Nyimbo 97
Mikhalidwe ya Yehova
1. M’lungu wokuzika mumphamvu,
Kasupe wa kuunika,
Chilengedwe chimanena;
Zambiri pa Armagedo.
2. Zimene mwapanga nzanzeru!
Ziti mwazipanga bwino.
Mawu anu timawona
Nzeru yanu yoŵalayo.
3. Mpando wanu ndiwolungama.
Mwadziŵitsa chilungamo.
Mutipatse khutu lomva,
Kuti tiwopetu inu.
4. Tinyadira m’chikondi chanu;
Tiri nachotu mangaŵa.
Tidzabukitsa mokondwa,
Mikhalidwe ya inuyo!