Mutu 6
Kumvera Ulamuliro Kumene Kuli Kopindulitsa
1. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kugonjera ku malinganizidwe amene alipo nkwanzeru ndi kopindulitsa?
MUNGAKHALE Nzeru m’kumvera, m’kusonyeza kugonjera ku malinganizidwe amene alipo. Ziribe kanthu kuti nkokondweretsa kotani kumene kungakhale nako, kuima pawekha kotherathu nkosafunika, nkosayenera. Palibe munthu mmodzi ali yense pa dziko lapansi amene angathe kuchita kanthu kali konse kapena kudziwa kanthu kali konse. Monga momwedi kuliri kuti ife tiri odalira pa mpweya, dzuwa, chakudya ndi madzi kaamba ka moyo, mofananamo timafunikira anthu ena ndi zimene iwo angathe kutchitira ngati titi tipindule ndi kusangalala ndi moyo.
2. Kodi ndi motani mmene kukhala kwa Yehova Mfumu Yaikulu kopambana kuyenera kuyambukirira miyoyo yathu?
2 Malinganizidwe a boma, maunansi a wolemba ntchito ndi wolembedwa ntchito, zomangira za banja, kugwirizana ndi mpingo Wachikristu, kukhala kwathu kwenikweniko pakati pa anthu, zonsezo zimaika mathayo ena pa ife. Tiri ndi mangawa a kanthu kena mobwezera zimene timalandira kuchokera kwa ena. Chofunika kwambiri m’kuchitira anthu mathayo amenewa ndicho kuzindikira kwathu mawu a Yehova Mulungu. Monga Mlengi, iye moyenerera ndiye Mfumu Yaikulu imene ife timalandirako zinthu zonse. M’masomphenya, mtumwi Yohane anamva akulu 24 akulengeza kuti: “Muyenera inu, Yehova, Mulungu wathudi, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, chifukwa chakuti munalenga zinthu zonse, chifukwa cha chifuniro chanu izo zinakhalako ndipo zinalengedwa.” (Chibvumbulutso 4:11, NW) Kupanga kwathu kubvomereza kofananako ponena za Yehova monga Wam’mwambamwamba sindiko nkhani ya mawu chabe. M’maunansi athu onse, tingathe kusonyeza kuti ife tiri ogonjera ku chifuniro cha Mulungu kaamba ka ife ndi kubvomereza Yesu Kristu kukhala Mbuye wathu woikidwa.
“CHIFUKWA CHA AMBUYE”
3, 4. Kodi ndani amene ali ‘zolengedwa za anthu’ zimene ife tiyenera kuzigonjera, ndipo kodi nchifukwa ninji izo ziyenera kusonyezedwa kukhala zotero?
3 Mtumwi Petro mwamphamvu anapereka lingaliro lokwezeka limeneli lonena za chifukwa chachikulu chogonjerera ku ulamuliro wa anthu. Iye analemba kuti: “Chifukwa cha Ambuye dzigonjetsereni ku cholengedwa chaumunthu chiri chonse: kaya kwa mfumu monga wamkulu kapena akazembe monga otumizidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa koma kukayamikira ochita zabwino.”—1 Petro 2:13, 14, NW.
4 ‘Zolengedwa zaumunthu’ zimene tiyenera kuzigonjera ndizo akuluakulu a maulamuliro opangidwa ndi anthu. Iwo ali ‘zolengedwa zaumunthu’ chifukwa chakuti anthu, osati Mulungu, walenga maudindo a mafumu ndi olamulira otsikirapo kapena abwanamkubwa. Wam’mwambamwamba wangolola amenewo kukhalapo ndipo akuwalekerera, popeza kuti iwo amatumikira chifuno chabwino pansi pa mikhalidwe iripoyi. Chifukwa cakuti pali maulamuliro a boma mololedwa ndi iye, munthu amene amawapandukira akupandukira “kakonzedwe ka Mulungu,” kakonzedwe kamene iye kufikira pa nthawi ino sanakaone kukhala koyenera kukathetsa ndi kuika m’malo mwake ufumu wakumwamba wokhala m’manja mwa Mwana wake. (Aroma 13:1, 2, NW) M’masiku a mtumwi Petro, mfumu Yachiroma kapena Kaisara anasankha abwanambkubwa kuti azikayendetsa zinthu m’zigawo za ufumuwo, kuphatikizapo Yudeya. Abwanamkubwa amenewa anali ndi thayo mwachindunji kwa mfumu m’kusungitsa lamulo ndi bata m’dera limene liri pansi pa ulamuliro wao. Pamene iwo anali kuchita ntchito zao, abwanamkubwawo ‘ankapereka chilango pa ochita zoipa’-olanda, achifwamba, mbala ndi oukira boma. Koma iwo anakaperekanso “chiyamiko kwa ochita zabwino,” ndiko kuti, kulemekeza anthu olungama mwa kuwachititsa kudziwidwa bwino ndi anthu onse monga anthu oyenera ndi mwa kutetezera iwo eniwo, chuma ndi zoyenera zao.
5. Kodi ife tiyenera kukhala ogonjera chifukwa cha yani, ndipo kodi nchifukwa ninji iye moyenerera akutchedwa “Ambuye”?
5 Si kwakukulukulu kuti apewe chilango ndi kudzipezera “chiyamiko” kuti Akristu akufulumizidwa kukhala ogonjera. Koma kuli “chifukwa cha Ambuye.” Ambuye ameneyu ndiye Yesu Kristu, pakuti mtumwi Petro poyambirira pomwe anamdziwikitsa kukhala wotero. (1 Petro 1:3) Malemba amanena za Mwana wa Mulungu kukhala “Ambuye wa akufa ndi amoyo.” (Aroma 14:9) Chifukwa cha chimenecho, iye, ali ndi udindo umene palibe wolamulira waumunthu ali yense anayamba wakhala nawo. Monga “Mbuye wa akufa,” Yesu Kristu angawaitanire pamaso pake mwa kuwabwezeretsa ku moyo. Ukulu wa umbuye wa Yesu umapyola pa kukhala kwake ndi ulamuliro pa amoyo ndi anthu akufa omwe. Pambuyo pa kuukitsidwa kwa iye mwini, Mwana wa Mulungu anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18, NW) Ndithudi, ndi nzeru kwa ife kumvera olamulira aumunthu chifukwa cha Uyo amene ali ndi ulamuliro waukulu kopambana, koposa umene iwo ali nao.
6, 7, Kodi ndi motani mmene timadzigonjetserera kwa olamulira a anthu “chifukwa cha Ambuye”?
6 Kodi nchiyani chimene chimatanthauzidwa ndi kudzigonjetsera ife eni kwa anthu okhala ndi udindo wapamwamba wa boma “chifukwa cha Ambuye”? Kuzindikira kwathu Yesu Kristu monga Mbuye wathu kuyenera kukhala mphamvu yosonkhezera yokhala kutseri kwa kugonjera koyenera olamulirawo. Mwana wa Mulungu anapereka chitsanzo chabwino kopambana ponena za nkhani imeneyi. Iye sanaukire zofuna za ulamuliro wa boma ndiponso iye sanaphunzitse ena kuchita motero. M’malo mwake, iye anafulumiza kuti: “Ngati munthu wokhala ndi ulamuliro akukakamiza kumperekeza mu utumika kwa mtunda umodzi, pita naye mitunda iwiri.” (Mateyu 5:41, NW) ‘Perekani kwa Kaisara zinthu za Kaisara.”—Mateyu 22:21.
7 Nthawi zina maboma angalamule anthu kulembetsa m’kaundula kaamba ka zifuno zosiyanasiyana, kapena iwo angapemphe kuchirikiza ntchito zina za kumanga chitaganya ndi za ulimi, mwina mwake mogwirizana ndi kupanga miseu, madamu kapena masukulu. (Yerekezerani ndi Luka 2:1-3.) M’nkhani zonsezi, ndithudi, chikumbu mtima Chachikristu chiyenera kulingaliridwa. Komabe, kumene kulibe nkhani yobvuta yolowetsedwamo imene ikabvutitsa chikumbu mtima chophunzitsidwa ndi Malemba, zingathe kuthandizira kupititsidwa patsogolo kwa “mbiri yabwino” pamene Mkristu achita zimene angathe kudzisonyeza iye mwini kukhala wombera ndi wogwirizanika. Kukakhala kosayenera kwambiridi kuyambitsa kutsutsana ndi iri yonse ya ntchitozo kapena kukhala wopandukira weniweni ulamuliro wa boma pa mlingo uli wonse. Chilangizo cha Baibulo ndicho “kukhala ogonjera ndi kukhala omvera maboma ndi maulamuliro monga olamulira, kukhala okonzekera kaamba ka ntchito iri yonse yabwino.” Mkhalidwe wa kukangana, kunyoza sumagwirizana ndi chiphunzitso ndi chitsanzo cha Mwana wa Mulungu—Tito 3:1, 2, NW.
“MONGA AKAPOLO A MULUNGU”
8. Kodi ndi mapindu otani amene angadze kuchokera ku kugonjera koyenera kwa olamulira?
8 Posonyeza m’mene kumvera ulamuliro koyenera kumatumikirira kupititsa patsogolo njira ya kulambira kowona, mtumwi Petro akulemba kuti: “Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa.” (1 Petro 2:15) Akristu, mwa kuchita zimene olamulira amazilingalira kukhala zabwino, zoyenera kapena kumvera lamulo pamene, pa nthawi imodzimodziyo, akusunga chikumbu mtima chabwino pamaso pa Mulungu, angayamikiridwe. Kumeneku kumachititsa kutontholetsedwa kwa anthu osadziwa amene monyenga amaneneza atumiki a Wam’mwambamwambayo za kukhala ouma khosi, osagonjera, osatsungula, oukira kapena ofuna kugubuduza boma. Khalidwe labwino la Akristulo motero limatsimikizira kukhala chitetezo chabwino kopambana pa kunenezedwa molakwa kwa dzina lao labwinolo.
9, 10. Kodi nchifukwa ninji kugonjera kwathu ku ulamuliro wa boma sikuli kofanana ndi kugonjera kwa kapolo woumirira kwa mbuye wake?
9 Koma kodi kumvera olamulira kwa Mkristu kumatanthauza ukapolo wobvutika kwa iwo, kukhala ogonjera kotheratu? Yankho louziridwa ndiro, Ayi. Mtumwi Petro akupitiriza kuti: “Khalani monga anthu aufulu, ndipo komabe osakhala ndi ufulu wanuwo, monga chophimbira zoipa, koma monga akapolo a Mulungu.”—1 Petro 2:16, NW.
