Nyimbo 51
Kukondweretsa Mtima wa Yehova
1. Mulungu, ife tasankha;
Kuchita chifuno chanu.
Tidzakhala ndi mbalitu
Yokondweretsa mtimanu.
2. Tisabwevuke kwa inu;
Woyesayo ndiwabodza.
Masiku onse tikondwe
Ndi malamulo anuwo.
3. Kapolo wanu wanzeru,
Athandiza ife tonse,
Atidyetsa m’nthaŵi yake,
Tichite chifuno chanu.
4. Mutipatse mzimu wanu,
Tikhale odalirika
Kubweretsa chitamando,
Kukondweretsa mtimanu.