo wake.” (1 Petro 2:7a) Iwo anazindikira kuti Yesu Kristu anali mwala wapangondya wamaziko wa mtengo wapatali kopambanadi umene Atate anaukhazika m’Ziyoni wakumwamba, kukwaniritsa mawu a Salmo 118:22 ndi Yesaya 8:14; 28:16. Chifukwa cha kukhala mogwirizana ndi kuwerengera Mwana wake kwa Yehova ndi kumkhulupirira monga mwala wapangondya wamaziko, okhulupirira a m’zaka za zana loyamba anatha kukhala ndi chitsimikiziro chakuti sadzakhala ndi kugwiritsidwa mwala, kusokonezeka kwa ziyembekezo zao. Palibe ali yense angathe kuononga maziko a chuma chambiri ndi a mtengo wapatali amene akhazikitsidwa mwamphamvu kumwamba ndipo motero kuchititsa kutayikiridwa kwa awo amene ziyembekezo zao zaikidwa mwamtima wonse pa iwo. Malinga ngati okhulupirira anakhalabe m’chigwirizano ndi Kristu, maziko osagwedezeka a mpingo, iwo anali otsimikizira kulandira cholinga cha chikhulupiriro chao, ndiko kuti, moyo wopanda mapeto. Komabe, osakhulupirira akakhala ndi kutayikiridwa kwakukulu. Mtumwi Petro akupitirizabe kuti:

“Koma kwa iwo osakhulupirira, Mwala umene omangawo anaukana, womwewo unayesedwa mutu wa pangondya; ndipo Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa; kwa iwo akukhumudwa ndi mawu, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.”—1 Petro 2:7b, 8.

10. Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu anakhalira “Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa”?

10 Chifukwa chakuti atsogoleri achimpembedzo ochuka Achiyuda anakana kulandira Mwana wa Mulungu monga chitsanzo chao ndi kumanga ziyembekezo zao za moyo wosatha pa iye, iwo anataya mwai waukulu kwambiri wa kukhala olowa nyumba Aufumu. Yesu Kristu anali atawachenjeza kuti: “Amisonkho [olapa] ndi akazi achiwerewere [olapa] amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 21:31) Njira yotengedwa ndi atsogoleri achipembedzo amenewo sinaletse Yesu kukhala “mutu wa pangondya,” mwala wokometsera wa “nyumba yauzimu.” Ndiponso, mwa kuchitira Yesu Kristu monga mwala umene unali wosayenera pa ntchito yao ya kumanga, anthu amenewa pa nthawi imodzimodziyo anakakamizikabe kumuona kukhala mwala umene unaima pa njira yao. Iwo sakanatha kunyalanyaza Mwana wa Mulungu pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro, pakuti ophunzira ake okhulupirika anapitirizabe molimba mtima kuchitira umboni za iye. (Machitidwe 5:28) Motero Yesu Kristu anakhala thanthwe pa limene onse amene anapitirizabe m’kusakhulupirira kukhumudwa ndi kukhala ndi kugwa kwatsoka. Monga momwe kuliridi kuti okhulupirira enieni aikidwa ku chipulumutso, momwemo awo amene adzitsimikizira kukhala osakhulupirira aikidwa ku kukhala ndi kutayikiridwa. Mwana wa Mulungu ananenanso ponena za iye mwini kuti: “Munthu ali yense wogwera pa mwala uwu adzaphwanyika. Ponena za ali yense amene udzamgwera, udzampera.”—–Luka 20:18, NW.

ZOTULUKAPO ZOCHOKERA ‘M’KUMKA KU MWALA WAMOYO’

11. Kodi ndi motani m’mene okhulupirira a m’zaka za zana loyamba anafikira pa kukhala ofanana ndi “miyala yamoyo”?

11 Okhulupirira a m’zaka za zana loyamba, mwa kulandira Yesu Kristu monga “mwala wamoyo” wamtengo wapatali wosankhidwa ndi Mulungu, anafikira pa kukhala onga “miyala yamoyo.” M’njira yotani? Iwo analeka kukhala ‘akufa m’zolakwa ndi machimo,’ m’malo mwake anakhala ndi “utsopano wa moyo” monga ana a Mulungu. (Aroma 6:5; Akolose 2:13, NW) Kupyolera mwa Kristu, “mwala wamoyo,” mapindu a moyo anaperekedwa kwa iwo. Komabe, iwo sanayenera kungokhala ngundangunda monga miyala yomangira yopanda moyo ndi kusachita chifuno chiri chonse chopindulitsa. Ayi, iwo anayenera kupanga nyumba yogwirizana. Kuti amange nyumba yogwirizana, iwo anafunikira kusonyeza mtundu umodzimodzi wa chikondi cha kudzipereka kwa wina ndi mnzake chimene Wopereka chitsanzo wao anachisonyeza kwa iwo. (Yohane 13:34) Iwo anayeneranso kukhala antchito, monga momwe analiri Yesu Kristu pa dziko lapansi. Mwana wa Mulungu anali womwerekera kwambiridi m’kuchita chifuniro cha Atate wake, akumalabadira zosowa za ena ndi kuwathandiza kuyamba njira yatsopano yomka ku moyo wamuyaya.—Yohane 4:34.

