Nyimbo 35
Njira Yoposa ya Chikondi
1. Mulungu ndiye chikondi,
Yendani m’chikondicho,
Cha Mulungu ndi cha mnansi;
Chiri chanu muzonse.
Nkana chidziŵitso chonse,
Lirime ndi ulosi,
Ngati chikondi chisoŵa,
Tikanakhala chabe.
2. Ngakhale talalikira
Ndiponso kupilira;
Tidzapindula motani.
Tikasoŵa chiyero?
Chikondicho nchachifundo,
Sichichita choipa,
Chikondi sichidzikuza,
Sichimachita nsanje.
3. Chikondi sichipsa mtima,
Sichikonda choipa.
Chimapilira molimba,
Chimakonda zabwino.
Chikondi chipitiriza
Potumikira M’lungu;
Chotero njira yoposa
Ndinjira ya chikondi.