10 Monga Akristu, tamasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Yohane 8:31-36) Mwana wa Mulungu watimasulanso ku kuopa imfa yachiwawa, njira ya kuopa imeneyi yakhozetsa Satana Mdierekezi kuchitisa anthu kukhala mu ukapolo, akumawayendetsa, kupyolera mwa malamulo a anthu otsendereza polamulira, kuchita mosemphana ndi chikumbu mtima chao. (Ahebri 2:14, 15) Komabe, chifukwa cha kukhala anthu aufulu, chikumbu mtima chathu sichingakhale chogonjera ku zolamula ndi ziopsezo za munthu ali yense kapena kagulu ka anthu. Kumvera kwathu olamulira kuli kodzifunira munthu mwini ndipo kumaikiridwa malire ndi malamulo apamwamba a Mfumu Yaikulu kopambana, Yehova Mulungu. Sitingathe kukhala akapolo obvutika a munthu aliyense, omapereka kumvera kosafunsa kanthu popanda kulingalira lamulo la Mulungu. Monga momwe mtumwi Petro anasonyezera, Akristu ali “akapolo a Mulungu.” Chifukwa cha chimenecho, ife mokondwa timagonjera ku zofuna za maulamuliro a maboma mpaka kufika pali ponse pamene palibe kuombana kwachindunji ndi kulambira kwathu Wam’mwambamwambayo. Ngati zitakhala mwa njira ina, tiyenera kutenga kaimidwe kamene kanasonyezedwa ndi Petro ndi atumwi ena pamene anali pamaso pa bwalo lalikulu la mirandu la Ayuda: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.” —Machitidwe 5:29, NW.
UFULU, WOKHALA NDI MALIRE
11. Kodi ndi kaimidwe ka maganizo kotani kulinga ku ulamuliro wa boma kamene kakapanga kugwiritsira ntchito molakwa ufulu Wachikristu?
11 Komabe, kukakhala kolakwa kwa ife kukhala ndi moyo monga ngati kuti maboma a ndale za dziko analibe ulamuliro pa ife, kuwanyoza m’nkhani zimene siziri zosemphana ndi lamulo la Mulungu. Mkhalidwe wopanda ulemu woterowo umapanga kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa Ufulu Wachikristu. Ufulu umene tiri nawo wamangika ndi kukhala kwathu akapolo a Mulungu. Sumapereka chilolezo chochotsera ziletso zoyenera, kuchita zoipa kapena kunyozetsa malamulo amene angatidodometse koma amene alinganizidwa kutetezera moyo ndi malo okhala. M’malo mwake, tiyenera kusonyeza mwa khalidwe lathu kuti timazindikira chifuno chabwino chimene, chiri kutseri kwa malamulo a pamseu, malamulo oletsa kuipitsa, ziletso za kusaka nyama ndi kusoza nsombba ndi ena ofanana nawo.
12. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira mtundu wa mathayo amene ife tiri nawo kwa ena?
12 Inde, tiri ndi mathayo kwa ena. Mtundu wa mathayo amenewa umayambukiridwa ndi unansi wakutiwakuti umene tiri nao ndi Yehova Mulungu ndipo ndi anthu anzathu. Mtumwi Petro akusonyeza mathayo amenewa ndipo akulangiza kuti: “Chitirani anthu onse ulemu, kondani gulu lonse la abale, opani Mulungu, lemekezani ufumu.”—1 Petro 2:17, NW.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu onse ali oyenera ulemu? (b) Kodi ife tiri ndi mangawa a chiyani kwa abale athu auzimu? (c) Kodi nchiyani chimene chiyenera kutsimikizira mtundu wa ulemu umene uyenera kuperekedwa kwa anthu? (d) Kodi nchiyani chimene tiri nacho mangawa kwa Mulungu yekha?
13 Anthu onse ali zipatso za kulenga kwa Mulungu ndipo anagulidwa ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu Kristu. Ndicho chifukwa chake ife moyenerera timawalemekeza, kuwachitira mwaulemu ndi mopanda tsankho. (Machitidwe 10:34, 35; 1 Timoteo 2:5, 6) “Komabe gulu lonse la abale,” nloyenereratu woposa ulemu wa nthawi zonse chabe umene uli woyenerera kwa anthu onse. Kwa abale athu, ife moonjezereka tiri ndi mangawa a chikondi chachikulu, chikondi chapamtima. Ndiponso, pamene kuli kwakuti mfumu ya pa dziko lapansi ndi akuluakulu ena ocheperapo ayenera kupatsidwa ulemu umene udindo wao umafunikiritsa, Mulungu Wam’mwambamwamba yekha ndiye amene ali ndi kuyenera kwa kuopedwa kwaulemu ndi kolambira. Chifukwa cha chimenecho, ulemu umene ukuperekedwa kwa munthu ali yense nthawi yonse uyenera kukhalandi polekezera kochititsidwa ndi kulingalira kwabwino Yehova Mulungu ndi malamulo ake. Mwa chitsanzo, palibe choletsa kutchula olamulira ndi maina ao aulemu amwambo pamene amenewa samapereka kwa iwo mtundu wa ulemu umene uli wa Mulungu yekha. Koma anthu okhoza kufa Sali apulumutsi a Akristu ndiponso sindiwo kumene kudzachokera madalitso onse. (Salmo 146:3, 5; Yesaya 33:22; Machitidwe 4:12; Afilipi 2:9-11) Chifukwa cha chimenecho, Mkristu woona samatcha anthu m’njira imene ikachititsa kukaikiridwa kwa kuopa kwake Mulungu ndi kukweza olamulira pamwamba kwambiri koposa m’mene malo ao a ntchito amafunira.
KODI AKULUAKULU ONSE ALI OYENERERA ULEMU?
14, 15. (a) Kodi nchifukwa ninji mkhalidwe wa wolamulira kapena mkulu wa boma sumayambukira ponena zakuti kaya Mkristu akamlemekeza? (b) Kodi tingaphunzirenji kuchokera m’njira imene mtumwi Paulo anachitira ndi akulu a boma?
14 Polingalira chilangizo cha Baibulo cha kulemekeza olamuliracho, anthu ena angafunse za mkulu wa boma wakutiwakuti: “kodi ndi motani m’mene ndingapatsire ulemu kapena kulemekeza munthu wina amene angakhale wa makhalidwe oipa?” Mfundo yoikumbukira ndiyo yakuti kakhalidwe ka makhalidwe a mkulu wa bomayo sindiko maziko a ulemu woterowo. M’malo mwake, ulamuliro umene iye amaimira ndi kuuchita umafunikiritsa mtundu wakutiwakuti wa ulemu. Pakanakhala kuti panalibe kulemekezedwa kwa ulamuliro woikidwa moyenera, pakanangokhala chipolowe chokhachokha, limodzi ndi kuwonongeka kwa chitaganya kotulukapo, kuphatikizapo kwa Akristu.
15 Machitidwe a mtumwi Paulo ndi akuluakulu a boma amasonyeza kuti chimene olamulira ali monga anthu chiribe kanthu ndimtundu wa ulemu umene uyenera kusonyezedwa kwa iwo. Wolemba mbiri wakale Tacitus analongosola Bwanamkubwa Wachiroma Felike kukhala munthu amene “anaganiza kuti akanatha kuchita choipa chiri chonse popanda kulangidwa, “ ndi amene, “anachita ulamuliro wa mfumu uli wonse wa nkhanza ndi zopa, anachita ulamuliro wa mfumu mu mkhalidwe wa ukapolo.” Komabe, molembekeza udindo umene Felike anali nao, Paulo mwaulemu anayamba kudzikanira kwake pamaso pa munthu ameneyu ndi mawu awa: “Podziwa bwino lomwe kuti inu mwaweruza mtundu uwu kwa zaka zambiri, mokondwa ndikulankhula modzitetezera pa zinthu zonena za ine mwini.” (Machitidwe 24:10, NW) Mosasamala kanthu za chenicheni chakuti Mfumu Agripa Herodi II anakwatira mlongo wake, Paulo anamsonyeza ulemu woyenera, mwa kunena kuti: “Ndidziyesa wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndizikanira lero pamaso panu, makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda.” (Machitidwe 26:2, 3) Ngakhale kuli kwakuti Bwanamkubwa Festo anali wolambira mafano, Paulo analankhula nayebe mwa monga “Wolemekezeka Inu.”—Machitidwe 26:25.
KUKHOMA MISONKHO
16. Kodi ndi uphungu wotani umene Akristu akupatsidwa pa Aroma 13:7?
16 Kuphatikiza pa kupatsa anthu mtundu wa ulemu umene umayenerana ndi ulamuliro wao, Akristu alinso pansi pa lamulo la Mulungu la kukhala osamalitsa ponena za kukhoma misonkho. Malemba amatiuza kuti: “Perekani kwa onse mangawa ao, kwe iye wofuna msonkho, msonkho; kwa iye wofuna thangata, thangata; kwa iye wofuna kuopedwa [chifukwa cha ulamuliro wake kuphatikizapo mphamvu ya moyo ndi imfa], kuopa kotero; kwa iye wofuna ulemu, ulemu woterowo,” (Aroma 13:7) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kukhoma misonkho ndi kukhala woona mtima m’kudziwitsa ndalama zopezedwa?
17. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kuona kukhomedwa kwa misonkho kukhala kofanana ndi kuperekedwa kwa ngongole? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala opereka chitsanzo chabwino m’kukhoma misonkho yonse?
17 Maulamuliro olamulirawo amapereka mautumiki ofunika kwambiri kutsimikiziritsa ubwino, chisungiko ndi thanzi la nzika zao. Amene akuphatikizidwamo ndiwo kukonzedwa kwa miseu, makonzedwe a magulu osungitsa malamulo, makhothi, masukulu, mautumiki a ukhondo, magulu a za mtengatenga ndi ena ofanana nawo. Kaamba ka mautumiki operekedwawo, boma liri loyenerera kulipiridwa. Chifukwa cha chimenecho, Akristu moyenerera amaona kukhoma misonkho ndi thangata monga kulipidwa kwa mangawa. M’mene kwenikweni maulamuliro olamulirawo adzagwiritsirira ntchito misonkho yolandiridwayo pambuyo pake sindiro thayo la Mkristu. Kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa msonkho kapena thangata wolandiridwa kochitidwa ndi akuluakulu sikumapatsa Mkristu kuyenera kwa kukana kulipira mangawa ake. M’kakonzedwe katsopano lino ka zinthu, iye amafunikira mautumiki a boma ndipo, chifukwa cha chimenecho, m’chikumbu mtima chabwino, amalipira zimene zikufunidwa. Pamene tifika pa kulipira munthu wina mangawa, kugwiritsira ntchito ndalama molakwa kwa munthu ameneyo sikukafafaniza ngongoleyo. Mofananamo, mosasamala kanthu za zimene maboma angachite, Mkristu samachotseredwa thayo lake la kukhoma misonkho ndi thangata. Iye ayenera kukhala chitsanzo chabwino m’kuchita mogwirizana ndi zofunika za lamulo m’kunena ndalama zolandiridwa kapena kugulidwa kwa zinthu zimene zimafunikira kuti ndalama za kasitomu zilipiridwe. Kusamalitsa kwake pa zinthu zimenezi kumapewetsa kudzetsa chitonzo pa iye ndi mpingo Wachikristu. Kumaikanso kulambira koona m’kaonededwe kabwino, molemekezetsa Mulungu ndi Kristu.
MAUNANSI A WOLEMBA NTCHITO NDI WOLEMBEDWA NTCHITO
18. Kodi maprinsipulo a malemba onena za unansi wa mbuye ndi kapolo angathe kugwiritsiridwa ntchito pa mikhalidwe yotani ya tsopano lino?