12. Kodi “miyala yamoyo” ikumangidwa kukhala chiyani, ndipo chotero ndi nchiyani chimene chiri thayo lao?

12 Mawu a mtumwi Petro mwamphamvu amagogomezera kuti Akristu amene akumangidwa ndi Mulungu kukhala nyumba yauzimu, chihema chopatulika kapena kachisi, ali ndi ntchito yofunika yoichita. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:5-17; 6:19.) Onani kuti Petro amati: “Inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima.” Inde, kachisi ameneyu wa “miyala yamoyo” alinso ‘unsembe woyera mtima.’ Mkristu ali yense wobadwa ndi mzimu, motero, ali wansembe, akumatumikira mokhulupirika pansi pa Wansembe Wamkulu wokwezeka Yesu Kristu. Mkristu woteroyo samafunikira munthu ali yense kapena bungwe la anthu kuti limuike pa udindo wa unsembe. Monga wansembe, ntchito yake ndiyo kupereka nsembe zauzimu zolandirika kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 2:5) Koma kodi nchiyani chimene chiri nsembe zimenezi?

13-15. Kodi nchiyani chimene chiri “nsembe zauzimu,” ndipo kodi ndi motani m’mene zimenezi zingatsimikiziridwire Mwamalemba?

13 Petro akunena kuti izo ndi “zauzimu,” chotero sindizo nsembe za nyama kapena za dzinthu zoperekdwa pa guwa lansembe lenileni. Nthawi ya kupereka nsembe zenizeni za mtundu umenewu inatha pamene Mwana wa Mulungu anadzipereka iye mwini kukhala nsembe yolandirika yotetezera machimo.—Ahebri 10:11,12.

14 Ngakhale m’Malemba Achihebri timapezamo zisonyezero za mtundu wa “nsembe zauzimu” zolandirika, monga ngati m’mavesi otsatirapo’wa: “Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko.” (Salmo 50:14) “Apereke nsembe zachiyamiko, nafotokozere ntchito zake ndi kupfuula mokondwera.” (Salmo 107:22) “Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.” (Salmo 141:2) “Tidzapereka mawu a milomo yathu ngati ng’ombe.” (Hoseya 14:2) Chotero “nsembe zauzimu” zikaphatikizamo zinthu zoterozo zonga ngati pemphero, chitamando ndi chiyamiko.

15 Malemba Achikristu Achigriki amatipatsa mfundo zina zoonjezereka. Timauzidwa kuti: “Kupyolera mwa iye [Kristu] tiyeni nthawi zonse tipereke kwa Mulungu nsembe ya chitamando, ndiko kuti, chipatso cha miromo yathu imene imapereka chilengezo chapoyera ku dzina lake. Ndiponso, musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana ndi ena zinthu, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zoterozo.” (Ahebri 13:15, 16, NW) Mu Afilipi 2:17, NW, mtumwi Paulo amanena za “nsembe ndi utumiki wapoyera zimene chikhulupiriro chakutsogoleraniko,” ndi pa zimene iye mwini anali “kutsanulidwa monga ngati nsembe ya chakumwa.” Mavesi amenewa akugogomezera kufinika kwa kukhala wodera nkhawa mokangalika ndi thanzi lauzimu ndi lakuthupi la ena, kukhala ofunitsitsa kuonongera iwowo nthawi, nyonga ndi chuma. Nkhawa yoteroyo imasonyezedwa mwa kuuza ena anthu anzathu uthenga wa Mulungu ndi kuthandiza anthu osowa mwakuthupi, monga momwe anachitira Wopereka Chitsanzo wao, Yesu Kristu. Tangoziganizirani, Wam’mwambamwambayo amalingalira zimene atumiki ake amachita kupititsa patsogolo thanzi la anthu anzao monga nsembe yokondweretsa yachitamando.

16, 17. Kodi pali zifukwa zabwino zotani zopereka “nsembe zauzimu” zoterozo ndi kulengeza “zoposazo” za Mulungu?

