Nyimbo 157
Lambirani Yehova mu Unyamata
1. Mkamwa mwa ana munatuluka
Mawu akutamandadi Yesu.
Inde, ana atamanda M’lungu,
Mogwirizana ndi akuluwo.
2. Makolo okonda chowonadi,
Aphunzitsa ana kuwopa Ya.
Oima kumbali ya Mulungu.
Ananu, mverani akondwere.
3. Anyamata, khalani oyera;
Phunzirani kudalira M’lungu.
Peŵani mayanjano oipa,
Aipitsa mkhalidwe wabwino.
4. Ngati ukumbuka M’lungu wako,
Kumtumikira muchowonadi,
Utakula udzasangalala,
Ndi kukondweretsa mtima wa Ya.