18 Unansi wa Mkristu ku ulamuliro wa boma sindiwo unansi wokha umene umafunikira kugonjera koyenera. Mwa chitsanzo, pa ntchito pake, iye angakhale wofunikira kumvera woyang’anira kapena kapitao. Kalekale m’zaka za zana loyamba C.E. pamene ukapolo unali wofala mu Ufumu Wachiroma, Akristu ambiri anapezeka akugwira ntchito monga akapolo kapena atumiki. Moyenerera, Mawu a Mulungu amafotokoza mathayo ao kulinga kwa Ambuye ao. Ife lero lino tingathe kugwiritsira ntchito malamulo a khalidwe labwino onena za kakhalidwe mu unansi wa mbuye ndi kapolo ku unansi wa wolemba ntchito ndi wolembedwa ntchito.
19. Kodi ndi uphungu wotani umene Petro anapereka kwa atumiki a m’nyumba Achikristu?
19 Polunjikitsa uphungu wake kwa atumiki a m’nyumba kapena a zapanyumba, mtumwi Petro analemba kuti:
“Antchito a m’nyumba azimvera ambuye ao limodzi ndi kupoa koyenera, osati kokha kwa abwino ndi ofatsa, komanso kwa awo obvuta kusangalatsa. Pakuti ngati munthu, chifukwa cha chikumbu mtima cha kwa Mulungu, apirira zachisoni ndi kubvutika mosalungama, uku ndiko chinthu chabwino. Pakuti pali kuyenera kotani ngati, pamene muchimwa ndi kumenyedwa, mupirira? Koma ngati muchita zabwino ndipo mubvutika, namupirira, chimenechi ndi chinthu chabwino kwa Mulungu.”—1 Petro 2:18-20.
20. (a) Kodi ndi motani mmene mtumiki wa m’nyumba angakhalire wogonjera ‘ndi mantha onse oyenera’? (b) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ikanachititsa kubvutika kwa kapolo Wachikristu?
20 Kodi kulabadira uphungu umenewu kunafunanji? Pamene anali kuchita mathayo ake monga kapolo, Mkristu anayenera kusonyeza kuopa koyenera ndi ulemu kwa mbuye wake, osafuna kusamkondweretsa. Kuopa kumeneku kunayenera kusonyezedwa ngakhale ngati mbuyeyo anatsimikizira kukhala wosalingalira bwino, waukali ndi wosanganizira bwino m’zofunsira zake. Mbuyeyo angakhale munthu amene anasuliza ngakhale ntchito imene inali itachitidwa bwino lomwe. Iye anagakhale atafunsira kuti kapolo Wachikristu achite zinthu zimene zinali zosemphana ndi lamulo la Mulungu. Chifukwa cha kumvera mokhulupirika zolamula za chikumbu mtima chake chaumulungu, kapolo Wachikristu angakhale atabvutika mosalungama chifukwa cha kukana kuba kapena kunamira mbuye wakeyo. Ndiponso, pa nthawi zina, kapolo angakhale anali munthu womamenyedwa ndi kutukwanidwa.
21. Kodi ndi ubwino wotani umene ukachokera m’kupirira kodekha kwa kapolo ku kuchitiridwa moipa?
21 Mogwirizana ndi uphungu wa Petro, kapolo Wachikristu sakaukira mbuye wake waukali. Iye akapiritizabe kuchita ntchito yake mosamalitsa, ndi kupirira modekha pochitiridwa moipa. Njira imeneyi ikakhala yabwino m’maso mwa Mulungu, pakuti sikachititsa kuonedwa molakwa kwa Chikristu. Ena angathe kuona kuti kulambira koona kwapereka mphamvu ya kuchita zabwino pa kapoloyo. Kukawasonkhezera kupenda Chikristu kuti aone m’mene kapolo wochitiridwa moipayo angasonyezere kudziletsa koyamikirika koteroko. Mosiyana ndi zimenezo, ngati kapoloyo analakwira mbuye wake ndipo anali kulangidwa mwamphamvu chifukwa cha kulakwako, anthu sakaona kuyenera kwenikweni kwa kulandira kwake chilango modekha.
22. Kodi ndi motani m’mene wolembedwa ntchito Wachikristu akafunira kudzisungira iye mwini pa ntchito?
22 Lero lino Mkristu amene akumana ndi mkhalidwe wobvuta kwenikweni pa ntchito angakhale wokhoza kupeza ntchito ina. Koma zimenezi sizingakhale zothekera nthawi zonse. Iye angakhale akugwiri ntchito ya kontrakiti kapena kukakamizika kugwira ntchito pansi pa mikhalidwe yosankondweretsa chifukwa chakuti ntchito zina sizingapezeke konse. Chotero mkhalidwe wake ungasiyane pang’ono kwambiri ndi uja wa mtumiki wa m’nyumba m’zaka za zana loyamba C.E. amene sakanatha kuchoka kwa mbuye wosalingalira bwino. Chotero, malinga ngati Mkristu apitirizabe kugwirira ntchito munthu wina, iye adzachita zonse zimene angathe kuchita ntchito yabwino kopambana, ndi kupirira modekha ndi mosandandaula ndi kuchitiridwa molakwa kuli konse kumene iye angakhale akuchitiridwa ndi kumene sikungathe kuletsedwa mwa njira Zamalemba. Iye akapiritizanso kuchitira wolemba ntchitoyo mwaulemu woyenera ndi molingalira.
CHITSANZO CHA YESU-CHILIMBIKITSO
23, 24. (a) Kodi ndi chitsanzo cha yani chimene chikatithandiza pamene tikuchitiridwa moipa chifukwa cha kuchita choyenera? (b) Kodi ameneyu anakumana ndi zotani, ndipo kodi ndi motani m’mene iye anachitira?
23 Mwachionekere, si kosabvuta nthawi zonse kwa aliyense kupirira chisalungamo. Komabe, mosangalatsa, ife tiri ndi chitsanzo chabwino kopambana choti titsatire, ndiko kuti, Ambuye wathu Yesu Kristu. Chitsanzo chake chingathe kukhala magwero enieni a chilimbikitso. M’kutonthoza akapolo Achikristu ochitiridwa moipa, mtumwi Petro anasonya ku chitsanzo cha Yesu, kuti:
“Kunena zoona, munaitaniridwa ku njira imeneyi, chifukwa chakuti ngakhale Kristu anakubvutikirani, nakusiyirani chitsanzo choti inu mutsatire mapazi ake mosamalitsa. Iye sanachite chimo, ndipo simunapezeka chinyengo m’kamwa mwake. Pamene iye anali kulalataridwa, sanabwezere kulalata. Pamene anali kubvutika, sanaopseze, koma anapitirizabe kudzipereka iye mwini kwa uyo woweruza molungama.”—1 Petro 2:21-22, NW.
24 Motero mtumwiyo anakumbutsa akapolo Achikristu kuti chimodzi cha zifukwa zimene iwo anaitaniridwa kukhala ophunzira a Mwana wa Mulungu chinali kusonyeza mzimu wofanana ndi wake pokumana ndi kubvutika kosayenera. Makamaka pa tsiku lotsirizira la moyo wake monga munthu pa dziko lapansi, Yesu Kristu anapirira zochuluka. Iye anapandidwa, ameneyedwa nkhonya, analabvuliridwa, anakwapulidwa ndi mkwapulo (umene mwina mwake unamangiriridwa ndi zibenthu za ntobvu kapena pfupa kapena waya waminga kuti uzing’amba thupi), ndipo, potsirizira pake, anakhomeredwa pa mtengo monga ngati mpandu woipitsitsa. Komabe, iye anadzigonjetsera ku zonyozetsa zonsezi, osalalatira konse kapena kuopseza anthu ochititsa kachitidwe kosakayenerera koteroko. Yesu Kristu anadziwa kuti njira yake ya moyo inali yoyera, koma sanachite zinthu monga momwe anafunira kudzidziwikitsa iye mwini kukhala woyenera. Iye anapereka njira yake kwa Atate, ali ndi chidaliro chakuti Mulungu wake ndi Atate akapereka chiweruzo cholungama m’malo mwake. Ifenso, tingathe kukhala otsimikizira kuti Wamphamvuyonse akuona zisalungamo ziri zonse zimene tingakumane nazo. Iye adzalinganiza mipimo ya chilungamo, malinga ngati ife tipirirabe modekha pobvutika. Ndithudi, ngati Mwana wopanda chimo wa Mulungu anali wofunitsitsa kupirira kuchitiridwa moipa, ife atsatiri akefe tiri ndi chifukwa chokulirapodi chochitira motero, pozindikira kuti ife ndife zolengedwa zochimwa.
25. Kodi ndi motani m’mene tapindulira ndi kubvutika kwa Kristu?
25 Kubvutika kumene Yesu Kristu anakumana nako kunali kwenikweni kaamba ka phindu lathu, kutipatsa ife chisonkhezero choonjezereka chomtsanzirira. Mbali imeneyi ikugogomezeredwa m’mawu ena a mtumwi Petro:
“Iye mwini anayamula machimo athu m’thupi lake la iye mwini pa mtengo, m’malo mwakuti ife tikafafaniziridwe machimo ndi kukhala ndi moyo m’chilungamo. Ndipo ‘mwa mikwingwirima yake inu munachiritsidwa.’ Pakuti inu munali ngati nkhosa, zosochera; koma tsopano mwabwerera kwa mbusa ndi woyang’anira wa miyoyo yanu.”—1 Petro 2:24, 25, NW.
26, 27. Kod kutibvutikira kwa Kristu kuyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa ife?
26 Chifukwa cha kukhala kwathu ochimwa, tiri osayenerera mphatso ya moyo. Baibulo limatiuza kuti: “Malipiro amene uchimo umalipira ndiwo imfa.” (Aroma 6:23, NW) Komabe, Yesu Kristu, mofunitsitsa anadzisenzera chilango cha machimo athu, akumafa monga nsembe mofanana ndi mwanawankhosa, wopanda chirema ndi wosandadaula kaamba ka ife. Kupyolera mwa kubvutika kwake ndi chilango chachikulu kopambana cha imfa yochitisa manyazi pa mtengo. Mwana wa Mulungu anapangitsa kukala kothekera kwa anthu okhulupirira kumasulidwa ku uchimo ndi kuyamba kukhala ndi moyo wa chilungamo. Polingalira kubvutika kwa Yesu Kristu kaamba ka ife, tiyeneradi kusonkhezeredwa kusonyeza chiyamikiro chachikulu kwambiri kaamba ka zimene iye watichitira. Uku kumanfunikira kuti ife titsanzire Yesu m’mbali zonse za moyo, kuphatikizapo kukhala kwathu ofunitsitsa kuchitiridwa moipa chifukwa cha chilungamo, monga momwe iye anachitira. Nthawi iriyonse imene tichitiridwa zoipa, tichita bwino kulingalira za kubvutika kumene Ambuye wathu anakumana nako.
