Nyimbo 69
Kudzipatulira Kwaumulungu ndi Chikhutiro
1. Kuti tidalitsidwe,
Tikhale okhutira,
Timveretu Mawu a Ya
Ndi umulungu wathu.
Kupembedza ndi kwa phindu,
Kupeŵetsadi machimo.
Tsiku n’tsiku M’njira ya Ya,
Kumachititsa changu.
2. Kukhutira n’za M’lungu,
Tipanga chosankhachi:
M’gwadireni, Dziŵitsani,
Wonani Ufumuwo.
Tilandira chiitano
Tiyende m’chipulumutso.
Mwachimwemwe Tiganiza
Kulipsira kwa M’lungu.
3. Tithokoza Mulungu,
Ngakhale tidedwatu,
Adalitsa Mapembedzo
Munthaŵi zovutazi.
Tisamalire cho’nadi,
Tichotsetu mantha onse.
Tikhaletu Okhutira
Ndi kudziŵa Chikristu.