Nyimbo 118
Kuchirikiza Nyumba ya Mulungu
1. A m’nyumba ya M’lungu tisonyeze
Kusanyalanyaza malo ake,
Za nyumba yolingaliridwayo
Kuti dzina lake lidzakhale.
Monga Nehemiya mosamala
Anabwezeretsa kulambira
Nafenso titero ndi ‘chachikhumi,’
Motero tisonyeza kumukonda.
(Korasi)
2. Banja la M’lungu ndi laumodzi,
Nyumba imene asamalira.
Kapolo wake amtumikira,
Chotero achititsa mtendere.
Tidze kwa M’lungu ndi ‘chuma’ chathu;
Zopereka zidzetsa ulemu.
Adalitsa bwino abanja lake,
Motero timtumikire mokondwa.
(KORASI)
Tichirikize nyumbayo.
‘Idzani mulambiremo.’
Nyumba yake ndiyo banja;
Adzakhalamotu kosatha.