27 Kulingalira koteroko kungathe kukhomereza pa maganizo athu kufunika kwa kuchita mogwirizana ndi chitsanzo cha Kristu kotero kuti tisaphonye chifuno cha kutibvutikira kwake kwakukuluko. Mu mkhalidwe wathu wochimwawu, ife tinali mu mkhalidwe womvetsa chisoni, wofanana ndi uja wa nkhosa zosochera zopanda chitsogozo cha mbusa wachikondi. Izi zinali choncho chifukwa chakuti, monga ochimwa, tinali kutali kwambiri ndi Mbusa wathu Wamkulu, Yehova Mulungu. Komabe, pa maziko a nsembe ya Yesu ndi kukhulupirira kwathu, kuyanjanitsidwa kwatheketsedwa. (Akolose 1:21-23) Chotero, talowa m’chisamaliro, chitetezo ndi chitsogozo chachikondi cha woyang’anira wa miyoyo yathu, ndiko kuti, Yehova Mulungu, ndi cha ‘mbusa wake wamkulu,’ Yesu Kristu. (1 Petro 5:2-4) Pamenepo, ndithudi, palibe kuchuluka kulikonse kwa kubvutikira chilungamo kumene kukakhala kwakukulu kwambiri kukupirira m’kusonyeza kuyamikira kwathu zimene Yesu Kristu wachita. Ha, ndi kwakukulu chotani nanga mmene kunaliri kutibvutikira kwa Kristu koposa kuchitiridwa moipa kuli konse kumene ife tingakumane nako kaamba ka iye!
MALINGANIZIDWE A NTCHITO NDI OKHULUPIRIRA
28, 29. (a) Kodi ndi uphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka kwa akapolo Achikristu okhala ndi ambuye okhulupirira? (b) Kodi nchifukwa ninji uphungu woterowo unali wofunika?
28 Komabe, si Akristu onse m’zaka za zana loyamba C.E., anali ndi ambuye osalingalira amene anachitiridwa nawo moipa. Chifukwa cha mikhalidwe ya anthu imene inalipo pa nthawiyo, ngakhale Akristu ena anali ndi akapolo. Pamene kapoloyo ndi mbuye wake anali ophunzira a Mwana wa Mulungu, amuna onsewo anafunikira kuona unansi wao wauzimu moyenera. Polunjikitsa chilangizo chake kwa akapolo okhala ndi ambuye okhulupirira, mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Iwo akukhala nawo ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupira ndi okondedwa, oyanjana nawo pa chokomacho.”—1 Timoteo 6:2.
29 Kodi nchifukwa ninji uphungu umenewu unali wofunika? Kapolo wokhulupirirayo anali wolowa nyumba limodzi ndi Kristu ndipo, chotero, anali ndi kufanana kwauzimu ndi mbuye wake wokhulupirirayo. Chifukwa cha chimenecho, kapoloyo anayenera kukhala maso kuti asalingalire kuti kufanana kwauzimu kumeneku kunafafaniza unansi wa ntchito yakuthupi wokhala pakati pawo ndi ulamuliro wa mbuyeyo mu unansi umenewo. Kaimidwe ka maganizo koteroko kakanatha mosabvuta kutsogolera ku kulowa m’thumba mbuye wakeyo, osachita zonse zimene angathe m’kuchita ntchito zake. Uphungu wa mtumwi Paulowo unakhala wosemphana ndi malingaliro alionse olakwa amene akapolo angakhale atapeza kuchokera ku unansi wao wa ubale ndi ziwalo zina za mpingo. Chifukwa cha kukhala mu unansi woterowo ndi ambuye wawo, iwo analidi ndi chifukwa champhamvu kwambiri chochitira ntchito zao m’njira yabwino kwambiri. Unali mwai wawo kuchitira kanthu kena mbale Wachikristu, ndipo uku kunayenera kukhala magwero a chisangalalo chachikulu kwa iwo.
30.Kodi nchifukwa ninji Mkristu lero lino ayenera kuchita zonse zimene angathe ngati iye akugwira ntchito pansi pa uyang’aniro wa wokhulupirira?
30 Mofananamo lero lino, ngati Mkristu akugwira ntchito akuyang’aniridwa ndi woyang’anira ntchito wokhulupirira kapena akugwirira ntchito wokhulupirira, iye ayenera kufuna kuchita zabwino zonse zimene angathe. Ndiye mbale wake amene akupeza mapindu kuchokera ku ntchito yake. Ngati iye atachita ntchito yopanda pake kapena kukhala wosafuna kugwira ntchito zolimba, iye akakhala wogwiritsa mwala ndi wokwiyitsa kwa mbale ameneyu. (Miyambo 10:26) Ha, kukakhala kupanda chikondi kotani nanga kumene iye akakhala akusonyeza kwa mbale amene iye ali ndi thayo la kumkonda! —1 Yohane 4:11.
31. Kodi ndi uphungu wotani umene ambuye Achikristu anafunikira kuukumbukira?
31 Ku mbali ina, ambuye Achikristu kapena olemba ntchito sanayenera kunyalanyaza chenicheni chakuti iwo, nawonso, anali ndi mbuye, Kristu. Kuzindikira kukhala kwao athayo kwa Mwana wa Mulungu kunayenera kuyambukira m’mene iwo anachitira ndi akapolo ao kapena antchito. Ponenapo mawu pa zimenezi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana, podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m’Mwamba.” —Akolose 4:1.
32. Kodi ndi thayo lotani limene tiri nalo kulinga kwa okhulupirira amene angakhale akugwira ntchito kapena akupereka utumiki kwa ife?
32 Ndiponso, ngati abale Achikristu akugwira ntchito kapena akutitumikira mu udindo wa madokotala, maloya, akatswiri a magetsi, opala matabwa, omangirira mapaipi, okonza zinthu, ndi zina zofanana nazo, ife ndithudi tidzafuna kuwapatsa malipiro oyenera. Kodi sikukakhala kosayenera kugwiritsira ntchito molakwa unansi wathu wauzimu mwa kuchedwetsa kulipira mbale Wachikristu pamene ife tikugwiritsira ntchito mbali yokulira ya ndalama zathu zopezedwa kaamba ka zosangalatsa zopambanitsa, machuti abwino kopambana kapena oonongetsa ndalama zochuluka? M’nkhani za bizinesi, kodi sitingafune kuti okhulupirira anzathu apeze ziri konse zimene iwo ali oyenerera kulandira? Ndithudi kuli bwino kwambiri pamene mwa njira imeneyo tingathe kuthandiza abale athu kupeza ndalama zokhalira moyo. Ngati kulingalira kwapadera ndalama zokhalira moyo. Ngati kulingalira kwapadera kusonyezedwa kwa ife, moyenerera timalingalira zimenezi moyamikira, tikumazindikira kuti okhulupirira anzathu sali athayo kutipatsa ndalama zapadera kapena chiyanjo koposa ena. Pamenepo, m’nkhani zonsezi, tingathe kusonyeza kuti timafuna kuchita zinthu zonse m’njira yokondweretsa Mutu wathu wakumwamba, Mwana wa Mulungu.
KUGONJERA KWAUKAZI
33. (a) Kodi ndi chilangizo chotani chimene chikuperekedwa kwa akazi Achikristu? (b) Mu 1 Petro 3:1, kodi nchiyani chimene chiri chapadera ponena za liwu lotanthauza “momwemonso”?
33 Ukwati ndiwo unansi winanso umene umafunikira kugonjera ku mutu. Chotero, Petro akugwirizanitsa kufotokoza kwake kugonjera kwaukazi ndi chilangizo chake chapapitapocho chonena za kugonjera pansi pa mikhalidwe yobvuta kwambiri mwa kuyamba ndi liwu Lachigriki lotanthauza “momwemonso.” Timawerenga kuti:
“Momwemonso, akazi inu, khalani ogonjera kwa amuna anu a inu eni, kuti, ngati ena ali osamvera mawu, iwo angapindulidwe popanda mawu kupyolera mwa khalidwe la akazi ao, chifukwa cha kukhala mboni zowona ndi maso za khalidwe lanu loyera limodzi ndi ulemu waukulu.”—1 Petro 3:1,2.
34. Kodi mtumwi Petro akulimbikitsa mkazi kukhala wogonjera pansi pa mkhalidwe wotani, ndipo kodi nchifukwa ninja kumeneku sikungakhale kosabvuta?
34 Mkhalidwe mu umene akazi Achikristu akulimbikitsidwira pano kukhala ogonjera uli wosayenera. Pamene mwamuna samalandira malamulo a khalidwe labwino a Mawu a Mulungu, iye angapangitse moyo kukhala wobvuta kwambiri kwa mkazi Wachikristu, akumakhala waukali ndi wosalingalira m’kuchita ndi mkaziyo. Koma zimenezi sizimamletsa kuchita mogwirizana ndi chenicheni chakuti mwamuna ndiye mutu wa banja. Chotero, paliponse pamene zopempha zake sizikuombana ndi lamulo la Mulungu, mkazi Wachikristu adzafuna kuchita zonse zimene angathe kukondweretsa mwamuna wake.
35. Kodi ndi motani mmene mkazi angapindulire mwamuna wake “popanda mawu”?
35 Monga momwe mtumwi Petro anasonyezera, chitsanzo chake chabwino kwambiri chingathandize mwamunayo kukhala wokhulupirira. Komabe, kupindula kwa mkazi mwamuna wake “popanda mawu,” sikumatanthauza kuti iye sakagawana naye malingaliro Amalemba, koma iye akalola machitidwe ake abwino kulankhula mopfuula kwambiri koposa mawu. Mwamunayo pamenepo akakhala wokhoza kuona kuti khalidwe la mkazi wake liri loyera kapena losadetsedwa m’kulankhula ndi ntchito ndi kuti iye ali ndi ulemu waukulu kwa iye.
36, 37. Malinga ndi kunena kwa Tito 2:3-5, kodi mkazi Wachikristu ayenera kupereka chisamaliro ku chiyani m’malo mwakuti akhale mkazi wopereka chitsanzo?
36 Zimene mtumwi Paulo analemba ponena za akazi zimapereka mfundo zina zoonjezereka ponena za chimene chingayembekezeredwe kwa mkazi Wachikristu. M’kalata yake kwa Tito, iye analongosola kuti:
“Akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera, osadyerekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma; kuti akalangize akazi ang’ono akonde amuna awo, akonde ana awo, akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwawo, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.”—Tito 2:3-5.
37 Malinga ndi kunena kwa chilangizo chimenechi, mkazi ayenera kufunafuna mosamalitsa kudzisungira mu mkhalidwe wosonyeza kuzindikira kwake chenicheni chakuti moyo wake wonse wathunthu umaonedwa ndi Yehova Mulungu ndi Ambuye Yesu Kristu. Iye adzagwira ntchito zolimba kugwiritsira ntchito lirime lake kumangirira ndi kulimbikitsa ena, osatembenukira kuugogodi kapena miseche yobvulaza. Kukhala wachikatikati m’kudya ndi kumwa kulinso koyenera. Monga mkazi ndi mai, mkazi Wachikristu ayenera kukhala wa chitsanzo chabwino m’chikondi chake, akumatsimikizira kuona kuti iye akuchita mbali yake m’kupereka zakudya zopatsa thanzi ndi kupangitsa panyumba kukhala paudongo ndi malo okondweretsa. Kukonda mwamuna wake ndi ana ake kumaphitikizamo kukhala kwake wofunitsisa kuika zabwino za banja patsogolo pa zake za iye mwini. Mwamuna sayenera kukhala wokhoza kupeza umboni wakuti mkazi wake akunyalanyaza kwambiri ntchito zake. Koma ayenera kukhala wokhoza kuona kuti, poyerekezera ndi akazi osakhulupirira, iye alidi wa chitsanzo chabwino.