16 Chifukwa cha zinthu zabwino kwambiri zimene Yehova Mulungu wachita kwa iwo kupyolera mwa Mwanayo, okhulupirira a m’zaka za zana loyamba anali ndi chifukwa chabwino chomvera kukhala osonkhezeredwa “kupereka nsembe zauzimu.” Pa nthawi ina iwo anali mu “mdima waukulu ndi opanda chiyembekezo. Pamene anali mbali ya dziko, iwo anali pansi pa ulamuliro wa “wolamulira” wake, Satana, “wolamulira wa mdima.” (Yohane 14:30; Akolose 1:13) Anthu osakhala Achiyuda anali osadziwa kanthu kotheratu ponena za Mulungu woona ndi zifuno zake. Iwo analibe chiyanjo pamaso pake. Mtumwi Petro anasonyeza chenicheni chimenechi pamene iye anati: “Kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.” (1 Petro 2:10) Inde, mwa kulandira Yesu Kristu, ponse pawiri Ayuda ndi osakhala Ayuda anakhala “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.” (1 Petro 2:9) Iwo “anasankhidwa” ndi Mulungu kukhala anthu ake, oitanidwa kukhala mafumu ndi ansembe mogwirizana ndi Yesu Kristu, kupanga mtundu wopatulidwira chifuno choyera kapena chopatulika, ndipo anagudwa kukhala chuma chake cha Wam’mwambamwambayo ndi mwazi wa mtengo wapatali wa Mwana wake. (Yerekezerani ndi Eksodo 19:5, 6; Chibvumbulutso 5:9, 10.) Ha, ndi chisonyezerezo chapadera chotani nanga cha chifundo m’mene chimenechi chinaliri kwa Israyeli wauzimu! Ziwalo za “mtundu woyera mtima” zinakhala ndi chidziwitso cha Mulungu ndi kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu. Zimenezo zinasiyana kwambiri ndi nthawiyo pamene iwo anali mu “mdima,” otalikirana ndi Wam’wambamwambayo ndi osadziwa chifuniro chake ndi chifuno.

17 Polingalira kukhala kwao atapatsidwa chibvomerezo cha Yehova ndi chiyanjo chosachiyenerera, ophunzira a Yesu Kristu amenewa anasonkhezeredwa kulengeza kwa onse zimene Wam’mwambamwambayo wawachitira mwa njira ya Mwana wake. Iwo sakanatha konse kuleka kulankhula ndi ena ponena za “zoposazo,” zochita zodabwitsa, za Atate wao wakumwamba.

18. Kodi ndi kugwiritsira ntchito kotani kwa ife eni kumene tiyenera kupanga kwa zimene talingalira m’mutu uno, ndipo chifukwa ninji?

18 Lero lino ophunzira onse oona a Yesu Kristu, kuphatikizapo awo a “khamu lalikulu” amene akugwirizana ndi “mtundu woyerawo,” mofananamo ayenera kuona kukhala osonkhezereka kukhala ndi miyoyo yolungama ndi kukhala okangalika m’kuthandiza ena kupeza chibvomerezo cha Mulungu. (Chibvumbulutso 7:9-15) Chiyenera kukhala chikhumbo cha mtima wathu kudzigwiritsira ntchiyo enife m’zoyesayesa za kuthangata anthu amene ali osowa mwauzimu. Kutsanizira kwathu koteroko Mwana wa Mulungu kudzachita zochuluka kupangitsa miyoyo yathu kukhala yabwino kwambiri. Ha, ndi chisangalalo chotani nanga chimene tingakhale nacho kukochera m’kuthandizira chimwemwe, kupeza bwino ndi kulimbikitsidwa kwa anthu anzathu! (Mwachitidwe 20:35) Ndipo mwakutero, timapeza chikondi ndi chiyamikiro cha awo amene ife timawaonongera mopanda dyera, nthawi yathu, nyonga ndi chuma. Pamene kuli kwakuti ena angalephere kusonyeza chiyamikiro, ife tiri chikhalirebe ndi chikhutiro chachikulu cha m’kati cha kukhala titakondweretsa Atate wathu wakumwamba. Ndipo chifukwa cha kuchita chifuniro chake, tingathe kukhala otsimikizira kupeza chithandizo ndi chitsogozo chake. (1 Yohane 3:22) Tiyenitu tipitirizebe kututa madalitso ochuluka kuchokera m’kutsanzira chitsanzo cha Uyo amene ali wamtengo wapatali kopambana m’maso mwa Yehova Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena