Nyimbo 119
Kugwiritsitsa “Chiyembekezo Chachimwemwe”
(Tito 2:13, NW)
1. Anthu afufuza mumdima kwazaka.
Izi nzachabe zosautsa mtima.
Kuipa tsopano kwachulukadi;
Mapeto omvetsa chisoni.
(Korasi)
2. Tikondwa kudziŵa chifukwa chimene
Mulungu walolera kuipako.
Kudzathetsedwa ndi Kristu Yesuyo.
Ambali yake adzaimba.
(Korasi)
3. Mutsiku lathu chilengezo chimveka.
Anthu sadzafunikira kuwopa.
‘M’lungu adzamasula chilengedwe.’
Tonse tiyang’ane mtsogolo.
(KORASi)
Kondwerani, Ufumuwo wadza.
Mwana wake azadzetsa ufulu.
Masoka a anthu adzachoka.
Tigwiritsitse chiyembekezochi.