LINGALIRO LA CHIKATIKATI LA KUDZIKOMETSERA
38. Kodi ndi uphungu wotani wonena za kudzikometsera umene tikuupeza pa 1 Petro 3:3, ndipo ndi motani mmene uyenera kumvedwera?
38 Chofunikanso, ndicho kuika kwa mkazi pa malo oyenera kudzikometsera. Mtumwi Petro anagogomezera kuti mkazi Wachikristu sayenera kuika chigogomezero chachikulu pa kudzipangitsa iye mwini kukhala wa maonekedwe okondweretsa mwa njira ya kudzikometsera kodzionetsera. Iye anati: “Musalole kudzikometsera kwanu kukhala kuja kwa kuluka tsitsi kwakunja ndi kwa kubvala zokongoletsa zagolidi kapena kubvala zobvala zakunja.” (1 Petro 3:3, NW) M’zaka za zana loyamba C.E., akazi anali kuononga nthawi yochuluka ndi kuyesayesa m’kuluka tsitsi lawo lalitalilo m’malukidwe ochititsa kaso, okongola kwambiri, kuphatikizapo kulipanga kuoneka ngati azeze, malipenga, zipukuta za maluwa ndi nduwira zachifumu. Ndiponso, iwo anadzikometsera iwo eni ndi zobvala zonyezimira kwambiri ndi maufuku agolidi, ndolo ndi makoza. Kwa mkazi Wachikristu, kusamalira mopambanitsa kudzikometsera pathupi koteroko kunali kosayenera, pakuti kukasonyeza kuti cholinga chake chachikulu m’moyo chinali iye mwini m’malo mwa kukhala kwake wokondweretsa kwa Yehova Mulungu ndi Ambuye Yesu Kristu. Ndiponso, akazi amene amakhalira moyo kudzisonyeza chabe kapena kusonyeza masitayelo amakhala mikhole ya kunyada, kaduka, ndi kufuna kutchuka, zimene zimachotsera maganizo ndi mtima mzimu wa kudekha ndi kubala kugwiritsidwa mwala ndi kusachedwa kukwiya.
39. Kodi nchifukwa ninji mkazi sayenera kunyalanyaza kawonekedwe kake?
39 Komabe, zimenezi sizimatanthauza kuti mkazi Wachikristu akapereka chisamaliro chochepera ku kaonekedwe kake. Popereka uphungu wofananawo ponena za kusayenera kwa kubvala kodzionetsera mtumwi Paulo nayenso anati: “Ndifuna kuti akazi adzibveke zobvala zolinganizidwa bwino, limodzi ndi kudekha ndi kulama maganizo.” (1 Timoteo 2:9, NW) Chotero mkazi Wachikristu achita bwino kukhala maso kuti sakusonyeza kaonekedwe koipa kwa mwamuna wake mwa kukhala wosasamala ponena za kabvalidwe kake, kupesa tsitsi ndi kaonekedwe ka thupi. Ndiponso, Baibulo limalongosola kuti “mkazi ndiye ulemerero wa mwamuna.” ( 1 Akorinto 11:7) Mwachionekere, mkazi waulesi, wautchisi sali thamo kapena ulemerero kwa mwamuna wake. Iye amaluluzitsa kaonekedwe kake m’maso mwa ena. Ndipo ngati mwamunayo amanyadira moyenera kaonekedwe ka iye mwini, mwa kusadzisamalira mkazi wake angakhale magwero akupsa mtima kwambiri. Chifukwa cha chimenecho, nkofunika kopambana kuti kubvala ndi kudzikometsera kwa mkazi Wachikristu kusonyeze kuti iye ali ndi kulingalira bwino m’kusankha chimene chiri chodekha, kapena choyenera, ndi choyenera kwa iye mwini.
“MZIMU WACHETE NDI WODEKHA”
40. (a) Kodi nchiyani chimene chimapangitsa mkazi Wachikristu kukhala wokongola kwenikweni? (b) Kodi “mzimu wachete ndi wodekha” suyenera kusokonezedwa ndi chiyani?
40 Komabe, kukongola kwenikweni kwa mkazi Wachikristu kuli m’chimene iye ali mu mtima. Mtumwi Petro mwanzeru anafulumiza kuti kudzikometsera kwake “kukhale munthu wamkati wa mtima m’chobvala chosaola cha mzimu wachete ndi wodekha, umene uli wamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu.” (1 Petro 3:4, NW) “Mzimu wachete ndi wodekha” umenewu suyenera kuyerekezeredwa molakwa ndi kaonekedwe ka kukoma kwakunja chabe. Mwachitsanzo, mkazi angakhale wolankhula mofatsa ndipo amagonjera modekha, mwa mawu, ku zofuna za mutu wa banja. Komabe, iye mu mtima, angayese kulamula mwamuna wake mwa kukhala wopanduka, wolinganiza chiwembu ndi kuchita mwamachenjera.
41. Kodi ndi motani m’mene mkazi angatsimikizirire kaya ngati “mzimu wachete ndi wodekha” uli mbali ya kudzikometsera kwake kwachikhalire?
41 Ponena za mhazi amene alidi ndi “mzimu wachete ndi wodekha,” mzimu wodzichepetsa umenewu uli chisonyezero cha chimene iye ali kwenikweni mkati. Kodi ndi motani m’mene mkazi angatsimikizirire kaya “mzimu” umenewu uli mbali ya kudzikometsera kwake kwachikhalire? Iye angadzifunse kuti: ‘Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene mwamuna wanga, nthawi zina, ali wosalingalira, wosaganiza bwino kapena apewa kusenza thayo lake? Kodi ine kawirikawiri ndimapsa mtima, kukalipa ndi kumdzudzula mwaukali chifukwa cha zolephera zake? Kapena, kodi ine nthawi zonse ndimayesa mwamphamvu kukhala chete mu mtima mwanga ndi kupewa kulimbana kwapoyera?’ Mkazi wokhala ndi “mzimu wachete ndi wodekha” samangoonekera kukhala wamtendere kunja kokha koma mofanana ndi volokano womawira mkati mwake, wokonzekera kuphulika. Ayi, pansi pa mikhalidwe yobvuta, iye amafunafuna kukhala wabata ngakhale mkhalidwe wake ponse pawiri kunja ndi mkati, zikumachititsa openyerera kugwidwa mtima kwambiri, ndi nyonga ya mkati imene iye amasonyeza ndi m’mene iye amachitira mokoma mtima.
42. Malinga ndi kumena kwa 1 Petro 3:5, 6 kodi ndani amene anali ndi “mzimu wachete ndi wodekha”?
42 “Mzimu wachete ndi wodekha” umenewo umalekanitsa akazi oopa Mulungu a m’nthawi za Chrikristu chisanakhale. Posonyeza chenicheni chimenechi, mtumwi Petro analemba kuti:
“Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna awo a iwo okha; monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chiri chonse.”—1 Petro 3:5,6.
43. Kodi nchiyane chimene chikusonyeza kuti Sara anali ‘mkazi woyera’ amene anayembekezera mwa Mulungu?
43 Monga mmodzi wa “akazi oyera mtima” wa m’nthawi ya Chikristu isanakhale, Sara anaika chiyembekezo chake ndi chidaliro mwa Yehova. Mosafanana ndi mkazi wo Loti amene molakalaka anayang’ana m’mbuyo ku Sodomu, naonongeka, Sara mofunitsitsa anasiya zosangalatsa za Uri napitirizabe kukhala ndi mwamuna wake, Abrahamu, m’mahema kwa nthawi yonse yotsala ya moyo wake. Limodzi ndi Abrahamu, iye anayembekezera malo okhala achikhalire pansi pa ulamuliro wa Mulungu. (Ahebri 11:8-12) Sara ndithudi sanaone chuma chakuthupi ndi zosangalatsa kukhala zofunika kwambiri. Iye anakhala ndi moyo mu mkhalidwe umene unabvumbula kapenyedwe kauzimu. Sara anazindikira kuti Mulungu akamfupa kwambiri pa nthawi ya chiukiriro. Mofananamo, akazi Achikristu, lero lino mwanzeru amapanga kukondweretsa Yehova Mulungu kukhala cholinga chachikulu m’moyo.-Yerekezerani ndi Miyambo 31:30.
44. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Sara anali ndi ulemu waukulu kwambiri kwa mwamuna wake?
44 Sara wokongolayo anali ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake. Pamene alendo osayembekezereka anafika, Abrahamu sanakaikire m’kunena kwa tsamwali wake wokhulupirikayo kuti: “Konza msanga miyeso itatu [.6 bushel; 22 liters] ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.” (Genesis 18:6) Tsiku lomwelo Sara anacha Abrahamu kukhala “ambuye.” Popeza kuti iye anatero mu mtima mwake ndipo osati ena akumva, zimenezi zikusonyeza bwino lomwe kuti iye anali, wogonjera kwa mwamuna wake, mu mtima. –Genesis 18:12.
45. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Sara sanali ndi umunthu wofooka?
45 Komabe, Sara sanali mkazi wa umunthu wofooka. Pamene iye anaona kuti Ismayeli, mwana wamwamuna wa mdzakazi Wachiigupto Hagara, anali “kuseka” Isake mwana wake wamwamuna, Sara analankhula mwamphamvu kwa Abrahamu, kuti: “Chotsa mdzakazi uyo ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m’nyumba pamodzi naye mwana wanga Isake.” Koma chakuti iye anali kupempha mwamphamvu kwa Abrahamu, osati mosayenera kuumiriza kapena kulamula, chikusonyezedwa ndi chibvomerezo cha Yehova cha pempho la Sara. Wamphamvuyonse anaona pempho loperekedwa ndi mzimu woyenera, ndipo analangiza Abrahamu kuzichita.—Genesis 21:9-12.
46, 47. (a) Kodi ndi motani m’mene mkazi amene amapereka malingaliro amphamvu ndipo amayambirira angasonyezere kuti iye ali wogonjera? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kuyembekezera kuchokera kwa mkazi woopa Mulungu?
