Nyimbo 139
Athandizeni Kukhala Olimba
Kuphunzitsa nkhosa za M’lungu
Ndi mwayi wapadera.
Yehova wawatsogolera.
Amakonda cho’nadi.
(KOLASI)
Yehovatu tikupempha
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
Mayesero akawagwera,
Timawapempherera.
Tayesetsa kuwaphunzitsa,
Ndipo adalitsidwa.
(KOLASI)
Yehovatu tikupempha
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
Akhale okudalirani,
Inu M’lungu ndi Yesu
Apirire pamayesero,
Akalandire moyo.
(KOLASI)
Yehovatu tikupempha
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
(Onaninso Luka 6:48; Mac. 5:42; Afil. 4:1.)