46 Mofananamo, Mkristu wachikazi wogonjera satofunikira kukhala wopanda mphamvu ya kupanga chosankha kapena wofooka. Iye angalongosole malingaliro ake a iye mwini otsimikizirika ndi kuyambira m’kuchita zinthu zina zimene ziri zofunika ku chimwemwe cha banja. Koma iye adzayesayesa kukumbukira zofuna ndi malingaliro a mwamuna wake, akumalola zimenezi kumtsogoza pogula zinthu, kukongoletsa nyumba kapena kusamalira ntchito zina za panyumba. Ngati iye ali wosatsimikizira ponena za lingaliro lake la pa ntchito ina kapena chogula chachikulu, iye angathe kupewa zobvuta mwa kufunsa pasadakhale. Mwa kufunafuna kuchita ntchito zake zaukazi m’njira imene iri yokondweretsa kwa Mulungu, iye adzakondweretsanso mwamuna wake, osampatsa chifukwa chiri chonse choyenera chopezera chifukwa. Mkazi woteroyo kawirikawiri amapeza malo a ulemu ndi kulemekezeka m’banja. Mkhalidwe wake umatsimikizra kukhala wofanana ndi uja wa nkazi wokhoza wofotokozedwa pa Miyambo 31:11, 28: “Mtima wa mwamuna waje umkhulupirira anake adzanyamuka nadzamucha wodala; mwamuna wake namtama.” Mwamuna amene ali ndi chidaliro chakuti mkazi wake adzachita mwanzeru ndi kusaika paupandu ubwino wa banja adzaona kukhala popanda kufunika kwa kuika timalamulo tambirimbiri toletsa machitidwe opanda nzeru. Padzangokhala kumvana kwabwino kwambiri pakati pao. Posamalira nkhani za banja, iye adzasangalala kugwiritsira ntchito maluso ake ndi kuyambirira mokwanira.
47 Kukhala mkazi woopa Mulungu mu lingaliro la Baibulo, mkazi Wachikristuyo afunikira kukhala wakhama ndi wokhoza kuyambirira m’kuthandiza ena. Chotero iye sadzakhala mkazi amene amangokhala chabe ‘mu mthunzi’ wa mwamuna wake. (Yerekezerani ndi Miyambo 31:13-22, 24, 27.) Zimenezi ziri zoonekera bwino kuchokera m’kufotokozedwa kwa akazi Achikristu amene anayenerera kuikidwa pa mapambo wapadera m’zaka za zana loyamba C.E. Timawerenga kuti: “Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.” (1 Timoteo 5:9, 10) Onani kuti mbiri yake ya ntchito zabwino ikabwerera m’mbuyo ku nthawi imene iye anali “mkazi wa mwamuna mmodzi.” Chotero sitikufuna kusokoneza “mzimu wa chete ndi wodekha” ndi chimene chingakhale kwenikweni kupanda kuyambirira ndi khama pa ntchito.
MAPINDU OCHOKERA M’KUSONYEZA MZIMU WONGA WA KRISTU
48. Kodi ndi motani mmene mkazi Wachikristu angakhalire wofanana kwambiri ndi Mwana wa Mulungu?
48 Popeza kuti Kristu ndiye ‘chitsanzo choti ophunzira ake onse achitsatire,’ mkazi Wachikristu adzafuna kupanga kuyesayesa kukhala wofanana kwambiri ndi iye pamene ayang’anizana ndi mikhalidwe yosayenera. (1 Petro 2:21) Uku kumafunikira kuti iye akhale woona mtima kwa iye mwini m’kupenda mawu ake ndi machitidwe. Ndiyeno, mwa kulingalira mwaphemphero chitsanzo cha Yesu Kristu ndi kupitirizabe kupempha Yehova Mulungu chithandizo cha mzimu wake woyera m’kukhala mkazi wabwino kwambiri, iye adzafikira pa kukhala ndi “mtima wa Kristu” mokulira kwambiri. (1 Akorinto 2:16) Kupita patsogolo kwake kudzafikira kukhala koonekera bwino kwa ena. Izi ziri choncho chifukwa chakuti pamene tiganiza zochuluka ponena za mikhalidwe yabwino kwambiri ndi machitidwe otamanditsa za munthu wina amene timamkonda, ndi pamenenso tidzafuna kukhala ngati ameneyo.
49-51. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru nthawi zonse kwa mkazi kugwiritsira ntchito malamulo a khalidwe labwino a Baibulo? (b) Kodi ndi mapindu abwino kwambiri otani amene angachokere ku kumamatira mokhulupirika ku Malemba? (c) Kodi ndi “chochititsa mantha” chotani chimene mkazi Wachikristu sayenera kuchiopa, ndipo chifukwa ninji?
49 Ngakhale pamene mwamuna ali wosalingalira, wosaganiza bwino kapena amapewa thayo, mkazi angathe kukhala ndi chidaliro chiri chonse chakuti kugwiritsira ntchito malamulo a khalidwe labwino a Baibulo kudzakhala ndi zotulukapo zabwino kopambana zothekera pansi pa mikhalidweyo. Zochepa zimapezedwa ndi mkazi amene amapanga nkhani yaikulu pa chosankha cholakwa chiri chonse chimene mwamuna wake wapanga, motero kunyalanyaza uphungu Wamalemba wa kukhala wogonjera. Anthu amayedzamira ku kudzitetezera ngakhale pamene iwo ali olakwa. Chotero, ngati mkazi apanga kukhala ‘nkhani yaikulu’ nthawi iri yonse imene mwamuna wake agwiritsira ntchito kulingalira kolakwa, iye angapeze kulabadira kumene kuli kosemphana ndi zimene iye akufunafuna. Mwamunayo angakhale wotsimikizira kwambiri kunyalayaza zimene mkaziyo akunena kuti atsimikizire kwa mkaziyo kuti iye sakufuna chilangizo chake. Ku mbali ina, ngati kachitidwe ka mkaziyo kasonyeza kuzindikira chenicheni chakuti anthu ochimwafe sitingapewe kotheratu zolakwa m’kusankha, iye angakhale woyedzamira kwambiri ku kulingalira malingaliro a mkaziyo nthawi yotsatirapo. Iye adzakuona kukhala kosabvuta kwambiri kuletsa kunyada kulowetsedwa mopambanitsa m’nkhaniyo.
50 Mwa kulimbikitsa mwamuna wake mu mkhalidwe wokoma mtima ndi wodekha, mkazi Wachikristu angamchititse kuganizira mwamphamvu ponena za m’mene iye akuchitira zinthu ndiyeno nkuyamba kupanga masinthidwe m’moyo wake. Pamene kuli kwakuti kupita patsogolo kungakhale kwapang’onopang’ono, mkaziyo amapeza mfupo ya pa nthawi yomweyo. Kodi iyo nchiyani? Iye amapewa kupanikizika kwambiri kwa malingaliro, kupweteka ndi kusakondweretsa kumene kulimbana kwapoyera ndi mwamuna wake kukatsogolerako.—Miyambo 14:29, 30.
51 Kumamatira kokhulupirika kwa mkazi ku Malemba m’khalidwe ndi kulankhula sikungachititse nthawi zonse mwamuna wake wosakhulupirira kukhala Mkristu. Koma mkaziyo amakhalabe ndi chikhutiro cha kudziwa kuti njira yake iri ‘yokondweretsa bwino kwa Mulungu.’ Njira yoyamikirika imene iye amachita nayo mathayo ake monga mkazi ndi mai iri mbali ya mbiri ya ntchito zabwino zimene ziri zofanana ndi chuma chosungidwa m’mwamba. Chuma chimenecho chidzakhala ndi chiongola dzanja chochuluka mu mpangidwe wa madalitso a Mulungu. (Mateyu 6:20) Pozindikira kufunika kwa kusunga kaimidwe kabwino ndi Mulungu, ayenera ‘kupitirizabe kuchita zabwino’ ndi kusaopa chiri chonse ‘chochititsa mantha” – kuchitiridwa moipa kulikonse, ziopsezo kapena chitsutso chimene chingatulukepo chifukwa cha kukhala kwake wophunzira wa Yesu Kristu. M’malo mwa kugonjera ku mantha ndi kutaya unansi wake ndi Yehova ndi Mwana wake, iye angaone chokumana nacho chake kukhala kubvutikira Kristu. Motero iye amadzitsimikizira kukhala mwana wamkazi wa Sara wogonjerayo, mkazi waumulungu wokhulupirika.
“MONGA MWA CHIDZIWITSO”
52. Kodi nchiyani chimene chiri chapadera ponena za kugwiritsira ntchito kwa Petro liwu Lachigriki lotanthauza “mofananamo” kapena “momwemonso” popereka uphungu kwa amuna Achrikristu?
52 Monga momwe kuliri kuti mkazi ali ndi ntchito zakutizakuti chifukwa cha unansi wake ndi mwamuna wake, chimodzimodzinso mwamuna chifukwa cha unansi wake ndi mkazi wake. Mtumwi Petro anakumbutsa amuna za zimenezi, akumagwiritsa ntchito liu Lachigriki lotembenuzidwa kukhala “mofananamo” kapena “momwemonso” kugwirizanitsa chilangizo chake kwa iwo ndi uphungu wake waitawo kwa akazi, kuti:
“Momwemonso amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti maphemphero anu angaletsedwe.”—1 Petro 3:7.
53. Kodi nchiyani chimene chiyenera kulamulira mkhalidwe umene mwamuna amakhalira ndi mkazi wake?
53 Kuli koonekera bwino lomwe kuti mtumwi wouziridwayo, iye mwini mwamuna wokwatira, choyamba akusonyeza chenicheni chakuti mmene mwamuna amakhalira limodzi kapena kukhala ndi mkazi wake kuyenera kulamuliridwa ndi “chidziwitso.” (Marko 1:30; 1 Akorinto 9:5) Ndithudi mwamuna akafuna kudziwa mkazi wake bwino lomwe-malingaliro ake, nyonga zake, zofooka zake, zokonda ndi zosazikonda. Koma, chofunikadi kwambiri, iye afunikira kufika pa kudziwa amene ali mathayo ake monga mwamuna Wachikristu. Mwa kudziwadi mkazi wake ndiponso kudziwa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu, mwamuna “angapitirizebe kukhala ndi mkazi wake monga mwa chidziwitso.’
54. Kodi kuchitidwa kwa umutu kumafunanji?
54 Malemba amasonyeza kuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi. Koma iye Sali mutu wotheratu, pakuti iye akufunidwa kugonjera ku umutu wa Yesu Kristu m’kusamalira nkhani za banja. “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu, limatiuza choncho Baibulo. (1 Akorinto 11:3) “Amuna,” analemba motero mtumwi Paulo, “kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:25) Chotero, m’mene Mwana wa Mulungu amachitira ndi mpingo Wachikristu kumatumikira monga chitsanzo kwa amuna m’kuchita mathayo ao a banja. Ndithudi palibe chiri chonse choumiriza kapena chankhanza ponena za kuchita umutu kwa Yesu Kristu pa mpingo. Iye anatofikira ngakhale pa kuutayira moyo wake. Chotero, umutu wa mwamuna sumamloleza kuchita ufumu pa mkazi wake, kumuika pa udindo wotsika, wonyozeka. M’malo mwake, umaika pa iye thayo la kukhala wodzipereka m’chikondi chake, kukhala wofunitsitsa kuika ubwino ndi zikondwerero za mkazi wake patsogolo pa zikhumbo ndi zokonda zake za iye mwini.
55. Popeza kuti Yesu Kristu ndiye chitsanzo, kodi nchiyani chimene amuna Achikristu ayenera kuchita?
55 Popeza kuti Yesu Kristu ndiye chitsanzo chao chabwino kopambana, amuna achita bwino kudzichititsa iwo eni kudziwa zimene iye anachita m’kuchita ndi ophunzira ake. Chofunikanso kwambiri, amuna ayenera kuyesayesa kuchita mogwirizana ndi chitsanzo cha Mwana wa Mulungu m’kuchita mathayo ao a banja. Lingalirani zowerengeka chabe za zinthu zambiri zimene Yesu Kristu anachita pamene anali pa dziko lapansi m’kusamalira ophunzira ake.
56, 57. (a) Kodi ndi motani mmene Mwana wa Mulungu anasonyezera chikondwerero chenicheni m’thanzi lauzimu la ophunzira ake? (b) Polingalira chitsanzo cha Yesu, kodi nchiyani chimene mwamuna angadzifunse yekha?
56 Mwana wa Mulungu anali wokondweretsedwa moona mtima ndi thanzi lauzimu la atsatiri ake. Ngakhale pamene iwo anali ochedwa kumvetsetsa nkhani zofunika kwambiri, iye sanakhale wosadekha kwa iwo. Iye anakhala ndi nthawi ya kumveketsa zinthu kwa iwo ndipo anatsimikizira kuona kuti iwo anamvetsetsa kuphunzitsa kwake. (Mateyu 16:6-12; Yohane 16:16-30) Pamene iwo anapitirizabe kukhala ndi bvuto m’kukhala ndi lingaliro la kuzindikira unansi wao kwa wina ndi mnzake, Yesu anabwereza mfundo zonena za kufunika kwa kutumikira ena. (Marko 9:33-37; 10:42-44; Luka 22:24-27) Pa usiku wake wotsirizira ali nawo iye analimbikitsa chiphunzitso chake chonena za kudzichepetsa mwa kutsuka mapazi ao, motero kuwapatsa chitsanzo. (Yohane 13:5-15) Yesu analingaliranso zofooka za ophunzira ake ndipo sanawapatse chidziwitso chochuluka mopambanitsa koposa chimene iwo akanachimvetsetsa pa nthawiyo.—Yohane 16:4, 12.
57 Chifukwa cha chimenecho, mwamuna Wachikristu, angadzifunse kuti: ‘ Kodi ine ndiri wodera nkhawa motani ndi thanzi lauzimu la mkazi wanga ndi ana? Kodi ine ndimatsimikizira kuona kuti iwo akumvetsetsa malamulo a khalidwe labwino a Baibulo? Pamene ndiona mikhalidwe ndi machitidwe olakwa, kodi ndimanena mosakuluwika chifukwa chake zimenezo ziri zolakwa ndi chifukwa chake masinthidwe ayenera kupangidwa? Kodi ndimalingalira zofooka zawo ndi kupenyetsetsa kuti sindikufunsira zochulukitsitsa?’
58. Kodi ndi motani mmene mwamuna angatsanzirire chitsanzo cha Yesu m’kulingalira zosowa zakuthupi za banja lake?
58 Mwana wa Mulungu analinso wamaso kuona chimene ophunzira ake anali kusowa mwa lingaliro lakuthupi. Pamene atumwi anabwerera kwa Yesu kuchokera ku ulendo wokalalikira nasimba za ntchito yawo, iye anati: “Idzani inu nokha padera ku malo a chipululu, mupumule, kamphindi.” (Marko 6:31) Mofananamo, mwamuna wanzeru amatsimikizira kuona kuti mkazi wake ndi ana ali ndi nthawi ya kumasula thupi ndi kusangulutsa kusintha pa zochita za tsiku ndi tsiku za moyo.
59, 60. (a) Kodi ndi motani m’mene Yesu Kristu anasonyezera chidaliro ndi kukhulupirira ophunzira ake? (b) Kodi ndi motani mmene zimenezi zingathandizire mwamuna m’kuchita umutu?
59 M’kuchita umutu, Yesu Kristu samachititsa ziwalo za mpingo kukhala zirimobe ndi mpambo wobvuta wa timalamulo. Iye anawapatsa malamulo ndi zitsogozo zofunika monga maziko a kufika kwao pa zosankha zoyenera m’kuchita ndi zobvuta za moyo. Chikondi chake cha kudzipereka, limodzi ndi chidaliro chake ndi chikhulupiriro mwa ophunzira ake, chifukwa cha chimenecho, “zimawasonkhezera” kuyankha mwa chikondi chofananacho, akumachita zimene angathe kumkondweretsa.—2 Akorinto 5:14, 15; yerekezerani ndi 1 Timoteo 1:12; 1 Yohane 5:2, 3.
60 M’njira yofananayo, kusonyeza chidaliro mwa mkazi wake kwa mwamuna kungachite zochuluka kusungitsa ukwati wachimwemwe. Mkazi amene ali ndi ufulu wochepa wa kugwiritsira ntchito kuyambirira m’kusamalira mathayo ake posapita nthawi adzataya chisangalalo m’ntchito yake. Iye adzaona kukhala akulepheretsedwa m’kugwiritsira ntchito chidziwitso chake, maluso ndi kukhoza, kukumachititsa kugwiritsidwa mwala. Ku mbali ina, pamene mwamuna wake asiyira nkhani zina zofunika ku kusankha kwake kwabwino, iye adzakhala ndi chisangalalo m’kuchita zinthu m’njira imene idzakondweretsa mwamuna wake.
‘KUWACHITIRA ULEMU MONGA CHOTENGERA CHOCHEPA MPHAMVU’
61-63. (a) Kodi Malemba amanenanji ponena za mmene mwamuna ayenera kuchitira ndi mkazi wake? (b) Kodi ndi zinthu zotani zimene mwamuna akapewa ngati amapatsadi mkazi wake malo olemekezeka? (c) Pamene tifika pa nkhani zofunika za banja, kodi nchiyani chimene mwamuna ayenera kukhala wofunitsitsa kuchita? (d) Kodi nchifukwa ninji sikuli kokwanira kungolingalira mawu onenedwa pamene mukupanga zosankha zotsirizira?
61 M’kukhala ndi mkazi monga mwa chidziwitso chake monga munthu ndi cha mathayo ake Amalemba kulinga kwa mkaziyo, mwamuna akakhalanso akumamchitira “ulemu monga chotengera chochepa mphamvu.” Chifukwa chakuti kupangidwa kwa thupi la mkazi kumasonyeza zofooka zochuluka za thupi pa iye koposa m’mene ziriri kwa amuna mwachisawawa, iye ali “chotengera chochepa mphamvu.” Koma iye ayenera kukhala ndi malo olemekezeka kapena aulemu m’banja. Mawu otsatirapo a mtumwi Paulo akusonyeza m’mene mwamuna angapatsire ulemu mkazi wake: “Mwa njira imeneyi amuna ayenera kukonda akazi ao monga matupi ao a iwo eni. Iye amene amakonda mkazi wake amadzikonda iye mwini, pakuti palibe munthu anadana nalo thupi lake ndi kale lonse; koma iye amalidyetsa ndi kulisamalira, monga momwe Kristu amachitiranso ndi mpingo.” —Aefeso 5:28, 29, NW.
62 Amuna nthawi zonse samanyozetsa zochita zawo, samadzipangitsa iwo eni kuonekera kukhala osakhoza kuchita zinthu, samachitira mwankhanza matupi awo, ndi kunyalanyaza kufunikira kwao kupuma ndi kusangulutsa. Iwo samafuna kukhala ndi mbiri ya kukhala “Opanda pake” koma amafuna kukhala ndi kaimidwe kolemekezeka m’maso mwa ena. Ngati mwamuna ali Mkristu kwenikweni, sadzapeputsa zofooka ziri zonse za mkazi wake zimene angakhale nazo, kumpepuza kapena mwa njira ina kumpangitsa kuona kukhala wotsika ndi wonyozeka. Iye adzapatsa mkazi wake mtundu wofananawo wa ulemu ndi kulingalira zimene iye amazifuna kaamba ka iye mwine, akumampangitsa kuona kukhala wofunidwa, woyamikiridwa ndi wofunika.
63 Kuti mkazi akhale ndi malo olemekezeka m’banja, mwamuna wake ayenera kukhala wofunitisitsa kukambitsirana nkhani za banja ndi iye m’njira yodekha ndi yolingalira bwino, kupeza maganizo ndi malingaliro ake. Mkazi ayenera kukhala wokhoza kutulutsa za kukhosi kwake momasuka, ali ndi chitisimikiziro chakuti zimene iye akunene m’kukambitsirana nkhani zofunika kwambiri sizidzangokankhiridwa pambali moyozera koma zidzalingaliridwa moyenerera ndi mwamuna wake. (Yerekezerani ndi Oweruza 13:21-23; 1 Samueli 25:23-34; Miyambo 1:5, 6, 8, 9.) Ndiponso, mwamuna afunikira kukhala maso kuona osati mawu olankhulidwa okha. Malingaliro a m’kati angathe kubvumbulidwa mwa kamvekedwe ka mawu, zimene nkhope ikusonyeza kapena kupanda kutenthedwa maganizo kapena kukondwa. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:13.) Mwamuna amene wafikira pa kudziwa mkazi wake sadzanyalanyaza zinthu zoterozo ndi kupitirizabe mosasamala ndi kanthu kena kamene kangachititse kupsa mtima kosafunika.
64. Kodi ndi liti pamene mwamuna sakagonjera kwa mkazi wake, ndipo kodi nchifukwa ninji kumeneku kuli kopindulitsa?
64 Ndithudi, monga mutu wa banja, pamene mwamuna ali wokhutiritsidwa maganizo kotheratu m’maganizo mwake kuti zabwino za banja lonse lathunthu zikaonongedwa mwa njira imeneyo, iye sakagonjera ku zikhumbo za mkazi wake. (Yerekezerani ndi Numeri 30:6-8.) Iye amazindikira kuti iye ali ndi thayo Mwamalemba la kuchirikiza chimene iye moona mtima amachikhulupirira kukhala choyenera, mosasamala kanthu za zisonyezero za malingaliro za mkazi wake. Pakuti kugwirizana kwa mwamuna ndi zofuna za mkazi wake mosemphana ndi kulingalira bwino kwambiri kwa mwamunako kukatanthauza kunyoza Mulungu, amene wapatsa mwamuna udindo wa umutu wa banja. Ndipo ngati zinthu pambuyo pake zinatsogolera ku zobvuta ku banjalo, zimenezi zikamchititsa kuipidwa ndi mkazi wake. Ku mbali ina, kukhala kwake woumirira zolimba pa chimene iye motsimikizirika amachikhulupirira kukhala njira yoyenera kukapindulitsa banja. Ngati chosankha chake chichitidwa mwapemphero ndi mogwirizana ndi malamulo a khalidwe labwino a Baibulo, mkazi wake angafikiredi pa kuona nzeru ya chosankha chopangidwacho ndi kukhala wokondwa kuti mwamuna wake anaumirira zolimba. Kumeneku kuyenera kuonjezera kumlemekeza kwake ndi kuthandizira chimwemwe chake ndi chija cha banja lonse lathunthu.
CHIFUKWA CHAUZIMU
65. Kodi ndi chifukwa chauzimu chotani chimene chiripo kwa mwamuna Wachikristu chokhalira ndi mkazi wake wokhulupirira “monga mwa chidziwitso”?
65 Pali chifukwa chosonkhezera chochititsa mwamuna Wachikristu kukhala ndi mkazi wake wokhulupirira “monga mwa chidziwitso,” akumapatsa mkaziyo ulemu. Sindicho phindu la mtendere woonjezereka chabe wa banja. Mtumwi Wachikristu Petro anasonyeza kwa okhulupirira anzake chifukwa chokulirapodi. Iye anasonyeza kuti amuna ali ‘olowa nyumba limodzi ndi akazi ao a chisomo cha moyo,’ Mwa njira ya imfa yake ya nsembe, Yesu Kristu anatsegulira onse amuna ndi akazi mwai wa kumasulidwa ku chitsutso cha uchimo ndi imfa, ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya. Chotero, mkazi angathe kukhala ndi kaimidwe kobvomerezeka pamaso pa Mulungu ndi Kristu mofanana ndi mwamuna wake. Pali chifukwa chachikulu tsono kwa mwamuna chokhalira wosamala kuti asachitire mkazi wake monga ngati kuti anali munthu wa mtengo wotsika wochepa m’maso mwa Mulungu koposa m’mene mwamunayo aliri.
66. Pamene nkhani za mu ukwati sizithetsedwa Mwamalemba, kodi nchifukwa ninji chibvulazo chachikulu kwambiri chauzimu chimatulukapo?
66 Ngati zinthu za mu ukwati sizichitidwa mogwirizana ndi chitsanzo cha Yesu Kristu ndi mpingo wake, kumeneku kumakhala ndi chiyambukiro choonoga pa mkhalidwe wauzimu wa onse awiri mwamuna ndi mkazi wake. Inde, ‘mapemphero angaletsedwe.’ M’banja limene muli kusachedwa kukangana, kukhumudwitsana, kusungirana nkhani kukhosi ndi kuchita mwaukali ndi mosalingalira bwino, nkobvuta kupempha Mulungu m’pemphero. Chifukwa cha kuona kukhala wotsutsidwa mu mtima, munthu sakakhala ndi ufulu wa kulankhula. (1 Yohane 3:21) Ndiponso, Yehova Mulungu wapereka zofunika zomvera mapemphero. Iye sadzamvetsera zopempha chithandizo za anthu amene ali opanda chifundo, osafunitsitsa kukhululukira zolakwa za ena. (Mateyu 18:21-35) Awo okha amene amayesayesa kuchititsa miyoyo yao kugwirizana ndi malamulo ake amamvedwa mwachiyanjo. (1 Yohane 3:22) Amuna kapena akazi amene amalephera kutsanzira mu ukwati wao chitsanzo cha Yesu Kristu ndi mpingo wake sangayembekezere kukhala ndi chithandizo cha Mulungu m’kuchita ndi zobvuta zao. Ku mbali ina, kumvera kokhulupirika ku chilangizo Chamlemba kumatsimikiziritsa chibvomerezo cha Mulungu ndi dalitso. Ndithudi, imeneyi ndi mphoto yabwino kwambiri imene imachokera ku kugonjera ku umutu wa Mwana wa Mulungu.
KUGONJERA MU MPINGO WACHIKRISTU
67. Malinga ndi kunena kwa Mateyu 23:8-11, kodi ndi mkhalidwe wotani umene uyenera kukhala mu mpingo Wachikristu?
67 Mu mpingo Wachikristu, mulinso kufunika kwenikweni kwa kuzindikira umutu wa Kristu. Kuzindikira kumeneku kudzayambukira kaimidwe ka maganizo ndi khalidwe la ziwalo zosiyanasiyana kulinga kwa china ndi chinzake. Malinga ndi kunena kwa mawu a Yesu iye mwini, mpingo wake unayenera kukhala ubale. Iye kwa ophunzira ake anati: “Inu, musamatchedwa Rabi, pakuti mmodzi ndiye mphunzitsi wanu, pamene inu nonse ndinu abale. Ndiponso, musamatcha aliyense atate pa dziko lapansi pano, pakuti mmodzi ndiye Atate wanu, Uyo wakumwamba. Ndipo musatchedwa ‘atsogoleri,’ pakuti mmodzi ndiye Mtsogoleri wanu, Kristu. Koma wamkulu kopambana pakati panu ayenera kukhala minisitala wanu [mtumiki, Kingdom Interlinear Translation].”—Mateyu 23:8-11.NW.
68, 69. (a) Popeza kuti mpingo uli ubale, kodi ndi kuchita monga momwe ufunira kotani kumene sikuyenera kuchitidwa? (b) Kodi nchiyani chimene Timoteo anayenera kukumbukira pochita ndi ziwalo za mpingo?
68 Chotero, palibe ali yense amene ayenera kuchita umbuye mu mpingo. Koma awo amene amatumikira monga akulu ndi aphunzitsi mu mpingomo ayenera kutsanzira Mbuyeyo, Kristu, m’kutumikira modzichepetsa abale ao. Komabe, popeza kuti mpingo uli ubale wopangidwa ndi achichepere ndi achikulire, amuna ndi akazi, chiwalo chiri chonse pachokha cha mpingowo sichiri chaufulu kuchita monga momwe chifunira kumene kukachititsa kuonongedwa kwa lingaliro lachibadwa la kuika zoyamba poyamba. Mtumwi Paulo analangiza Timoteo kuti: “Usadzudzule mwamphamvu munthu wachikulire. Mosiyana ndi zimenezo, m’dandaulire monga atate, anyamata monga abale, akazi achikulire monga amai, akazi achichepere monga alongo limodzi ndi chiyero chonse.”—1 Timoteo 5:1, 2, NW.
69 Pa nthawi imene mtumwiyo analemba mawu amenewa, Timoteo mwachionekere anali m’zaka zake za makumi atatu. Ngakhale kuli kwakuti anali kutumikira monga mkulu woikidwa, iye anali kulangizidwa kukumbukira kuti iye anali chikhalirebe wachichepere pang’ono. Ngati munthu wachikulire anafunikira kuongoleredwa, Timoteo sanayenera kukhala waukali kwa iye koma kumsonkhezera ndi kaimidwe ka maganizo kaulemu ka mwana wamwamuna pamaso pa atate wake. (Yerekezerani ndi njira yaulemu imene Yakobo anapemphedwera ndi ana ake amuna, monga momwe zalembedwera pa Genesis 43:2-10.) Akazi achikulire, nawonso, anayenera kusonyezedwa kulingalira ndi kukoma mtima kumene kunali koyenerera kuperekedwa kwa mai. Ndipo ngakhale ndi amuna achichepere Timoteo sanayenera kungochita monga momwe afunira, koma anayenera kuchita nawo monga momwe iye akanachitira ndi abale akuthupi okondedwa. Chifukwa cha chikoka champhamvu chimene amuna amakhala nacho kulinga kwa akazi, kunali koyenera kopambana kuti Timoteo achenjezedwe za kuchitira akazi achichepere monga “alongo ake akuthupi limodzi ndi chiyero chonse.” Zimenezi zinatanthauza kuti, m’kucheza kwake ndi akazi achichepere Achikristu, iye anayenera kukhalabe woyera, wopanda utchisi kapena wadongo m’malingaliro ake, mawu ndi machitidwe.
70. (a) Kod nchifukwa ninji mzimu wa kogonjera ukufunika m’malo mwakuti khalidwe loyenera lisungidwe mu mpingo? (b) Kodi nchiyani chimene chingathandize munthu kusunga mzimu wa kugonjera?
70 Mu unanasi wathu ndi ziwalo zina za mpingo, timafunikira mzimu wa kudzichepetsa m’malo mwakuti tisunge malo athu ndi kusaipitsa lingaliro lachibadwa la khalidwe labwino ndi kuyenera. Pamenepo, moyenera, mtumwi Petro analangiza kuti: “Inu anyamata, khalani ogonjera kwa akulu.” (1 Petro 5:5, NW) Anyamata ayenera kuyesayesa kugwirizana ndi achikulire, makamaka akulu oikidwa a mpingo. Ndithudi kukakhala kosayenera kwa mnyamata kulankhula ndi munthu wachikulire kapena kuwachitira m’njira imene ikakhala yosanganizirika ngati anali kuchita ndi atate wake wakuthupi. Koma kodi nchiyani chimene mnymata angachite kuti asungebe mzimu wa kugonjera? Iye angakuone kukhala kopindulitsa kulingalira za mikhalidwe yabwino ya abale achikulire ndi mbiri yao ya utumiki wokhulupirika. Kumeneku kungathandizire kuonjezeredwa kwa chikondi chake ndi chiyamikiro kaamba ka iwo.—Yerekezerani ndi Ahebri 13:7, 17.
71. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi ‘kudzimangira kwathu ndi kudzichepetsa maganizo’?
71 Ndithudi, Petro anachita zoposa ndi kulimbikitsa chabe anyamata kukhala ogonjera kwa akulu. Iye anaonjezanso kuti: “Nonsenu dzibvekeni kudzichepetsa maganizo kwa wina ndi mnzake.” Mawu a chinenero choyambirira otembenuzidwa kukhala “dzibvekeni kudzichepetsa maganizo” ali ndi lingaliro la kuyesa kumanga kudzichepetsa maganizo koteroko pa iye mwini ndi mfundo. “Kudzichepetsa maganizo” kumeneko kunayenera kukhala ngati eproni kapena malaya obvalidwa ndi kapolo. Chifukwa cha chimenecho, mzimu umene Petro analimbikitsa uli uja wa kufunitsitsa kutumikira ndi kupindulitsa ena. Ha, ndi kwabwino kwambiri chotani nanga mmene kuliri pamene tichitira ena onse mu mpingo mwaulemu ndi mokuza, kuwapatsa ulemu umene iwo akuuyenerera! Njira imeneyi imatsogolera ku dalitso la Yehova ndi chiyanjo, pakuti Petro akuonjeza kuti: “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amapatsa chisomo kwa anthu odzichepetsa.”—1 Petro 5:5, NW.
72. Kodi ndi mfupo zotani zimene zimachokera m’kusonyeza kugonjera koyenera?
72 Ndithudi, kusonyeza kwathu mtundu wa kugonjera umene umagwirizana ndi Malemba Oyera kumapereka mfupo zochuluka. Sikudzachititsa konse mkhalidwe woipa kuipitsitsa koma kudzatipatsa chikumbu mtima chabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu. Kugonjera ku maulamuliro a boma, eni ntchito, oyang’anira ntchito kapena mwamuna wosakhulupirira kungathe kupereka umboni wabwino kwambiri ponena za phindu la Chikristu choona ndipo kungathandize ena kukhala ophunzira a Mwana wa Mulungu, ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya. Ponena za ife, tingathe kukhala ndi chitsimikirziro chakuti Yehova Mulungu adzatifupa kwambiri kaamba ka kukhala titatsatira njira imene iri yokondweretsa kwambiri m’maso mwake. Inde, kugonjera koyenera ku ulamuliro ndiko mbali yofunika kwambiri ya kusangalala kwathu ndi njira yabwino kopambana ya moyo pa tsopano lino.